Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 14

Ufumu Umene Udzalamulila Dziko Lonse

Ufumu Umene Udzalamulila Dziko Lonse

Kodi ungaudziŵe Ufumu umene tikunenapo?— Inde, ndi Ufumu wa Mulungu, ndipo Ufumu umenewu udzapanga dziko lonse kukhala paladaiso. Kodi ungakonde kuphunzila zambili za Ufumu umenewu?—

Ufumu uliwonse umakhala ndi mfumu. Ndipo mfumu imalamulila anthu a m’dziko lake. Kodi udziŵa amene adzalamulila mu Ufumu wa Mulungu?— Ndi Yesu Kristu. Iye akhala kumwamba. Posacedwapa, iye adzakhala Mfumu ndipo adzalamulila aliyense padziko lonse lapansi. Kodi uganiza kuti tidzasangalala Yesu akayamba kulamulila monga Mfumu padziko lonse lapansi?—

Kodi ungakonde kuti ukacite ciani m’Paladaiso?

Tidzasangalala kwambili. Mu Paladaiso, anthu sadzakangana kapena kucita nkhondo. Anthu onse adzakondana. Sikudzakhala kudwala kapena kufa. Anthu akhungu adzaona, ogontha adzamva, ndipo amene sayenda adzathamanga ndi kulumpha-lumpha. Onse adzakhala ndi zakudya zokwanila. Nyama zidzakhala paubwenzi ndi nyama zina ndiponso ndi anthu. Anthu amene anafa adzauka. Amuna ndi akazi ambili amene waphunzila m’kabuku kano monga Rabeka, Rahabi, Davide ndi Eliya naonso adzauka kuti akhale ndi moyo. Akadzauka, kodi ungakonde kuti ukaonane nao?—

Yehova amakukonda ndipo afuna kuti uzisangalala. Ngati upitilizabe kuphunzila za Yehova ndi kumumvela, udzakhala ndi moyo kosatha m’paladaiso wokongola. Kodi izi ndiye zimene ufuna?—

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

  • Yesaya 2:4; 11:6-9; 25:8; 33:24; 35:5, 6

  • Yohane 5:28, 29; 17:3