Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 1

“Ufumu Wanu Ubwere”

“Ufumu Wanu Ubwere”

CHOLINGA CHA MUTUWU

Kumvetsa zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu

1, 2. Kodi atumwi atatu a Yesu anamva Yehova akulankhula mawu oti chiyani, ndipo anatani atamva zimenezi?

 KODI Yehova Mulungu atakuuzani kuti muchite zinazake mungatani? Mosakayikira mukhoza kuchita zimene wakuuzanizo ngakhale zitakhala zovuta bwanji.

2 Chikondwerero cha Pasika wa mu 32 C.E. chitachitika, atumwi atatu a Yesu omwe mayina awo ndi Petulo, Yakobo ndi Yohane, anauzidwa kuti achite zinazake. (Werengani Mateyu 17:1-5.) Atumwiwa atakwera “m’phiri lalitali” ndi Mbuye wawo, anaona masomphenya osonyeza Yesu atakhala Mfumu yaulemelero kumwamba. Masomphenyawo ankaoneka ngati zinthuzo zikuchitikadi moti Petulo ankafuna kuchitapo kanthu. Petulo atayamba kulankhula kumwamba kunapanga mtambo. Kenako Petulo ndi atumwi anzakewo anakhala ndi mwayi womwe ndi anthu ochepa okha anakhalako nawo. Iwo anamva Yehova akulankhula. Yehova atanena mawu otsimikizira kuti Yesu ndi Mwana wake, ananenanso kuti: “Muzimumvera.” Atumwiwo anatsatiradi zimene Yehova anawauzazo. Anamvera zimene Yesu anaphunzitsa ndipo analimbikitsa ena kuti nawonso azimvera Yesu.​—Mac. 3:19-23; 4:18-20.

Yesu ankafotokoza kwambiri za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse

3. N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizimvera Mwana wake, nanga ndi nkhani iti imene tikufunikira kuimvetsa?

3 Mawu akuti “muzimumvera,” analembedwa m’Baibulo kuti nafenso tiziwatsatira. (Aroma 15:4) N’chifukwa chiyani tikufunika kumumvera? Chifukwa chakuti Yesu amalankhula m’malo mwa Yehova ndipo zinthu zonse zimene Yesu ankaphunzitsa n’zimene Atate wake ankafuna kuti tizidziwe. (Yoh. 1:1, 14) Yesu anaphunzitsa nkhani yokhudza Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse. Ufumuwu ndi boma lakumwamba lolamuliridwa ndi Mesiya ndi anthu okwana 144,000. Popeza Yesu ankaphunzitsa kwambiri za Ufumuwu, tingachite bwino kuyesetsa kuti tiumvetse. (Chiv. 5:9, 10; 14:1-3; 20:6) Koma poyamba, tiyeni tione kuti n’chifukwa chiyani Yesu ananena zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu.

“Zosefukira Mumtima”

4. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti kuchokera pansi pa mtima wake ankaganizira kwambiri za Ufumu?

4 Yesu ankaganizira kwambiri za Ufumuwu. Tikutero chifukwa chakuti zimene munthu amalankhula zimasonyeza zimene zili mumtima mwake. Pajatu Yesu ananena kuti: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.” (Mat. 12:34) Nthawi zonse Yesu ankakonda kulankhula za Ufumu. M’mabuku a Uthenga Wabwino amafotokoza za Ufumu maulendo oposa 100 ndipo ambiri mwa mawu amenewa ananenedwa ndi Yesu. Ufumuwo unali mfundo yaikulu ya zimene ankalalikira n’chifukwa chake ananena kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Yesu ataukitsidwa, anapitirizabe kulankhula za Ufumu kwa ophunzira ake. (Mac. 1:3) Izi zikusonyeza kuti kuchokera pansi pa mtima wake, Yesu ankaona Ufumuwo kukhala wofunika kwambiri, n’chifukwa chake ankakonda kulankhula za Ufumuwo.

5-7. (a) Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amaganiziranso kwambiri za Ufumu kuchokera pansi pa mtima? Perekani chitsanzo. (b) Kodi ifeyo tingasonyeze bwanji kuti timaganizira za Ufumuwo kuchokera pansi pa mtima?

5 Yehova amaganiziranso kwambiri za Ufumuwo. Paja Yehova ndi amene anatuma Mwana wake wobadwa yekha kubwera padziko lapansi ndipo chilichonse chimene Mwanayo ankalankhula kapena kuphunzitsa chinachokera kwa Yehovayo. (Yoh. 7:16; 12:49, 50) Komanso nkhani zonena za moyo wa Yesu ndiponso utumiki wake, zomwe zinalembedwa m’mabuku anayi a Uthenga Wabwino, zinachokera kwa Yehova. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimaganizira za Ufumu wa Mulungu kuchokera pansi pa mtima?’

6 Tayerekezani kuti mukusankha zithunzi zoti muike mu abamu ya banja lanu. Muli ndi zithunzi zambiri moti sizingatheke kuika zonse mu abamuyo. Kodi mungatani? Mukhoza kusankha zithunzi zabwino zokhazokha. Mabuku a Uthenga Wabwino ali ngati abamu imene imatithandiza kumudziwa bwino Yesu. Yehova sanauze olemba mabuku a Uthenga Wabwino kuti alembe zonse zimene Yesu ananena komanso kuchita ali padziko lapansi. (Yoh. 20:30; 21:25) M’malomwake, mzimu wa Yehova unawathandiza kuti alembe zinthu zokhazo zimene zingatithandize kumvetsa cholinga cha utumiki wa Yesu komanso kumvetsa zinthu zofunika kwambiri kwa Yehova. (2 Tim. 3:16, 17; 2 Pet. 1:21) Chifukwa chakuti mabuku a Uthenga Wabwino amafotokoza zinthu zambiri zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu, ndiye kuti Yehova amaganiziranso kwambiri za Ufumuwo kuchokera pansi pa mtima. Komanso kufotokozedwa kwa Ufumu wa Mulungu m’mabuku a Uthenga wabwino ndi umboni wakuti Yehova akufuna kuti ifeyo tidziwe zambiri zokhudza Ufumuwo.

7 Ndiyetu tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimaganizira za Ufumu wa Mulungu kuchokera pansi pa mtima?’ Ngati timatero tidzakhala ofunitsitsa kumvera zimene Yesu ananena ndiponso zimene anaphunzitsa zokhudza Ufumuwu. Tidzaonanso kufunika kwa Ufumuwu, mmene udzabwerere komanso nthawi imene udzabwere.

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzabwera Bwanji?

8. Kodi Yesu anafotokoza bwanji mwachidule kufunika kwa Ufumu?

8 Ganizirani pemphero la chitsanzo. Yesu anafotokoza kufunika kwa Ufumu pogwiritsa ntchito mawu osavuta kumva. M’pempheroli anafotokoza zimene Ufumuwu udzachite ndipo lili ndi mfundo 7. Mfundo zitatu zoyambirira zimakhudza zolinga za Yehova zomwe ndi kuyeretsa dzina lake, kubwera kwa Ufumu wake komanso kukwaniritsidwa kwa chifuniro chake padziko lapansi monga mmene zilili kumwamba. (Werengani Mateyu 6:9, 10.) Mfundo zitatuzi n’zogwirizana chifukwa Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wolamuliridwa ndi Mesiya kuti ayeretse dzina lake komanso kukwaniritsa chifuniro chake.

9, 10. (a) Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani ukadzabwera? (b) Kodi inuyo mukufunitsitsa kuona lonjezo lopezeka m’Baibulo liti litakwaniritsidwa?

9 Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani ukadzabwera? Tikamapemphera kuti, “Ufumu wanu ubwere,” timakhala tikupempha kuti Ufumuwo uyambe kugwira ntchito. Ufumuwo ukadzabwera udzachotsa anthu onse oipa kuphatikizapo maboma onse a anthu ndipo udzabweretsa dziko latsopano lachilungamo. (Dan. 2:44; 2 Pet. 3:13) Ndiyeno Ufumuwo udzasintha dziko lonse lapansi kuti likhale paradaiso. (Luka 23:43) Anthu amene anamwalira, omwe Mulungu akuwakumbukira, adzaukitsidwa n’kukhalanso ndi abale awo. (Yoh. 5:28, 29) Anthu omvera adzakhalanso angwiro ndipo adzasangalala ndi moyo mpaka kalekale. (Chiv. 21:3-5) Pamapeto pake, chifuniro cha Yehova Mulungu chidzachitika padziko lonse lapansi ngati mmene kulili kumwamba. Kodi simukufunitsitsa kudzaona malonjezo opezeka m’Baibulowa akukwaniritsidwa? Ndiyeno nthawi iliyonse imene mukupemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere, mumakhala mukupempha kuti malonjezo amenewa akwaniritsidwe.

10 N’zoonekeratu kuti Ufumu wa Mulungu ‘sunabwerebe’ kuti udzachite zimene timanena m’pemphero la chitsanzo chifukwa padakali pano maboma a anthu akulamulirabe ndipo sitili m’dziko latsopano. Koma chosangalatsa n’chakuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa. Mutu wotsatira ufotokoza zambiri za nkhani imeneyi. Koma tsopano tiyeni tikambirane zimene Yesu ananena zokhudza nthawi imene Ufumuwo udzakhazikitsidwe komanso nthawi imene udzabwere.

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzakhazikitsidwa Liti?

11. Kodi Yesu anasonyeza chiyani zokhudza kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu?

11 Yesu anasonyeza kuti Ufumuwo sukhazikitsidwa nthawi imene iyeyo anali padziko lapansi ngati mmene ophunzira ake ena ankaganizira. (Mac. 1:6) Kuti timvetse zimenezi tiyeni tikambirane mafanizo awiri amene Yesu ananena. Fanizo lachiwiri analinena pasanadutse zaka ziwiri kuchokera pamene ananena fanizo loyambali.

12. Kodi fanizo la tirigu ndi namsongole likusonyeza bwanji kuti Ufumu sunakhazikitsidwe m’nthawi ya atumwi?

12 Fanizo la tirigu ndi namsongole. (Werengani Mateyu 13:24-30.) Yesu ayenera kuti ananena fanizo limeneli chakumayambiriro kwa chaka cha 31 C.E., ndipo kenako anafotokoza tanthauzo lake kwa ophunzira ake. (Mat. 13:36-43) Mfundo yaikulu ya fanizoli inali yakuti: Pambuyo poti atumwi amwalira, Mdyerekezi adzafesa namsongole (Akhristu onyenga) pakati pa tirigu (“ana a ufumu” kapena kuti Akhristu odzozedwa). Tirigu ndi namsongole zinasiyidwa kuti zikulire limodzi mpaka nthawi yokolola yomwe ndi “mapeto a nthawi ino.” Chakumayambiriro kwa nthawi yokolola, namsongole adzazulidwa. Kenako, tirigu adzasonkhanitsidwa. Choncho fanizoli likusonyeza kuti Ufumu udzakhazikitsidwa pambuyo poti tirigu ndi namsongole zakula, osati m’nthawi ya atumwi. Ndiye monga tikudziwira, nthawi imeneyi inatha ndipo nthawi yokolola inayamba mu 1914.

13. Kodi Yesu anafotokoza fanizo lotani pofuna kusonyeza kuti sadzaikidwa kukhala Mfumu akadzangobwerera kumwamba?

13 Fanizo la ndalama za mina. (Werengani Luka 19:11-13.) Yesu ananena fanizo limeneli m’chaka cha 33 C.E. ali pa ulendo wake womaliza wopita ku Yerusalemu. Ena mwa anthu amene ankamumvetsera ankaganiza kuti akakhazikitsa Ufumu akakafika ku Yerusalemu. Pofuna kuthandiza anthu amene anali ndi maganizo olakwikawa kudziwa kuti Ufumuwo unali kudzakhazikitsidwa m’tsogolo, Yesu anadziyerekezera ndi “munthu wina wa m’banja lachifumu” amene “anapita kudziko lakutali kuti akalandire ufumu.” a M’fanizoli, “dziko lakutali” likuimira kumwamba komwe Yesu anapita kukalandira Ufumu kwa Atate wake. Koma Yesu ankadziwa kuti akadzapita kumwamba sakakhala Mfumu nthawi yomweyo. Anayenera kukhala kudzanja lamanja la Mulungu kuyembekezera nthawi yake. Ndipo anayembekezera kwa zaka zambiri.​—Sal. 110:1, 2; Mat. 22:43, 44; Aheb. 10:12, 13.

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzabwera Liti?

14. (a) Kodi Yesu anayankha bwanji funso limene ophunzira ake anamufunsa? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu kumatithandiza kudziwa chiyani za kukhalapo kwake komanso za Ufumu?

14 Kutatsala masiku ochepa kuti Yesu aphedwe, atumwi ake anayi anamufunsa kuti: “[Kodi] chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mat. 24:3; Maliko 13:4) Poyankha, Yesu anafotokoza ulosi umene uli m’chaputala 24 ndi 25 cha buku la Mateyu. Mu ulosi umenewu Yesu anafotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene zidzachitike padziko lapansi zomwe ndi chizindikiro cha nthawi ya “kukhalapo” kwake. Chiyambi cha kukhalapo kwake chinali kudzachitika pa nthawi yofanana ndi kukhazikitsidwa kwa Ufumu ndipo mapeto a kukhalapo kwake anali kudzachitika pa nthawi yofanana ndi kubwera kwa Ufumuwo. Tili ndi umboni wosonyeza kuti ulosi wa Yesuwu unayamba kukwaniritsidwa m’chaka cha 1914. b N’chifukwa chake chaka chimenechi chimadziwika kuti ndi chaka chimene Ufumuwo unakhazikitsidwa komanso chiyambi cha kukhalapo kwake.

15, 16. Kodi mawu akuti “m’badwo uwu” amanena za ndani?

15 Ndiyeno kodi Ufumu wa Mulungu udzabwera liti? Yesu sanatchule nthawi yeniyeni imene Ufumuwo udzabwere. (Mat. 24:36) Koma ananena zinazake zimene zikutitsimikizira kuti Ufumuwu uli pafupi kwambiri. Yesu ananena kuti Ufumu udzabwera pambuyo poti “m’badwo uwu” waona kukwaniritsidwa kwa chizindikiro cha ulosi. (Werengani Mateyu 24:32-34.) Kodi mawu akuti “m’badwo uwu” amanena za ndani? Tiyeni tione zimene Yesu ankatanthauza ponena mawu amenewa.

16 “M’badwo uwu.” Kodi Yesu ankanena za anthu omwe sanali Akhristu? Ayi. Kumbukirani kuti Yesu ankafotokoza ulosi umenewu kwa atumwi ake ochepa amene “anafika kwa iye mwamseri.” (Mat. 24:3) Pa nthawiyi n’kuti atumwiwo atatsala pang’ono kudzozedwa ndi mzimu woyera. Kumbukiraninso nkhani imene ankakambirana pa nthawiyi. Asanafotokoze za “m’badwo uwu,” Yesu ananena kuti: “Tsopano phunzirani mfundo imeneyi pa fanizo ili la mkuyu: Nthambi yake yanthete ikaphuka ndi kuchita masamba, mumadziwa kuti dzinja lili pafupi. Inunso chimodzimodzi, mukadzaona zinthu zonsezi, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni.” Otsatira a Yesu odzozedwa ndi mzimu, osati anthu omwe si Akhristu, ndi amene adzaone zimene iye analoserazi komanso kuzindikira kuti Yesu “ali pakhomo penipeni.” Choncho, pamene Yesu ananena za “m’badwo uwu” ankanena za otsatira ake odzozedwa.

17. Kodi mawu akuti “m’badwo” komanso akuti “zinthu zonsezi” amatanthauza chiyani?

17 “Sudzatha wonse kuchoka kufikira zinthu zonsezi zitachitika.” Kodi zimenezi zidzachitika motani? Kuti tiyankhe funso limeneli, tikufunika kudziwa zinthu ziwiri: Tanthauzo la mawu akuti “m’badwo” ndi mawu akuti “zinthu zonsezi.” Mawu akuti “m’badwo” amanena za anthu a misinkhu yosiyanasiyana amene akhala limodzi ndi moyo pa nthawi inayake. M’badwo umakhala ndi pothera ndipo sutenga nthawi yaitali. (Eks. 1:6) Mawu akuti “zinthu zonsezi” amaphatikizapo zochitika zonse zimene Yesu ananena kuti zidzachitika pa nthawi ya kukhalapo kwake, yomwe inayamba m’chaka cha 1914, ndipo idzatha pa nthawi ya “chisautso chachikulu.”​—Mat. 24:21.

18, 19. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti “m’badwo uwu,” ndipo ife tikuphunzirapo chiyani?

18 Ndiye kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti “m’badwo uwu”? M’badwo umenewu wapangidwa ndi magulu awiri a Akhristu odzozedwa omwe anakhalapo ndi moyo nthawi yofanana. Gulu loyamba ndi la Akhristu odzozedwa amene anaona chiyambi cha kukwaniritsidwa kwa chizindikiro mu 1914, ndipo gulu lachiwiri ndi la Akhristu omwe anadzozedwa gulu loyambalo lidakalipo. Anthu ena a m’gulu lachiwirili adzakhalabe ndi moyo pa nthawi imene chisautso chachikulu chizidzayamba. Magulu awiriwa akupanga m’badwo umodzi, chifukwa anakhala ndi moyo limodzi kwa kanthawi onse atadzozedwa kale. c

19 Kodi mfundo imeneyi ikutiphunzitsa chiyani? Zimene zikuchitika masiku ano padziko lonse zikutitsimikizira kuti Yesu ndi Mfumu. Tikudziwanso kuti Akhristu odzozedwa omwe ali m’gulu la “m’badwo uwu” akukalamba koma sadzamwalira onse chisautso chachikulu chisanayambe. Choncho, tikhoza kunena kuti Ufumu wa Mulungu ubwera posachedwapa n’kuyamba kulamulira dziko lonse lapansi. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kuona kukwaniritsidwa kwa zimene Yesu anatiphunzitsa kuti: “Ufumu wanu ubwere.”

20. Kodi ndi mfundo yaikulu iti imene tikambirane m’bukuli, nanga m’mutu wotsatira tikambirana chiyani?

20 Nthawi zonse tizikumbukira zimene Yehova mwiniwake ananena zokhudza Mwana wake. Iye anati: “Muzimumvera.” Monga Akhristu oona, ndife ofunitsitsa kutsatira malangizo a Mulungu amenewa. Timafunitsitsa kudziwa zinthu zonse zimene Yesu ananena komanso kuphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu. Zimene Ufumuwu wachita kale komanso zimene udzachite m’tsogolo ndi mfundo yaikulu imene tikambirane m’bukuli. Mutu wotsatira ufotokoza zinthu zochititsa chidwi zonena za kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu kumwamba.

a Anthu amene ankamvetsera fanizo la Yesu ayenera kuti atamva fanizoli anaganizira za Arikelao, yemwe anali mwana wa Herode Wamkulu. Herode asanafe anasankha mwana wake Arikelao kuti ndi amene adzalowe m’malo mwake ndipo adzalamulira ku Yudeya ndi madera ena. Koma Arikelao asanayambe kulamulira, anafunika kuyenda ulendo wautali kupita ku Roma kuti akapemphe chilolezo kwa Kaisara Augusto.

c Mkhristu aliyense amene anadzozedwa pambuyo pa imfa ya wodzozedwa womaliza wa m’gulu loyamba, lomwe mu 1914 linaona “chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka,” sali m’gulu la “m’badwo uwu.”​—Mat. 24:8.