Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 3

Yehova Anaulula Colinga Cake

Yehova Anaulula Colinga Cake

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Yehova amathandiza anthu amene amamuopa kumvetsetsa colinga cake pang’onopang’ono

1, 2. Kodi Yehova waulula bwanji colinga cake ponena za anthu?

MAKOLO acikondi amakambilana ndi ana ao nkhani zokhudza banja lao. Koma io amasamala kuti asauze ana zinthu zonse pa nthawi imodzi. Amauza anao zinthu zokhazo zimene akuona kuti angakwanitse kumva malinga ndi msinkhu wao.

2 Mofanana ndi zimenezi, Yehova wakhala akuulula pang’onopang’ono colinga cake kwa anthu. Koma iye wakhala akucita zimenezi panthawi yoyenela. Tsopano tiyeni tikambilane mwacidule mmene Yehova waululila coonadi cokhudza Ufumu kucokela paciyambi.

N’cifukwa Ciani Tifunikila Ufumu?

3, 4. Kodi Yehova anakonzelatu kuti anthu adzacimwe? Fotokozani.

3 Paciyambi, Ufumu wa Mesiya sunali mbali ya colinga ca Yehova. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti Yehova sanakonzeletu kuti anthu adzacimwe. Iye analenga anthu ndi ufulu wodzisankhila zocita. Ndipo iye anauza Adamu ndi Hava za colinga cake kwa anthu. Mulungu anati: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi.” (Gen. 1:28) Yehova anawauzanso kuti azilemekeza miyezo yake ya cabwino ndi coipa. (Gen. 2:16, 17) Adamu ndi Hava anali ndi ufulu wosankha kumvela Mulungu. Iwo ndi ana ao akanamvela Mulungu, sipakanafunika Ufumu wa Kristu kuti udzakwanilitse colinga ca Mulungu. Dziko lonse lapansi likanadzazidwa ndi anthu angwilo olambila Yehova.

4 Kupanduka kwa Satana, Adamu ndi Hava sikunapangitse Yehova kusintha colinga cake cakuti padziko lonse lapansi pakhale anthu angwilo. M’malomwake, Yehova anangosintha njila yokwanilitsila colinga cakeco. Colinga ca Mulungu sicili ngati sitima. Iyo imayenda pa njanji pokha, ndipo anthu ena akaononga njanjiyo sitima imalephela kufika kumene ikupita. Yehova akanena colinga cake, palibe cinthu ciliconse cimene cingalepheletse colingaco. (Ŵelengani Yesaya 55:11.) Ngati pali zopinga zina, Yehova amagwilitsila nchito njila ina yatsopano kuti akwanilitse colinga cake. * (Eks. 3:14, 15) Pakakhala pofunika, Iye amauza atumiki ake okhulupilika za njila yatsopanoyo imene adzagwilitsila nchito kuti akwanilitse colinga cakeco.

5. N’ciani cimene Yehova anacita pambuyo pa kupanduka kwa mu Edeni?

5 Cifukwa ca kupanduka kwa mu Edeni, Yehova anakonza zokhazikitsa Ufumu. (Mat. 25:34) Pamene anthu analibe ciyembekezo, Yehova anaulula njila imene adzagwilitsila nchito kuti athandize anthu kukhalanso angwilo ndi kuthetsa mavuto onse amene anayamba cifukwa ca ulamulilo woipa wa Satana. (Gen. 3:14-19) Koma Yehova sanaulule zonse zokhudza Ufumu pa nthawi imodzi.

Yehova Anayamba Kuvumbula Coonadi Cokhudza Ufumu

6. N’ciani cimene Yehova analonjeza? Nanga sanaulule ciani?

6 Mu ulosi woyambilila, Yehova analonjeza kuti “mbeu” idzaphwanya mutu wa njoka. (Ŵelengani Genesis 3:15.) Komabe, panthawiyo Mulungu sanaulule amene adzakhala mbeu imeneyo ndi amene adzakhala mbeu ya njoka. Ndipo panatenga zaka pafupifupi 2,000 kuti Yehova afotokoze zambili pankhaniyi. *

7. N’cifukwa ciani Mulungu anasankha Abulahamu? Nanga tikuphunzilapo mfundo yofunika iti pamenepa?

7 Pambuyo pake, Yehova anauza Abulahamu kuti mbeu imene analonjeza idzakhala mbadwa yake. Mulungu anasankha Abulahamu cifukwa cakuti iye ‘anamvela mau [a Yehova.’] (Gen. 22:18) Pamenepa tikuphunzilapo mfundo yofunika kwambili yakuti Yehova amaulula colinga cake kwa anthu okhawo amene amamuopa.—Ŵelengani Salimo 25:14.

8, 9. Ndi mfundo ziti zokhudza mbeu yolonjezedwa zimene Yehova anaulula kwa Abulahamu ndi Yakobo?

8 Pamene Yehova anali kulankhula ndi bwenzi lake Abulahamu kudzela mwa mngelo, Iye anaulula mfundo ina yofunika kwambili yokhudza mbeu yolonjezedwa. Mfundo yake inali yakuti mbeu imeneyo idzakhala munthu. (Gen. 22:15-17; Yak. 2:23) Koma kodi munthu ameneyo angaphwanye bwanji mutu wa njoka? Nanga njokayo ndani? M’kupita kwa nthawi, Mulungu anaulula mayankho a mafunso amenewa.

9 Yehova anakonza zakuti mbeu yolonjezedwayo idzacokele mwa mdzukulu wa Abulahamu, Yakobo, amene anali kukhulupilila kwambili Mulungu. (Gen. 28:13-22) Kudzela mwa Yakobo, Yehova anaulula kuti Wolonjezedwayo adzakhala mbadwa ya Yuda, mwana wa Yakobo. Yakobo ananenelatu kuti mbadwa ya Yuda imeneyo idzapatsidwa “ndodo yacifumu,” imene ndi cizindikilo ca ulamulilo wa mfumu, ndi kuti “mitundu ya anthu idzamumvela.” (Gen. 49:1, 10) Kudzela mwa mau a Yakobo amenewa, Yehova anasonyeza kuti Wolonjezedwayo adzakhala mfumu.

10, 11. N’cifukwa ciani Yehova anaulula colinga cake kwa Davide ndi Danieli?

10 Patapita zaka pafupi-fupi 650 kucokela nthawi ya Yuda, Yehova anaulula zinthu zina zokhudza colinga cake kwa Mfumu Davide, amene anali mbadwa ya Yuda. Yehova ananena kuti Davide anali “munthu wapamtima pake.” (1 Sam. 13:14; 17:12; Mac. 13:22) Cifukwa cakuti Davide anali kuopa Mulungu, Yehova anacita naye pangano lakuti imodzi mwa mbadwa zake idzalamulila kosatha.—2 Sam. 7:8, 12-16.

11 Pambuyo pa zaka 500, Yehova kudzela mwa Danieli anaulula caka ceniceni cimene Wodzozedwa ameneyu, kapena kuti Mesiya, adzaonekela padziko lapansi. (Dan. 9:25) Yehova anali kuona kuti Danieli anali “munthu wokondedwa kwambili.” (Dan. 6:16; 9:22, 23) Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Danieli anali kulemekeza kwambili Yehova ndi kumutumikila nthawi zonse.—Dan. 6:16; 9:22, 23.

12. Kodi Mulungu anauza Danieli kuti acite ciani? Nanga n’cifukwa ciani anamuuza kucita zimenezo?

12 Yehova anagwilitsila nchito aneneli okhulupilika monga Danieli kulemba zinthu zambili zokhudza mbeu yolonjezedwa kapena kuti Mesiya. Komabe, nthawi inali isanakwane yakuti Yehova athandize atumiki ake kumvetsetsa zimene iye anawauza kulemba. Mwacitsanzo, Danieli ataona masomphenya a kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu, Mulungu anamuuza kuti atseke ndi kumata ulosiwo mpaka mtsogolo pa nthawi yoikika ya Yehova. Mulungu ananena kuti panthawiyo, anthu “adzadziŵa zinthu zambili zoona.”—Dan. 12:4.

Yehova anagwilitsila nchito anthu okhulupilika monga Danieli kuti alembe mfundo zofunika zokhudza Ufumu wa Mesiya

Yesu Anafotokoza Colinga ca Mulungu

13. (a) Ndani anali mbeu yolonjezedwa? (b) Kodi Yesu anamveketsa bwanji ulosi wolembedwa pa Genesis 3:15?

13 Yehova anasonyezelatu kuti Yesu ndiye mbeu yolonjezedwa, mbadwa ya Davide imene idzalamulila monga Mfumu. (Luka 1:30-33; 3:21, 22) Pamene Yesu anayamba utumiki wake, zinali ngati kuti dzuŵa latuluka ndi kuunikila anthu kuti adziŵe colinga ca Mulungu. (Mat. 4:13-17) Mwacitsanzo, Yesu anaunikila anthu kuti “njoka” yochulidwa pa Genesis 3:14, 15 ndi Mdyelekezi, “wopha anthu,” ndi “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44) M’masomphenya amene Yesu anaonetsa Yohane, Iye anafotokoza kuti “njoka yakale ija” ndi “iye wochedwa Mdyelekezi ndi Satana.” * (Ŵelengani Chivumbulutso 1:1; 12:9.) M’masomphenya omwewo, Yesu anasonyeza kuti iye monga mbeu yolonjezedwa adzakwanilitsa ulosi umene unapelekedwa mu Edeni mwa kuononga Satana.—Chiv. 20:7-10.

14-16. Kodi ophunzila a Yesu m’nthawi ya atumwi anali kumvetsetsa mfundo zonse za coonadi zimene iye anali kuwaphunzitsa? Fotokozani.

14 Monga mmene tinaonela kuciyambi kwa Nkhani 1 ya buku lino, Yesu anali kukamba kwambili zokhudza Ufumu wa Mulungu. Koma iye sanafotokozele ophunzila ake zonse zimene io anafuna kudziŵa. Ngakhale kuti Yesu anali kufotokozela otsatila ake mfundo za coonadi mwatsatanetsatane, io sanali kumvetsetsa mfundo zimene iye anali kuwaphunzitsa mpaka patapita nthawi kapena zaka zambili. Ganizilani zitsanzo izi.

15 Mu 33 C.E., Yesu anamveketsa bwino mfundo yakuti olamulila anzake a Mfumu ya Ufumu wa Mulungu adzatengedwa padziko lapansi ndi kuukitsidwa kuti akakhale ndi moyo wauzimu kumwamba. Koma ophunzila ake sanamvetsetse mfundo imeneyi panthawiyo. (Dan. 7:18; Yoh. 14:2-5) M’caka cimeneco, Yesu anakambanso mafanizo oonetsa kuti padzatenga nthawi yaitali kuti Ufumu wa Mulungu ukhazikitsidwe pambuyo pakuti iye wapita kumwamba. (Mat. 25:14, 19; Luka 19:11, 12) Ophunzilawo sanamvetsetse mfundo yofunika imeneyi, ndipo pambuyo pake Yesu ataukitsidwa, io anam’funsa kuti: “Kodi mubwezeletsa Ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?” Panthawiyo, Yesu sanafune kuwauza zambili. (Mac. 1:6, 7) Yesu anakambanso kuti padzakhala “nkhosa zina,” zimene sizili mbali ya “kagulu ka nkhosa” ka anthu amene adzalamulila naye mu Ufumu. (Yoh. 10:16; Luka 12:32) Otsatila a Kristu sanali kudziŵa bwino kuti magulu aŵili amenewa amaimila ndani mpaka pamene Ufumu unakhazikitsidwa mu 1914.

16 Pamene anali padziko lapansi, Yesu anali ndi zinthu zambili zimene akanauza ophunzila ake, koma anadziŵa kuti io sakanakwanitsa kuzimvetsetsa zonse. (Yoh. 16:12) N’zoona kuti panali zinthu zambili zokhudza Ufumu zimene zinaululidwa m’nthawi ya atumwi. Koma nthawi yakuti anthu amvetsetse zimenezo inali isanakwane.

Coonadi Ciculuka ‘m’Nthawi Yamapeto’

17. N’ciani cimene tifunika kucita kuti timvetsetse coonadi cokhudza Ufumu? Nanga n’ciani cina cimene cimafunika?

17 Yehova anauza Danieli kuti ‘m’nthawi yamapeto,’ anthu ambili “adzayenda uku ndi uku ndipo adzadziŵa zinthu zambili zoona” zokhudza colinga ca Mulungu. (Dan. 12:4) Anthu amene akufuna coonadi afunika kucita khama kuti acipeze. Buku lina limanena kuti liu la Ciheberi limene analitembenuza kuti “kuyenda uku ndi uku” limakamba za munthu amene amaphunzila zinthu mosamala kwambili. Komabe, ngakhale titaphunzila Baibulo mosamala kwambili, sitingamvetsetse coonadi cokhudza Ufumu. Tingamvetsetse coonadi cimeneci pokhapo ngati Yehova watithandiza.—Ŵelengani Mateyu 13:11.

18. Kodi anthu oopa Yehova aonetsa bwanji kuti ali ndi cikhulupililo ndi kuti ndi odzicepetsa?

18 Yehova anaulula coonadi cokhudza Ufumu pang’onopang’ono kuyambila kale mpaka m’caka ca 1914. Iye akucita cimodzimodzi masiku ano otsiliza. Monga mmene tidzaonela m’Nkhani 4 ndi 5, pa zaka 100 zapitazi, anthu a Mulungu akhala akusintha kamvedwe kao ka coonadi. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova sakuwathandiza? Kutalitali. Iye amawathandiza. N’cifukwa ciani amatelo? Cifukwa cakuti atumiki a Yehova ali ndi makhalidwe amene iye amakonda. Makhalidwe amenewa ndi cikhulupililo ndi kudzicepetsa. (Aheb. 11:6; Yak. 4:6) Atumiki a Yehova amakhulupilila kuti malonjezo ake onse amene ali m’Baibulo adzakwanilitsidwa. Iwo amasonyeza kudzicepetsa mwa kuvomeleza kuti nthawi zina samvetsetsa bwinobwino mmene malonjezowo adzakwanilitsidwila. Magazini ya Watch Tower ya March 1, 1925 inasonyeza kuti atumiki a Mulungu ndi odzicepetsa. Iyo inati: “Timadziŵa kuti Ambuye ndi amene amamasulila Mau ake, ndi kuti iye adzamasulila Mauwo kwa anthu ake m’njila imene akuona kuti ndi yoyenela ndiponso panthawi yake yoikika.”

“Ambuye . . . adzamasulila Mau ake kwa anthu ake m’njila imene akuona kuti ndi yoyenela ndiponso panthawi yake yoikika”

19. N’ciani cimene Yehova watithandiza kumvetsetsa tsopano? Cifukwa?

19 Pamene Ufumu unakhazikitsidwa mu 1914, anthu a Mulungu sanali kudziŵa bwino mmene maulosi okhudza Ufumuwo adzakwanilitsidwila. (1 Akor. 13:9, 10, 12) Cifukwa cofunitsitsa kuti malonjezo a Mulungu akwanilitsidwe, nthawi zina tinali kulakwitsa kamvedwe kathu. M’kupita kwa nthawi, tinazindikila kuti mfundo ina ya m’magazini ya Watch Tower imene taigwila mau m’ndime 18 ndi yoona. Magaziniyo inati: “Kunena zoona ulosi sitingaumvetsetse mpaka pamene wakwanilitsidwa kapena pamene ukukwanilitsidwa.” Popeza kuti tsopano tikukhala kumapeto kwa masiku otsiliza, maulosi ambili okhudza Ufumu akwanilitsidwa kale ndipo ena akukwanilitsidwa. Yehova wathandiza anthu ake kumvetsetsa bwino colinga cake cifukwa cakuti io ndi odzicepetsa, ndipo amalola kuwongoleledwa. Inde, coonadi caculuka masiku ano.

Kusintha kwa Kamvedwe Kumayesa Anthu a Mulungu

20, 21. Kodi kusintha kwa kamvedwe ka coonadi kunawakhudza bwanji Akristu a m’nthawi ya atumwi?

20 Yehova akatithandiza kusintha kamvedwe kathu ka coonadi m’pamene timadziŵika kuti tili ndi mtima wokonda coonadi kapena ai. Kukhala ndi cikhulupililo ndi kudzicepetsa kungatithandize kuvomeleza pakakhala kusintha kulikonse pa kamvedwe ka coonadi. Kusintha kwa conco kunakhudza Akristu amene anali ndi moyo m’zaka za m’ma 50 C.E. Mwacitsanzo, yelekezelani kuti ndinu Mkristu waciyuda amene mukukhala m’nthawi imeneyo, ndipo mumalemekeza kwambili Cilamulo ca Mose ndi kunyadila kukhala mbali ya mtundu wa Isiraeli. Ndiyeno, mwalandila makalata ocokela kwa mtumwi Paulo ofotokoza kuti Akristu safunikanso kutsatila Cilamulo ndi kuti Yehova anakana mtundu wa Isiraeli, ndipo akusonkhanitsa Isiraeli wauzimu wopangidwa ndi Ayuda ndi anthu amitundu ina. (Aroma 10:12; 11:17-24; Agal. 6:15, 16; Akol. 2:13, 14) Kodi inuyo mukanacita ciani?

21 Akristu odzicepetsa anavomeleza mfundo zouzilidwa zimene Paulo anafotokoza, ndipo Yehova anawadalitsa. (Mac. 13:48) Koma ena anakhumudwa ndi zimenezi ndipo anafuna kutsatila maganizo ao. (Agal. 5:7-12) Iwo akanapanda kusintha maganizo ao, akanataya mwai wokalamulila ndi Kristu.—2 Pet. 2:1.

22. Kodi mukukhudzika bwanji ndi kamvedwe kathu katsopano ka colinga ca Mulungu?

22 M’zaka zaposacedwapa, Yehova watithandiza kumvetsetsa bwino mfundo zokhudza Ufumu. Mwacitsanzo, iye watithandiza kudziŵa bwino nthawi imene anthu omwe adzakhala nzika za Ufumu adzalekanitsidwa ndi anthu osamvela ngati mmene nkhosa ndi mbuzi zimalekanitsidwila. Iye watithandizanso kudziŵa nthawi pamene ciŵelengelo conse ca Akristu a 144,000 cidzakwanila. Mulungu watiphunzitsanso tanthauzo la mafanizo a Ufumu amene Yesu anakamba ndi nthawi imene wodzozedwa womaliza adzaukitsidwa kuti akakhale kumwamba. * Kodi inu mumakhudzika bwanji ndi kamvedwe kathu katsopano ka coonadi kameneka? Kodi zimenezi zimalimbitsa cikhulupililo canu? Kodi mumaona kamvedwe katsopano kameneka monga umboni wakuti Yehova akuphunzitsabe anthu ake odzicepetsa? Nkhani zotsatila m’buku lino zidzakuthandizani kukhulupilila kwambili kuti Yehova akuvumbula pang’onopang’ono colinga cake kwa anthu amene amamuopa.

^ par. 4 Dzina la Mulungu linacokela ku liu la Ciheberi limene limatanthauza kuti “kukhala.” Dzina la Yehova limaonetsa kuti iye amakwanilitsa malonjezo ake. Onani bokosi lakuti “Tanthauzo la Dzina la Mulungu,” patsamba 43.

^ par. 6 Nthawi imeneyi ingaoneke yaitali kwambili masiku ano. Koma tiyenela kukumbukila kuti kale anthu anali kukhala ndi moyo nthawi yaitali kwambili. Mwacitsanzo, panali anthu anai amene moyo wao unalowelana kucokela nthawi ya Adamu kufika nthawi ya Abulahamu. Adamu anakhalabe ndi moyo mpaka pamene Lameki, atate wake wa Nowa anabadwa. Lameki anakhalabe ndi moyo mpaka pamene Semu, mwana wa Nowa anabadwa. Semu anakhalabe ndi moyo mpaka pamene Abulahamu anabadwa.—Gen. 5:5, 31; 9:29; 11:10, 11; 25:7.

^ par. 13 Dzina lakuti “Satana” limapezeka nthawi zokwana 18 m’Malemba a Ciheberi. Koma dzina limeneli limapezeka nthawi zokwana 30 m’Malemba a Cigiriki Acikristu. Malemba a Ciheberi sanafotokoze kwambili za Satana, koma anafotokoza kwambili zokhudza Mesiya. Pamene Mesiya anabwela, iye anathandiza anthu kumudziŵa bwino Satana, ndipo Malemba Acigiliki Acikristu amafotokoza bwino zimenezi.

^ par. 22 Kuti mumve za kamvedwe katsopano kameneka, onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995, patsamba 23 mpaka 28; January 15, 2008, patsamba 20-24; July 15, 2008, patsamba 17 mpaka 21, ndi Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013, patsamba 15 mpaka 20.