Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 4

Yehova Analemekeza Dzina Lake

Yehova Analemekeza Dzina Lake

CHOLINGA CHA MUTUWU

Zimene anthu a Mulungu anachita kuti alemekeze dzina la Mulungu

1, 2. Kodi Baibulo la Dziko Latsopano limalemekeza bwanji dzina la Mulungu?

 LACHIWIRI m’mawa pa December 2, 1947, kagulu ka abale odzozedwa a pa Beteli ku Brooklyn, New York, kanayamba kugwira ntchito inayake yaikulu komanso yovuta kwambiri. Ntchitoyi inali yomasulira Baibulo ndipo inatenga zaka 12. Pofika pa March 13, 1960, lomwe linali Lamlungu, abalewa anamaliza ntchito yomasulira Baibuloyi. Patapita miyezi itatu kuchokera pa tsikuli, M’bale Nathan Knorr anatulutsa Baibulo lathunthu la Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika pa June 18, 1960 pamsonkhano womwe unachitikira ku Manchester, m’dziko la England. Anthu amene anabwera pamsonkhanowu anasangalala kwambiri chifukwa cha kutulutsidwa kwa Baibuloli. M’bale wokamba nkhani anafotokoza bwino mmene anthu onse amene anapezeka pamsonkhanowo anamvera. Iye ananena kuti: ‘Lero ndi tsiku lachisangalalo kwa Mboni za Yehova zonse padziko lapansi.’ Chinthu china chochititsa chidwi ndi Baibulo limeneli, chimene chinali chosangalatsa kwambiri, ndi mmene anagwiritsira ntchito dzina lenileni la Mulungu.

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linatulutsidwa m’chaka cha 1950 pamsonkhano wakuti, Kuwonjezeka Kwa Teokalase (Kumanzere: Ku Sitediyamu ya Yankee ku New York City; Kumanja: Ku Ghana)

2 Mabaibulo ambiri sagwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Koma atumiki a Yehova odzozedwa anakaniratu maganizo a Satana oti anthu asadziwe dzina la Mulungu. Mawu oyambirira a m’Baibulo latsopanoli anati: “Chinthu chapadera kwambiri m’Baibulo lino n’chakuti tabwezeretsa dzina la Mulungu m’malo ake oyenerera.” Zimenezi n’zoona chifukwa dzina la Mulungu, lomwe ndi Yehova, limapezeka m’Baibuloli nthawi zoposa 7,000. Umenewutu ndi umboni wakuti Baibulo limeneli likulemekeza dzina la Atate wathu wakumwamba, lomwe ndi Yehova.

3. (a) Kodi abale athu anazindikira mfundo iti yokhudza tanthauzo la dzina la Mulungu? (b) Kodi lemba la Ekisodo 3:13, 14 limatanthauza chiyani? (Onani bokosi lakuti, “ Tanthauzo la Dzina la Mulungu.”)

3 M’zaka zoyambirira, Ophunzira Baibulo ankaona kuti dzina la Mulungu limatanthauza kuti “Ine ndine yemwe ndiri Ine.” (Eks. 3:14, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Ndipo Nsanja ya Olonda ya January 1, 1926, inanena kuti: “Dzina lakuti Yehova limasonyeza kuti palibe amene anamulenga, . . . alibe chiyambi ndiponso alibe mapeto.” Komabe, pa nthawi imene omasulira Baibulo la Dziko Latsopano ankayamba ntchito yawo, Yehova anawathandiza kudziwa kuti dzinalo silimangotanthauza kuti palibe amene anamulenga koma limatanthauzanso kuti iye ndi Mulungu amene ali ndi cholinga ndipo amakwaniritsa cholinga chakecho. Iwo anazindikira kuti dzina la Yehova limatanthauza kuti “Amachititsa Kuti Zinthu Zikhalepo Kapena Kuti Zichitike.” Mwachitsanzo, Iye ndi amene anachititsa kuti chilengedwechi chikhalepo kuphatikizaponso angelo ndi anthu komanso Iye ndi amene akuchititsa kuti cholinga ndiponso chifuniro chake zizichitika. Komano, n’chifukwa chiyani dzina la Mulungu likufunika kulemekezedwa? Nanga ifeyo tingatani kuti tililemekeze?

Kuyeretsedwa Kwa Dzina la Mulungu

4, 5. (a) Kodi timatanthauza chiyani tikamapemphera kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe”? (b) Kodi Mulungu adzayeretsa bwanji dzina lake ndipo adzachita liti zimenezi?

4 Yehova amafuna kuti anthu azilemekeza dzina lake. Ndipotu zimene Yesu anatchula koyambirira kwa pemphero lake lachitsanzo zimatithandiza kudziwa kuti cholinga chachikulu cha Mulungu ndi kuyeretsa dzina lake. Yesu anati: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mat. 6:9) Kodi tikamatchula mfundo imeneyi m’pemphero timakhala tikutanthauza chiyani?

5 Monga mmene tinaonera m’mutu woyamba wa bukuli, mfundo yakuti “Dzina lanu liyeretsedwe” ndi imodzi mwa mfundo zitatu zimene Yesu anatchula m’pemphero lake lachitsanzo zomwe n’zogwirizana kwambiri ndi chifuniro cha Yehova. Mfundo zinazo ndi zakuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike.” (Mat. 6:10) Choncho, tikamapempha kuti “Ufumu wanu ubwere” komanso kuti “chifuniro chanu chichitike,” timakhala tikupempha kuti Yehova achitepo kanthu pobweretsa Ufumu wake ndi kuchititsa kuti chifuniro chake chichitike padziko lapansi. Ndipo tikamapempha kuti “dzina lanu liyeretsedwe” timakhala tikupempha kuti Yehova achitepo kanthu kuti ayeretse dzina lake lomwe lakhala likunyozedwa kuyambira pamene Adamu ndi Hava anam’pandukira m’munda wa Edeni. Kodi Yehova adzayankha bwanji pemphero limeneli? Iye ananena kuti: “Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu limene linali kudetsedwa pakati pa mitundu ina ya anthu.” (Ezek. 36:23; 38:23) Yehova adzayeretsa dzina lake akadzawononga anthu onse oipa pa Aramagedo.

6. Kodi tingatani kuti tiziyeretsa nawo dzina la Mulungu?

6 M’mbuyo monsemu, Yehova wakhala akulola kuti atumiki ake azigwira nawo ntchito yoyeretsa dzina lake. Sitingachititse kuti dzina la Mulungu likhale lopatulika chifukwa ndi lopatulika kale kwambiri. Ndiye tingaliyeretse bwanji? Yesaya ananena kuti: “Yehova wa makamu ndi amene muyenera kumuona kuti ndi woyera.” Ndipo pofotokoza za anthu ake Yehova anati: “Iwo adzayeretsa dzina langa . . . , ndipo adzalemekeza kwambiri Mulungu wa Isiraeli.” (Yes. 8:13; 29:23) Choncho, timayeretsa dzina la Mulungu tikamaliona kuti ndi lapamwamba kwambiri komanso kuti ndi losiyana ndi mayina onse. Timaliyeretsanso tikamadziwa chimene limatanthauza komanso tikamathandiza anthu ena kuliona kuti ndi loyera. Komanso timasonyeza kuti timalemekeza dzina la Mulungu tikamaona kuti Yehova ndi Wolamulira wathu ndiponso tikamamvera malangizo ake ndi mtima wathu wonse.​—Miy. 3:1; Chiv. 4:11.

Anawakonzekeretsa Kulemekeza Komanso Kudziwika ndi Dzina la Mulungu

7, 8. (a) N’chifukwa chiyani panatenga nthawi kuti anthu a Mulungu ayambe kudziwika ndi dzina lake? (b) Kodi tikambirana chiyani?

7 Atumiki a Yehova anayamba kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu m’mabuku awo kuyambira m’zaka za m’ma 1870. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya August 1879, komanso buku la nyimbo lomwe linatulutsidwa chaka chomwecho, zinali ndi dzina lakuti Yehova. Izi zikusonyeza kuti Yehova anaona kuti anthu ake akufunika kudziwa kaye zinthu zina zokhudza dzinali asanawalole kuyamba kudziwika ndi dzina lake loyera. Kodi Yehova anawakonzekeretsa bwanji Ophunzira Baibulo kuti ayambe kudziwika ndi dzina lake?

8 Tikaona zimene zinachitika chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800 ndi kumayambiriro kwa 1900, timaona mmene Yehova anathandizira anthu ake kumvetsa mfundo zofunika zokhudza dzina lake. Tiyeni tione mfundo zitatu zimenezi.

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani nkhani zimene zinkatuluka m’magazini oyambirira a Nsanja ya Olonda zinkafotokoza kwambiri za Yesu? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinasintha kuyambira m’chaka cha 1919, ndipo zotsatira zake zinali zotani? (Onaninso bokosi lakuti, “ Mmene Nsanja ya Olonda Yakhala Ikulemekezera Dzina la Mulungu.”)

9 Mfundo yoyamba, atumiki a Yehova anamvetsa kufunika kwa dzina la Mulungu. Ophunzira Baibulo okhulupirika ankaona kuti nkhani ya dipo ndi mfundo yaikulu imene Baibulo limaphunzitsa. N’chifukwa chake magazini a Nsanja ya Olonda ankafotokoza za Yesu mobwerezabwereza. Mwachitsanzo, m’chaka choyambirira chomwe magaziniwa anayamba kutuluka, dzina la Yesu linatchulidwa kwambiri kuposa dzina la Yehova. Pofotokoza zimene zinkachitika m’zaka zoyambirira za Ophunzira Baibulo, Nsanja ya Olonda ya March 15, 1976, inanena kuti Akhristuwo “ankalemekeza kwambiri” Yesu. Koma m’kupita kwa nthawi, Yehova anawathandiza kudziwa kuti Baibulo limalemekeza kwambiri dzina lenileni la Mulungu. Magaziniyi inanena kuti chifukwa cha mfundo imeneyi, kuyambira m’chaka cha 1919, Ophunzira Baibulo “anayamba kulemekeza kwambiri Yehova, yemwe ndi Atate wake wakumwamba wa Mesiya.” Ndipotu kungoyambira mu 1920 mpaka mu 1929, magazini ya Nsanja ya Olonda inatchula dzina la Mulungu kwa nthawi zoposa 6,500.

10 Chifukwa chakuti abalewa anayamba kulemekeza kwambiri dzina la Yehova, anasonyeza kuti amalikonda kwambiri. Iwo anakonza zoti ‘alengeze dzina la Yehova’ ngati mmene Mose anachitira. (Deut. 32:3; Sal. 34:3) Chifukwa cha zimenezi, Yehova anaona chikondi chawo padzina lake ndipo anawakomera mtima monga mmene Malemba amanenera.​—Sal. 119:132; Aheb. 6:10.

11, 12. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinasintha m’mabuku athu chaka cha 1919 chitangodutsa? (b) Kodi Yehova anathandiza atumiki ake kudziwa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?

11 Mfundo yachiwiri, Akhristu oona anadziwa kufunika kwa ntchito imene anapatsidwa ndi Mulungu. Chaka cha 1919 chitadutsa, Akhristu odzozedwa amene ankatsogolera gulu ankafuna kumvetsa bwino ulosi wa Yesaya. Atamvetsa bwino ulosiwu, zimene ankafalitsa m’magazini athu zinasintha kwambiri ndipo zinakhaladi “chakudya pa nthawi yoyenera.” N’chifukwa chiyani tikutero?​—Mat. 24:45.

12 Chaka cha 1919 chisanafike, Nsanja ya Olonda inali isanafotokozepo mwatsatanetsatane tanthauzo la zimene Yesaya ananena. Iye anati: “‘Inu ndinu mboni zanga,’ akutero Yehova. ‘Ndinu mtumiki wanga amene ndakusankhani.’” (Werengani Yesaya 43:10-12.) Chaka cha 1919 chitangodutsa, mabuku athu anayamba kufotokoza kwambiri uthenga wa m’Baibulo umenewu ndiponso kulimbikitsa odzozedwa onse kuti azigwira nawo ntchito yochitira umboni imene Yehova anawapatsa. Kuyambira mu 1925 mpaka mu 1931, chaputala 43 cha buku la Yesaya chinafotokozedwa m’magazini a Nsanja ya Olonda maulendo 57. Magazini iliyonse inkafotokoza m’mene mawu a Yesaya akugwirira ntchito kwa Akhristu. Zimenezi zikusonyeza kuti pa zaka zimenezi Yehova ankathandiza anthu ake kudziwa ntchito imene ayenera kugwira. Yehova anachita zimenezi kuti Akhristuwo “ayesedwe kaye ngati ali oyenerera.” (1 Tim. 3:10) Ophunzira Baibulo asanayambe kudziwika ndi dzina la Mulungu anafunika kusonyeza mwa zochita zawo kuti analidi mboni zake.​—Luka 24:47, 48.

13. Kodi Mawu a Mulungu amasonyeza bwanji kuti kuyeretsa dzina la Mulungu ndi nkhani yofunika kwambiri?

13 Mfundo yachitatu, anthu a Yehova anadziwa kufunika koyeretsa dzina la Mulungu. M’zaka za m’ma 1920 anthu a Yehovawa anazindikira kuti kuyeretsa dzina la Mulungu ndi nkhani yofunika kwambiri. Kodi Mawu a Mulungu amasonyeza bwanji zimenezi? Tiyeni tione zitsanzo ziwiri. Kodi chifukwa chachikulu chimene Mulungu anapulumutsira Aisiraeli ku Iguputo chinali chiyani? Yehova anafotokoza kuti: “Kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.” (Eks. 9:16) Ndipo n’chifukwa chiyani Yehova anamvera chisoni Aisiraeli atamupandukira? Yehova ananenanso kuti: “Ndinachita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina.” (Ezek. 20:8-10) Kodi Ophunzira Baibulo anaphunzira chiyani pa malemba amenewa ndiponso malemba ena a m’Baibulo?

14. (a) Kodi anthu a Mulungu anazindikira chiyani chakumapeto kwa zaka za m’ma 1920? (b) Chifukwa chophunzira Baibulo mozama, kodi Ophunzira Baibulo anayamba kuchita chiyani pa nkhani yolalikira? (Onaninso bokosi lakuti, “ Chifukwa Chachikulu Cholalikirira.”)

14 Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1920, anthu a Mulungu anazindikira kufunika kwa zimene Yesaya ananena zaka 2,700 m’mbuyomo. Ponena za Yehova, Yesaya ananena kuti: “Inu munatsogolera anthu anu kuti mudzipangire dzina lokongola.” (Yes. 63:14) Ophunzira Baibulo anamvetsa kuti nkhani yofunika kwambiri ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu osati kuti iwowo apulumutsidwe. (Yes. 37:20; Ezek. 38:23) Mu 1929, buku lachingelezi lakuti Prophecy linanena mwachidule mfundo imeneyi kuti: “Kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi nkhani yofunika kwambiri m’chilengedwe chonse.” Kusintha kwa kamvedwe kumeneku kunathandiza atumiki a Mulungu kuti azilalikira za dzina la Yehova ndiponso kuliyeretsa.

15. (a) Pofika m’zaka za m’ma 1930, kodi abale athu anamvetsa chiyani? (b) Kodi imeneyi inali nthawi yoyenera ya chiyani?

15 Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930, abale athu anamvetsa kufunika kwa dzina la Mulungu, ntchito imene Mulungu anawapatsa komanso nkhani imene ndi yofunika kwambiri m’chilengedwe chonse. Tsopano Yehova anaona kuti inali nthawi yoyenerera kuti atumiki ake ayambe kudziwika ndi dzina lake. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tione zinthu zina zimene zinachitika.

Yehova Anatenga “Anthu Odziwika ndi Dzina Lake”

16. (a) Kodi Yehova amalemekeza dzina lake m’njira yaikulu iti? (b) Kodi poyamba ndani amene ankadziwika monga anthu a Mulungu?

16 Yehova anakonza zoti padziko lapansi pakhale gulu la anthu amene azidziwika ndi dzina lake ndipo imeneyi ndi njira yaikulu imene akulemekezera dzina lake. Kuyambira m’chaka cha 1513 B.C.E., mtundu wa Isiraeli unkadziwika monga anthu a Yehova. (Yes. 43:12) Koma Aisiraeli analephera kusunga pangano ndi Mulungu, ndipo m’chaka cha 33 C.E. sanapitirizenso kukhala pa ubwenzi wapadera ndi Mulungu. Zimenezi zitangochitika, Yehova “anacheukira anthu a mitundu ina . . . kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14) Anthu amenewa anali Akhristu odzozedwa ochokera m’mitundu yosiyanasiyana ndipo anayamba kudziwika kuti ndi “Isiraeli wa Mulungu.”​—Agal. 6:16.

17. Kodi Satana anakwanitsa kuchita chiyani?

17 Chaka cha 44 C.E. chisanafike, otsatira Khristu “anayamba kutchedwa Akhristu, motsogoleredwa ndi Mulungu.” (Mac. 11:26) Poyamba dzinali linali lapadera chifukwa Akhristu oona okha ndi amene ankadziwika ndi dzinali. (1 Pet. 4:16) Koma monga mmene Yesu ananenera m’fanizo la tirigu ndi namsongole, Satana anachita zonse zomwe akanatha kuti Akhristu onyenga azidziwikanso kuti ndi Akhristu. Zimenezi zinachititsa kuti kwa zaka zambiri pasakhale kusiyana pakati pa Akhristu oona ndi Akhristu onyenga. Koma zinthu zinasintha ‘m’nthawi yokolola’ imene inayamba mu 1914, chifukwa angelo anayamba kulekanitsa Akhristu oona ndi Akhristu onyenga.​—Mat. 13:30, 39-41.

18. Kodi n’chiyani chimene chinathandiza abale athu kudziwa kuti akufunika dzina lina?

18 Kapolo wokhulupirika atasankhidwa mu 1919, Yehova anathandiza anthu ake kudziwa ntchito imene anayenera kugwira. Anaona kuti ntchito yolalikira ku nyumba ndi nyumba ndi imene inkawasiyanitsa ndi Akhristu onyenga. Atazindikira mfundo imeneyi, anaonanso kuti dzina lakuti Ophunzira Baibulo silinkawasiyanitsa kwambiri ndi Akhristu onyenga. Cholinga chawo sichinali kungophunzira Baibulo koma kulalikira za Mulungu ndiponso kulemekeza dzina lake. Ndiye kodi ndi dzina liti limene likanakhala loyenera chifukwa cha ntchito imene ankagwirayi? Funso limeneli linayankhidwa m’chaka cha 1931.

Pulogalamu ya msonkhano umene unachitika m’chaka cha 1931

19, 20. (a) Kodi pamsonkhano umene unachitika mu 1931 panawerengedwa chigamulo chosangalatsa chiti? (b) Kodi abale athu anatani atamva za dzina lawo latsopano?

19 M’mwezi wa July chaka cha 1931, Ophunzira Baibulo okwana 15,000 anapita ku Columbus, Ohio ku America kuti akachite msonkhano. Anthuwa anadabwa kwambiri ndi zilembo ziwiri zimene zinalembedwa pamwamba pa pulogalamu ya msonkhanowo. Zilembo zake zinali J ndi W. Ena ankaganiza mawu osiyanasiyana oimira zilembozi. Kenako Lamlungu, pa July 26, M’bale Joseph Rutherford anawerenga chigamulo chimene chinali ndi mawu a mphamvu akuti: “Tikufunitsitsa kuti tizidziwika komanso kutchedwa ndi dzina lakuti, Mboni za Yehova.” Atangonena mawu amenewa, anthu onse amene anasonkhana anazindikira kuti zilembo zija zinkaimira Jehovah’s Witnesses, lomwe ndi dzina lachingelezi la Mboni za Yehova, lochokera pa Yesaya 43:10.

20 Anthu onse amene anasonkhanawo anafuula komanso kuwomba m’manja kwa nthawi yaitali atamva chigamulo chimenechi. Chifukwa chakuti msonkhanowu unkaulutsidwanso pawailesi, anthu a m’mayiko ambiri ankatha kumva phokoso la chisangalalo lomwe linkachitika ku Columbus. Mwachitsanzo, Ernest ndi Naomi Barber omwe anali ku Australia pa nthawiyi, ananena kuti: “Anthu atawomba m’manja ku America, abale a mumzinda wa Melbourne anadumpha chifukwa chosangalala ndipo anaomba m’manja kwa nthawi yaitali. Sitidzaiwala zimene zinachitika tsiku limeneli.” a

Dzina la Mulungu Likulengezedwa Padziko Lonse

21. Kodi dzina latsopanoli linawalimbikitsa bwanji pa ntchito yolalikira?

21 Atumiki a Mulungu analimbikitsidwa kugwira ntchito yolalikira chifukwa chodziwika ndi dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova. Edward ndi Jessie Grimes anali nawo pamsonkhano umene unachitika m’chaka cha 1931 ku Columbus, ndipo pa nthawi imeneyi ankachita upainiya ku America. Iwo ananena kuti: “Tinachoka kunyumba tili Ophunzira Baibulo koma tinabwerera tili Mboni za Yehova. Tinasangalala kwambiri chifukwa tinayamba kudziwika ndi dzina lomwe linkatithandiza kulemekeza dzina la Mulungu wathu.” Msonkhanowu utangotha, Mboni zina zinayamba kugwiritsa ntchito njira yatsopano pofuna kulemekeza dzina la Yehovali. Akafika panyumba ya munthu ankapereka kakhadi komwe kanali ndi uthenga wakuti: “Ndine mmodzi wa mboni za YEHOVA ndipo ndikulalikira za Ufumu wa YEHOVA Mulungu wathu.” N’zoonekeratu kuti anthu a Mulungu ankanyadira kudziwika ndi dzina la Yehova ndipo anali okonzeka kulengeza dzinali padziko lonse lapansi.​—Yes. 12:4.

“Tinachoka kunyumba tili Ophunzira Baibulo koma tinabwerera tili Mboni za Yehova”

22. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu a Yehova ali ndi dzina lapadera?

22 Tsopano papita zaka zambiri kuchokera pa nthawi imene Yehova anathandiza abale odzozedwa kuti ayambe kudziwika ndi dzina lapaderali. Kuyambira m’chaka cha 1931, Satana walephera kusokoneza anthu kuti asadziwe anthu a Mulungu komanso chipembedzo choona. Panopa tikudziwika kwambiri ndi dzina la Mulungu wathu. (Werengani Mika 4:5; Malaki 3:18.) Anthu ambiri amadziwa kuti timagwiritsa ntchito dzina la Mulungu wathu moti munthu wina akangotchula dzina lakuti Yehova, anthu amaganiza kuti ndi wa Mboni za Yehova. Pamenepatu zipembedzo zonyenga zalephera kubisa dzina la Yehova ndipo kulambira koona ‘kwakhazikika pamwamba pa nsonga za mapiri.’ (Yes. 2:2) Masiku ano anthu akulemekeza kwambiri kulambira koona komanso dzina lopatulika la Yehova.

23. Malinga ndi Salimo 121:5, kodi ndi mfundo iti yonena za Yehova imene imatilimbikitsa kwambiri?

23 N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova akutiteteza ndipo adzapitiriza kutiteteza kwa Satana. (Sal. 121:5) Kunena zoona, tili ndi zifukwa zomveka zonena mawu ofanana ndi mawu amene wamasalimo analemba akuti: “Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala cholowa chake.”​—Sal. 33:12.

a Kuti mudziwe mmene ankagwiritsira ntchito wailesi onani Mutu 7, tsamba 72-74.