Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 6

Anthu Amene Akulalikira​—Atumiki Anadzipereka Mofunitsitsa

Anthu Amene Akulalikira​—Atumiki Anadzipereka Mofunitsitsa

CHOLINGA CHA MUTUWU

Mfumu inakonza gulu la anthu loti lizilalikira

1, 2. Kodi Yesu analosera za ntchito yaikulu yotani, nanga zimenezi zingatichititse kukhala ndi funso liti?

 NTHAWI zambiri atsogoleri andale amalonjeza zinthu koma sakwaniritsa zimene alonjezazo. Ngakhale atsogoleri amene ali ndi zolinga zabwino amalephera kukwaniritsa zimene alonjeza. Koma chosangalatsa n’chakuti, Yesu Khristu ndi wosiyana ndi atsogoleri amenewa chifukwa nthawi zonse amakwaniritsa zimene walonjeza.

2 Atakhala Mfumu m’chaka cha 1914, Yesu anali wokonzeka kukwaniritsa ulosi umene ananena zaka 1,900 m’mbuyomo. Atatsala pang’ono kufa, Yesu analosera kuti: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mat. 24:14) Iye ananena kuti zimene analoserazi zikamadzakwaniritsidwa udzakhala umboni wakuti wayamba kulamulira monga Mfumu. Koma funso lofunika kwambiri n’lakuti: Kodi Mfumu ikanakwanitsa bwanji kukonza gulu la anthu loti lizilalikira m’masiku otsiriza, nthawi imene anthu adzakhala odzikonda, opanda chikondi komanso osakonda Mulungu? (Mat. 24:12; 2 Tim. 3:1-5) Tiyenera kupeza yankho la funso limeneli chifukwa nkhaniyi imakhudza Mkhristu woona aliyense.

3. Kodi Yesu ankakhulupirira kuti zinthu zidzakhala bwanji, nanga n’chiyani chinam’pangitsa kukhulupirira zimenezi?

3 Taonaninso bwinobwino zimene Yesu ananena palembali. Mawu akuti “udzalalikidwa” akusonyeza kuti ankakhulupirira zimene ananena. Yesu ankakhulupirira kuti m’masiku otsiriza padzakhala anthu amene adzadzipereka mofunitsitsa. Koma kodi n’chiyani chinamuchititsa kukhulupirira zimenezi? Anaphunzira kuchokera kwa Atate ake. (Yoh. 12:45; 14:9) Ali kumwamba, Yesu ankaona kuti Yehova amakhulupirira atumiki ake omwe amasonyeza mtima wodzipereka. Tiyeni tione mmene Yehova anasonyezera kuti amakhulupirira atumiki ake.

“Anthu Ako Adzadzipereka Mofunitsitsa”

4. Kodi Yehova anauza Aisiraeli kuti agwire nawo ntchito yotani, nanga iwo anatani atauzidwa zimenezi?

4 Kumbukirani zimene zinachitika pamene Yehova anauza Mose kuti amange chihema, kapena kuti tenti, choti Aisiraeli azichigwiritsa ntchito monga malo olambirirapo. Kudzera mwa Mose, Yehova anapempha anthu onse kuti athandize nawo pa ntchito imeneyi. Mose anawauza kuti: “Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa apereke kwa Yehova zinthu.” Kodi anthuwo anachita chiyani? Anthuwo “anapitirizabe kubweretsa . . . nsembe zawo zaufulu tsiku lililonse.” Anabweretsa zinthu zambiri moti anachita ‘kuwaletsa kubweretsa zinthuzo.’ (Eks. 35:5; 36:3, 6) Zimene Aisiraeli anachita zinasonyeza kuti Yehova sanalakwitse kuwakhulupirira.

5, 6. Malinga ndi Salimo 110:1-3, kodi Yehova komanso Yesu ankayembekezera kuti atumiki a Mulungu adzakhala ndi mtima wotani m’masiku otsiriza?

5 Yehova ankayembekezera kuti m’masiku otsiriza atumiki ake adzakhalanso ndi mtima wodzipereka. Kuli zaka 1,000 kuti Yesu abadwe padziko lapansi, Yehova anauza Davide kuti alembe zimene zidzachitike Mesiya akadzayamba kulamulira. (Werengani Salimo 110:1-3.) Yesu akadzangoikidwa kukhala Mfumu adani ake adzayamba kumutsutsa, koma adzakhala ndi gulu la anthu amene adzakhala pambuyo pake kuti azimutumikira. Gulu la anthuli silidzakakamizidwa kutumikira Mfumuyi. Ngakhale achinyamata adzadzipereka mofunitsitsa n’kupanga gulu lalikulu kwambiri lomwe tingaliyerekezere ndi mame a m’bandakucha. a

Anthu amene akutumikira mu Ufumuwu ndi ambiri ngati mame (Onani ndime 5)

6 Yesu ankadziwa kuti ulosi umene unalembedwa pa Salimo 110 unkanena za iyeyo. (Mat. 22:42-45) N’chifukwa chake anali ndi chikhulupiriro chakuti adzakhala ndi anthu omwe adzadzipereke mofunitsitsa kuti agwire nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino padziko lonse lapansi. Kodi zimene zakhala zikuchitika m’mbuyomu zasonyezadi kuti Mfumuyi ili ndi gulu la anthu oti azilalikira m’masiku otsiriza ano?

“Ndi Udindo Komanso Mwayi Wanga Kulengeza Nawo Uthengawu”

7. Kodi Yesu ataikidwa kukhala Mfumu anachita chiyani pokonzekeretsa otsatira ake?

7 Atangoikidwa kukhala Mfumu, Yesu anayamba kukonzekeretsa otsatira ake kuti athe kugwira ntchito yaikuluyi. Monga mmene tinaonera m’Mutu 2, Yesu anagwira ntchito yoyendera komanso kuyeretsa kuyambira m’chaka cha 1914 mpaka kumayambiriro kwa chaka cha 1919. (Mal. 3:1-4) Kenako mu 1919, anasankha kapolo wokhulupirika kuti azitsogolera otsatira ake. (Mat. 24:45) Kuyambira nthawi imeneyi, kapoloyu wakhala akupereka chakudya chauzimu kudzera m’mabuku komanso nkhani zomwe zimakambidwa pamisonkhano zimene zimanena momveka bwino kuti Mkhristu aliyense ali ndi udindo wolalikira.

8-10. Kodi misonkhano inalimbikitsa bwanji anthu kugwira ntchito yolalikira? Perekani chitsanzo. (Onaninso bokosi lakuti, “ Misonkhano Yakale Yomwe Inalimbikitsa Ntchito Yolalikira.”)

8 Nkhani za pamsonkhano. Ophunzira Baibulo ankafunitsitsa kutsogoleredwa ndi Yehova moti nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha, anachita msonkhano ku Cedar Point, Ohio, ku America. Msonkhanowu unachitika kuyambira pa September 1 mpaka 8 m’chaka cha 1919 ndipo aka kanali koyamba kuti akhale ndi msonkhano waukulu. Pa tsiku lachiwiri la msonkhanowo, M’bale Rutherford anakamba nkhani ndipo ananena mosapita m’mbali kuti: “Ntchito ya Mkhristu padziko lapansi ndi . . . kulengeza uthenga wa ufumu wa Ambuye.”

9 Msonkhanowu unafika pachimake pa tsiku lachitatu pamene M’bale Rutherford anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Uthenga Wopita kwa Antchito Anzathu,” yomwe inatulukanso mu Nsanja ya Olonda ndipo inali ndi mutu wakuti, “Kulengeza Ufumu.” M’baleyu ananenanso kuti: “Mkhristu aliyense ayenera kudzifunsa kuti: N’chifukwa chiyani ndili ndi moyo? Yankho lake liyenera kukhala lakuti, Ambuye wandikomera mtima kuti ndikhale kazembe wake n’cholinga choti ndigwire nawo ntchito yogwirizanitsanso anthu ndi Mulungu. Ndi udindo komanso mwayi wanga kulengeza nawo uthengawu.”

10 M’nkhaniyi, M’bale Rutherford analengeza za kutuluka kwa magazini yatsopano ya The Golden Age (yomwe panopa timati Galamukani!). Cholinga cha magaziniyi chinali kuthandiza anthu kudziwa za Ufumu, womwe umapatsa anthu chiyembekezo. Kenako anafunsa anthu amene anali pamsonkhanowo kuti amene akufuna kugwira nawo ntchito yogawira magaziniyi aimirire. Lipoti la msonkhanowo linanena kuti: “Zinali zosangalatsa kwambiri chifukwa anthu 6,000 amene anasonkhana anaimirira nthawi imodzi posonyeza kuti akufunitsitsa kugwira nawo ntchito imeneyi.” b Apa zikuonekeratu kuti Mfumu inali ndi anthu amene anali ofunitsitsa kulengeza za Ufumu.

11, 12. Kodi Nsanja ya Olonda ina imene inatuluka m’chaka cha 1920 inanena kuti ntchito imene Yesu analosera idzachitika liti?

11 Magazini. Magazini a Nsanja ya Olonda anayamba kufotokoza kufunika kwa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu imene Yesu analosera. Tiyeni tione zinthu zina zimene zinafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda m’zaka za m’ma 1920.

12 Kodi ndi uthenga uti umene unali kudzalengezedwa pokwaniritsa ulosi wa pa Mateyu 24:14? Kodi ntchitoyi inali kudzachitika liti? Pofotokoza za uthengawu, nkhani ya mutu wakuti “Uthenga Wabwino Wonena za Ufumu” imene inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1920, inanena kuti: “Uthenga wabwino umene tikufotokoza pano ndi wonena za kutha kwa dongosolo lakale la zinthu limene likulowedwa m’malo ndi ufumu wa Mesiya.” Nkhaniyi inanenanso za nthawi imene uthengawu udzalengezedwe. Inati: “Uthenga umenewu uyenera kulengezedwa kuyambira pa nthawi ya nkhondo yaikulu yapadziko lonse [nkhondo yoyamba yapadziko lonse] mpaka pa nthawi ya ‘chisautso chachikulu.’” Ndiyeno magaziniyo inanenanso kuti: “Ino ndi nthawi yoyenera . . . kulengeza padziko lonse uthenga wabwino umenewu kwa anthu amene ali m’matchalitchi amene amati ndi achikhristu.”

13. Kodi Nsanja ya Olonda ina imene inatuluka mu 1921 inalimbikitsa bwanji Akhristu odzozedwa kukhala ndi mtima wodzipereka?

13 Kodi anthu a Mulungu ankafunika kukakamizidwa kuti agwire ntchito imene Yesu analoserayi? Ayi. Nkhani ya mutu wakuti, “Khalani Olimba Mtima” yomwe inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 1921, inalimbikitsa Mkhristu wodzozedwa aliyense kuti akhale ndi mtima wodzipereka. Wodzozedwa aliyense analimbikitsidwa kudzifunsa kuti: “Kodi si mwayi waukulu komanso udindo wanga kugwira nawo ntchito yolalikirayi?” Kenako nkhaniyi inapitiriza kuti: “Tikukhulupirira kuti ngati mutamaona kuti kugwira ntchitoyi ndi mwayi wanu mudzakhala ngati Yeremiya, amene mawu a Ambuye anali ngati ‘moto woyaka umene unatsekeredwa m’mafupa ake,’ ndipo unamulimbikitsa kuti asasiye kulalikira.” (Yer. 20:9) Mawu olimbikitsa amenewa anasonyeza kuti Yehova komanso Yesu amakhulupirira anthu amene ali okhulupirika ku Ufumuwu.

14, 15. Mu 1922, kodi Nsanja ya Olonda ina inalimbikitsa Akhristu odzozedwa kuti azilalikira pogwiritsa ntchito njira ziti?

14 Kodi Akhristu oona anagwiritsa ntchito njira zotani polalikira uthenga wa Ufumu? Nkhani ya mutu wakuti, “Utumiki Wofunika,” yomwe inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1922, inalimbikitsa Akhristu odzozedwa kuti “azigawira mabuku ndi magazini komanso azilalikira kwa anthu m’makomo, popereka umboni wakuti ufumu wa kumwamba wayandikira.”

15 Apa n’zoonekeratu kuti kuyambira m’chaka cha 1919, Khristu wakhala akugwiritsa ntchito kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kuti azifotokoza mobwerezabwereza kuti Mkhristu aliyense ali ndi mwayi komanso udindo wolengeza za uthenga wa Ufumu. Koma kodi Ophunzira Baibulo oyambirira anachita chiyani atalimbikitsidwa kuti azigwira nawo ntchito yolalikira za Ufumuwu?

“Anthu Okhulupirika Adzadzipereka”

16. Kodi akulu ena anachita chiyani atamva kuti Akhristu onse ayenera kugwira ntchito yolalikira?

16 M’zaka za m’ma 1920 ndi m’ma 1930, ena sankafuna kuti Akhristu onse odzozedwa azigwira nawo ntchito yolalikira. Nsanja ya Olonda ya November 1, 1927, inafotokoza zimene zinkachitika kuti: “Pali ena mumpingo amene ali ndi udindo monga akulu . . . omwe sakulimbikitsa abale kuti azilalikira ndiponso iwowo sakumalalikira. . . . Amaseka akamauzidwa kuti ayenera kupita khomo ndi khomo kukalalikira za uthenga wa Mulungu ndiponso za Mfumu ndi Ufumu wake.” Nkhaniyi inanena mosapita m’mbali kuti: “Tsopano nthawi yafika yoti Akhristu okhulupirika aike chizindikiro anthu amenewa ndipo aziwapewa. Komanso awauze kuti sayenera kupatsidwa udindo monga akulu.” c

17, 18. Kodi mipingo yambiri inatani italandira malangizo kuchokera kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, nanga anthu ambiri achita zotani m’zaka 100 zapitazi?

17 Koma n’zosangalatsa kuti mipingo yambiri inatsatira malangizo ochokera kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amenewa. Abalewa ankaona kuti ndi mwayi wawo kugwira nawo ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu. Nsanja ya Olonda ya March 15, 1926, inanena kuti: “Anthu okhulupirika adzadzipereka . . . kuti agwire nawo ntchito yolengeza uthengawu.” Anthu okhulupirikawa anakwaniritsa ulosi wopezeka pa Salimo 110:3, ndipo anasonyeza kuti anali kumbali ya Mfumu yomwenso ndi Mesiya.

18 Pa zaka 100 zapitazi, anthu mamiliyoni ambiri akhala akudzipereka kuti agwire nawo ntchito yolalikira za Ufumu. M’mitu yotsatirayi tikambirana njira ndi zinthu zimene akhala akugwiritsa ntchito polalikira komanso zotsatirapo zake. Koma poyamba, tiyeni tikambirane chimene chapangitsa kuti anthu mamiliyoni ambiri adzipereke kugwira nawo ntchito yolalikira za Ufumu ngakhale kuti akukhala m’dziko limene anthu ake ndi odzikonda. Pamene tikukambirana mfundo imeneyi, aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani ndimagwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino?’

“Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba”

19. N’chifukwa chiyani timatsatira malangizo a Yesu akuti, “pitirizani kufunafuna ufumu choyamba”?

19 Yesu analangiza otsatira ake kuti: “Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba.” (Mat. 6:33) N’chifukwa chiyani timatsatira malangizo amenewa? Chifukwa timadziwa kuti Ufumuwu ndi wofunika ndiponso kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumuwu pokwaniritsa zolinga zake. Monga taonera m’mutu wapitawu, mzimu woyera wakhala ukuthandiza anthu kumvetsa pang’onopang’ono mfundo zochititsa chidwi zonena za Ufumuwu. Mfundo zochititsa chidwi zikatifika pamtima timayamba kukhala ndi maganizo ofuna kutsatira malangizo amene Yesu anapereka.

Akhristu amasangalala akapeza choonadi cha Ufumu ngati mmene anachitira munthu amene anapeza chuma chobisika uja (Onani ndime 20)

20. Kodi fanizo la Yesu la chuma chobisika limasonyeza bwanji kuti otsatira ake adzamvera lamulo lakuti apitirize kufunafuna Ufumu choyamba?

20 Yesu ankadziwa kuti otsatira ake adzamvera langizo lakuti apitirize kufunafuna Ufumu choyamba. Tiyeni tione zimene ananena m’fanizo la chuma chobisika. (Werengani Mateyu 13:44.) Pamene munthu wa m’fanizoli ankagwira ntchito m’munda, anapeza chuma chobisika ndipo nthawi yomweyo anazindikira kuti chinali chamtengo wapatali. Kodi anachita chiyani? Lembali limayankha kuti: “Chifukwa cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.” Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tikamvetsa mfundo zonena za Ufumu n’kuzindikira kuti n’zamtengo wapatali, tidzakhala okonzeka kusintha zinthu zina kuti tiyambe kuika zinthu za Ufumu pa malo oyamba m’moyo wathu. d

21, 22. Kodi anthu okhulupirika ku Ufumu amasonyeza bwanji kuti akufunafuna Ufumu choyamba? Perekani chitsanzo.

21 Anthu okhulupirika amene ali kumbali ya Ufumuwu amasonyeza, osati ndi mawu okha koma ndi zochita zawo, kuti akufunafuna Ufumu choyamba. Pamene akugwira ntchito yolalikira za Ufumuwu amadzipereka ndi moyo wawo wonse ndipo amagwiritsa ntchito luso komanso chuma chawo. Ambiri alolera kudzimana zinthu zina n’cholinga choti ayambe utumiki wa nthawi zonse ndipo aona okha umboni wakuti Yehova amadalitsa anthu amene amaika zinthu za Ufumu poyamba m’moyo wawo. Tiyeni tione chitsanzo cha atumiki ena amene anachita zimenezi.

22 Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1920, Avery ndi Lovenia Bristow ankatumikira monga akopotala (apainiya) chakum’mwera kwa dziko la United States. Patapita zaka zambiri, Lovenia ananena kuti: “Kuyambira nthawi imeneyo, ine ndi Avery takhala tikusangalala kwambiri kuchita upainiya. Nthawi zina sitinkadziwa kuti tipeza bwanji ndalama zogulira mafuta a galimoto kapena zinthu zofunika pakhomo. Koma Yehova ankatithandiza ndipo sitinasiye kuchita upainiya. Nthawi zonse tinkakhala ndi zinthu zofunikira pa moyo wathu.” Lovenia amakumbukira kuti nthawi ina akutumikira mumzinda wa Pensacola ku Florida, analibe ndalama komanso zinthu zina zapakhomo. Atafika pakhomo kuchokera muutumiki anapeza majumbo awiri akuluakulu mmene munali zinthu zosiyanasiyana zimene ankafunikira. Anapezanso kapepala komwe kanali ndi mawu akuti: “Landirani katunduyu. Mpingo wa Pensacola umakukondani kwambiri.” Pambuyo pochita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zambiri, Lovenia ananena kuti: “Yehova sataya anthu ake. Amakhala wokhulupirika kwa anthu amene amamukhulupirira.”

23. Kodi mumamva bwanji chifukwa chopeza choonadi, ndipo ndinu wofunitsitsa kuchita chiyani?

23 N’zoona kuti sitingachite zofanana pa ntchito yolalikira chifukwa moyo wathu ndi wosiyana. Komabe, tingasonyeze kuti timaona kuti kugwira ntchito yolalikira ndi mwayi waukulu ngati timadzipereka ndi mtima wonse. (Akol. 3:23) Popeza timaona kuti choonadi chimene tinapezachi ndi chamtengo wapatali, ndife ofunitsitsa kuchita zonse zomwe tingathe kuti titumikire Mulungu. Inunso yesetsani kuchita zimenezi.

24. Fotokozani chinthu chimodzi chimene Ufumuwu wachita m’masiku otsiriza ano.

24 Pa zaka 100 zapitazi, Mfumu yakhala ikukwaniritsa mawu aulosi amene analembedwa pa Mateyu 24:14. Ndipo siinachite kukakamiza anthu kuti agwire ntchito yolalikirayi. Pambuyo pophunzira choonadi otsatira ake adzipereka kuti agwire ntchito yolalikira. Ntchito yolengeza uthenga wabwino padziko lonse lapansi ndi mbali ya chizindikiro chakuti Yesu wayamba kulamulira komanso ndi chinthu chimodzi mwa zinthu zikuluzikulu zimene Ufumuwu wachita m’masiku otsiriza ano.

a M’Baibulo, mawu akuti mame, nthawi zambiri amatanthauza kuchuluka kwa zinthu.​—Gen. 27:28; Mika 5:7.

b Kabuku kamutu wakuti Kwa Amene Apatsidwa Ntchitoyi kananena kuti: “Cholinga chathu pogawira magazini ya The Golden Age kunyumba ndi nyumba ndi kulengeza uthenga wa ufumu. . . . Choncho, tikafotokoza uthenga wathu tiyenera kugawira magaziniyi, kaya munthu wavomera kulembetsa kuti azilandira magaziniwa mwezi ndi mwezi kapena ayi.” Kuyambira nthawi imeneyi abale ankalimbikitsidwa kuti azipempha anthu kulembetsa n’cholinga choti azilandira magazini a The Golden Age komanso Nsanja ya Olonda mwezi uliwonse. Kuyambira pa February 1, 1940, anthu a Yehova analimbikitsidwa kuti azigawira magazini ngakhale kwa anthu amene sanalembetse kuti azilandira magaziniwa mwezi ndi mwezi komanso kuti azipereka lipoti la magazini amene agawira.

c Nthawi imeneyo mpingo unkachita kuvotera abale kuti akhale akulu. Choncho mpingo ukanatha kukana kuvotera abale amene sankafuna kugwira ntchito yolalikira. M’mutu 12 tidzakambirana mmene zinasinthira kuti abale ayambe kuikidwa motsogoleredwa ndi mzimu.

d Yesu ananena mfundo yofanana ndi imeneyi m’fanizo lake la wamalonda amene anapita kukafufuza ngale yamtengo wapatali. Wamalondayu atapeza ngaleyi anapita kukagulitsa zonse zimene anali nazo n’kukagula ngaleyo. (Mat. 13:45, 46) Mafanizo awiriwa akutiphunzitsa kuti tikhoza kuphunzira choonadi cha Ufumu m’njira zosiyanasiyana. Anthu ena amachita kufufuza choonadi pomwe ena amaphunzira mosachivutikira. Kaya tinaphunzira bwanji choonadi, koma tonse timasiya zinthu zina kuti tiike zinthu za Ufumu pamalo oyamba pa moyo wathu.