Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 8

Zida Zogwilitsila Nchito Polalikila—Kusindikiza Mabuku Ogaŵila Padziko Lonse Lapansi

Zida Zogwilitsila Nchito Polalikila—Kusindikiza Mabuku Ogaŵila Padziko Lonse Lapansi

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Yehova akupitilizabe kutipatsa zida zofunika kuti tilalikile anthu ocokela m’dziko lililonse, fuko lililonse, ndi cinenelo ciliconse

1, 2. (a) M’nthawi ya atumwi, n’ciani cinathandiza kuti uthenga wabwino ufalikile kumadela onse mu Ufumu wa Roma? (b) Pali umboni wotani wakuti Yehova akuticilikiza masiku ano? (Onani bokosi lakuti “Uthenga Wabwino m’Zinenelo Zoposa 670.”)

PA PENTEKOSITE wa mu 33 C.E., ophunzila analandila mphatso yolankhula m’zinenelo zosiyanasiyana monga umboni wakuti anali kuyanjidwa ndi Mulungu. Anthu amene anapita ku Yelusalemu panthawiyo anadabwa ndi zimene anamva. Iwo anaona kuti anthu a ku Galileya anali kulankhula zinenelo zacilendo mosavutikila, ndipo alendowo anacita cidwi ndi uthenga umene anali kulengeza. (Ŵelengani Machitidwe 2:1-8, 12, 15-17) Patsikulo, ophunzila analalikila uthenga wabwino kwa anthu ocokela kumadela osiyanasiyana, ndipo m’kupita kwa nthawi uthengawo unafalikila kumadela ambili mu Ufumu wa Roma.—Akol. 1:23.

2 Masiku ano, atumiki a Mulungu samalankhula zinenelo zosiyanasiyana mozizwitsa. Ngakhale ndi conco, io amalalikila m’zinenelo zambili kuposa m’nthawi ya atumwi cifukwa amamasulila uthenga wa Ufumu m’zinenelo zoposa 670. (Mac. 2:9-11) Atumiki a Mulungu afalitsa mabuku ambilimbili m’zinenelo zoculuka cakuti uthenga wa Ufumu wafika kumbali zonse za dziko. * Umenewu ndi umboni wina wosatsutsika wakuti Yehova akugwilitsila nchito Mfumu Yesu Kristu kutsogolela nchito yolalikila. (Mat. 28:19, 20) Tsopano tiyeni tikambilane zida zocepa cabe zimene takhala tikugwilitsila nchito polalikila kwa zaka 100 zapitazi. Pamene tikukambilana zimenezi, onani mmene Mfumuyo yakhala ikutiphunzitsila kuti tizicita cidwi ndi anthu ndiponso kuti tikhale aphunzitsi a Mau a Mulungu.—2 Tim. 2:2.

Mfumu Ikonzekeletsa Atumiki Ake Kubyala Mbeu za Coonadi

3. N’cifukwa ciani timagwilitsila nchito zida zosiyanasiyana polalikila?

3 Yesu anayelekezela “mau a Ufumu” ndi mbeu, ndiponso mtima wa munthu ndi nthaka. (Mat. 13:18, 19) Mlimi amagwilitsila nchito zida zosiyanasiyana kukonza bwino nthaka kuti mbeu zikakule bwino. Mofananamo, atumiki a Yehova akhala akugwilitsila nchito zida zosiyanasiyana pokonzekeletsa mitima ya anthu mamiliyoni ambili kuti alandile uthenga wa Ufumu. Zina mwa zida zimenezo zinangogwila nchito kwa nthawi yocepa. Zida zina, monga mabuku ndi magazini, zikugwilabe nchito yofunika kwambili ngakhale masiku ano. Monga mmene tinaphunzilila m’Nkhani 7, kale atumiki a Mulungu anali kugwilitsila nchito njila zofalitsila uthenga wa ufumu kwa anthu ambili panthawi imodzi. Koma m’nkhani ino tikambilana zida zimene zawathandiza kulalikila munthu aliyense payekhapayekha.—Mac. 5:42; 17:2, 3.

Kupanga magalamafoni ndi zokuzila mau, ku Toronto, m’dziko la Canada

4, 5. Kodi ulaliki wa pagalamafoni unali kucitika motani? Nanga ulalikiwo sunali kukwanilitsa mbali iti kwenikweni?

4 Nkhani zojambulidwa. Zaka za m’ma 1930 ndi m’ma 1940, ofalitsa anali kugwilitsila nchito magalamafoni oyenda nao pofalitsa nkhani za m’Baibulo zojambulidwa. Nkhani iliyonse sinali kukwana mphindi 5. Nkhanizo nthawi zina zinali kukhala ndi mitu yaifupi monga yakuti “Utatu,” “Puligatoliyo,” ndi “Ufumu.” Kodi nkhanizo anali kuzigwilitsila nchito bwanji muulaliki? M’bale Clayton Woodworth Jr, amene anabatizidwa mu 1930 ku United States, anati: “Ndinali kunyamula galamafoni yaing’ono yooneka ngati kasutukesi, yomwe inali ndi kasipuling’i koithandiza kugwila nchito. Inali yosavuta kuigwilitsila nchito cifukwa inali ndi kacida kenakake kamene ndinali kuichela nayo kuti munthu akangotuluka iyambe kulila. Ndikafika pakhomo, ndinali kutsegula galamafoni yanga, kuichela, n’kugogoda pakhomo. Mwininyumba akatsegula citseko, ndinali kunena kuti, ‘Ndili ndi uthenga wofunika kwambili umene ndifuna kuti inu mumvetsele.’” Kodi anthu anali kumvetsela? M’bale Woodworth anati: “Nthawi zambili anthu anali kumvetsela. Koma anthu ena anali kungotseka citseko. Ndipo nthawi zina anali kuganiza kuti ndinali kugulitsa magalamafoni.”

Podzafika mu 1940, panali nkhani zojambulidwa zosiyanasiyana zoposa 90, ndipo zimbale za nkhanizo zoposa 1 miliyoni zinapangidwa

5 Podzafika m’caka ca 1940, panali nkhani zojambulidwa zosiyanasiyana zokwana 90, ndi zimbale za nkhanizo zopitilila 1 miliyoni. M’bale John E. Barr, amene anali kucita upainiya ku Britain panthawiyo, ndipo pambuyo pake anatumikila m’Bungwe Lolamulila, anati: “Kuyambila mu 1936 mpaka mu 1945, ndinali kuyenda ndi galamafoni nthawi zonse. Ndipo kunena zoona, sindinali kumva bwino ngati sindinayende nayo. Kungomva mau a m’bale Rutherford pagalamafoni pamene uli muulaliki, kunali kolimbikitsa kwambili. Zinali kukhala ngati ali nawe limodzi. Komabe, ulaliki wa pagalamafoni sunali kufika pamtima anthu kwenikweni.”

6, 7. (a) Kodi makadi aulaliki anali ndi ubwino wotani? Koma ndi vuto lanji limene nthawi zina anali kucititsa? (b) Kodi Yehova wakhala akutithandiza bwanji kudziŵa kulankhula?

6 Makadi Aulaliki. Kuyambila mu 1933, ofalitsa analimbikitsidwa kugwilitsila nchito makadi aulaliki polalikila nyumba ndi nyumba. Khadi laulaliki linali masentimita 7.6 mu lifupi, ndi 12.7 mu litali. Pakhadili panali ulaliki wacidule ndi dzina la cofalitsa cimene mwininyumba angaombole. Wofalitsa anali kungopatsa mwininyumbayo khadilo ndi kum’pempha kuti aŵelenge zimene zilipo. Mlongo wina dzina lake Lilian Kammerud, amene pambuyo pake anadzatumikila monga mmishonale ku Puerto Rico ndi Argentina, anati: “Ndinasangalala ndi njila yogwilitsila nchito makadi aulaliki.” Pofotokoza cifukwa cimene anasangalalila ndi njila imeneyi, iye anati: “Ndinali kuvutika kuti ndiyambe kulankhula ndi anthu. Conco khadili linandithandiza kuzoloŵela kukambilana ndi anthu popanda vuto.”

Makadi Aulaliki (Citaliyana)

7 M’bale David Reusch, amene anabatizidwa mu 1918, anati: “Makadi aulaliki anathandiza kwambili abale, cifukwa cakuti poyamba ambili anali kulephela kulankhula mau oyenela akapita muulaliki.” Koma si nthawi zonse pamene njila imeneyi inali yothandiza. M’bale Reusch anati: “Nthawi zina tinali kukumana ndi anthu amene anali kuganiza kuti sititha kulankhula. N’zoona kuti m’lingalilo lina tinalidi osatha kulankhula. Koma panthawiyi, Yehova anali kutiphunzitsa kuzoloŵela kukumana ndi anthu. Posapita nthawi, iye anayamba kutithandiza kudziŵa kulankhula potiphunzitsa kukambilana Malemba ndi anthu mwaluso. Iye wakhala akucita zimenezi kupyolela mu Sukulu ya Ulaliki imene inayamba m’ma 1940.”—Ŵelengani Yeremiya 1:6-9.

8. N’ciani cimene muyenela kucita kuti Kristu akuphunzitseni?

8 Mabuku. Kuyambila mu 1914, gulu la Yehova lalemba mabuku osiyanasiyana oposa 100 ofotokoza nkhani za m’Baibulo. Ena a mabukuwa anawalemba kuti athandize ofalitsa kukhala alaliki aluso. Mlongo wina wa ku Denmark dzina lake Anna Larsen, amene wakhala wofalitsa kwa zaka pafupifupi 70, anati: “Yehova anatithandiza kukhala alaliki aluso kupyolela mu Sukulu ya Ulaliki ndi mabuku ogwilitsila nchito m’sukuluyi. Ndikumbukila kuti buku loyamba pamabukuwa linali lakuti Theocratic Aid to Kingdom Publishers (Cithandizo ca Teokalase kwa Ofalitsa Ufumu, limene linatuluka mu 1945. Lotsatila linali lakuti Equipped for Every Good Work (Okonzeka Kucita Nchito Iliyonse Yabwino), limene linatuluka mu 1946. Masiku ano tili ndi buku lakuti Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, limene linatuluka mu 2001. Zoonadi, Yehova watithandiza kukhala atumiki oyenelela kupyolela mu Sukulu ya Ulaliki ndi mabuku ena. (2 Akor. 3:5, 6) Kodi munalembetsa kale m’Sukulu ya Ulaliki? Kodi mumanyamula buku lanu la Pindulani popita ku misonkhano mlungu uliwonse ndi kutsatila wotsogoza sukulu pamene akuligwilitsila nchito? Ngati mumatelo, ndiye kuti mukulola Kristu kukuphunzitsani kukhala mlaliki waluso.—2 Akor. 9:6; 2 Tim. 2:15.

9, 10. Kodi mabuku athandiza bwanji panchito yobyala ndi kuthilila mbeu za coonadi?

9 Yehova watithandizanso kupyolela m’gulu lake potipatsa mabuku otithandiza kufotokoza ziphunzitso zazikulu za m’Baibulo. Mwacitsanzo, buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, limene linatuluka mu 1968, linathandiza kwambili pophunzitsa anthu coonadi. Utumiki wa Ufumu wa November 1968 unanena kuti: “Anthu oculuka akufuna buku la Coonadi, moti m’mwezi wa September abale anayamba kugwila nchito ndi usiku womwe kufakitale yosindikiza mabuku ya ku Brooklyn.” Nkhaniyo inanenanso kuti: “Panthawi inayake m’mwezi wa August tinacita kusindikiza mabuku ena oonjezela opitilila 1,500,000 kuti anthu onse ofuna mabukuwa alandile.” Podzafika mu 1982, tinali titatulutsa mabuku oposa 100 miliyoni m’zinenelo 116. Pazaka 14 kucokela mu 1968 mpaka 1982, buku la Coonadi linathandiza anthu oposa 1 miliyoni kukhala Mboni za Yehova. *

10 Mu 2005, buku lina lapadela lophunzitsila Baibulo linatuluka. Buku limeneli ndi lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni. Mabuku okwana 200 miliyoni afalitsidwa kale m’zinenelo 256. Kodi zotsatilapo zake zakhala zotani? Pa zaka 7 cabe, kucokela mu 2005 mpaka mu 2012, anthu pafupi-fupi 1,200,000 anakhala ofalitsa uthenga wabwino. Pa zaka zimenezi, ciŵelengelo ca anthu amene timaphunzila nao Baibulo cakwela kucoka pa anthu pafupifupi 6,000,000 kufika pa 8,700,000. Mosakaikila, Yehova wakhala akudalitsa khama lathu lobyala ndi kuthilila mbeu za Ufumu.—Ŵelengani 1 Akorinto 3:6, 7.

11, 12. Mogwilizana ndi Malemba omwe ali m’ndime izi, kodi magazini athu anali kuwakonzela magulu ati a anthu?

11 Magazini. Poyamba, magazini ya The Watch Tower inali kulembedwela anthu a “kagulu ka nkhosa” amene ndi “oitanidwa kumwamba.” (Luka 12:32; Aheb. 3:1) Pa October 1, 1919, gulu la Yehova linatulutsa magazini ina imene colinga cake cinali kufika pamtima anthu ena onse. Ophunzila Baibulo ndiponso anthu ena anali kukonda kwambili magazini imeneyo cakuti kwa zaka zambili inali kufalitsidwa kwambili kuposa Nsanja ya Mlonda. Poyamba, magaziniyo inali kuchedwa The Golden Age, koma mu 1937, inayamba kuchedwa Consolation. Ndiyeno mu 1946, inayamba kuchedwa Galamukani!

12 Kwa zaka zambili, maonekedwe ndi kalembedwe ka Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani zakhala zikusintha, koma colinga cake sicinasinthe. Colinga ca magazini amenewa ndi kulengeza Ufumu wa Mulungu ndi kutithandiza kukhulupilila kwambili Baibulo. Masiku ano, tili ndi Nsanja ya Mlonda yophunzila ndi yogaŵila. Nsanja ya Mlonda yophunzila amailembela “anchito ake apakhomo,” amene ndi “kagulu ka nkhosa” ndi a “nkhosa zina.” * (Mat. 24:45; Yoh. 10:16) Nsanja ya Mlonda yogaŵila amaikonzela anthu amene akalibe kudziŵa coonadi koma amalemekeza Baibulo ndi Mulungu. (Mac. 13:16) Galamukani! amailembela anthu amene sadziŵa zambili zokhudza Baibulo ndi Mulungu woona, Yehova.—Mac. 17:22, 23.

13. N’ciani cimakucititsani cidwi ndi magazini athu? (Kambilanani chati cakuti “Zofalitsa Zimene Zagaŵilidwa Padziko Lonse.”)

13 Pamene caka ca 2014 cinali kuyamba, magazini a Galamukani! oposa 44 miliyoni ndi a Nsanja ya Mlonda pafupifupi 46 miliyoni anali kusindikizidwa mwezi uliwonse. Magazini ya Galamukani inali kumasulidwa m’zinenelo pafupifupi 100, ndipo Nsanja ya Mlonda inali kumasulidwa m’zinenelo zoposa 200. Mwacionekele, magazini amenewa ndi amene amamasulidwa ndi kufalitsidwa kwambili padziko lonse lapansi kuposa magazini ena alionse. Ndipo izi n’zomveka, cifukwa magaziniwa ali ndi uthenga umene Yesu ananena kuti udzalalikidwa padziko lonse lapansi.—Mat. 24:14.

14. N’ciani cimene atumiki a Mulungu akhala akucita mwakhama? Nanga n’cifukwa ciani amacita zimenezo?

14 Baibulo. Mu 1896, M’bale Russell ndi anzake anasintha dzina la bungwe limene anali kugwilitsila nchito kusindikiza mabuku kuti liphatikizepo liu lakuti Baibulo. Bungwelo linayamba kudziŵika ndi dzina lakuti Watch Tower Bible and Tract Society. Kusinthaku kunali koyenelela cifukwa cakuti Baibulo ndilo cida cacikulu comwe takhala tikugwilitsila nchito kwambili pofalitsa uthenga wabwino wa Ufumu. (Luka 24:27) Mogwilizana ndi dzina la bungwe lalamulo limeneli, atumiki a Mulungu akhala akucita khama kufalitsa Baibulo ndi kulimbikitsa anthu kuti aziliŵelenga. Mwacitsanzo, mu 1926, pamakina athu tinasindikiza Baibulo lakuti The Emphatic Diaglott, la Malemba Acigiliki Acikristu lolembedwa ndi Benjamin Wilson. Kuyambila mu 1942, tinasindikiza ndi kugaŵila makope pafupifupi 700,000 a Baibulo lathunthu lochedwa King James Version. Patangopita zaka ziŵili, tinayamba kusindikiza Baibulo lakuti American Standard Version, limene lili ndi dzina lakuti Yehova m’malo okwanila 6,823. Podzafika mu 1950, tinali titagaŵila Mabaibulo oposa 250,000.

15, 16. (a) N’ciani cimakusangalatsani ndi Baibulo Ladziko Latsopano? (Kambilanani bokosi lakuti “Kufulumizitsa Nchito Yomasulila Baibulo.”) (b) Kodi muyenela kucita ciani kuti Yehova akhudze mtima wanu?

15 Mu 1950, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Acigiliki Acikristu lacingelezi linatuluka. Ndipo Baibulo lathunthu lacingelezi la Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika linatuluka mu 1961. Baibulo limeneli limalemekeza Yehova cifukwa linabwezeletsa dzina lake m’malo ake enieni mogwilizana ndi Malemba oyambilila aciheberi. Dzina la Mulungu limapezekanso nthawi zokwana 237 m’Malemba Acigiliki Acikristu. Kuti atsimikizile kuti Baibulo la Dziko Latsopano ndi lolondola ndiponso losavuta kuŵelenga, Baibulo limeneli lakonzedwa kangapo, ndipo posacedwapa, mu 2013 linakonzedwanso. Pofika m’cakaci, makope oposa 201 miliyoni a Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu kapena mbali yake anafalitsidwa m’zinenelo 121.

16 Kodi anthu ena akamba ciani pambuyo poŵelenga Baibulo la Dziko Latsopano m’cinenelo cao? Mwamuna wina wa ku Nepal anati: “Zinali zovuta kwa anthu ambili kuti amvetsetse Baibulo lakale la Cinapali cifukwa cakuti mau ake ndi acikale. Koma tsopano n’zosavuta kumvetsetsa Baibulo cifukwa linalembedwa mogwilizana ndi mmene anthu amalankhulila masiku ano.” Mai wina wa ku Central African Republic atayamba kuŵelenga Baibulo la Cisango, analila ndi kunena kuti: “Cinenelo cimene cili m’Baibulo ili candikhudza mtima kwambili.” Mofanana ndi mai ameneyu, aliyense wa ife angalole Yehova kum’khudza mtima mwa kuŵelenga Mau ake tsiku lililonse.—Sal. 1:2; Mat. 22:36, 37.

Kuyamikila Zida ndi Maphunzilo Amene Tapatsidwa

17. Mungasonyeze bwanji kuti mumayamikila zida ndi maphunzilo amene mumapatsidwa? Ndi mapindu otani amene mungapeze mukacita zimenezo?

17 Kodi inuyo mumayamikila zida ndi maphunzilo amene Mfumu Yesu Kristu wakhala akutipatsa? Kodi mumapatula nthawi yoŵelenga zofalitsa zimene gulu la Mulungu limapeleka ndi kuzigwilitsila nchito pothandiza ena? Ngati mumatelo, ndiye kuti mungavomeleze mau a mlongo Opal Betler amene anabatizidwa pa October 4, 1914. Iye anati: “Kwa zaka zambili, ine ndi mwamuna wanga [Edward] tinali kugwilitsila nchito galamafoni ndi makadi aulaliki. Tinali kugwilitsila nchito mabuku, tumabuku, ndi magazini polalikila nyumba ndi nyumba. Tinali kuyenda maulendo apadela okalalikila, ndipo tinali kugaŵila tumapepala twa uthenga. M’kupita kwa nthawi, tinaphunzitsidwa kupanga maulendo obwelelako ndi kucititsa maphunzilo a Baibulo kwa anthu acidwi. Pa umoyo wathu takhala ndi zocita zambili ndiponso osangalala.” Yesu ananena kuti atumiki ake adzatangwanika ndi nchito yobyala mbeu za coonadi ndi kukolola, ndipo adzasangalala pamodzi cifukwa ca nchitoyi. Mofanana ndi Opal, anthu mamiliyoni ambili adzionela okha kuti mau a Yesu amenewa ndi oona.—Ŵelengani Yohane 4:35, 36.

18. Ndi mwai waukulu uti umene tili nao?

18 Anthu ambili amene akalibe kukhala atumiki a Mfumu amaona kuti anthu a Mulungu ndi “osaphunzila ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Koma n’zocititsa cidwi kuti Mfumuyo yakhala ikugwilitsila nchito anthu wambawo kusindikiza mabuku amene afalitsidwa kwambili kuposa mabuku ena alionse. Koma koposa zonse, Mfumuyi yatiphunzitsa ndi kutilimbikitsa kugwilitsila nchito zida zimenezi pofalitsa uthenga wabwino kwa anthu a mitundu yonse. Ndi mwai wamtengo wapatali kwambili kugwila nchito limodzi ndi Kristu yobyala mbeu za coonadi ndi kukolola ophunzila.

^ par. 2 Pa zaka 10 zokha zapitazi, atumiki a Yehova asindikiza mabuku oposa 20 biliyoni ophunzilila Baibulo. Kuonjezela pamenepo, anthu oposa 2.7 biliyoni amatha kugwilitsila nchito Webu saiti yathu ya jw.org.

^ par. 9 Mabuku ena amene athandiza ofalitsa kuphunzitsa anthu Baibulo ndi awa: Zeze wa Mulungu (lofalitsidwa mu 1921), “Mulungu Akhale Oona” (lofalitsidwa mu 1946), Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha (lofalitsidwa mu 1982), ndi Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha (lofalitsidwa mu 1995).

^ par. 12 Onani Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013, tsamba 29, ndime 13. Mu Nsanja ya Mlonda imeneyi muli kamvedwe katsopano ponena za anthu amene ali m’gulu la “anchito ake apakhomo.”