Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 13

Alaliki a Ufumu Amapeleka Milandu Yao ku Khoti

Alaliki a Ufumu Amapeleka Milandu Yao ku Khoti

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Monga mmene Yesu analoselela, nthawi zina anthu ake amaimbidwa milandu cifukwa ca nchito yao yolalikila

1, 2. (a) Kodi atsogoleli acipembedzo anacita ciani ndi nchito yolalikila? Nanga atumwi anacita ciani? (b) N’cifukwa ciani atumwi anakana kumvela lamulo loletsa kulalikila?

MPINGO wacikristu utangokhazikitsidwa kumene ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E., Satana anaukila mpingowo. Iye anali kufuna kufafaniza mpingowo usanakule ndi kulimba. Mosataya nthawi, Satana mwamacenjela anasonkhezela atsogoleli acipembedzo kuti aletse nchito yolalikila za Ufumu. Koma atumwi anapitilizabe kulalikila molimba mtima, ndipo amuna ndi akazi ambili anakhala “okhulupilila Ambuye.”—Mac. 4:18, 33; 5:14.

Atumwi anasangalala “cifukwa cakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenela kucitilidwa cipongwe cifukwa ca dzina la Yesu”

2 Otsutsawo anakwiya kwambili ndipo anaukilanso atumwiwo. Panthawiyo, io anaika atumwi onse m’ndende. Koma usiku wa tsikulo, mngelo wa Yehova anatsegula zitseko za ndendeyo ndi kutulutsa atumwiwo. Ndipo m’mamawa kutaca, io anayambanso kulalikila. Zitatelo, adani ao anawagwilanso ndi kuwatengela kwa olamulila amene anawaimba mlandu wophwanya lamulo loletsa kulalikila. Poyankha, atumwi anakamba molimba mtima kuti: “Ife tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.” Atamva zimenezi, olamulilawo anakwiya kwambili cakuti anafuna “kungowapha” atumwiwo. Koma panthawi yovutayo, Gamaliyeli, yemwe anali mphunzitsi wa Cilamulo wolemekezedwa anacenjeza olamulilawo kuti: “Musamale . . . Alekeni amuna amenewa musalimbane nao.” Zodabwitsa n’zakuti olamulilawo anamvela malangizo ake, ndipo anamasula atumwiwo. Kodi amuna okhulupilikawo anacita ciani? Mopanda mantha, io anapitilizabe “mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Kristu, Yesu.”—Mac. 5:17-21, 27-42; Miy. 21:1, 30.

3, 4. (a) Kodi Satana wakhala akugwilitsila nchito njila iti poukila anthu a Mulungu? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino ndi m’nkhani ziŵili zotsatila?

3 Zimenezi zinacitika mu 33 C.E, ndipo aka kanali koyamba kuti olamulila otsutsa atengele mpingo wacikristu kukhoti. Koma ici cinali ciyambi cabe ca milandu yotelo. (Mac. 4:5-8; 16:20; 17:6, 7) Masiku ano, Satana amasonkhezelabe anthu otsutsa kulambila koona kuti acititse olamulila a boma kuletsa nchito yathu yolalikila. Otsutsawo akhala akuimba milandu anthu a Mulungu m’njila zosiyanasiyana. Iwo amanena kuti timasokoneza mtendele m’dziko, kapena kuti ndife anthu ovutitsa. Ena amanena kuti ndife anthu oukila boma, ndipo enanso amanena kuti ndife anthu amalonda. Nthawi zina, abale athu akhala akupita kukhoti kuti akapeleke umboni wotsutsa zimene anali kuwaneneza. Kodi zotsatila za milandu ya kukhotiyo zakhala zotani? Kodi ziweluzo zimene zinapelekedwa ku makhoti zaka zambili zapitazo zimakukhudzani bwanji inuyo panokha? Tiyeni tikambilane milandu ingapo ya kukhoti kuti tione mmene yathandizila “pa kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.”—Afil. 1:7.

4 M’nkhani ino tikambilana zimene tacita poteteza ufulu wathu wolalikila. M’nkhani ziŵili zotsatila tidzakambilana zimene tacita pomenyela ufulu wathu n’colinga cakuti tipitilizebe kumvela Ufumu wa Mulungu ndi kukhalabe olekana ndi dziko.

Timacilikiza Ufumu wa Mulungu Mokhulupilika Osati Kusokoneza Mtendele

5. Cakumapeto kwa zaka za m’ma 1930, n’cifukwa ciani alaliki a Ufumu anali kumangidwa? Nanga abale otsogolela anaganiza zocita ciani?

5 Cakumapeto kwa zaka za m’ma 1930, akuluakulu a mizinda ndi madela m’dziko la United States of America anayesa kuumiliza a Mboni za Yehova kuti azikatenga mapepala acilolezo ku boma akafuna kulalikila. Koma abale athu anakana kucita zimenezo. Iwo anali kudziŵa kuti mapepalawo angalandidwe. Anali kukhulupilanso kuti palibe boma limene lili ndi mphamvu yoletsa Akristu kugwila nchito yolalikila uthenga wa Ufumu imene Yesu analamula. (Maliko 13:10) Zotsatilapo zake zinali zakuti alaliki ambili a Ufumu anamangidwa. Ataona zimenezi, abale amene anali kutsogolela gulu panthawiyo anaganiza zopeleka nkhaniyi ku khoti. Iwo anali kufuna kukapeleka umboni wakuti Bomalo linaphwanya ufulu wolambila wa Mboni za Yehova. M’caka ca 1938, panacitika cinthu cina cimene cinapangitsa kuti pakhale mlandu waukulu wa kukhoti umene unasintha zinthu. N’ciani cinacitika?

6, 7. N’ciani cinacitikila banja la M’bale Cantwell?

6 Paciŵili m’mawa, pa April 26, 1938, m’bale Newton Cantwell wa zaka 60 ndi mkazi wake, Esther, ndiponso ana ake aamuna atatu, Henry, Russell, ndi Jesse anapita mu mzinda wa New Haven, m’dela la Connecticut. Onse 5 anali apainiya apadela. Iwo anali kudziŵa kuti sadzabwelela kunyumba tsiku lomwelo. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anali atamangidwapo moti anali kudziŵa kuti nthawi ina iliyonse angamangidwenso. Ngakhale zinali conco, m’bale Cantwell ndi banja lake anali kufunitsitsabe kulalikila uthenga wa Ufumu. Iwo anagwilitsila nchito magalimoto aŵili paulendo wao wopita ku New Haven. M’bale Cantwell anali kuyendetsa galimoto imene inanyamula mabuku ofotokoza Baibulo ndi magalamafoni, ndipo Henry yemwe anali ndi zaka 22, anali kuyendetsa galimoto imene inali ndi zokuzila mau. Monga mmene anali kuganizila, anakumana ndi apolisi patangopita maola oŵelengeka.

7 Poyamba, apolisiwo anagwila Russell, amene anali ndi zaka 18, kenako anagwilanso m’bale ndi mlongo Cantwell. Ali capatali ndithu, Jesse, amene anali ndi zaka 16, anali kuona pamene apolisi anali kutenga makolo ake ndi acibale ake. Henry anali kulalikila m’dela lina la mzindawo. Conco, Jesse, yemwe anali wang’ono pa onse anangotsala yekha. Ngakhale zinali conco, iye anatenga galamafoni yake ndi kupitiliza kulalikila. Amuna aŵili acikatolika anamulola kuti atsegule galamafoniyo kuti amvetsele nkhani ya M’bale Rutherford ya mutu wakuti “Adani.” Koma pamene anali kumvetsela, amunawo anakwiya kwambili cakuti anafuna kumumenya. Jesse anangocokapo mwaulemu, koma patangopita kanthawi kocepa anakumana ndi apolisi. Iwo anamugwilanso ndi kupita naye kupolisi. Apolisiwo anaona kuti mlongo Cantwell analibe mlandu, koma M’bale Cantwell ndi ana ake aamuna anawapeza ndi mlandu. Komabe, abalewo anamasulidwa tsiku lomwelo pabelo.

8. N’cifukwa ciani khoti linapeza Jesse Cantwell ndi mlandu wakuti anali munthu wovutitsa?

8 Patapita miyezi yocepa, mu September 1938, banja la m’bale Cantwell linakaonekela ku khoti la mu mzinda wa New Haven. M’bale Cantwell, Russell, ndi Jesse anawapeza ndi mlandu wopemphapempha ndalama kwa anthu popanda cilolezo. Ngakhale kuti abale anacita apilo ku khoti lalikulu la Connecticut, Jesse anamupeza ndi mlandu wakuti anali wosokoneza mtendele kapena kuti munthu wovutitsa. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti amuna aŵili aja amene anamvetsela nkhani ya pa galamafoni ananena kuti nkhaniyo inali kunyoza cipembedzo cao ndipo inawakwiitsa. Abale amene anali kutsogolela gulu sanakhutile ndi ciweluzoco. Conco anacita apilo ku khoti lalikulu kwambili m’dziko la United States.

9, 10. (a) Kodi Khoti lalikulu ku United States linaweluza bwanji mlandu wa M’bale Cantwell ndi banja lake? (b) Timapindula bwanji ndi ciweluzo cimene cinapelekedwa?

9 Kuyambila pa March 29, 1940, woweluza wamkulu Charles E. Hughes ndi oweluza ena 8, anayamba kumvetsela zolankhula za M’bale Hayden Covington. M’baleyu anali loya woimila Mboni za Yehova. * Pamene loya wa boma wa dela la Connecticut anakamba mfundo zake pofuna kutsimikizila kuti Mboni za Yehova ndi anthu ovutitsa, woweluza wina anamufunsa kuti: “Kodi si zoona kuti anthu ambili anali kukhumudwa ndi uthenga umene Yesu Kristu anali kulengeza?” Loya wa bomayo anayankha kuti: “Inde, anali kukhumudwa, ndipo ngati ndikukumbukila bwino, Baibulo limafotokozanso zimene zinacitikila Yesu cifukwa colalikila uthengawo.” Mau amenewa anavumbula zambili. Mosadziŵa, loyayo anasonyeza kuti Mboni za Yehova zinali monga Yesu, ndipo bomalo linali monga anthu amene anamuweluza. Pa May 20, 1940, Khotilo linapeleka cigamulo cokomela Mboni.

M’bale Hayden Covington (kutsogolo, pakati), M’bale Glen How (kumanzele), ndi anthu ena akutuluka m’khoti atapambana mlandu

10 Kodi cigamulo ca Khoti cimeneco cinali capadela m’njila yotani? Cinali capadela cifukwa cinathandiza kuti olamulila a boma kapena a madela osiyanasiyana a m’dzikolo azilemekeza ufulu wa kulambila umene munthu aliyense ali nao. Kuonjezela pamenepo, Khotilo linaona kuti Jesse “sanacite . . . ciliconse cosokoneza mtendele.” Conco, cigamuloco cinasonyezelatu kuti Mboni za Yehova si anthu osokoneza mtendele. Cigamulo cimeneco cinali capadela kwambili kwa atumiki a Mulungu. Kodi tikupindula bwanji ndi cigamuloci masiku ano? Loya wina amenenso ndi wa Mboni za Yehova anati: “Ufulu wa kulambila umene ife a Mboni tili nao masiku ano umatipatsa mwai wolalikila uthenga wa ciyembekezo kwa anthu m’madela athu.”

Ndife Alengezi a Coonadi Osati Oukila Boma

Quebec’s Burning Hate for God and Christ and Freedom Is the Shame of All Canada

11. Ndi nchito yapadela iti imene abale athu anagwila ku Canada? Ndipo n’cifukwa ciani?

11 M’zaka za m’ma 1940, Mboni za Yehova ku Canada zinakumana ndi citsutso coopsa. Motelo, mu 1946, abale athu kumeneko anagwila nchito kwa masiku 16 yogaŵila kapepala kauthenga kapadela, (Quebec’s Burning Hate for God and Christ and Freedom Is the Shame of All Canada) n’colinga cakuti asonyeze kuti Boma la dzikolo linali kuphwanya ufulu wao wa kulambila. Kapepala ka masamba anai kameneko kanaulula kuti atsogoleli acipembedzo ndi amene anali kusonkhezela anthu kuukila Mboni za Yehova, kupangitsa apolisi kuwacitila nkhanza ndiponso kuti magulu aciwawa azivutitsa abale athu m’cigawo ca Quebec. Kapepalako kananenso kuti, “Apolisi akupitilizabe kumanga Mboni za Yehova popanda cifukwa, ndipo pali milandu pafupifupi 800 imene Mboni za Yehova zikuimbidwa ku Greater Montreal.”

12. (a) Kodi anthu otsutsa anamva bwanji ndi nchito yapadela yogaŵila kapepala kauthenga? (b) Kodi abale athu anaimbidwa mlandu wotani? (Onani mau amunsi.)

12 Ataona zimenezi, Mtsogoleli wa cigawo ca Quebec, dzina lake Maurice Duplessis, mogwilizana ndi Kadinala Villeneuve wa Chalichi ca Roma Katolika, analengeza kuti “adzakhaulitsa Mboni za Yehova mopanda cifundo.” Conco, ciŵelengelo ca milandu ya Mboni cinakwela mofulumila kucoka pa 800 kufika pa 1,600. Mlongo wina amene anali mpainiya anati: “Apolisi anatigwila maulendo ambilimbili cakuti sitingathe kukumbukila kuti anatigwila kangati.” Mboni za Yehova zimene zinapezeka zikugaŵila kapepalako zinaimbidwa mlandu wofalitsa “nkhani zabodza.” *

13. Ndani anali oyamba kuimbidwa mlandu woukila boma? Nanga khoti linapeleka ciweluzo cotani?

13 Mu 1947, M’bale Aimé Boucher ndi ana ake aakazi Gisèle, wa zaka 18, ndi Lucille, wa zaka 11, anali oyamba kuimbidwa mlandu woukila boma. Koma anthu amenewo sanali ovutitsa. Iwo anagaŵila kapepala kapadelako (Quebec’s Burning Hate) pafupi ndi famu yao m’dela lakumapili kumwela kwa mzinda wa Quebec. Mbale Boucher anali munthu wodzicepetsa ndi wofatsa amene anali kugwila nchito pa famu yake yaing’ono, ndipo nthawi zina anali kupita ku Quebec pa hosi yake imene inali kukoka kangolo. Ngakhale zinali conco, a m’banja la m’baleyu anacitilidwa zinthu zankhanza zimene zinachulidwa m’kapepalako. Woweluza wa khotilo, yemwe anali kudana ndi Mboni, anakana umboni wosonyeza kuti M’bale Boucher ndi ana ake ndi osalakwa. M’malomwake, iye anagwilizana ndi zonena za anthu zakuti kapepalako kanali kusonkhezela ciwawa, ndi kuti m’bale Boucher ndi ana ake ali ndi mlandu. Mwacidule tinganene kuti woweluzayo anali kutanthauza kuti, kukamba zoona n’kulakwa. M’bale Boucher ndi Gisèle anawapeza ndi mlandu wofalitsa nkhani zabodza, zolimbikitsa anthu kugalukila boma. Ngakhale Lucille, yemwe anali wacicepele anagona kupolisi masiku aŵili. Abale anacita apilo ku khoti lalikulu kwambili m’dziko la Canada, ndipo khotilo linavomela kuweluza nkhaniyo.

14. Kodi abale ku Quebec anacita ciani panthawi yacizunzo?

14 Panthawiyo, abale ndi alongo athu olimba mtima ku Quebec anapitiliza kulalikila uthenga wa Ufumu ngakhale kuti anali kuzunzidwa mwankhanza. Nthawi zambili zotsatilapo zake zinali zabwino. N’zocititsa cidwi kuti pambuyo pa zaka zinai kucokela pamene nchito yogaŵila kapepalako inayamba mu 1946, ciŵelengelo ca Mboni ku Quebec cinakwela kucoka pa 300 kufika pa 1,000. *

15, 16. (a) Ndi ciweluzo cotani cimene Khoti lalikulu ku Canada linapeleka pa mlandu wa M’bale Boucher ndi banja lake? (b) Kodi abale ndi anthu ena anakhudzidwa bwanji ndi cipambano cimeneco?

15 Mu June 1950, oweluza 9 a Khoti lalikulu ku Canada anaweluza nkhani ya M’bale Aimé Boucher. Pambuyo pa miyezi 6, pa December 18, 1950, Khotilo linapeleka cigamulo cokomela Mboni za Yehova. N’cifukwa ciani linatelo? M’bale Glen How, yemwe anali loya wa Mboni, anafotokoza kuti Khotilo linavomeleza kuti “kuukila” kumatanthauza kucita kapena kukamba zinthu zoyambitsa ciwawa kapena kupandukila boma. Koma kapepalako “sikanakambe zinthu zotelo. Kanangofotokoza zinthu mogwilizana ndi ufulu wa kulankhula umene anthu ali nao.” M’bale How ananenanso kuti: “Ndinadzionela ndekha mmene Yehova anatithandizila kuti tipambane mlanduwo.” *

16 Cigamulo ca Khoti lalikulu cimeneco cinali cipambano cosaiwalika ca Ufumu wa Mulungu. Cigamuloco cinapangitsa kuti milandu ina 122 imene Mboni za Yehova zinali kuimbidwa ku Quebec ithetsedwe. Cigamuloco cinapangitsanso kuti nzika za ku Canada ndi za m’maiko ena a m’bungwe la British Commonwealth zikhale ndi ufulu wopeleka madandaulo ao ku boma. Kuonjezela apo, cigamuloco cinalepheletsa colinga ca atsogoleli acipembedzo ndi akuluakulu a boma ku Quebec cofuna kuletsa Mboni za Yehova kulambila mwaufulu. *

Ndife Alaliki Acangu a Ufumu wa Mulungu Osati Amalonda

17. Kodi maboma ena amayesa bwanji kusokoneza nchito yathu yolalikila?

17 Mofanana ndi Akristu oyambilila, atumiki a Yehova masiku ano sacita nao malonda mau a Mulungu. (Ŵelengani 2 Akorinto 2:17.) Komabe, maboma ena amafuna kusokoneza nchito yathu yolalikila mwa kugwilitsila nchito malamulo a zamalonda. Tsopano tiyeni tikambilane milandu iŵili ya kukhoti imene zigamulo zake zinasonyeza kuti Mboni za Yehova si anthu amalonda koma ndi atumiki a Mulungu.

18, 19. N’ciani cimene akuluakulu a boma ku Denmark anacita pofuna kusokoneza nchito yolalikila?

18 Ku Denmark. Pa October 1, 1932, m’dziko la Denmark anakhazikitsa lamulo loletsa anthu kugulitsa mabuku popanda kalata yacilolezo ca boma. Koma abale athu anaona kuti si bwino kukatenga cilolezoco. Tsiku lotsatila, ofalitsa asanu anathela tsiku lonse akulalikila m’tauni ya Roskilde imene ili pa mtunda wa makilomita oposa 30 kucokela kumadzulo kwa mzinda wa Copenhagen, likulu la dzikolo. M’madzulo a tsikulo, mmodzi mwa ofalitsa dzina lake August Lehmann sanaonekele. Iye anali atagwidwa ndi apolisi cifukwa coomboletsa mabuku popanda cilolezo.

19 Pa December 19, 1932, August Lehmann anakaonekela ku khoti. Iye anavomela kuti anali kugaŵila anthu mabuku ofotokoza Baibulo, koma anakana zakuti anali kugulitsa mabuku. Oweluza a khotilo anavomeleza zimenezi, ndipo anati: “Munthu ameneyu . . . amatha kudzipezela ndalama. Ndipo nchito yakeyi sinam’pindulitse mwanjila iliyonse, komanso alibe colinga cofuna kupeza ndalama iliyonse. Mmalomwake, nchitoyi yamutaitsa ndalama.” Poweluza mokomela Mboni, Khotilo linanena kuti zimene Lehmann anali kucita “si malonda.” Komabe adani a anthu a Mulungu anali otsimikiza mtima kuletsa nchito yolalikila m’dzikolo. (Sal. 94:20) Loya wa boma anacita apilo ku Khoti lalikulu m’dzikolo. Kodi abale athu anacita ciani?

20. Ndi cigamulo cotani cimene Khoti lalikulu ku Denmark linapeleka? Nanga abale athu anacita ciani?

20 Patatsala mlungu umodzi kuti Khotilo liweluze mlanduwo, Mboni za Yehova ku Denmark zinagwila nchito yolalikila mwacangu kwambili. Pa Laciŵili, October 3, 1933, Khotilo linapeleka cigamulo comwe cinagwilizana ndi ca khoti laling’ono. Cigamuloco cinali cakuti m’bale August Lehmann sanaphwanye lamulo loletsa kugulitsa malonda popanda cilolezo. Zimenezi zinatanthauza kuti Mboni za Yehova zinali ndi ufulu wopitiliza kulalikila. Pofuna kuyamikila Yehova cifukwa cowathandiza kupambana mlanduwu, abale ndi alongo anaonjezelanso cangu cao pa nchito yolalikila. Kucokela nthawi imene Khotilo linapeleka ciweluzoco, abale athu ku Denmark akhala akulalikila popanda citsutso ciliconse ca boma.

Mboni zolimba mtima ku Denmark m’ma 1930

21, 22. Kodi Khoti lalikulu ku United States linagamula bwanji mlandu wa M’bale Murdock?

21 Ku United States. Pa Sondo pa February 25, 1940, mpainiya wina dzina lake Robert Murdock, Jr., ndi Mboni zina 7, anagwidwa ndi apolisi pamene anali kulalikila mu mzinda wa Jeannette, umene uli pafupi ndi Pittsburgh, m’dela la Pennsylvania. Iwo anawapeza ndi mlandu wogaŵila mabuku popanda kalata yacilolezo. Atacita apilo ku Khoti lalikulu kwambili m’dziko la United States, Khotilo linavomela kuweluza mlanduwo.

22 Pa May 3, 1943, Khoti Lalikulu linapeleka ciweluzo cokomela Mboni. Khotilo linakana kuti munthu azitenga cilolezo cifukwa cakuti potenga cilolezoco anali kufunika kulipila “ndalama, ndipo zimenezi zinali kuphwanya ufulu wa kulambila mosiyana ndi malamulo a m’dzikolo.” Khotilo linathetsa lamulo la mumzinda wa Jeannette, ndipo linanena kuti lamulolo “linaphwanya ufulu umene anthu ali nao wofalitsa nkhani ndi kulambila.” Pofotokoza mmene anthu ambili anaonela nkhaniyo m’Khotilo, Woweluza wamkulu dzina lake William O. Douglas anakamba kuti nchito ya Mboni za Yehova “ndi kulalikila komanso kugaŵila mabuku.” Iye anapitiliza kuti: “Kucita zimenezi n’kofanana . . . ndi kupemphela m’chalichi ndiponso kulalikila pa guwa.”

23. Timapindula bwanji ndi zigamulo zimene zinapelekedwa mu 1943?

23 Cigamulo ca Khoti lalikulu cimeneci cinali cipambano cacikulu kwambili kwa anthu a Mulungu. Cinatsimikizila kuti ndife atumiki acikristu osati anthu amalonda. Pa tsiku losaiwalika limenelo mu 1943, Mboni za Yehova zinapambana milandu 12 pa milandu 13 m’Khotilo, kuphatikizapo mlandu wa M’bale Murdock. Zigamulozi zakhala zitsanzo poweluza milandu yaposacedwapa panthawi imene anthu otsutsa ayetsa kuimitsa nchito yolalikila uthenga wa Ufumu poyela ndi ku nyumba ndi nyumba.

“Ife Tiyenela Kumvela Mulungu Monga Wolamulila, Osati Anthu”

24. Timacita ciani ngati boma laletsa nchito yathu yolalikila?

24 Monga atumiki a Yehova, timayamikila kwambili boma likatipatsa ufulu wolalikila uthenga wa Ufumu. Koma boma likaletsa nchito yathu yolalikila, timasintha njila zolalikilila ndi kupitilizabe kulalikila mwa njila zina. Mofanana ndi atumwi, “tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.” (Mac. 5:29; Mat. 28:19, 20) Komabe, timapeleka nkhaniyo ku khoti kuti acotse ciletso pa nchito yathu. Onani zitsanzo ziŵili izi.

25, 26. N’zocitika ziti zimene zinapangitsa kuti abale acite apilo ku Khoti lalikulu ku Nicaragua? Nanga zotsatila zake zinali zotani?

25 Ku Nicaragua. Pa November 19, 1952, m’bale Donovan Munsterman, yemwe anali mmishonale ndiponso woyang’anila nthambi, anapita ku Ofesi Yoona za Oloŵa ndi Kutuluka M’dziko ku Managua, likulu la dziko la Nicaragua. Iye analamulidwa kuti akaonane ndi Arnoldo García amene anali woyang’anila ofesiyo. Woyang’anila ofesiyo anauza m’bale Munsterman kuti Mboni za Yehova m’dzikolo “sizikuloledwa kulalikila ziphunzitso zao kapena kucita zinthu zokhudza kulambila.” M’baleyo atafunsa cifukwa cake, woyang’anila ofesiyo anakamba kuti Mboni za Yehova zinalibe cilolezo ca boma cogwilila nchito yao yolalikila ndiponso kuti anthu anali kuwaganizila kuti ndi a cipani ca Cikomyunizimu. Ndani anali kuwaneneza? Anali atsogoleli a Chalichi ca Roma Katolika.

Abale ku Nicaragua panthawi ya ciletso

26 Pasanapite nthawi yaitali, M’bale Munsterman anapita ku ofesi ya Unduna Woona za Boma ndi Zacipembedzo, ndiponso kwa Pulezidenti Anastasio Somoza García kukapempha kuti acotse ciletsoco, koma sizinathandize. Conco, abale anasintha zocita zao. Iwo anatseka Nyumba za Ufumu, ndipo anayamba kusonkhana m’tumagulu tung’onotung’ono. Ndiponso analeka kulalikila poyela, koma anapitilizabe kulalikila uthenga wa Ufumu mwa njila zina. Panthawi imodzimodziyo, io analemba kalata yopempha Khoti lalikulu ku Nicaragua kuti lithetse ciletsoco. Manyuzipepala ambili anafalitsa za ciletsoco ndi zimene zinali m’kalata imene abale analemba. Conco, Khotilo linavomela kuweluza nkhani yokhudza ciletsoco. Kodi zotsatila zake zinali zotani? Pa June 19, 1953, Khoti lalikulu linapeleka cigamulo cokomela Mboni za Yehova. Khotilo linaona kuti ciletsoco cinali kuphwanya ufulu wolankhula, wotsatila cikumbumtima, ndi ufulu wa kulambila. Khotilo linalamulanso kuti boma la Nicaragua likhale pa unansi wabwino ndi Mboni za Yehova.

27. N’cifukwa ciani anthu a ku Nicaragua anadabwa ndi cigamulo ca Khoti lalikulu? Nanga abale anaciona bwanji cigamuloco?

27 Anthu a ku Nicaragua anadabwa kuti Khotilo linapeleka cigamulo cokomela a Mboni. Izi zisanacitike, atsogoleli acipembedzo anali ndi mphamvu kwambili cakuti Khotilo linali kuwaopa. Naonso akuluakulu a bomalo anali ndi mphamvu kwambili moti kaŵilikaŵili Khotilo linali kuopa kutsutsana nao. Abale athu anali kukhulupilila kuti anapambana mlanduwo mothandizidwa ndi Mfumu yao, ndipo anapitiliza kulalikila.—Mac. 1:8.

28, 29. Kodi zinthu zinasintha bwanji ku Zaire m’zaka za m’ma 1980?

28 Ku Zaire. Ca m’ma 1980, m’dziko la Zaire, limene tsopanso limachedwa Democratic Republic of Congo, munali Mboni pafupifupi 35,000. Cifukwa ca kupita patsogolo kwa zinthu za Ufumu m’dzikolo, abale anali kumanga maofesi ena panthambi. Mu December, 1985, abale anacita msonkhano wa maiko ku Kinshasa, likulu la dzikolo. Anthu 32,000 ocokela m’maiko osiyanasiyana anapezeka pamsonkhanowo umene unacitikila pa sitediyamu ya mumzindawo. Koma zinthu zinayamba kusintha pakati pa atumiki a Yehova. Kodi cinacitika n’ciani?

29 Panthawiyo, M’bale Marcel Filteau, yemwe anali mmishonale wocokela ku Quebec, m’dziko la Canada, amene anakumanapo ndi cizunzo mu ulamulilo wa Duplessis anali kutumikila ku Zaire. Iye anafotokoza zimene zinacitika: “Pa March 12, 1986, abale otsogolela m’dzikolo analandila kalata yonena kuti gulu la Mboni za Yehova ndi loletsedwa m’dziko la Zaire.” Kalata ya ciletsoyo inasainidwa ndi pulezidenti wa dzikolo, Mobutu Sese Seko.

30. Ndi cosankha cacikulu citi cimene Komiti ya Nthambi m’dziko la Zaire inafunika kupanga? Koma io anaganiza zocita ciani?

30 Tsiku lotsatila, wailesi yaboma m’dzikolo inalengeza kuti: “Sitidzamvanso za Mboni za Yehova mu [Zaire].” Nthawi yomweyo cizunzo cinayamba. Nyumba za Ufumu zinaonongedwa, ndipo abale athu analandidwa katundu, kugwidwa ndi apolisi, kuikidwa m’ndende, ndi kumenyedwa. Ngakhale ana a Mboni anaikidwa m’ndende. Pa October 12, 1988, boma linalanda katundu wa gulu lathu ndiponso gulu lina la asilikali linayamba kukhala m’nyumba za ku nthambi. Abale otsogolela gulu m’dzikolo anacondelela Pulezidenti Mobutu kuti acotse ciletsoco, koma sanawayankhe. Panthawiyo, abale a m’Komiti ya Nthambi anafunika kupanga cosankha cacikulu. Iwo anafunika kusankha kaya “kupeleka nkhaniyo ku Khoti Lalikulu kapena kuyembekezela.” M’bale Timothy Holmes, amene anali mmishonale ndiponso wogwilizanitsa Komiti ya Nthambi m’dzikolo, anati: “Tinadalila Yehova kuti atipatse nzelu ndi kutitsogolela.” Abale a m’komitiyo atapemphela ndi kukambilana nkhaniyo, anaona kuti nthawi yabwino yopita kukhoti inali isanakwane. M’malomwake, io anaika maganizo ao pa kusamalila abale ndi kufunafuna njila zothandiza kuti apitilize kulalikila.

“Panthawi ya mlanduwo, tinaona mmene Yehova amasinthila zinthu”

31, 32. Ndi cigamulo cocititsa cidwi citi cimene Khoti lalikulu ku Zaire linagamula? Kodi abale athu anakhudzidwa bwanji ndi cigamuloco?

31 Patapita zaka zingapo, cizunzo cinayamba kucepa, ndipo boma la m’dzikolo linayamba kulemekeza ufulu wa anthu. Conco, abale a m’Komiti ya Nthambi m’dzikolo anaona kuti nthawi yakwana yakuti acite apilo nkhaniyo ku Khoti Lalikulu. N’zocititsa cidwi kuti Khotilo linavomela kuweluza nkhaniyo. Pa January 8, 1993, pambuyo pa zaka pafupifupi 7 kucokela pamene pulezidenti anaika ciletso, Khotilo linalamula kuti boma linaphwanya malamulo poletsa Mboni za Yehova kulambila mwaufulu, ndipo ciletsoco cinacotsedwa. Koma kupeleka cigamulo cimeneci sikunali kopepuka. Mwa kuthetsa lamulo limene pulezidenti anaika m’dzikolo, oweluza a Khotilo anaika miyoyo yao pangozi. M’bale Holmes anati: “Panthawi ya mlanduwo, tinaona mmene Yehova amasinthila zinthu.” (Dan. 2:21) Cikhulupililo ca abale cinalimba kwambili pamene tinapambana mlanduwo. Iwo anaona kuti Mfumu Yesu, inathandiza anthu ake kudziŵa nthawi yoyenela yothetsela nkhaniyo ndi mmene angaithetsele.

Mboni za Yehova ku Democratic Republic of Congo zikusangalala cifukwa cakuti zili ndi ufulu wolambila Yehova

32 Ciletso citacotsedwa, boma linalola ofesi ya nthambi kuitanitsa amishonale kuti abwele m’dzikolo, kumanga ofesi ina ya nthambi, ndi kuitanitsa mabuku ofotokoza Baibulo. * Atumiki a Mulungu padziko lonse amasangalala kwambili akaona mmene Yehova amatetezela anthu ake mwakuuzimu.—Yes. 52:10.

“Yehova Ndiye Mthandizi Wanga”

33. Taphunzila ciani pambuyo pokambilana mwacidule milandu ina ya kukhoti?

33 Nkhani zimene takambilana zokhudza milandu ina yomwe tinapambana, ndi umboni wakuti Yesu akukwanilitsa lonjezo lake. Iye analonjeza kuti: “Ine ndidzakuuzani mau oti munene ndi kukupatsani nzelu, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.” (Ŵelengani Luka 21:12-15.) Nthawi zina, Yehova amacititsa kuti pakhale anthu okhala ngati Gamaliyeli kuti ateteze anthu Ake. Iye amacititsanso oweluza ndi maloya olimba mtima kuweluza milandu mwacilungamo. Yehova wabunthitsa zida za adani athu. (Ŵelengani Yesaya 54:17.) Citsutso sicingalepheletse nchito ya Mulungu.

34. N’cifukwa ciani n’zocititsa cidwi kuti timapambana milandu ya ku khoti? Nanga zimenezi zimapeleka umboni wotani? (Onani nkhani yakuti “ Zipambano za Kukhoti Zimene Zinapititsa Patsogolo Nchito Yolalikila za Ufumu.”)

34 N’cifukwa ciani n’zocititsa cidwi kwambili kuti timapambana milandu kukhoti? Kumbukilani kuti ife a Mboni za Yehova si ndife anthu ochuka kapena amphamvu. Sitivota, kuthandiza pa makampeni, kapena kunyengelela atsogoleli andale kuti aticitile zinazake. Ndiponso ambili a ife amene timaima m’makhoti akuluakulu kukamba milandu, timaonedwa monga “anthu osaphunzila ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Motelo, tinganene kuti sicapafupi kuti makhoti aweluze milandu motikomela, ndi kupeleka cigamulo cotsutsa adani athu andale ndi acipembedzo amene ndi amphamvu kwambili. Ngakhale ndi conco, kaŵilikaŵili makhoti akhala akupeleka zigamulo zotikomela. Milandu imene tapambana imapeleka umboni wakuti tikuyenda “monga otsatila Khristu, okhala pamaso pa Mulungu.” (2 Akor. 2:17) Conco, tinganene monga mmene mtumwi Paulo ananenela kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.”—Aheb. 13:6.

^ par. 9 Mlandu wa m’bale Cantwell unali woyamba pa milandu 43 ya ku Khoti lalikulu ku United States imene M’bale Hayden Covington anakamba poteteza abale. M’bale Covington anamwalila mu 1978. Mkazi wake, Dorothy, anatumikila mokhulupilika mpaka pamene anamwalila mu 2015 ali ndi zaka 92.

^ par. 12 Ciweluzoci cinazikidwa pa lamulo limene linakhazikitsidwa mu 1606. Lamulo limenelo linapeleka mphamvu kwa oweluza kuti azim’patsa mlandu munthu ngati aona kuti zimene munthuyo anakamba ndi zoyambitsa mkangano ngakhale kuti anakamba zoona.

^ par. 14 Mu 1950, ku Quebec kunali apainiya 164, kuphatikizapo amishonale 63, amene anavomela kukatumikila m’delalo ngakhale kuti munali citsutso coopsa.

^ par. 15 M’bale W. Glen How, amene anali loya wolimba mtima, anakamba milandu yambilimbili kukhoti poteteza Mboni za Yehova ku Canada ndi maiko ena kuyambila mu 1943 mpaka mu 2003.

^ par. 16 Kuti mudziŵe zambili za mlandu umenewu, onani nkhani yakuti “The Battle Is Not Yours, but God’s,” m’magazini yacingelezi ya Galamukani! ya April 22, 2000, patsamba 18 mpaka 24.

^ par. 32 Pambuyo pake, gulu la asilikalilo linacoka ku nthambi, koma ofesi ina ya nthambi inamangidwa pamalo ena.