Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 15

Kumenyela Ufulu wa Kulambila

Kumenyela Ufulu wa Kulambila

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Mmene Kristu wathandizila otsatila ake kukhala gulu lodziŵika mwalamulo ndiponso kukhala ndi ufulu wotsatila malamulo a Mulungu

1, 2. (a) N’ciani cimasonyeza kuti ndinu nzika ya Ufumu wa Mulungu? (b) N’cifukwa ciani nthawi zina Mboni za Yehova zimamenyela ufulu wao wolambila?

KODI ndinu nzika ya Ufumu wa Mulungu? Popeza ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova, mwacionekele ndinu nzika ya Ufumuwo. Nanga pali umboni wotani wosonyeza kuti ndinudi nzika ya Ufumuwo? Kukhala nzika ya Ufumu wa Mulungu sikudalila kukhala ndi ciphaso, kapena kalata inayake yacilolezo ca boma. Koma kukhala nzika ya Ufumu kumadalila mmene mumalambilila Yehova Mulungu. Kulambila koona kumaphatikizapo zambili osati cabe zimene mumakhulupilila. Kumaphatikizapo kumvela malamulo a Ufumu wa Mulungu. Kulambila kwathu kumakhudza umoyo wathu wonse, kuphatikizapo mmene timalelela ana, ndi zimene timacita pa nkhani zina zokhudza thanzi lathu.

2 Komabe, nthawi zambili anthu m’dzikoli salemekeza ufulu wathu monga nzika za Ufumu wa Mulungu. Iwo salemekezanso malamulo a Ufumuwo. Maboma ena acititsa kuti tisamalambile mwaufulu ndipo ena atiletselatu kulambila. Nthawi zina, nzika za Kristu zimapita kukhoti pomenyela ufulu wao wotsatila malamulo a Mfumu Mesiya. Kodi zimenezi ziyenela kutidabwitsa? Iyai. M’nthawi zakale, kaŵilikaŵili anthu a Yehova anali kulimbana ndi zopinga zina kuti akhale ndi ufulu wolambila Yehova.

3. Ndi vuto lotani limene anthu a Mulungu m’nthawi ya Mfumukazi Esitere anakumana nalo?

3 Mwacitsanzo, m’nthawi ya Mfumukazi Esitere, anthu a Mulungu anafunika kucitapo kanthu kuti asaphedwe. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Hamani, yemwe anali Nduna Yaikulu ndi yoipa, anauza Mfumu ya ku Perisiya, Ahasiwero, kuti zingakhale bwino kuti Ayuda onse aphedwe popeza kuti malamulo ao anali “osiyana ndi malamulo a anthu ena onse.” (Esitere 3:8, 9, 13) Kodi Yehova anasiya atumiki ake osawathandiza? Ai ndithu. Iye anadalitsa khama la Esitere ndi Moredekai cifukwa cakuti anakadandaula kwa mfumu ya ku Perisiya kuti iteteze anthu a Mulungu.—Esitere 9:20-22.

4. Tikambilana ciani m’nkhani ino?

4 Nanga bwanji masiku ano? Monga tinaonela m’nkhani yapita, nthawi zina olamulila a maiko amatsutsa Mboni za Yehova. M’nkhani ino, tikambilana zimene maboma ena acita pofuna kuti tisamalambile Mulungu mwaufulu. Tikambilana mbali zitatu izi zofunika kwambili: (1) ufulu wathu wodziŵika monga gulu ndiponso ufulu wolambila, (2) ufulu wosankha cithandizo ca mankhwala mogwilizana ndi mfundo za m’Baibulo, ndi (3) ufulu wa makolo wolela ana mogwilizana ndi mfundo za Yehova. Pa mbali iliyonse, tiphunzila mmene nzika zokhulupilika za Ufumu wa Mesiya zatetezela molimba mtima ufulu wao wokhala nzika za Ufumuwo. Tiphunzilanso mmene Mulungu wadalitsila khama lao.

Kumenyela Ufulu Wodziŵika Mwalamulo Monga Gulu Ndiponso Maufulu Ena

5. Kodi Akristu oona amapindula bwanji gulu lao likadziŵika mwalamulo?

5 Kodi timafunika kucita kudziŵika ndi boma mwalamulo kuti tilambile Yehova? Iyai. Koma kudziŵika mwalamulo kumathandiza kuti tikhale ndi ufulu wa kulambila. Mwacitsanzo, timafunika cilolezo ca boma kuti tizisonkhana mwaufulu m’Nyumba za Ufumu ndi pa Malo a Misonkhano, ndiponso kuti tizisindikiza ndi kuitanitsa mabuku ophunzilila Baibulo. Timafunikanso cilolezo kuti tizilalikila uthenga wabwino kwa ena mwaufulu. M’maiko ambili, Mboni za Yehova ndi zodziŵika mwalamulo, ndipo zili ndi ufulu wolambila monga mmene amacitila anthu a zipembedzo zina. Nanga timacita ciani ngati boma lakana kuti Mboni za Yehova zikhale zodziŵika monga gulu lacipembedzo, kapena ngati laphwanya ufulu wathu m’njila zina?

6. Kodi Mboni za Yehova ku Australia zinakumana ndi mavuto otani kumayambililo kwa zaka za m’ma 1940?

6 Ku Australia. Cakumayambililo kwa zaka za m’ma 1940, bwanamkubwa wa ku Australia ananena kuti zikhulupililo zathu “zimaletsa” anthu kumenya nkhondo. Conco, Mboni za Yehova zinaletsedwa cakuti abale athu analibe ufulu wosonkhana kapena kulalikila. Ofesi ya nthambi inatsekedwa, ndipo Nyumba za Ufumu zinalandidwa. Ngakhale kukhala ndi mabuku athu ophunzilila Baibulo kunali koletsedwa. Pambuyo polambila Mulungu mobisa kwa zaka zingapo, Mboni za ku Australia zinapeza mpumulo pamene Khoti Lalikulu m’dzikolo linacotsa ciletsoco pa June 14, 1943.

7, 8. Fotokozani zimene abale athu ku Russia akhala akucita pomenyela ufulu wao wa kulambila.

7 Ku Russia. Kwa zaka zambili, Mboni za Yehova zinali zoletsedwa mu ulamulilo wa Cikomyunizimu. Koma mu 1991, a Mboni analembetsa ku boma monga gulu lacipembedzo. Mayiko omwe kale anali kuchedwa Soviet Union atagaŵikana, abale athu anapatsidwa ufulu wodziŵika monga gulu ku Russia mu 1992. Koma patangopita nthawi yocepa, anthu ena otsutsa, makamaka amene anali kugwilizana ndi Chalichi ca Orthodox ku Russia, anada nkhawa cifukwa cakuti ciŵelengelo ca Mboni cinali kukwela mofulumila. Kucokela mu 1995 mpaka mu 1998, otsutsa anasumila Mboni za Yehova milandu isanu ikuluikulu. Pa milandu yonseyo, woweluza sanapeze umboni uliwonse wosonyeza kuti abale athu anali olakwa. Mu 1998, otsutsawo anasumila abale athu mlandu wophela anthu ufulu. Poyamba, Mboni za Yehova zinapambana mlanduwo, koma otsutsawo anakana ciweluzoco, ndipo anacita apilo. M’mwezi wa May m’caka ca 2001, abale athu analuza mlanduwo ku khoti la apilo. Mu October caka cimeneco, mlanduwo unayamba kuzengedwanso. Zotsatila zake zinali zakuti mu 2004, boma linatseka bungwe lovomelezeka mwalamulo la Mboni za Yehova m’dzikolo.

8 Cifukwa ca zimenezi, abale athu anayamba kuzunzidwa. (Ŵelengani 2 Timoteyo 3:12.) Mboni za Yehova zinali kuvutitsidwa ndi kumenyedwa, ndipo mabuku athu anali kulandidwa. Kumanga nyumba zolambililamo kapena kucita lendi nyumba zakuti alambililemo kunali kovuta kwambili. Tangoganizilani mmene abale athu anamvela pa nthawi ya mavuto amenewa. Mboni za Yehova zinacita apilo mlandu wao ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya mu 2001, ndipo mu 2004, Mboni zinapeleka mfundo zina zokhudza mlanduwo ku Khotilo. Mu 2010, Khotilo linapeleka cigamulo cake. Khotilo linaona kuti boma la Russia linaletsa Mboni za Yehova kulambila mwaufulu cifukwa cakuti zipembedzo zina zinali kudana ndi a Mboni. Conco, Khotilo linagamula kuti ziweluzo za makhoti aang’ono zinali zolakwika cifukwa cakuti panalibe umboni wakuti Mboni za Yehova zinacita colakwa. Khotilo linaonanso kuti boma la Russia linacita zimenezo n’colinga cofuna kulanda ufulu wa kulambila wa Mboni. Malinga ndi cigamuloco, Mboni za Yehova ziyenela kukhala ndi ufulu wa kulambila. Ngakhale kuti akuluakulu ena a boma la Russia akali kunyalanyaza cigamulo ca Khotilo, anthu a Mulungu m’dzikolo amalimbikitsidwa kwambili ndi zipambano za ku Khoti monga zimenezi.

Titos Manoussakis (Onani ndime 9)

9-11. Kodi anthu a Yehova amenyela bwanji ufulu wa kulambila m’dziko la Greece? Nanga zotsatilapo zake zakhala zotani?

9 Ku Greece. Mu 1983, M’bale Titos Manoussakis anali kucita lendi cipinda ca nyumba ina ku Heraklion mumzinda wa Crete n’colinga cakuti kagulu kocepa ka Mboni za Yehova kazicitilamo misonkhano. (Aheb. 10:24, 25) Patapita nthawi yocepa, wansembe wina wa Chalichi ca Orthodox anasumila a Mboni mlandu ku boma kuti liwaletse kusonkhana pa nyumbayo. N’cifukwa ciani anacita zimenezo? Cifukwa cakuti zikhulupililo za Mboni za Yehova n’zosiyana ndi za Chalichi ca Orthodox. Khoti linayamba kuzenga mlandu M’bale Titos Manoussakis ndi Mboni zina zitatu kuti anaphwanya malamulo. Khotilo linawalipilitsa ndalama, ndipo linagamula kuti akhale m’ndende miyezi itatu. Monga nzika zokhulupilika za Ufumu wa Mulungu, abalewo anaona kuti ciweluzo ca khotilo cinaphwanya ufulu wao wa kulambila. Conco, anacita apilo nkhaniyo ku makhoti ena a m’dzikolo, ndipo pamapeto pake nkhaniyo inakafika ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

10 Mu 1996, Khotilo linapeleka cigamulo cimene cinakhwethemula maganizo anthu otsutsa kulambila koona, ndipo linati: “Mboni za Yehova zili m’gulu la ‘zipembedzo zodziŵika’ mogwilizana ndi malamulo a ku Greece.” Linanenanso kuti zimene makhoti aang’ono anagamula pankhaniyo “zinaphwanya ufulu wa kulambila wa osuma mlanduwo.” Khotilo linagamulanso kuti si udindo wa boma la Greece “kuona ngati zikhulupililo za cipembedzo kapena zimene cipembedzoco cimacita polambila n’zovomelezeka kapena ai.” Motelo, Khotilo linathetsa milandu ya Mboni za Yehova, ndipo linalamula kuti bomalo lizilemekeza ufulu wao wa kulambila.

11 Koma comvetsa cisoni n’cakuti cigamuloco sicinathetse mavuto ku Greece. Mu 2012, khoti la ku Kassandreia, m’dzikolo, linathetsa mlandu wina wofanana ndi umenewu womwe unatenga zaka pafupifupi 12. Amene anayambitsa mlanduwo ndi bishopu wa Chalichi ca Orthodox. Khoti lalikulu kwambili ku Greece linaweluza mlanduwo mokomela anthu a Mulungu. Pa ciweluzoco, khotilo linafotokoza kuti malamulo a m’dzikolo amapatsa anthu ufulu wa kulambila, ndipo linatsutsa mlandu umene a Mboni za Yehova anali kuzengedwa kaŵilikaŵili wakuti io si cipembedzo codziŵika. Khotilo linati: “Ziphunzitso za ‘Mboni za Yehova’ n’zodziŵika bwino, ndipo pacifukwa cimeneco, io ndi cipembedzo codziŵika.” Tsopano abale ndi alongo mumpingo waung’ono ku Kassandreia akusangalala cifukwa cakuti ali ndi ufulu wosonkhana m’Nyumba yao ya Ufumu.

12, 13. Ku France, kodi otsutsa akhala akucita ciani pofuna ‘kuyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo’? Ndipo zotsatilapo zake zakhala zotani?

12 Ku France. Anthu ena amene amatsutsa anthu a Mulungu ‘amayambitsa mavuto mwa kupanga malamulo.’ (Ŵelengani Masalimo 94:20.) Mwacitsanzo, m’zaka za m’ma 1990, akuluakulu oona za msonkho ku France anayamba kupenda kayendetsedwe ka ndalama za bungwe lovomelezedwa mwalamulo la Mboni za Yehova m’dzikolo (Association Les Témoins de Jéhovah). Woyang’anila kayendetsedwe ka ndalama anafotokoza colinga ca kupendako. Iye anati: “Kupendaku kungapangitse kuti bungweli litsekedwe kapena kuimbidwa mlandu wophwanya malamulo . . . . Mwacionekele, kucita zimenezi kudzasokoneza kwambili nchito ya bungweli kapena kulithetselatu m’dziko lathu.” Pambuyo pa kupendako, sanapeze colakwika ciliconse, koma akuluakulu oona za msonkho anakweza kwambili msonkho umene bungwe la Mboni m’dzikolo linali kupeleka. Zimenezi zikanapangitsa kuti abale athu atseke ofesi ya nthambi ndi kugulitsa nyumba za ofesiyo n’colinga cakuti alipile msonkhowo. Ciweluzo cimeneci cinali cowawa kwambili, koma anthu a Mulungu sanagwe mphwayi. Mboni za Yehova zinatsutsa mwamphamvu ciweluzo copanda cilungamo cimeneci, ndipo pamapeto pake zinapeleka nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya mu 2005.

13 Khotilo linapeleka cigamulo cokomela Mboni za Yehova pa June 30, 2011. Linanena kuti cifukwa cakuti munthu aliyense ali ndi ufulu wa kulambila, Bomalo silifunika kupenda ngati zikhulupililo za cipembedzo kapena zimene cipembedzoco cimacita polambila n’zoyenela kapena ai, koma pokhapo ngati pali vuto lalikulu. Kuonjezela pamenepo, Khotilo linati: “Msonkhowo unapangitsa . . . kuti bungwe la Mboni za Yehova lisoŵe zinthu zofunika kwambili, ndipo zimenezi zinacititsa kuti a Mboni azilephela kulambila mwaufulu.” Anthu a Yehova anasangalala kwambili cifukwa cakuti boma la France linabweza ndalama za msonkho zimene linatenga ku bungwe la Mboni m’dzikolo, ndipo linapelekanso ciongoladzanja. Komanso bomalo linamvela cigamulo ca Khotilo cakuti siliyenela kulanda ofesi ya nthambi imeneyo.

Tingapemphelele abale ndi alongo athu nthawi zonse amene akukumana ndi mavuto cifukwa ca malamulo opondeleza amene ali m’dziko lao

14. Kodi mungacite ciani kuti muthandize pa nkhani yomenyela ufulu wa kulambila?

14 Monga mmene Esitere ndi Moredekai anacitila, anthu a Yehova masiku ano amamenyela ufulu wao wolambila Yehova m’njila imene iye amafuna. (Esitere 4:13-16) Kodi inuyo mungathandize bwanji pa nchito yomenyela ufulu imeneyi? Mungathandize mwa kupemphelela abale ndi alongo athu nthawi zonse amene akukumana ndi mavuto cifukwa ca malamulo opondeleza amene ali m’dziko lao. Mapemphelo otelo angathandize kwambili abale ndi alongo athu amene akuzunzidwa kapena kukumana ndi mavuto osiyanasiyana. (Ŵelengani Yakobo 5:16.) Kodi Yehova amayankha mapemphelo otelo? Milandu yosiyanasiyana imene tapambana kukhoti ndi umboni wakuti amatelo.—Aheb. 13:18, 19.

Ufulu Wosankha Cithandizo Camankhwala Mogwilizana ndi Zikhulupililo Zathu

15. Ndi zinthu ziti zimene anthu a Mulungu ayenela kuganizila pa nkhani yogwilitsila nchito magazi?

15 Monga mmene tinaonela m’Nkhani 11, nzika za Ufumu wa Mulungu zakhala zikulandila malangizo omveka bwino a m’Malemba oletsa kugwilitsila nchito magazi molakwika kumene kwafala kwambili masiku ano. (Gen. 9:5, 6; Lev. 17:11; ŵelengani Machitidwe 15:28, 29.) Ngakhale kuti timakana kuikidwa magazi, ife ndi mabanja athu timafuna kulandila cithandizo ca mankhwala cabwino malinga ngati cithandizoco sicisemphana ndi malamulo a Mulungu. Makhoti akuluakulu m’maiko ambili azindikila kuti anthu ali ndi ufulu wolandila kapena kukana cithandizo ca mankhwala mogwilizana ndi cikumbumtima cao ndiponso zikhulupililo zao. Komabe, m’maiko ambili, anthu a Mulungu akumana ndi mavuto aakulu pankhani imeneyi. Ganizilani zitsanzo zotsatilazi.

16, 17. Kodi mlongo wina ku Japan analandila cithandizo cotani ca mankhwala cimene cinamukhumudwitsa? Nanga mapemphelo ake anayankhidwa bwanji?

16 Ku Japan. Mai wina ku Japan wochedwa Misae Takeda wa zaka 63, anafunika kucitidwa opaleshoni yaikulu. Monga nzika ya Ufumu wa Mulungu, iye anafotokozela a dokotala momveka bwino kuti sanali kufuna kuikidwa magazi. Koma patapita miyezi ingapo, iye anakhumudwa atamva kuti anaikidwa magazi pamene anali kucitidwa opaleshoni. Mlongo Takeda ataona kuti anamuphwanyila ufulu ndi kumucita cinyengo, anasumila mlandu madokotala ndi acipatala mu June 1993. Mlongoyo anali wofatsa ndi wodzicepetsa ndiponso wacikhulupililo colimba. Iye anapeleka umboni molimba mtima ataimilila m’bwalo lakhoti lodzaza ndi anthu kwa ola lathunthu ngakhale kuti anali kudwala. Iye anamwalila patangopita mwezi umodzi kucokela pamene anakaonekela komaliza kukhoti. Kodi sitikucita cidwi ndi kulimba mtima kwa mlongoyu ndi cikhulupilo cake? Mlongo Takeda ananena kuti nthawi zonse anali kupemphela kwa Yehova kuti adalitse khama lake pa mlanduwo. Iye anali ndi cikhulupililo cakuti Mulungu adzayankha mapemphelo ake. Kodi Mulungu anayankhadi mapemphelowo?

17 Pambuyo pa zaka zitatu Mlongo Takeda atamwalila, Khoti lalikulu ku Japan linapeleka cigamulo comukomela. Khotilo linanena kuti dokotalayo anaphwanyila mlongo wathuyo ufulu wosankha pamene anamuika magazi. Pa February 29, 2000, Khotilo linagamula kuti “ufulu wosankha” pankhani ngati zimenezi “uyenela kulemekezedwa ndi kuonedwa kukhala nkhani yaumwini.” Mlongo Takeda anacita khama kwambili kumenyela ufulu wake wosankha cithandizo ca mankhwala mogwilizana ndi cikumbumtima cake cophunzitsidwa Baibulo. Cifukwa ca khama lakelo, tsopano Mboni za Yehova ku Japan zingathe kusankha cithandizo ca mankhwala popanda kukakamizidwa kuikidwa magazi.

Pablo Albarracini (Onani ndime 18 mpaka 20)

18-20. (a) Kodi khoti lalikulu ku Argentina linasonyeza bwanji kuti munthu ali ndi ufulu wogwilitsila nchito khadi la cidziŵitso kwa madokotala pokana kuikidwa magazi? (b) Tingaonetse bwanji kuti timagonjela ulamulilo wa Kristu pa nkhani ya magazi?

18 Ku Argentina. Kodi nzika za Ufumu wa Mulungu zingacite ciani kuti munthu wina asazipangile cosankha ca mankhwala zikadwala mwakayakaya? Nzika iliyonse iyenela kunyamula cikalata covomelezeka mwalamulo comwe cingathandize acipatala kudziŵa maganizo ake pankhaniyi. Izi n’zimene Pablo Albarracini anacita. M’mwezi wa May caka ca 2012, acifwamba a mfuti anafuna kumulanda katundu ndipo anamuombela maulendo angapo. Iye anaikidwa m’cipatala koma anali wokomoka moti sakanatha kufotokoza maganizo ake pankhani ya kuikidwa magazi. Komabe, M’bale Albarracini anali ndi khadi la cidziŵitso kwa madokotala losainidwa bwino limene anasaina zaka zinai zimenezi zisanacitike. Iye anali wodwala kwambili ndipo madokotala anaona kuti afunika kuikidwa magazi kuti apulumutse moyo wake. Ngakhale zinali conco, io anali okonzeka kutsatila zofuna zake pankhaniyi. Koma atate ake a Pablo omwe sanali a Mboni za Yehova, anakatenga cilolezo ku khoti kuti mwana waoyo aikidwe magazi.

19 Mwamsanga loya woimila mkazi wa M’bale Pablo anacita apilo. Patangopita maola oŵelengeka, khoti lalikulu linaletsa madokotala kutsatila lamulo la khoti laling’onolo, ndipo linawauza kuti atsatile zofuna za wodwalayo zimene zinalembedwa pa khadi la cidziŵitso kwa madokotala. Atate ake a Pablo anacita apilo ku Khoti Lalikulu kwambili m’dzikolo. Koma Khotilo linaona kuti “panalibe umboni woonetsa kuti Pablo anasaina mosalingalila bwino kapena mokakamizidwa [khadi lake la cidziŵitso kwa madokotala losonyeza kukana kuikidwa magazi].” Khotilo linati: “Munthu aliyense woganiza bwino kapena wamkulu ali ndi ufulu wopeleka malangizo pankhani ya umoyo [wake], ndipo angasankhe kulandila cithandizo cinacake ca mankhwala kapena kucikana . . . Dokotala amene akuthandiza munthuyo ayenela kutsatila malangizowo.”

Kodi munasaina khadi lanu la cidziŵitso kwa madokotala?

20 M’bale Albarracini anacila tsopano. Iye ndi mkazi wake ndi osangalala kuti anasaina khadi la cidziŵitso kwa madokotala. Mwa kucita zinthu zooneka ngati zocepa koma zofunika kwambili zimenezi, M’bale Albarracini anasonyeza kuti amagonjela ulamulilo wa Kristu, Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kodi inu ndi banja lanu munasaina makadi anu ndipo mumawanyamula?

April Cadoreth (Onani ndime 21 mpaka 24)

21-24. (a) Zinatheka bwanji kuti Khoti Lalikulu ku Canada lipeleke cigamulo cabwino pa nkhani yokhudza acinyamata ndiponso kugwilitsila nchito magazi? (b) Kodi nkhani imeneyi ingalimbikitse bwanji acinyamata amene akutumikila Yehova?

21 Ku Canada. Makhoti ambili amadziŵa kuti makolo ali ndi ufulu wosankhila ana ao cithandizo ca mankhwala cabwino kwambili. Nthawi zina, makhoti amalamula kuti wacicepele wokhwima maganizo ayenela kupatsidwa ufulu wosankha cithandizo ca mankhwala. Zotele n’zimene zinacitikila April Cadoreth. Pamene anali ndi zaka 14, April anagonekedwa m’cipatala cifukwa ca matenda a kucuca magazi mkati mwa thupi. Miyezi ingapo zimenezi zisanacitike, iye anali atasaina khadi la Chidziŵitso kwa Madokotala lokhala ndi malangizo okana kuikidwa magazi ngakhale atadwala mwakayakaya. Dokotala amene anali kuthandiza April ananyalanyaza malangizo a pa khadilo, ndipo anakapempha cilolezo ca khoti kuti amuike magazi. Conco, iye anaikidwa mabotolo atatu a magazi mwacikakamizo. April anaona kuti zimene anamucitilazo n’zofanana ndi kumugwilila.

22 April ndi makolo ake anakasuma mlandu kukhoti cifukwa ca nkhaniyo. Patapita zaka ziŵili, mlanduwo unakafika ku Khoti Lalikulu m’dzikolo. Mogwilizana ndi malamulo a m’dzikolo tinganene kuti April analuza mlanduwo. Koma atacita apilo, khotilo linagamula mlanduwo mokomela iye ndi ana ena amene amafuna kusankha okha cithandizo camankhwala cimene akufuna. Khotilo linanena kuti: “Pa nkhani ya cithandizo camankhwala, acinyamata osakwana zaka 16 afunika kupatsidwa ufulu woonetsa ngati ndi okhwima maganizo cakuti angathe kusankha okha cithandizo ca mankhwala.”

23 Cigamuloci ndi cosangalatsa cifukwa cakuti Khoti Lalikululo linasonyeza kuti ana okhwima maganizo ali ndi ufulu wosankha cithandizo ca mankhwala. Cigamuloci cisanapelekedwe, makhoti ku Canada anali kupatsa mphamvu acipatala yopeleka cithandizo ciliconse camankhwala kwa mwana wosakwana zaka 16 malinga ngati khotilo laona kuti cithandizoco n’cabwino kwa mwanayo. Koma pambuyo pa cigamuloci, makhoti m’dzikolo alibenso ulamulilo wouza acipatala kupeleka cithandizo camankhwala kwa mwana wosakwana zaka 16 popanda kumupatsa mpata woonetsa ngati angakwanitse kupanga yekha cosankha pankhaniyi.

“Ndimasangalala kwambili kudziŵa kuti zocita zanga zinathandiza kuti dzina la Mulungu lilemekezedwe ndi kuonetsa kuti Satana ndi wabodza”

24 Kodi khama lao pa nkhaniyi linali ndi zotsatilapo zabwino? April anayankha kuti: “Inde, zinalipo.” Iye tsopano ali ndi thanzi labwino, ndipo akucita upainiya. Iye ananenanso kuti: “Ndimasangalala kwambili kudziŵa kuti zocita zanga zinathandiza kuti dzina la Mulungu lilemekezedwe ndi kuonetsa kuti Satana ndi wabodza.” Zimene April anacita zikusonyeza kuti ana athu angathe kucita zinthu molimba mtima, ndi kuonetsa kuti ndi nzika zenizeni za Ufumu wa Mulungu.—Mat. 21:16.

Ufulu Wolela Ana Mogwilizana ndi Mfundo za Yehova

25, 26. Ndi mavuto ati amene amabwela nthawi zina ngati mwamuna ndi mkazi asudzulana?

25 Yehova anapatsa makolo udindo wolela ana ao mogwilizana ndi mfundo zake. (Deut. 6:6-8; Aef. 6:4) Udindo umenewu ndi wovuta, koma umavuta kwambili ngati mwamuna ndi mkazi asudzulana. Anthu amakhala ndi maganizo osiyana kwambili pankhani ya mmene ayenela kulelela ana. Mwacitsanzo, kholo limene ndi Mboni limafunitsitsa kuti ana ake aleledwe motsatila mfundo zacikristu, pamene kholo limene si Mboni lingakane zimenezo. Ndipo kholo limene ndi Mboni liyenela kukumbukila kuti ngakhale kuti kusudzulana kumathetsa ukwati, udindo wolela ana sukutha.

26 Kholo lomwe si Mboni lingapemphe khoti kuti lipatsidwe ufulu wolela mwana wake kapena ana ake n’colinga cakuti anao asaphunzile coonadi. Ena amanena kuti mwana akakhala wa Mboni za Yehova samakula bwino. Iwo anganene kuti anawo azimanidwa mwai wocita zikondwelelo za tsiku la kubadwa ndi za maholide ena, ndiponso kuti akadzadwala kwambili sadzaikidwa magazi kuti “apulumutse moyo wao.” Koma ubwino wake ndi wakuti, popeleka cigamulo, makhoti ambili amaganizila zimene zidzathandiza mwanayo osati zakuti cipembedzo cina n’coipa kapena ai. Tiyeni tione zitsanzo zina zokhudza nkhaniyi.

27, 28. Kodi Khoti Lalikulu ku Ohio linanenapo ciani pa cinenezo cakuti mwana akaleledwa ndi a Mboni za Yehova sakula bwino?

27 Ku United States. Mu 1992, Khoti lalikulu ku Ohio linaweluza mlandu wa tate wina amene si Mboni. Iye ananena kuti mwana wake sadzakula bwino akaphunzitsidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Khoti laling’ono linavomeleza zimenezo, ndipo linapatsa tateyo ufulu wolela mwanayo. Khotilo linapatsa amai ake, a Jennifer Pater, ufulu wakuti azikaona mwanayo. Koma linawalamula kuti “asamamuphunzitse zikhulupililo za Mboni za Yehova kapena kumufotokozela ciliconse cokhudza Mboni.” Cigamuloco cinatanthauza kuti Mlongo Pater analibe ufulu wokambilana ndi mwana wao, Bobby, nkhani za m’Baibulo ndiponso mfundo za makhalidwe abwino. Kodi muganiza kuti mlongoyo anamva bwanji? Iye anakhumudwa kwambili, koma ananena kuti anaphunzila kukhala woleza mtima ndi kuyembekezela Yehova kuti acitepo kanthu. Mothandizidwa ndi gulu la Yehova, loya woimila mlongoyo anacita apilo ku Khoti Lalikulu ku Ohio.

28 Khoti lalikululo linatsutsa cigamulo ca khoti laling’ono, ndipo linanena kuti “makolo ali ndi ufulu wonse wophunzitsa ana ao, kuphatikizapo kuwaphunzitsa makhalidwe abwino ndi mfundo za cipembedzo.” Khoti lalikululo linanena kuti khoti laling’ono silinapeleke umboni woonetsa kuti mfundo zimene Mboni za Yehova zimayendela zingapangitse kuti mwana asakule bwino. Linanenanso kuti khoti laling’ono linalibe mphamvu zoletsa kholo kulela mwana cifukwa ca nkhani yacipembedzo. Conco, Khoti lalikululo linaona kuti panalibe umboni uliwonse wosonyeza kuti zikhulupililo za Mboni zingapangitse kuti mwanayo asakule bwino.

Makhoti ambili apeleka ufulu kwa makolo acikristu wolela ana ao

29-31. N’cifukwa ciani mlongo wina ku Denmark analandidwa mphamvu zolela mwana wake? Nanga Khoti lalikulu m’dzikolo linaweluza bwanji nkhaniyo?

29 Ku Denmark. Mlongo Anita Hansen anakumana ndi vuto ngati limeneli pamene mwamuna amene anasudzulana naye anapempha khoti lina kuti limupatse mphamvu yolela mwana wao wa zaka 7, dzina lake Amanda. Ngakhale kuti khoti laling’ono linali litapatsa kale Mlongo Hansen mphamvu zolela mwanayo mu 2000, atate ake a Amanda anacita apilo ku khoti lalikulu, ndipo linasintha cigamulo ca khoti laling’ono ndi kupatsa tateyo ufulu wolela mwanayo. Khotilo linanena kuti popeza kuti maganizo a makolowo anali osiyana cifukwa cosiyana zikhulupililo, tateyo ndi amene anali woyenela kutenga mwanayo. Conco, tinganene kuti Mlongo Hansen analandidwa mphamvu zolela Amanda cifukwa cakuti ndi wa Mboni za Yehova.

30 Nthawi zina Mlongo Hansen anali kuvutika kwambili maganizo ndi nkhaniyi cakuti anali kusowa conena popemphela. Iye anati: “Koma mau a pa Aroma 8:26 ndi 27 anali kunditonthoza kwambili. Nthawi zonse ndinali kuona kuti Yehova anali kudziŵa zimene ndinali kufuna kunena. Iye anali kundiyang’anila, ndipo nthawi zonse anali kundithandiza.”—Ŵelengani Salimo 32:8; Yesaya 41:10.

31 Mlongo Hansen anacita apilo ku Khoti Lalikulu kwambili ku Denmark. Pogamula mlanduwo, Khotilo linati: “Taweluza mlandu wokhudza kulela mwanayu malinga ndi zimene zidzathandiza kuti iye akhale ndi tsogolo labwino.” Khotilo linanenanso kuti cigamulo ca mlanduwo cinapelekedwa mogwilizana ndi mmene kholo lililonse la mwanayo limacitila pakakhala mikangano, osati mogwilizana ndi “ziphunzitso ndiponso zikhulupililo” za Mboni za Yehova. Mlongo Hansen anasangalala kwambili pamene Khotilo linaona kuti iye ndiye woyenela kutenga mwanayo, ndipo khotilo linamubwezela mwanayo.

32. Kodi Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya lathandiza bwanji kuti makolo a Mboni asamasalidwe?

32 Maiko ena ku Ulaya. Nthawi zina, makhoti onse m’dziko amalephela kuthetsa milandu yokhudza kulela ana, ndipo amapeleka milanduyo kumakhoti akuluakulu. Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya laweluzapo milandu yotele. Poweluza milandu iŵili yokhudza kulela ana, Khotili linavomeleza kuti makhoti aang’ono m’maiko ena anaweluza mokondela pakati pa makolo a Mboni ndi makolo amene si a Mboni cifukwa cosiyana cipembedzo. Khotili linanena kuti kucita zimenezi ndi tsankho, ndipo linanena kuti “kuweluza mlandu pa cifukwa ca cipembedzo ca munthu n’kulakwa.” Mai wina wa Mboni amene anapindula ndi cigamulo ca Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya anafotokoza mmene anamvelela. Iye anati: “Ndinakhumudwa kwambili pamene anali kundiimba mlandu wakuti ndikufuna kuononga ana anga, pamene ineyo ndinali kungowaphunzitsa coonadi cimene ndi cinthu camtengo wapatali.”

33. Kodi makolo amene ndi Mboni angagwilitsile nchito bwanji mfundo ya pa Afilipi 4:5?

33 Komabe, makolo a Mboni amene akucita khama kuti akhale ndi ufulu wokhomeleza mfundo za m’Baibulo m’mitima ya ana ao ayenela kuyesetsa kukhala ndi mzimu wololela. (Ŵelengani Afilipi 4:5.) Makolo a Mboni amasangalala kukhala ndi ufulu wophunzitsa ana ao njila za Mulungu. Panthawi imodzimodziyo, afunika kuzindikila kuti kholo limene si Mboni nalonso lili ndi ufulu wolela mwana ngati likufuna kutelo. Kodi kholo limene ndi Mboni liyenela kuona bwanji udindo wake wophunzitsa mwana wake?

34. N’ciani cimene makolo acikristu akuphunzilapo pa zimene Ayuda a m’nthawi ya Nehemiya anacita?

34 Tingaphunzile mfundo zothandiza pa zimene zinacitika m’nthawi ya Nehemiya. Panthawiyo, Ayuda anacita khama kuti amange mipanda ya Yerusalemu. Iwo anadziŵa kuti kucita zimenezo kudzawateteza pamodzi ndi mabanja ao kwa anthu a mitundu ina amene anali adani ao. Pa cifukwa cimeneci, Nehemiya analimbikitsa Ayuda kuti: “Menyelani nkhondo abale anu, ana anu aamuna, ana anu aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.” (Neh. 4:14) Kwa Ayudawo, kucita zimenezo kunali kofunika kwambili. Mofananamo, masiku ano, makolo amene ndi Mboni za Yehova amacita khama kuphunzitsa coonadi ana ao kuti akule bwino. Iwo amadziŵa kuti anawo amakumana ndi ziyeso zambili kusukulu ndi m’dela limene amakhala. Ana amakumana ndi ziyeso zina ngakhale kunyumba kudzela pa wailesi, pa TV, kapena pa Intaneti. Makolo, citani khama kuti muteteze ana anu kuti akule bwino mwakuuzimu.

Khalani ndi Cikhulupililo Cakuti Yehova Adzacilikizabe Kulambila Koona

35, 36. Kodi Mboni za Yehova zapindula bwanji cifukwa ca khama lao pomenyela ufulu wao m’njila zosiyanasiyana? N’ciani cimene mwatsimikiza mtima kucita?

35 Yehova wakhala akudalitsa khama la gulu lake masiku ano pomenyela ufulu wa kulambila. Pa milandu yomenyela ufulu wao, anthu a Mulungu kaŵilikaŵili amapeleka umboni wamphamvu m’makhoti ndiponso kwa anthu onse. (Aroma 1:8) Kuonjezela pamenepo, milandu ya kukhoti imene anthu a Mulungu apambana yapangitsa kuti anthu ambili amene si Mboni akhalenso ndi ufulu osiyanasiyana. Komabe, monga anthu a Mulungu, colinga cathu si kusintha malamulo kapena kufuna kudzilungamitsa. Koma colinga cacikulu ca Mboni za Yehova ndi kumenyela ufulu wao wa kulambila, ndiponso kuthandiza kuti kulambila koona kupite patsogolo.—Ŵelengani Afilipi 1:7.

36 Tifunika kuphunzilapo kanthu pa cikhulupililo ca anthu amene anacita khama pomenyela ufulu wolambila Yehova. Tiyeni nafenso tikhale okhulupilika ndipo tikhale ndi cikhulupililo cakuti Yehova akucilikiza nchito yathu, ndiponso kuti adzapitiliza kutipatsa mphamvu kuti ticite cifuno cake.—Yes. 54:17.