Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 16

Kusonkhana Kuti Tilambire Mulungu

Kusonkhana Kuti Tilambire Mulungu

CHOLINGA CHA MUTUWU

Kuona kufunika kwa misonkhano yathu komanso kukambirana mmene yakhala ikuchitikira m’mbuyomu

1. Kodi ophunzira a Yesu atasonkhana Yehova anawapatsa chiyani, ndipo zinawathandiza bwanji?

 YESU atangoukitsidwa, ophunzira ake anasonkhana kuti alimbikitsane. Koma chifukwa choopa adani awo, anakhoma zitseko zonse za nyumba yomwe anasonkhanayo. Mantha amenewa anatha Yesu ataonekera pakati pawo n’kunena kuti: “Landirani mzimu woyera.” (Werengani Yohane 20:19-22.) Patapita nthawi, ophunzirawo anasonkhananso ndipo Yehova anawapatsa mzimu woyera. Mzimuwo unawathandiza pa ntchito yolalikira imene anafunika kugwira.​—Mac. 2:1-7.

2. (a) Kodi Yehova amatipatsa bwanji mphamvu ndipo n’chifukwa chiyani timafunikira mphamvu zimenezi? (b) Kodi Kulambira kwa Pabanja n’kofunika bwanji? (Onani mawu a m’munsi komanso bokosi lakuti, “ Kulambira kwa Pabanja,” patsamba 175.)

2 Nafenso timakumana ndi mavuto ofanana ndi amene abale athuwa anakumana nawo. (1 Pet. 5:9) Abale athu ena amaopa anthu ndipo timafunikira mphamvu imene Yehova amapereka n’cholinga choti tipitirizebe kugwira ntchito yolalikira. (Aef. 6:10) Nthawi zambiri Yehova amatipatsa mphamvu imeneyi kudzera m’misonkhano imene timakhala nayo. Panopa tili ndi mwayi wopezeka pamisonkhano yampingo kawiri pa mlungu. Timasonkhana pa Msonkhano wa Onse ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda ndiponso pamsonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. a Timasangalalanso ndi misonkhano ikuluikulu 4 imene timakhala nayo pa chaka, yomwe ndi msonkhano wachigawo, misonkhano yadera iwiri komanso Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Kodi kuyesetsa kupezeka pamisonkhano yonseyi n’kothandiza bwanji? Nanga kale misonkhano imeneyi inkachitika bwanji? Kodi tiyenera kuiona bwanji misonkhano imeneyi?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonkhana?

3, 4. Kodi Yehova amafuna kuti anthu ake azichita chiyani? Perekani zitsanzo.

3 Kuyambira kalekale, Yehova amafuna kuti anthu ake azisonkhana pamodzi kuti azimulambira. Mwachitsanzo, mu 1513 B.C.E., Yehova anapereka Chilamulo kwa Aisiraeli ndipo limodzi mwa malamulo a m’Chilamulocho linali lakuti azisunga Sabata n’cholinga choti mabanja azikhala ndi mpata womulambira komanso wophunzira Chilamulo. (Deut. 5:12; 6:4-9) Aisiraeli ankati akatsatira lamulo limeneli, mabanja awo ankakhala olimba ndipo mtundu wonse unkakhala woyera komanso wolimba mwauzimu. Koma mtunduwu ukapanda kutsatira Chilamulo, n’kusiya kusonkhana kuti alambire Yehova, Mulungu ankawakwiyira.​—Lev. 10:11; 26:31-35; 2 Mbiri 36:20, 21.

4 Taganiziraninso zimene Yesu ankachita. Iye anali ndi chizolowezi chopita ku sunagoge pa tsiku la Sabata mlungu uliwonse. (Luka 4:16) Yesu atafa n’kuukitsidwa, ophunzira ake anapitiriza kusonkhana mlungu uliwonse ngakhale kuti pa nthawi imeneyo sankayenera kutsatira lamulo lokhudza Sabata. (Mac. 1:6, 12-14; 2:1-4; Aroma 14:5; Akol. 2:13, 14) Pamisonkhano imeneyi, si kuti Akhristuwa ankangolandira malangizo komanso kulimbikitsidwa, koma ankaperekanso nsembe zotamanda Mulungu kudzera m’mapemphero, ndemanga ndiponso nyimbo.​—Akol. 3:16; Aheb. 13:15.

Ophunzira a Yesu anasonkhana kuti alimbikitsane

5. N’chifukwa chiyani timapita kumisonkhano yamlungu ndi mlungu komanso kumisonkhano ikuluikulu? (Onani bokosi lakuti “ Misonkhano Yapachaka Imene Imathandiza Anthu a Mulungu Kukhala Ogwirizana,” patsamba 176.)

5 N’chimodzimodzinso masiku ano, tikakhala pamisonkhano yamlungu ndi mlungu komanso pamisonkhano ikuluikulu imene timakhala nayo pa chaka, timalandira mphamvu ya mzimu woyera, timalimbikitsa ena kudzera m’zimene timachita chifukwa cha chikhulupiriro komanso timasonyeza kuti ndife atumiki a Ufumu wa Mulungu. Koma chofunika kwambiri n’chakuti timakhala ndi mwayi wolambira Yehova kudzera m’mapemphero athu, ndemanga komanso nyimbo. Misonkhanoyi imakonzedwa mosiyana ndi misonkhano imene Aisiraeli komanso Akhristu oyambirira ankakhala nayo, komabe misonkhano yathu ndi yofunika ngati mmene misonkhano yakaleyo inalili. Koma kodi misonkhano yathu inkachitika bwanji m’mbuyomu?

Misonkhano Imene Timakhala Nayo Mlungu Uliwonse Imalimbikitsa “Chikondi Ndi Ntchito Zabwino”

6, 7. (a) Kodi cholinga cha misonkhano yathu n’chiyani? (b) Kodi misonkhano ya timagulu ta Ophunzira Baibulo inkasiyana bwanji?

6 M’bale Charles Taze Russell atayamba kufufuza choonadi m’Mawu a Mulungu, anazindikira kufunika koti azisonkhana ndi anthu omwe anali ndi cholinga chofanana ndi chake. Mu 1879, M’bale Russell analemba kuti: “Ineyo pamodzi ndi anthu ena a ku Pittsburgh, tinakonza zoti Lamlungu lililonse tizikumana kuti tizifufuza Malemba.” Anthu amene ankawerenga Zion’s Watch Tower ankalimbikitsidwa kuti azisonkhana pamodzi ndipo pofika m’chaka cha 1881, misonkhano inkachitika Lamlungu ndi Lachitatu lililonse ku Pittsburgh, Pennsylvania. Nsanja ya Olonda ya November 1895, inanena kuti cholinga cha misonkhanoyi ndi kulimbikitsa “Akhristu kuti azikondana komanso azigwirizana,” ndiponso kupereka mpata kwa anthu amene asonkhanawo kuti azilimbikitsana.​—Werengani Aheberi 10:24, 25.

7 Kwa zaka zambiri, gulu lililonse la Ophunzira Baibulo linkachita misonkhanoyi mosiyana ndi linzake. Mwachitsanzo, kalata imene gulu lina la Ophunzira Baibulo a ku United States linalemba yomwe inafalitsidwa mu 1911, inanena kuti: “Timasonkhana pafupifupi ka 5 mlungu uliwonse.” Iwo ankasonkhana Lolemba, Lachitatu, Lachisanu ndipo Lamlungu ankasonkhana kawiri. Gulu lina la ku Africa linalemba kalata yomwe inafalitsidwa mu 1914, ndipo inati: “Timasonkhana kawiri pamwezi. Misonkhano yathu imayamba Lachisanu ndipo imatha Lamlungu.” Koma patapita nthawi misonkhanoyi inayamba kuchitika motsatira dongosolo limene tikutsatira masiku ano. Tiyeni tione mmene msonkhano uliwonse umene timakhala nawo pa mlungu wakhala ukuchitikira m’mbuyomu.

8. Kodi ndi nkhani zina ziti zimene zinkakambidwa pamisonkhano ya onse yoyambirira?

8 Msonkhano wa Onse. Mu 1880, patangotha chaka chimodzi kuchokera pamene M’bale Russell anayamba kufalitsa magazini ya Zion’s Watch Tower, anayamba kutsatira chitsanzo cha Yesu ndipo anayamba ulendo wopita m’madera osiyanasiyana kukalalikira. (Luka 4:43) Zimene M’bale Russell ankachita pa ulendowu ndi zimene zinayambitsa msonkhano umene masiku ano timati Msonkhano wa Onse. Polengeza za ulendowu, Nsanja ya Olonda inanena kuti M’bale Russell “akufunitsitsa kukambira anthu onse nkhani ya mutu wakuti ‘Zinthu Zokhudza Ufumu wa Mulungu.’” Mu 1911, pambuyo poti mipingo yakhazikitsidwa m’mayiko ambiri, mpingo uliwonse unkalimbikitsidwa kutumiza wokamba nkhani woyenerera kumadera oyandikana nawo n’cholinga choti akakambe nkhani. Nkhanizi zinalipo 6 ndipo zinali ndi mitu yosiyanasiyana, zina zinkanena za chiweruzo pomwe zina zinkanena za dipo. Nkhani iliyonse ikatha, ankalengeza dzina la wokamba nkhaniyo komanso mutu wa nkhani ya mlungu wotsatira.

9. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zakhala zikusintha pa Msonkhano wa Onse, ndipo inuyo mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira msonkhano umenewu?

9 Mu 1945, Nsanja ya Olonda inalengeza za kuyamba kwa ntchito yochititsa Misonkhano ya Onse padziko lonse. Nkhani zimene zinkayenera kukambidwa pamisonkhanoyi zinalipo 8 ndipo zinkanena za “mavuto akuluakulu amene analipo pa nthawiyo.” Kwa zaka zambiri, anthu amene ankachititsa misonkhanoyi ankakamba nkhani zopatsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndipo nthawi zina ankakamba nkhani zokonza okha. Koma m’chaka cha 1981, okamba nkhani onse anauzidwa kuti azikamba mfundo za m’maautilaini amene amatumizidwa kumipingo. b M’mbuyo monsemu mpaka m’chaka cha 1990, maautilaini ena a nkhani za onse ankakhala ndi mbali yofunsa maganizo a omvera kapena zitsanzo. Koma kuyambira m’chaka chimenechi, malangizo okambira nkhani anasintha ndipo wokamba nkhaniyo amayenera kufotokoza yekha mfundo zonse. Kusintha kwina kunachitika mu January 2008 pamene nthawi yokambira nkhaniyi inasintha kuchoka pa mphindi 45 kufika pa mphindi 30. Ngakhale kuti msonkhanowu wakhala ukusinthasintha, nkhani za onse zokonzedwa bwino zikupitirizabe kulimbitsa chikhulupiriro chathu pa Mawu a Mulungu komanso kupitiriza kutiphunzitsa zinthu zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu. (1 Tim. 4:13, 16) Kodi inuyo mumayesetsa kuitanira anthu amene si Mboni komanso maulendo anu obwereza kuti adzamvetsere nawo nkhani zofunika zochokera m’Baibulo zimenezi?

10-12. (a) Kodi ndi kusintha kotani komwe kwakhala kukuchitika pa nkhani ya mmene Phunziro la Nsanja ya Olonda liyenera kuchitikira? (b) Kodi tingachite bwino kudzifunsa mafunso ati?

10 Phunziro la Nsanja ya Olonda. Mu 1922, abale amene ankatumizidwa ndi Watch Tower Society kuti akakambe nkhani m’mipingo yosiyanasiyana komanso kuti akatsogolere pa ntchito yolalikira, ananena kuti zingakhale bwino ngati patakonzedwa zoti mlungu uliwonse pazikhala msonkhano wophunzira Nsanja ya Olonda. Zimene ananenazo zinayamba kuchitikadi, ndipo poyamba misonkhano yophunzira Nsanja ya Olonda inkachitika mkati mwa mlungu kapena Lamlungu.

Phunziro la Nsanja ya Olonda, ku Ghana, mu 1931

11 Nsanja ya Olonda ya June 15, 1932, inafotokoza malangizo ena a mmene msonkhano umenewu uyenera kuchitikira. Magaziniyi inanena kuti mipingo iyenera kutengera chitsanzo cha msonkhano umene unkachitika ku Beteli ndipo m’bale m’modzi ankayenera kutsogolera msonkhanowo. Abale atatu ankakhala kutsogolo kwa malo omwe msonkhanowo ukuchitikira ndipo ankalandirana kuwerenga ndime. Nkhani za nthawi imeneyo sizinkakhala ndi mafunso, choncho m’bale amene akuchititsa msonkhanowo ankauza omvera kuti azifunsa mafunso ogwirizana ndi nkhani imene akukambiranayo. Kenako ankapempha omvera kuti ayankhe mafunsowo. Ngati zimene anthuwo ayankha sizolondola kwenikweni, wochititsayo ankayenera kufotokozera “mwachidule.”

12 Poyamba, mpingo uliwonse unkaloledwa kusankha magazini imene anthu ambiri mumpingomo akufuna kuphunzira. Koma Nsanja ya Olonda ya April 15, 1933, inanena kuti mipingo yonse iyenera kuphunzira magazini imene yangotuluka kumene. Mu 1937, panaperekedwa malangizo akuti Nsanja ya Olonda iziphunziridwa Lamlungu. Malangizo ena omwe anachititsa kuti msonkhanowu usinthe n’kumachitika ngati mmene umachitikira masiku ano anatuluka mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1942. Choyamba, magaziniyi inanena kuti m’munsi mwa tsamba lililonse la nkhani yomwe akuphunzirayo muzikhala mafunso ndipo azigwiritsa ntchito mafunso amenewo pokambirana. Inanenanso kuti msonkhanowu uzichitika kwa ola limodzi. Inalimbikitsanso omvera kuti akamayankha aziyesa kuyankha “m’mawu awoawo” m’malo momangowerenga yankho pandime. Mpaka pano kapolo wokhulupirika akupitirizabe kugwiritsa ntchito Phunziro la Nsanja ya Olonda popereka chakudya chauzimu pa nthawi yake. (Mat. 24:45) Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimakonzekera phunziro la Nsanja ya Olonda mlungu uliwonse? Kodi ndimayesetsa kuyankha ngati zili zotheka?’

13, 14. (a) Fotokozani mmene Phunziro la Baibulo la Mpingo linkachitikira m’mbuyomu. (b) Kodi n’chiyani chimakusangalatsani kwambiri ndi msonkhano umenewu?

13 Phunziro la Baibulo la Mpingo. M’zaka za m’ma 1890, pambuyo poti mabuku angapo a Millennial Dawn atulutsidwa, wophunzira Baibulo wina, dzina lake H. N. Rahn yemwe ankakhala mumzinda wa Baltimore, ku Maryland, U.S.A., ananena kuti zingakhale bwino patakonzedwa zoti anthu azisonkhana m’timagulu kuti aziphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito mabuku a Millennial Dawn. Poyamba misonkhanoyi inkachitikira m’nyumba za anthu ndipo inali yongoyeserera. Koma pofika mu September 1895, timaguluti tinali titakhazikitsidwa m’mizinda yambiri m’dziko la United States ndipo zinthu zinkayenda bwino. Nsanja ya Olonda ya mwezi umenewu inanena kuti zingakhale bwino Ophunzira Baibulo onse atamachita misonkhano imeneyi. Inanenanso kuti wochititsa phunziroli ayenera kukhala amene ali ndi luso lowerenga. Ankayenera kuwerenga chiganizo chimodzi kenako n’kudikira kuti omvera apereke ndemanga. Akamaliza kuwerenga ndi kukambirana ziganizo zonse za mundime, wochititsayo ankayenera kuwerenga malemba onse amene ali mundimeyo. Pambuyo pokambirana mutu wonse, aliyense amene wabwera ankayenera kufotokoza mwachidule mfundo zikuluzikulu za nkhaniyo.

14 Dzina la msonkhano umenewu lakhala likusintha kangapo konse. Nthawi ina msonkhanowu unkadziwika kuti Phunziro la Baibulo la Abereya, potengera chitsanzo cha Abereya a m’nthawi ya atumwi omwe ankafufuza Malemba mosamala kwambiri. (Mac. 17:11) Patapita nthawi, dzinali linasintha n’kumadziwika kuti Phunziro la Buku la Mpingo. Koma masiku ano timati Phunziro la Baibulo la Mpingo ndipo mpingo wonse umasonkhana pamodzi mu Nyumba ya Ufumu, osati m’nyumba za anthu. Pa zaka zimenezi, pamsonkhanowu anthu akhala akuphunzira mabuku osiyanasiyana, timabuku ngakhalenso nkhani za mu Nsanja ya Olonda. Kuyambira kalekale, anthu onse omwe abwera ankalimbikitsidwa kupereka ndemanga zawo. Msonkhano umenewu watithandiza kwambiri kuti tidziwe bwino Baibulo. Kodi inuyo nthawi zonse mumakonzekera ndiponso kupereka ndemanga mmene mungathere?

15. Kodi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu inakonzedwa ndi cholinga chotani?

15 Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Carey Barber, yemwe pa nthawiyo ankatumikira ku likulu lathu ku Brooklyn, New York, ananena kuti: “Lolemba usiku pa February 16, 1942, abale onse a m’banja la Beteli anaitanidwa kuti alembetse mu msonkhano womwe kenako unayamba kudziwika kuti Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.” M’bale Barber, yemwe patapita zaka zambiri anayamba kutumikira m’Bungwe Lolamulira, ananena kuti sukuluyi ndi “chimodzi mwa zinthu zikuluzikulu zimene Yehova wachitira anthu ake masiku ano.” Maphunziro amenewa anathandiza kwambiri abale kuti akhale ndi luso pophunzitsa komanso polalikira, moti kuyambira mu 1943, kabuku kakuti Course in Theocratic Ministry kanayamba kupezeka m’mipingo pa dziko lonse. Nsanja ya Olonda ya June 1, 1943, inanena kuti Sukulu ya Utumiki wa Mulungu inakonzedwa n’cholinga chothandiza anthu a Mulungu kuti “azidziphunzitsa okha kuti akhale ndi luso pochitira umboni ndiponso kulengeza za Ufumu.”​—2 Tim. 2:15.

16, 17. Kodi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu inkangophunzitsa anthu kulankhula bwino kokha? Fotokozani.

16 Poyamba anthu ambiri ankaona kuti kulankhula pagulu la anthu n’kovuta kwambiri. M’bale Clayton Woodworth, Jr., yemwe bambo ake anamangidwa osalakwa limodzi ndi M’bale Rutherford ndi anthu ena mu 1918, anafotokoza mmene anamvera atangolowa sukuluyi mu 1943. M’bale Woodworth ananena kuti: “Zinkandivuta kwambiri kukamba nkhani. Lilime ndinkalimva kulemera, mkamwa munkauma ndipo mawu anga ankamveka amazenene.” Koma luso lake litayamba kuwonjezeka, M’bale Woodworth anayamba kupatsidwa nkhani zosiyanasiyana pamisonkhano. Kuwonjezera pa kulankhula bwino, sukuluyi inamuphunzitsa kufunika kokhala wodzichepetsa komanso kudalira Yehova. Iye ananena kuti: “Ndinazindikira kuti payekha wokamba nkhani si wofunika. Koma ngati atakonzekera bwino komanso atadalira Yehova, omvera angasangalale kumvetsera nkhani yake ndipo angaphunzirepo kanthu.”

17 Mu 1959, alongo analimbikitsidwa kulembetsa nawo m’sukuluyi. Mlongo Edna Bauer anafotokoza mmene zinalili chilengezo chimenechi chitaperekedwa pamsonkhano. Iye ananena kuti: “Ndikukumbukira mmene alongo anasangalalira atamva chilengezo chimenechi. Anaona kuti umenewu ndi mwayi wawo.” Kwa zaka zambiri abale ndi alongo ambiri ankalembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu kuti aziphunzitsidwa ndi Yehova. Masiku ano timaphunzitsidwa pa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu.​—Werengani Yesaya 54:13.

18, 19. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinkachitika pa Msonkhano wa Utumiki? (b) N’chifukwa chiyani timaimba nyimbo pamisonkhano yathu? (Onani bokosi lakuti, “ Kuimba Nyimbo Zokhala Ndi Mfundo za Choonadi.”)

18 Msonkhano wa Utumiki. M’chaka cha 1919 n’kuti abale atayamba kale kuchita misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda. Pa nthawi imeneyo amene ankakhala nawo pamsonkhano umenewu ndi okhawo amene kwenikweni ntchito yawo inali kugawa mabuku. Kwa miyezi ingapo m’chaka cha 1923, Msonkhano wa Utumiki unkachitika kamodzi pa mwezi ndipo anthu onse mumpingo ankakhalapo. Pofika mu 1928, mipingo inalimbikitsidwa kumakhala ndi Msonkhano wa Utumiki mlungu uliwonse ndipo mu 1935, Nsanja ya Olonda inalimbikitsa mipingo yonse kuti mfundo za pamsonkhanowu azizitenga mu Director (m’kupita kwa nthawi inasintha n’kumadziwika kuti Informant ndipo kenako tinkati Utumiki wa Ufumu). Kenako msonkhanowu unayamba kumaikidwa pa m’ndandanda wa misonkhano ya mpingo.

19 Masiku ano msonkhano umene umachitika mkati mwa mlungu umatithandiza kudziwa zimene tingachite mu utumiki. (Mat. 10:​5-13) Ngati mumalandira Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, kodi mumakonzekera komanso kuyeserera njira zosiyanasiyana zolalikira zimene zimapezekamo?

Msonkhano Wofunika Kwambiri pa Chaka

Kuyambira m’nthawi ya atumwi, Akhristu akhala akusonkhana chaka chilichonse kuti achite Chikumbutso cha imfa ya Khristu (Onani ndime 20)

20-22. (a) N’chifukwa chiyani timakumbukira imfa ya Yesu? (b) Kodi inuyo mumapindula bwanji chifukwa chopezeka pa Chikumbutso chaka chilichonse?

20 Yesu anauza otsatira ake kuti azikumbukira imfa yake mpaka pamene adzabwere. Chikumbutso cha imfa ya Khristu chimachitika kamodzi pa chaka, ngati mmene mwambo wa Pasika unkachitikira. (1 Akor. 11:23-26) Chaka chilichonse, anthu mamiliyoni ambiri amabwera kumsonkhano umenewu. Msonkhanowu umakumbutsa odzozedwa za mwayi womwe ali nawo wolamulira nawo mu Ufumu. (Aroma 8:17) Kwa a nkhosa zina, msonkhano umenewu umawathandiza kulemekeza kwambiri ndiponso kukhala okhulupirika kwa Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.​—Yoh. 10:16.

21 M’bale Russell ndi abale ena anaona kufunika kochita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndipo ankadziwa kuti uyenera kuchitika kamodzi kokha pa chaka. Nsanja ya Olonda ya April 1880, inanena kuti: “Kwa zaka zambiri anthu ambiri kuno ku Pittsburgh takhala ndi chizolowezi . . . chochita Pasika [Chikumbutso] ndiponso kudya zizindikiro za thupi ndi magazi a Ambuye wathu.” Pasanapite nthawi anayamba kukonza zoti misonkhano ikuluikulu izichitika pa nthawi yofanana ndi nthawi ya Chikumbutso. Nthawi yoyamba imene chiwerengero cha anthu opezeka pamsonkhanowu chinasungidwa ndi mu 1889, pamene anthu 225 anapezeka pamsonkhanowu ndipo anthu 22 anabatizidwa.

22 Masiku ano sitichita Chikumbutso pa nthawi yofanana ndi nthawi ya misonkhano ikuluikulu, koma timaitanira anthu onse a m’dera lathu ku Nyumba ya Ufumu kapena kunyumba ya lendi kuti tidzakhale nawo limodzi pa mwambowu. M’chaka cha 2013, anthu oposa 19 miliyoni anapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Panopa tili ndi mwayi waukulu chifukwa sikuti timangopezeka pa Chikumbutso koma timaitaniranso anthu ena kuti adzakhale nawo pa mwambo wofunika kwambiriwu. Kodi inuyo mumayesetsa mmene mungathere kuitanira anthu ambiri ku Chikumbutso chaka chilichonse?

Kodi Timaiona Bwanji Misonkhano Yathu?

23. Kodi mumaiona bwanji misonkhano yathu?

23 Atumiki a Yehova okhulupirika saona kuti langizo loti azisonkhana pamodzi ndi lopanikiza. (Aheb. 10:24, 25; 1 Yoh. 5:3) Mwachitsanzo, Mfumu Davide inkakonda kupita kunyumba yolambirirako Yehova. (Sal. 27:4) Ndipo ankasangalala kwambiri akamalambira Yehova pamodzi ndi anthu enanso omwe ankakonda Mulungu. (Sal. 35:18) Yesu ndi chitsanzo china chabwino. Ngakhale pamene anali wamng’ono, ankafunitsitsa kukhala m’nyumba yolambiriramo Atate ake.​—Luka 2:41-49.

Kufunitsitsa kwathu kusonkhana pamodzi kumasonyeza kuti timaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni

24. Kodi tikapita kumisonkhano timakhala ndi mwayi wosonyeza chiyani?

24 Tikapita kumisonkhano, timasonyeza kuti timakonda Yehova komanso kuti timafuna kulimbikitsa okhulupirira anzathu. Timasonyezanso kuti tikufunitsitsa kuphunzira makhalidwe amene nzika za Ufumu wa Mulungu ziyenera kukhala nawo, chifukwa maphunziro amenewa amaperekedwa pamisonkhano ya mlungu ndi mlungu ndiponso pamisonkhano ikuluikulu. Kuwonjezera pamenepo, misonkhano yathu imatiphunzitsa kuti tikhale ndi luso komanso kutipatsa mphamvu zomwe zingatithandize kupirira pogwira ntchito yofunika kwambiri, yomwe ndi imodzi mwa zinthu zikuluzikulu zimene Ufumu wa Mulungu ukuchita masiku ano. Ntchitoyi ndi yofufuza anthu komanso kuwaphunzitsa kuti akhale otsatira a Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu. (Werengani Mateyu 28:19, 20.) Kufunitsitsa kwathu kusonkhana pamodzi kumasonyeza kuti timaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni. Choncho, nthawi zonse tiyeni tiziona kuti misonkhano yathu ndi yofunika kwambiri.

a Kuwonjezera pa misonkhano ya mpingo yomwe imachitika mlungu uliwonse, banja lililonse kapena munthu aliyense amalimbikitsidwa kuti azikhala ndi nthawi yophunzira Baibulo payekha kapena kuchita kulambira kwa pabanja.

b Pofika m’chaka cha 2013, gulu linali litatulutsa maautilaini a nkhani za onse oposa 180.