Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 17

Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu

Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu

CHOLINGA CHA MUTUWU

Kuona mmene masukulu a gulu athandizira atumiki a Ufumu kuti azisamalira bwino maudindo awo

1-3. Kodi Yesu anawonjezera bwanji ntchito yolalikira, nanga zimenezi zikutichititsa kukhala ndi mafunso ati?

 KWA ZAKA ziwiri, Yesu analalikira dera lonse la Galileya. (Werengani Mateyu 9:35-38.) Anafika m’mizinda ndi midzi yambiri ndipo ankaphunzitsa m’masunagoge komanso kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Kulikonse kumene ankapita kukalalikira, anthu ambiri ankamutsatira. Ataona zimenezi, Yesu ananena kuti “zokolola n’zochuluka” ndipo pakufunika kuwonjezera antchito ena.

2 Yesu anakonza zowonjezera ntchito yolalikirayi. Anachita zimenezi potumiza atumwi ake 12 “kukalalikira ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:1, 2) N’kutheka kuti atumwiwo anali ndi mafunso ambiri okhudza mmene angagwirire ntchitoyi. Koma asanawatumize Yesu mwachikondi anawaphunzitsa ngati mmene Atate ake akumwamba anamuphunzitsira.

3 Pamenepa tikhoza kukhala ndi mafunso angapo: Kodi Yesu anaphunzitsidwa chiyani ndi Atate ake? Kodi Yesu anawaphunzitsa chiyani atumwi ake? Nanga bwanji masiku ano, kodi Mfumu yomwenso ndi Mesiya yaphunzitsa ophunzira ake kugwira ntchito yolalikira? Ngati yawaphunzitsa, kodi yawaphunzitsa bwanji?

“Ndimalankhula . . . Ndendende Mmene Atate Anandiphunzitsira”

4. Kodi Yesu anaphunzitsidwa liti ndipo anaphunzitsidwira kuti?

4 Yesu anavomereza kuti anaphunzitsidwa ndi Atate ake. Pamene ankachita utumiki wake, Yesu ananena kuti: “Ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.” (Yoh. 8:28) Kodi Yesu anaphunzitsidwa liti ndipo anaphunzitsidwira kuti? N’zachidziwikire kuti Yesu, yemwe ndi Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu, anayamba kuphunzitsidwa atangolengedwa. (Akol. 1:15) Kwa zaka zambirimbiri, Mwanayu anakhala kumwamba pambali pa Atate ake akumvetsera komanso kuphunzira kwa ‘Mlangizi Wamkulu.’ (Yes. 30:20) Chifukwa cha zimenezi, Mwanayo anaphunzira makhalidwe, ntchito komanso cholinga cha Atate ake.

5. Kodi Yehova anaphunzitsa chiyani Mwana wake zokhudza utumiki umene anafunika kudzachita padziko lapansi?

5 Pa nthawi yake yoyenerera, Yehova anaphunzitsa Mwana wake za utumiki umene anafunika kudzachita padziko lapansi. Taonani ulosi umene umafotokoza mmene Mlangizi Wamkulu ankaphunzitsira Mwana wake woyamba kubadwa. (Werengani Yesaya 50:4, 5.) Ulosiwu unanena kuti Yehova ankadzutsa Mwana wake “m’mawa uliwonse.” Mawu amenewa akunena za mphunzitsi amene amadzutsa wophunzira wake m’mamawa kuti akamuphunzitse. Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo linanena kuti: “Yehova . . . ankamutenga Yesu ngati mwana wasukulu ndipo ankamuphunzitsa mfundo zoyenera kukalalikira komanso mmene angalalikirire.” Pa sukulu imeneyi, Yehova anaphunzitsa Mwana wake ‘zimene ayenera kunena ndi zimene ayenera kulankhula.’ (Yoh. 12:49) Yehova anaphunzitsanso Mwana wake mmene angaphunzitsire anthu. a Ali padziko lapansi, Yesu anagwiritsa ntchito zimene anaphunzirazo, osati pochita utumiki wake wokha komanso pophunzitsa otsatira ake kukwaniritsa utumiki wawo.

6, 7. (a) Kodi ndi mfundo ziti zimene Yesu anauza atumwi ake, ndipo mfundo zimenezi zinawathandiza bwanji? (b) Kodi Yesu waonetsetsa kuti otsatira ake alandira maphunziro otani masiku ano?

6 Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani atumwi ake? Malinga ndi Mateyu chaputala 10, anawaphunzitsa mfundo zomveka bwino zokhudza utumiki wawo kuphatikizapo mfundo zotsatirazi: kumene ayenera kukalalikira (vesi 5, 6), uthenga woti akalalikire (vesi 7), kufunika kodalira Yehova (vesi 9, 10), mmene angayambire kukambirana ndi munthu (vesi 11-13), zimene angachite ngati wina wakana kumvetsera uthenga wawo (vesi 14, 15), komanso zimene ayenera kuchita akamazunzidwa (vesi 16-23). b Mfundo zomveka zimene Yesu anauza atumwi ake zinawathandiza kuti atsogolere ntchito yolalikira za uthenga wabwino m’nthawi yawo.

7 Nanga bwanji masiku ano? Yesu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, wapatsa otsatira ake ntchito yofunika kwambiri yolalikira “uthenga wabwino uwu wa ufumu . . . padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Kodi Mfumu yatiphunzitsa mmene tingagwirire ntchito yofunikayi? Inde yatiphunzitsa. Ngakhale kuti ili kumwamba, Mfumuyi yaonetsetsa kuti otsatira ake alandira maphunziro omwe angawathandize kulalikira komanso kusamalira maudindo a mumpingo.

Kuphunzitsa Atumiki Kuti Azilalikira

8, 9. (a) Kodi cholinga chachikulu cha Sukulu ya Utumiki wa Mulungu chinali chiyani? (b) Kodi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu yakuthandizani bwanji inuyo pochita utumiki wanu?

8 Gulu la Yehova lakhala likugwiritsa ntchito misonkhano ikuluikulu komanso misonkhano ya pampingo, monga Msonkhano wa Utumiki, kuphunzitsa anthu a Mulungu mmene angagwirire ntchito yolalikira. Koma kuyambira m’zaka za m’ma 1940, abale amene ankatsogolera gulu lathu pa nthawiyo anayamba kuphunzitsa atumiki a Mulungu kudzera m’masukulu osiyanasiyana.

9 Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Monga taonera m’Mutu 16, sukuluyi inayamba mu 1943. Kodi cholinga cha sukuluyi chinali kungophunzitsa anthu kuti azikamba bwino nkhani pamisonkhano ya mpingo? Ayi. Cholinga chachikulu cha sukuluyi chinali kuphunzitsa anthu a Mulungu kuti azigwiritsa ntchito mphatso yawo ya kulankhula polemekeza Yehova mu utumiki, ndipo cholinga chimenechi sichinasinthe. (Sal. 150:6) Abale ndi alongo amene analembetsa m’sukuluyi ankaphunzitsidwa kugwira bwino ntchito yawo monga atumiki a Ufumu. Masiku ano abale ndi alongo amaphunzitsidwa kudzera mu msonkhano wa mkati mwa mlungu.

10, 11. Kodi ndani amene angalowe Sukulu ya Giliyadi panopa, ndipo kodi cholinga cha zinthu zimene amaphunzitsa kusukuluyi n’chiyani?

10 Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Sukuluyi inayamba Lolemba pa February 1, 1943, ndipo cholinga chake chinali kuphunzitsa apainiya komanso ena omwe anali mu utumiki wa nthawi zonse kuti akakhale amishonale m’mayiko ena. Koma kuyambira mu October 2011, panakhala kusintha pa nkhani ya anthu oyenera kulowa m’sukuluyi. Panopa omwe angalowe m’sukuluyi ndi okhawo amene ali kale mu utumiki wa nthawi zonse monga apainiya apadera, oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo, amene akutumikira pa Beteli komanso amishonale omwe sanalowepo m’sukuluyi.

11 Kodi cholinga cha zinthu zimene amaphunzitsa ku Sukulu ya Giliyadi n’chiyani? M’bale wina yemwe wakhala mlangizi kwa nthawi yaitali ananena kuti: “Cholinga chake ndi kulimbitsa chikhulupiriro cha ophunzirawo pophunzira mozama Mawu a Mulungu komanso kuwathandiza kuti akhale ndi makhalidwe abwino amene angawathandize kupirira mavuto omwe angakumane nawo pa utumiki wawo. Komanso, cholinga chachikulu cha zimene amaphunzirazo ndi kulimbikitsa ophunzirawo kuti akhale ndi mtima wofunitsitsa kulalikira.”​—Aef. 4:11.

12, 13. Kodi Sukulu ya Giliyadi yathandiza bwanji ntchito yolalikira? Perekani chitsanzo.

12 Kodi Sukulu ya Giliyadi yathandiza bwanji ntchito yolalikira padziko lonse? Kuyambira mu 1943, anthu oposa 8,500 alowa m’sukulu imeneyi, c ndipo amishonale omwe analowa sukulu ya Giliyadi atumikira m’mayiko oposa 170. Amishonalewa amagwiritsa ntchito bwino zimene aphunzira ndipo amachita zimenezi polalikira mwakhama komanso pophunzitsa ena kuti nawonso azilalikira mwakhama. Nthawi zambiri amishonale amayambitsa ntchito yolalikira m’madera amene kulibe ofalitsa Ufumu kapena kutsogolera ntchitoyi m’madera amene kuli ofalitsa ochepa.

13 Taganizirani zimene zinachitika ku Japan, komwe ntchito yolalikira monga gulu inasiyiratu pa nthawi imene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkachitika. Pofika mu August 1949, ku Japan kunali ofalitsa osapitirira 10. Koma kumapeto kwa chaka chimenechi, amishonale 13 oti analowapo Sukulu ya Giliyadi anayamba kulalikira ku Japan. Kenako amishonale ena anabweranso kudzagwira nawo ntchitoyi. Poyamba amishonalewa ankalalikira kwambiri m’mizinda ikuluikulu koma kenako anayamba kulalikiranso m’mizinda ina. Iwo ankalimbikitsa ophunzira awo komanso abale ndi alongo ena kuti ayambe upainiya. Khama la amishonalewa silinapite pachabe chifukwa panopa ku Japan kuli olengeza Ufumu oposa 216,000, ndipo olengeza Ufumu 40 pa 100 alionse akuchita upainiya. d

14. Kodi masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu amatipatsa umboni wa chiyani? (Onaninso bokosi lakuti, “ Masukulu Amene Amaphunzitsa Atumiki a Ufumu,” patsamba 188.)

14 Masukulu ena ophunzitsa atumiki a Mulungu. Masukulu ngati Sukulu ya Utumiki Waupainiya, Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja komanso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira anathandiza ophunzira kukhala anthu auzimu komanso kuti azitsogolera ntchito yolalikira mwakhama. e Sukulu zimenezi ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti Mfumu yathu ikuphunzitsa mokwanira otsatira ake kuti akwanitse utumiki wawo.​—2 Tim. 4:5.

Maphunziro Omwe Amathandiza Abale Kusamalira Maudindo Apadera

15. Kodi abale amene ali ndi udindo amatsatira bwanji chitsanzo cha Yesu?

15 Kumbukirani ulosi wa Yesaya womwe unanena zoti Yesu adzaphunzitsidwa ndi Mulungu. Pa sukuluyi, Mwanayo anaphunzira ‘mmene angamuyankhire munthu wotopa.’ (Yes. 50:4) Yesu anagwiritsa ntchito malangizo amenewo atabwera padziko lapansi. Iye anatsitsimula “ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa.” (Mat. 11:28-30) Potsatira Yesu, abale amene ali ndi maudindo apadera afunika kumachita zinthu zotsitsimula abale ndi alongo. Pa chifukwa chimenechi, pakhazikitsidwa masukulu osiyanasiyana n’cholinga chothandiza abale amaudindo kuti azitha kuthandiza bwino okhulupirira anzawo.

16, 17. Kodi cholinga cha Sukulu ya Utumiki wa Ufumu n’chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi.)

16 Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Kalasi yoyamba ya sukuluyi inayamba pa March 9, 1959, ku South Lansing, New York. Oyang’anira oyendayenda komanso atumiki a mipingo ankaitanidwa kukalowa m’sukuluyi yomwe inali ya mwezi umodzi. Patapita nthawi, zimene ankaphunzira m’sukuluyi anazimasulira m’zinenero zina ndipo sukuluyi inayamba kuchitika m’mayiko osiyanasiyana. f

M’bale Lloyd Barry akuphunzitsa mu Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Japan, m’chaka cha 1970

17 Pofotokoza cholinga cha Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1962 linanena kuti: “M’dziko limene anthu tonsefe ndife otanganidwa, m’bale amene ali ndi udindo woyang’anira mpingo wa Mboni za Yehova ayenera kuchita zinthu mwadongosolo kuti azitha kusamalira zosowa za aliyense mumpingo komanso kuti akhale dalitso kwa abale ndi alongowo. Zimenezi sizikutanthauza kuti asamasamalire banja lake koma kuti ayenera kuchita zinthu moganiza bwino. Kunena zoona atumiki a mipingo padziko lonse ali ndi mwayi wophunzitsidwa mu Sukulu ya Utumiki wa Ufumu kuti akwanitse kuchita zimene Baibulo limanena pa utumiki wawo.”​—1 Tim. 3:1-7; Tito 1:5-9.

18. Kodi anthu onse a Mulungu amapindula bwanji ndi Sukulu ya Utumiki wa Ufumu?

18 Kodi anthu onse a Mulungu apindula bwanji ndi Sukulu ya Utumiki wa Ufumu? Akulu komanso atumiki othandiza akamagwiritsa ntchito zimene aphunzira m’sukuluyi amakhala olimbikitsa kwa okhulupirira anzawo ngati mmene Yesu anachitira. Kodi inuyo mumayamikira mkulu kapena mtumiki wothandiza akakuuzani mawu olimbikitsa, akamamvetsera mwatcheru kapena akabwera kunyumba kwanu kudzakulimbikitsani? (1 Ates. 5:11) Kukhala ndi abale amene analowa m’sukulu imeneyi m’mipingo ndi dalitso lalikulu kwambiri.

19. Kodi ndi masukulu ena ati amene Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa imayang’anira, nanga cholinga cha masukuluwo n’chiyani?

19 Masukulu ena ophunzitsa atumiki a Mulungu. Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira imayang’anira masukulu ena amene amaphunzitsa abale omwe ali ndi udindo m’gulu la Yehova. Masukulu amenewa amakonzedwa n’cholinga chothandiza abale omwe ndi akulu mumpingo, oyang’anira oyendayenda ndiponso abale omwe ali m’Makomiti a Nthambi kuti azisamalira bwino maudindo awo. Maphunzirowa, omwe mfundo zake zimakhala zochokera m’Baibulo, amalimbikitsa abalewa kuti azikhala olimba mwauzimu. Amawalimbikitsanso kuti azitsatira mfundo za m’Baibulo pochita zinthu ndi nkhosa zimene Yehova anawapatsa kuti aziyang’anire.​—1 Pet. 5:1-3.

Kalasi yoyamba ya Sukulu Yophunzitsa Utumiki imene inachitika ku Malawi, m’chaka cha 2007

20. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu sanalakwitse pamene ananena kuti tonsefe ‘taphunzitsidwa ndi Yehova’? Kodi inuyo muziyesetsa kuchita chiyani?

20 Apa n’zoonekeratu kuti Mfumu yomwenso ndi Mesiya yaonetsetsa kuti otsatira ake aphunzitsidwa bwino. Maphunziro amenewa akhala akuchitika mwadongosolo chifukwa Yehova anaphunzitsa Mwana wake kenako Mwanayo waphunzitsa otsatira ake. Mpake kuti Yesu ananena kuti tonsefe ‘taphunzitsidwa ndi Yehova.’ (Yoh. 6:45; Yes. 54:13) Choncho, tiyeni tonsefe tizigwiritsa ntchito maphunziro amene Mfumu yathu ikutipatsa. Ndipo tizikumbukira kuti cholinga chachikulu cha maphunziro onsewa ndi kutithandiza kukhala olimba mwauzimu kuti tikwanitse kuchita utumiki wathu.

a Kodi tikudziwa bwanji kuti Atate anaphunzitsa Mwana mmene angalalikirire? Taganizirani izi: Pophunzitsa, Yesu ankagwiritsa ntchito kwambiri mafanizo ndipo zimenezi zinakwaniritsa ulosi umene unalembedwa zaka zambirimbiri asanabadwe. (Sal. 78:2; Mat. 13:34, 35) Apa n’zoonekeratu kuti amene ananena ulosi umenewu, yemwe ndi Yehova, anadziwiratu kuti Mwana wake azidzaphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito mafanizo kapena miyambi.​—2 Tim. 3:16, 17.

b Patapita miyezi ingapo, Yesu “anasankha anthu ena 70 ndi kuwatumiza awiriawiri” kuti akalalikire. Koma asanawatumize anawaphunzitsa mmene angalalikirire.​—Luka 10:1-16.

c Ena analowa Sukulu ya Giliyadi maulendo angapo.

d Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene amishonale omwe analowa mu Sukulu ya Giliyadi athandizira anthu padziko lonse, onani mutu 23 wa buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom.

e Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja komanso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira zinaphatikizidwa kukhala sukulu imodzi ndipo ikudziwika ndi dzina lakuti Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu.

f Masiku ano akulu onse amalowa mu Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Sukuluyi imachitika pakapita zaka zingapo ndipo nthawi imene imatenga imakhala yosiyanasiyana. Kuyambira m’chaka cha 1984 atumiki othandiza anayambanso kulowa nawo sukuluyi.