Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 18

Mmene Timapezera Ndalama Zoyendetsera Ntchito za Ufumu

Mmene Timapezera Ndalama Zoyendetsera Ntchito za Ufumu

CHOLINGA CHA MUTUWU

Kuona zimene zimachititsa anthu a Yehova kupereka ndalama zothandizira pa ntchito ya Ufumu komanso mmene amaperekera ndalamazi

1, 2. (a) Kodi M’bale Russell anamuyankha bwanji munthu amene ankafuna kudziwa mmene amapezera ndalama zoyendetsera ntchito za Ophunzira Baibulo? (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutuwu?

 PA NTHAWI ina, munthu wina wa tchalitchi cha Reformed Church anapita kwa M’bale Charles T. Russell n’kumufunsa mmene amapezera ndalama zoyendetsera ntchito za Ophunzira Baibulo.

 M’bale Russell anamuuza kuti: “Sitimayendetsa mbale ya zopereka.”

 Munthuyo anafunsanso kuti: “Ndiye mumapeza bwanji ndalama?”

 M’bale Russell anayankha kuti: “Simungakhulupirire nditakuuzani mmene timapezera ndalama. Anthu amati akabwera kumisonkhano yathu saona mbale ya zopereka ikuyendetsedwa. Koma akaona malo olambirirawo amadziwa kuti pamafunika kugula zinthu zokonzera malowo. Ndiyeno amadzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndipereke ndalama zothandizira pamalo amenewa?’”

 Munthu uja anayang’ana M’bale Russell modabwa kwambiri.

 M’bale Russell anamuuza kuti: “Zimenezi n’zimene zimachitika. Nawonso anthu amene abwera kudzasonkhana amandifunsa kuti, ‘Kodi ndingapereke bwanji ndalama zothandizira pa ntchitoyi?’ Anthu amene zinthu zikuwayendera ndipo ali ndi ndalama, amafuna kuthandiza pa ntchito ya Ambuye. Ngati munthu alibe ndalama sitimukakamiza kupereka.” a

2 M’bale Russell ananena zimene zimachitikadi. Kuyambira kale kwambiri anthu a Mulungu akhala akupereka ndalama zothandizira kulambira koona. M’mutu uno, tikambirana zitsanzo za m’Malemba za anthu amene anapereka zinthu pothandiza kulambira koona komanso zimene zakhala zikuchitika m’nthawi yathu ino. Tikamakambirana mmene timapezera ndalama zoyendetsera ntchito za Ufumu, aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndingatani kuti ndithandize nawo pa ntchito ya Ufumu?’

“Aliyense Amene Ali Ndi Mtima Wofunitsitsa Apereke”

3, 4. (a) Kodi Yehova amakhulupirira kuti anthu amene amamulambira akhoza kuchita chiyani? (b) Kodi Aisiraeli anathandiza bwanji pa ntchito yomanga chihema?

3 Yehova amakhulupirira amene amamulambira. Iye amadziwa kuti anthu amene amamulambira akapatsidwa mwayi wopereka zinthu zothandizira pa ntchito yake amapereka ndi mtima wonse. Tiyeni tione zitsanzo ziwiri za m’nthawi ya Aisiraeli.

4 Atatulutsa Aisiraeli mu Iguputo, Yehova anawauza kuti amange chihema, kapena kuti tenti, choti azilambiriramo. Kuti amange chihemachi komanso kuti akonze zinthu zogwiritsira ntchito pachihemapo pankafunika zinthu zambiri. Yehova analankhula ndi Mose kuti apereke mwayi kwa anthu wopereka zinthu zothandizira pa ntchitoyi. Iye anati: “Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa apereke kwa Yehova.” (Eks. 35:5) Kodi anthuwo, omwe kwa nthawi yaitali ankagwira “ntchito yaukapolo wa mtundu uliwonse,” anatani atamva mawu amenewa? (Eks. 1:14) Anapereka moolowa manja golide, siliva ndiponso zinthu zina zamtengo wapatali, zomwe mwina anapatsidwa ndi Aiguputo omwe ankawagwiritsa ntchito ya ukapolo. (Eks. 12:35, 36) Aisiraeli anapereka zinthu zambiri kuposa zimene zinkafunikira, moti anachita ‘kuwaletsa kubweretsa zinthuzo.’​—Eks. 36:4-7.

5. Kodi Aisiraeli anatani Davide atawapatsa mwayi wopereka zinthu zothandiza pa ntchito yomanga kachisi?

5 Patapita zaka 475, nayenso Davide anapereka “chuma chapadera” kuti athandize pa ntchito yomanga kachisi, yemwe anali malo oyamba olambiriramo padziko lapansi. Kenako anapatsa Aisiraeli anzake mwayi woti apereke zinthu zothandizira pa ntchitoyi powafunsa kuti: “Ndani lero ali wokonzeka kupereka mphatso kwa Yehova?” Anthuwo “anapereka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Mbiri 29:3-9) Chifukwa chodziwa kumene zoperekazo zinkachokera, Davide anauza Yehova m’pemphero kuti: “Pakuti chilichonse n’chochokera kwa inu, ndipo tapereka kwa inu zochokera m’dzanja lanu.”​—1 Mbiri 29:14.

6. N’chifukwa chiyani ntchito za Ufumu masiku ano zimafuna ndalama, nanga zimenezi zimabweretsa mafunso otani?

6 Mose komanso Davide sanakakamize anthu a Mulungu kuti apereke zinthu. Anthu anapereka zinthuzo mwa kufuna kwawo. Nanga bwanji masiku ano? Nafenso timadziwa kuti pamafunika ndalama kuti ntchito ya Ufumu wa Mulungu iyende. Pamafunika zinthu zambiri kuti tisindikize ndiponso kuti tigawe mabaibulo komanso mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo. Pamafunikanso zinthu zambiri kuti timange ndi kukonza malo amene timasonkhanapo ndiponso maofesi a nthambi. Pamafunikanso zinthu zambiri kuti tithandize okhulupirira anzathu pa nthawi ya mavuto. Zimenezi zimabweretsa mafunso akuti: Kodi timapeza bwanji ndalama zogwirira ntchito zimenezi? Kodi anthu otsatira Mfumu amakakamizidwa kupereka ndalama?

“Sitidzapemphetsa Kwa Anthu Kapena Kuwachonderera Kuti Athandize pa Ntchito Imeneyi”

7, 8. N’chifukwa chiyani anthu a Yehova sapemphetsa ndalama kwa anthu?

7 M’bale Russell ndi anzake anakana kutsatira njira zimene matchalitchi amene amati ndi achikhristu amatsatira pofuna kupeza ndalama. M’magazini yachiwiri ya Nsanja ya Olonda, yomwe inali ndi nkhani ya mutu wakuti “Kodi Mukufuna Magazini ya ‘Zion’s Watch Tower’?,” M’bale Russell ananena kuti: “‘Sitikayikira zoti YEHOVA ndi amene akutsogolera ntchito yofalitsa magazini ino ya ‘Zion’s Watch Tower,’ motero sitidzapemphetsa kwa anthu kapena kuwachonderera kuti athandize pa ntchito imeneyi. Mwiniwakeyo, amene ananena kuti: ‘Siliva ndi golidi yense wa m’mapiri ndi wanga,’ akadzalephera kupereka ndalama zokwanira, tidzadziwa kuti nthawi yosiya kufalitsa magaziniyi yakwana.” (Hag. 2:7-9) Panopa papita zaka zoposa 130 ndipo Nsanja ya Olonda komanso gulu limene limafalitsa magaziniyi likupitirizabe kugwira ntchito.

8 Anthu a Yehova samapemphetsa ndalama. Samayendetsa mbale ya zopereka kapena kutumiza makalata opempha ndalama. Samachitanso bizinezi, madansi kapena mipikisano kuti apeze ndalama. Amatsatira zimene Nsanja ya Olonda ina ya kale kwambiri inanena kuti: “Sitinaganizirepo kuti kupemphetsa ndalama ndi njira yoyenera yopezera ndalama pa ntchito ya Ambuye, ngati mmene matchalitchi ena amachitira . . . Timaona kuti kupemphetsa ndalama m’dzina la Ambuye n’kulakwa komanso kunyoza Ambuye ndipo iye sadalitsa ntchitoyo kapena amene akupereka ndamalazo.” b

“Aliyense Achite Mogwirizana Ndi Mmene Watsimikizira Mumtima Mwake”

9, 10. Tchulani chifukwa chimodzi chimene timaperekera zinthu mwa kufuna kwathu.

9 Monga nzika za Ufumu, nafenso masiku ano sitikakamizidwa kupereka zinthu pothandiza ntchito za Ufumu. M’malomwake, timasangalala kupereka ndalama zathu komanso zinthu zina kuti tithandize nawo pa ntchito za Ufumu. N’chifukwa chiyani timafunitsitsa kupereka zinthuzi? Tikambirana zifukwa zitatu.

10 Choyamba, timapereka zinthu mwa kufuna kwathu chifukwa timakonda Yehova ndipo timafuna “kuchita zinthu zomukondweretsa.” (1 Yoh. 3:22) Yehova amasangalala ndi munthu amene amapereka kuchokera pansi pa mtima. Tiyeni tikambirane mawu a mtumwi Paulo ofotokoza zimene Mkhristu ayenera kuchita akafuna kupereka. (Werengani 2 Akorinto 9:7.) Mkhristu woona sapereka mokakamizika kapena monyinyirika. M’malomwake, amapereka chifukwa chakuti “watsimikizira mumtima mwake” kuti apereke. c Zimenezi zikutanthauza kuti amayamba waona zinthu zimene zikufunikira kenako amaganizira mmene angathandizire. Yehova amakonda munthu woteroyo chifukwa “Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” Pa vesi limeneli, Baibulo lina linanena kuti: “Mulungu amakonda anthu amene amakonda kupereka.”

Nawonso ana a ku Mozambique amakonda kupereka

11. N’chiyani chimatichititsa kuti tizipereka kwa Yehova mphatso zabwino kwambiri?

11 Chachiwiri, timapereka zinthu chifukwa timaona kuti imeneyi ndi njira imodzi yothokozera Yehova pa zimene watichitira. Tiyeni tione mfundo ina yopezeka mu Chilamulo cha Mose yomwe ingachititse munthu kudzifufuza kuchokera pansi pa mtima. (Werengani Deuteronomo 16:16, 17.) Popita kuzikondwerero zitatu zomwe zinkachitika pa chaka, mwamuna aliyense wachiisiraeli ankafunika kupereka mphatso “yolingana ndi madalitso amene Yehova” wamupatsa. Choncho, asanapite kuzikondwererozo, ankafunika kuwerengetsera kaye madalitso amene walandira komanso kudzifufuza kuchokera pansi pa mtima n’cholinga choti asankhe mphatso yoyenera kukapereka. Ifenso tikamaganizira njira zambiri zimene Yehova watidalitsira, timafunitsitsa kumupatsa mphatso zabwino kwambiri. Mphatso zimene timapereka kuchokera pansi pa mtima, zomwe zimaphatikizapo ndalama, zimasonyeza kuti timayamikira kwambiri madalitso amene Yehova watipatsa.​—2 Akor. 8:12-15.

12, 13. Kodi zinthu zimene timapereka mwa kufuna kwathu zimasonyeza bwanji kuti timakonda Mfumu? Kodi aliyense amapereka zochuluka bwanji?

12 Chachitatu, tikamapereka zinthu mwa kufuna kwathu timasonyeza kuti timakonda Mfumu yathu Yesu Khristu. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyeni tione zimene Yesu anauza ophunzira ake usiku wake womaliza ali padziko lapansi. (Werengani Yohane 14:23.) Yesu ananena kuti: “Ngati munthu amandikonda, adzasunga mawu anga.” “Mawu” amene Yesu ananena akuphatikizapo lamulo loti tizilalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Timasonyeza kuti tikusunga “mawu” mwa kuchita zonse zomwe tingathe pogwiritsa ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu komanso ndalama zathu kuti tithandize pa ntchito yolalikira za Ufumu. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timakonda Mfumu yomwenso ndi Mesiya.

13 Monga nzika za Ufumu zokhulupirika timapereka ndalama zathu posonyeza kuti timafunitsitsa kuthandiza pa ntchito za Ufumu. Koma kodi tingapereke zochuluka bwanji? Aliyense amasankha yekha malinga ndi zimene angakwanitse. Komabe, okhulupirira anzathu ambiri alibe zinthu zambiri za m’dzikoli. (Mat. 19:23, 24; Yak. 2:5) Koma anthu amenewa amalimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova pamodzi ndi Mwana wake amayamikira ngakhale zopereka zochepa ngati zaperekedwa kuchokera pansi pa mtima.​—Maliko 12:41-44.

Njira Zolandirira Ndalama

14. Kwa zaka zambiri, kodi Mboni za Yehova zinkagawira bwanji mabuku awo?

14 Kwa zaka zambiri mabuku amene Mboni za Yehova zakhala zikugawira anali ndi mtengo. Ankayesetsa kuti mtengo umenewu ukhale wotsika n’cholinga choti ngakhale anthu osauka azitha kupeza mabuku athu. Komabe ngati munthu ali ndi chidwi koma alibe ndalama iliyonse, ofalitsa anali okonzeka kungomupatsa mabukuwo. Cholinga cha ofalitsa Ufumuwo chinali choti anthu ambiri a mtima wabwino akhale ndi mwayi wowerenga komanso wopindula ndi mabuku athu.

15, 16. (a) Kuyambira mu 1990, kodi Bungwe Lolamulira linasintha bwanji mmene tinkagawira mabuku athu? (b)  Kodi anthu amene akufuna kupereka ndalama zothandizira ntchito za Ufumu amakazipereka kuti? (Onaninso bokosi lakuti, “ Kodi Zopereka Zathu Zimapita Kuti?”)

15 M’chaka cha 1990, Bungwe Lolamulira linayamba kusintha njira yogawira mabuku athu. Kuyambira chaka chimenecho abale ndi alongo a ku United States, anayamba kugawira mabuku athu onse popanda mtengo uliwonse. Kalata imene inatumizidwa kumipingo yonse ya m’dzikoli inanena kuti: “Mabuku ndi magazini athu aziperekedwa kwa ofalitsa ndiponso kwa anthu achidwi popanda kuwauza mtengo weniweni woti apereke asanalandire zinthuzo. . . . Aliyense amene akufuna kupereka ndalama n’cholinga choti zithandize pa ntchito yophunzitsa Baibulo akhoza kupereka koma angalandirebe mabuku athu ngakhale atapanda kupereka ndalamayo.” Kusintha kumeneku kunathandiza anthu kudziwa kuti cholinga chathu chachikulu ndi kuthandiza anthu mwauzimu komanso kuti ntchito yathu imayendetsedwa ndi ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Kusinthaku kunathandizanso anthu kudziwa kuti “mawu a Mulungu sitichita nawo malonda.” (2 Akor. 2:17) Patapita nthawi, mayiko onse anayamba kutsatira njira imeneyi.

16 Kodi anthu amene akufuna kupereka ndalama zothandizira ntchito za Ufumu amakazipereka kuti? Mu Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova anaikamo mabokosi amene munthu akhoza kuponyamo ndalama. Munthu amathanso kupereka ndalamazi kudzera ku mabungwe ovomerezeka mwa lamulo a Mboni za Yehova. Chaka chilichonse m’magazini ya Nsanja ya Olonda mumakhala nkhani yofotokoza mmene anthu angaperekere ndalamazi.

Kodi Ndalamazi Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?

17-19. Kodi zopereka zimagwiritsidwa ntchito bwanji: (a) pa ntchito yapadziko lonse, (b) pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu padziko lonse, (c) polipirira zinthu pa mpingo?

17 Ntchito Yapadziko Lonse. Ndalama za m’bokosi la “Ntchito Yapadziko Lonse” zimagwiritsidwa ntchito kulipirira zinthu pa ntchito yolalikira padziko lonse. Zinthu zimenezi ndi monga kulipira zinthu zosindikizira mabuku omwe amafalitsidwa padziko lonse, kumanga ndi kukonza maofesi a nthambi, nyumba za Beteli komanso kuyendetsa masukulu osiyanasiyana ophunzitsa atumiki a Mulungu. Amagwiritsanso ntchito ndalamazi posamalira amishonale, oyang’anira oyendayenda komanso apainiya apadera. Ndalamazi zimagwiranso ntchito pothandiza okhulupirira anzathu pa nthawi ya mavuto. d

18 Kumanga Nyumba za Ufumu padziko lonse. Ndalama za m’bokosi la “Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Padziko Lonse” zimagwiriritsidwa ntchito kuthandiza mipingo kuti imange kapena kukonza Nyumba za Ufumu. Anthu akamapereka ndalama m’bokosi limeneli zimathandiza kuti papezeke ndalama zokwanira zothandiziranso mipingo ina. e

19 Kulipirira zinthu pa mpingo. Ndalama za m’bokosi la “Zopereka Zothandiza pa Mpingo” zimagwiritsidwa ntchito kulipirira zinthu zofunika pampingo komanso posamalira Nyumba ya Ufumuyo. Nthawi zina akulu akhoza kuona kuti ndi bwino kutumizako ndalama ku ofesi ya nthambi kuti zikagwiritsidwe ntchito pothandiza ntchito yapadziko yonse. Zikatero akulu amafunsa kaye mpingo wonse ndipo ukavomereza amatumiza ndalamazo ku ofesi ya nthambi. Mwezi uliwonse, m’bale amene amasamalira ndalama za mpingo amakonza lipoti limene limawerengedwa ku mpingo.

20. Kodi mungalemekeze bwanji Yehova ndi zinthu zanu “zamtengo wapatali”?

20 Tikaganizira zimene zimafunika kuti ntchito yolalikira za Ufumu komanso ntchito yopanga ophunzira padziko lonse iyende bwino, timafunitsitsa ‘kulemekeza Yehova ndi zinthu zathu zamtengo wapatali.’ (Miy. 3:9, 10) Zinthu zathu zamtengo wapatali zimaphatikizapo mphamvu zathu, maganizo athu komanso zinthu zauzimu zimene taphunzira. Timafunitsitsa kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi pogwira ntchito ya Ufumu. Koma kumbukiraninso kuti zinthu zathu zamtengo wapatali zikuphatikizapo chuma chimene tili nacho. Choncho tiyeni tiziyesetsa kupereka zimene tingakwanitse pamene tingakwanitse kutero. Zinthu zimene timapereka zimalemekeza Yehova komanso zimasonyeza kuti tikufuna kuthandiza Ufumu womwe wolamulira wake ndi Mesiya.

a Nsanja ya Olonda ya July 15, 1915, tsamba 218-219.

b Nsanja ya Olonda ya August 1, 1899, tsamba 201.

c Katswiri wina wolemba mabuku ananena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “watsimikizira” amatanthauza kuti munthuyo amayamba waganiza kaye. Iye ananenanso kuti: “Ngakhale kuti munthu amasangalalabe ngakhale atapereka osakonzekera, ayenera kuganizira kaye komanso kutsatira dongosolo lake.”​—1 Akor. 16:2.

d Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yothandiza anthu pa nthawi ya mavuto, werengani Mutu 20.

e Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yomanga Nyumba za Ufumu, werengani Mutu 19.