Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 19

Ntchito Yomanga Yomwe Imalemekeza Yehova

Ntchito Yomanga Yomwe Imalemekeza Yehova

CHOLINGA CHA MUTUWU

Ntchito yomanga yomwe ikuchitika padziko lonse imathandiza ntchito za Ufumu

1, 2. (a) Kodi atumiki a Yehova amasangalala kuchita chiyani? (b) Kodi n’chiyani chimene Yehova amaona kuti n’chofunika kwambiri?

 KUYAMBIRA kale kwambiri atumiki a Yehova okhulupirika akhala akusangalala kumanga nyumba zimene zimalemekeza dzina lake. Mwachitsanzo, Aisiraeli anasangalala kuthandiza nawo pomanga chihema ndiponso kupereka zinthu zosiyanasiyana zofunikira pa ntchitoyi.​—Eks. 35:30-35; 36:1, 4-7.

2 Sikuti kwenikweni Yehova amaona kuti zipangizo zomangirazo ndi zimene zimalemekeza dzina lake ndipo samaona kuti zinthu zimenezi ndi zimene zili zofunika kwambiri. (Mat. 23:16, 17) Chimene Yehova amaona kuti n’chofunika kwambiri ndi kulambira kumene atumiki ake amachita, kudzipereka kwawo komanso kugwira kwawo ntchito mwakhama. Zimenezi zili ngati mphatso za mtengo wapatali zimene zimalemekeza dzina la Yehova. (Eks. 35:21; Maliko 12:41-44; 1 Tim. 6:17-19) Mfundo imeneyi ndi yomveka chifukwa nyumba zimene zimamangidwazo zimatha m’kupita kwa nthawi. Mwachitsanzo, chihema komanso kachisi uja panopa kulibe koma Yehova sanaiwale kuwolowa manja komanso ntchito yaikulu imene atumiki ake okhulupirika anagwira pomanga zinthu zimenezi.​—Werengani 1 Akorinto 15:58; Aheberi 6:10.

3. Kodi tikambirana chiyani m’mutu umenewu?

3 Atumiki a Yehova amasiku ano amagwiranso ntchito yomanga malo olambirira. Ndipo n’zochititsa chidwi kuona zimene takwanitsa kuchita motsogoleredwa ndi Mfumu yathu Yesu Khristu. Uwu ndi umboni wakuti Yehova wadalitsa khama lathu. (Sal. 127:1) M’mutu umenewu tiona zina mwa ntchito zimene zagwiridwa komanso mmene zalemekezera Yehova. Tionanso zimene anthu ena omwe anagwira nawo ntchito imeneyi ananena.

Kumanga Nyumba za Ufumu

4. (a) N’chifukwa chiyani tikufunikira malo ambiri olambirira? (b) N’chifukwa chiyani nthambi zambiri zaphatikizidwa? (Onani bokosi lakuti, “ Kusintha kwa Maofesi a Nthambi.”)

4 Monga mmene tinaonera m’Mutu 16, Yehova amafuna kuti tizisonkhana n’kumamulambira. (Aheb. 10:25) Misonkhano imeneyi sikuti imangolimbitsa chikhulupiriro chathu basi, koma imatilimbikitsanso kugwira ntchito yolalikira. Pamene masiku otsiriza akupita kumapeto, Yehova akupitiriza kulimbikitsa anthu ake kuti ntchitoyi igwiridwe mwachangu. Zimenezi zachititsa kuti anthu ambiri azilowa m’gulu lake chaka chilichonse. (Yes. 60:22) Kuchuluka kwa nzika za Ufumu kumeneku kukuchititsa kuti pafunike kumanga nyumba zina zosindikizira mabuku athu. Pakufunikanso kuwonjezera malo olambirirako.

5. N’chifukwa chiyani dzina lakuti Nyumba ya Ufumu lili loyenerera? (Onaninso bokosi lakuti, “ Tchalitchi cha Kuwala Kwatsopano.”)

5 Gulu la masiku ano la anthu a Yehova litangoyamba, Ophunzira Baibulo anayamba kuona kufunika kokhala ndi malo awoawo osonkhana. Zikuoneka kuti malo osonkhanira oyamba kumangidwa anali a ku West Virginia, ku America, omwe anamangidwa mu 1890. Pofika m’zaka za m’ma 1930, anthu a Yehova anali atamanga kapena kukonzanso nyumba zambiri koma nyumba zolambirira zimenezi zinalibe dzina lapadera. Koma mu 1935, M’bale Rutherford anapita ku Hawaii komwe abale ankamanga nyumba yolambirira komanso ofesi ya nthambi yatsopano. M’bale Rutherford atafunsidwa za dzina limene angapereke ku nyumbayo anayankha kuti: “Bwanji titaitchula kuti ‘Nyumba ya Ufumu’? Chifukwatu ndi zimene tikuchita. Tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu.” (Mat. 24:14) Pasanapite nthawi dzina loyenerera limeneli linayamba kuperekedwa ku nyumba zambiri zimene zinkagwiritsidwa ntchito ndi mipingo ya anthu a Yehova padziko lonse.

6, 7. Kodi pulogalamu yomanga Nyumba za Ufumu mofulumira yathandiza bwanji?

6 Pofika m’zaka za m’ma 1970, panayamba kufunika Nyumba za Ufumu zambiri. Zimenezi zinachititsa kuti abale a ku United States akonze njira zomangira mwachangu nyumba zokongola komanso zogwirizana ndi ntchito yake. Pofika m’chaka cha 1983, nyumba pafupifupi 200 zinali zitamangidwa ku United States ndi ku Canada. Kuti ntchitoyi iziyenda bwino, abale anayamba kukhazikitsa makomiti oyang’anira ntchito ya zomangamanga. Njira imeneyi inathandiza kwambiri moti mu 1986, Bungwe Lolamulira linavomereza dongosolo limeneli ndipo pofika chaka cha 1987, ku United States kunali kutakhazikitsidwa Makomiti Omanga Achigawo okwana 60. a Pofika m’chaka cha 1992 makomiti ena anali atakhazikitsidwa ku Argentina, ku Australia, ku France, ku Germany, ku Japan, ku Mexico, ku South Africa ndi ku Spain. Kunena zoona, timafunika kuthandiza abale amene akugwira ntchito mwakhama m’makomiti omanga Nyumba za Ufumu komanso Malo a Misonkhano chifukwa ntchito imene akugwirayo ndi utumiki wopatulika.

7 Nyumba za Ufumu zomangidwa mwachangu zimenezi zimachitira umboni kwa anthu a m’deralo. Mwachitsanzo, nyuzipepala ina ya ku Spain inali ndi nkhani ya mutu wakuti “Chikhulupiriro Chimasuntha Mapiri.” Poikira ndemanga mmene Nyumba ya Ufumu ya m’tauni ya Martos inamangidwira, nyuzipepalayo inanena kuti: “Kodi zingatheke bwanji kuti padzikoli, lomwe anthu ake ambiri ndi odzikonda, anthu ongodzipereka ochokera m’madera osiyanasiyana [a m’dziko la Spain] apite ku tauni ya Martos n’kukamanga nyumba yomwe yaposa nyumba zonse pa nkhani ya kumalizidwa pa nthawi yochepa kwambiri, kumangidwa bwino komanso mwadongosolo?” Nkhaniyi inayankha funso limeneli pogwira mawu a wa Mboni wina yemwe anadzipereka kugwira nawo ntchitoyi. Iye anati: “Zonsezi zatheka chifukwa chakuti timaphunzitsidwa ndi Yehova.”

Kumanga Malo Olambirira M’mayiko Osauka

8. Kodi Bungwe Lolamulira linavomereza chiyani m’chaka cha 1999, ndipo n’chifukwa chiyani?

8 Pamene timafika kumapeto kwa zaka za m’ma 1900, anthu ambiri a m’mayiko osauka anayamba kulowa m’gulu la Yehova. Abale a m’mipingo ina anayesetsa kumanga malo oti azisonkhanako. Koma m’mayiko ena, abale ndi alongo ankanyozedwa komanso kusalidwa chifukwa Nyumba zawo za Ufumu zinali zosaoneka bwino poyerekeza ndi malo amene anthu a m’zipembedzo zina ankapemphererapo. Koma kuyambira m’chaka cha 1999, Bungwe Lolamulira linavomereza pulogalamu yothandiza kuti ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka izichitika mofulumira. Kuti zimenezi zitheke anayamba kugwiritsa ntchito ndalama zochokera m’mayiko olemera kuti pakhale “kufanana” pa kumangidwa kwa Nyumba za Ufumu m’mayiko olemera ndi m’mayiko osauka. (Werengani 2 Akorinto 8:13-15.) Abale ndi alongo ochokera m’mayiko ena anadzipereka kuti agwire nawo ntchito yomangayi.

9. Kodi ndi ntchito iti imene inkaoneka ngati yosatheka, koma kodi anthu a Mulungu akwanitsa kuchita chiyani?

9 Poyamba, ntchitoyi inkaoneka kuti ndi yaikulu kwambiri. Lipoti la mu 2001 linasonyeza kuti pankafunika Nyumba za Ufumu zoposa 18,300 m’mayiko 88 osauka. Chifukwa chakuti mzimu wa Mulungu komanso Mfumu yathu Yesu Khristu akutithandiza, palibe ntchito yosatheka. (Mat. 19:26) Kuchokera mu 1999 kufika mu 2013, zomwe ndi zaka pafupifupi 15 zokha, anthu a Mulungu akwanitsa kumanga Nyumba za Ufumu zokwana 26,849. b Yehova akupitirizabe kudalitsa ntchito yolalikira ndipo pofika chaka cha 2013, panali pakufunikirabe Nyumba za Ufumu zina pafupifupi 6,500 m’mayiko osauka ndipo panopa, chaka chilichonse pamafunika Nyumba za Ufumu zina zambirimbiri.

Kumanga Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka kumakhala ndi mavuto ake

10-12. Kodi ntchito yomanga Nyumba za Ufumu yalemekeza bwanji dzina la Yehova?

10 Kodi ntchito yomanga Nyumba za Ufumu zatsopano yalemekeza bwanji dzina la Yehova? Lipoti lochokera ku ofesi ya nthambi ya ku Zimbabwe linati: “Tikamanga Nyumba ya Ufumu yatsopano, nthawi zambiri mwezi ukamatha chiwerengero cha anthu obwera kumisonkhano chimawonjezeka kawiri.” Zikuoneka kuti m’mayiko ambiri anthu amayamba kufika pamisonkhano yathu tikakhala ndi malo abwino osonkhana. Nyumba ya Ufumu ikangomangidwa, anthu ambiri amayamba kusonkhana moti imadzaza ndipo timafunika kumanganso ina. Komabe sikuti anthuwo amangokopeka ndi kukongola kwa Nyumba za Ufumu kokha. Chikondi chimene anthu omanga nyumbazo amasonyezana n’chimene chimachititsa anthu kuti azichita chidwi ndi gulu la Yehova. Tiyeni tione zitsanzo za zimenezi.

11 Indonesia. Munthu wina yemwe ankaonerera anthu akumanga Nyumba ya Ufumu atazindikira kuti anthu onse omwe ankagwira ntchitoyo anangodzipereka ananena kuti: “Anthu inu ndi odabwitsa kwambiri. Ndaona kuti aliyense akugwira ntchito mwakhama komanso mosangalala ngakhale kuti simulandira malipiro. Ndikuganiza kuti palibe gulu lililonse lachipembedzo lomwe lingafanane ndi lanuli.”

12 Ukraine. Mzimayi wina yemwe tsiku lililonse ankadutsa pamalo amene ankamangapo Nyumba ya Ufumu anazindikira kuti anthu amene ankagwira ntchito pamalowa anali a Mboni za Yehova ndipo ankamanga Nyumba ya Ufumu. Iye ananena kuti: “Ndinali nditamva za Mboni za Yehova kuchokera kwa mng’ono wanga yemwe ndi wa Mboni. Nditaona mmene anthu ankagwirira ntchitoyi, ndinasankha kuti nanenso ndilowe m’banja lauzimu limeneli chifukwa ndinaona kuti anthu ake amakondana kwambiri.” Mzimayi ameneyu anavomera kuphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa m’chaka cha 2010.

13, 14. (a) Kodi inuyo mukuphunzirapo chiyani pa zimene banja lina linachita litaona mmene abale ankagwirira ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu? (b) Kodi inuyo mungathandize bwanji kuti Nyumba ya Ufumu yanu izilemekeza dzina la Yehova?

13 Argentina. Munthu wina ndi mkazi wake anapita kwa m’bale amene ankayang’anira ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu. Munthuyo anati: “Takhala tikuona zonse zomwe mukuchita pomanga nyumbayi ndipo . . . tikufuna kuphunzira za Mulungu m’nyumba imeneyi.” Kenako munthuyo anafunsa kuti: “Kodi tingachite chiyani kuti tizidzasonkhana nawo m’nyumba imeneyi?” Banjali linavomera kuti liyamba kuphunzira Baibulo kokha ngati abale angalole kuti aliyense wa m’banja lawo athandize nawo ntchito yomangayo. N’zosangalatsa kuti abale anawalola kuti agwire nawo ntchitoyo.

14 N’kutheka kuti simunagwire nawo ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu imene mukusonkhana panopa, koma mukhoza kuthandiza kuti Nyumba ya Ufumuyo izilemekeza dzina la Yehova. Mwachitsanzo, mukhoza kuitana anthu amene mumaphunzira nawo Baibulo, anthu amene mumachitako maulendo obwereza komanso anthu ena a m’dera lanu kuti adzasonkhane nanu ku Nyumba ya Ufumu. Mukhozanso kugwira nawo ntchito yoyeretsa komanso kukonza malo anu olambiriramo. Komanso ngati mutasunga ndalama inayake, mukhoza kuipereka kuti ithandize pokonza Nyumba ya Ufumu yanu kapena kuti ithandize pa ntchito yomanga nyumba zimenezi padziko lonse. (Werengani 1 Akorinto 16:2.) Kuchita zinthu zonsezi kumalemekezetsa dzina la Yehova.

Antchito Amene ‘Amadzipereka Mofunitsitsa’

15-17. (a) Kodi ntchito yambiri ya zomangamanga imagwiridwa ndi ndani? (b) Kodi mwaphunzirapo chiyani pa zimene mabanja ena omwe agwira nawo ntchito zomangamanga m’mayiko ena ananena?

15 Ntchito yaikulu imene imachitika pomanga Nyumba za Ufumu, Malo a Misonkhano komanso maofesi a nthambi imagwiridwa ndi abale ndi alongo a m’deralo. Koma nthawi zambiri amathandizidwa ndi abale ndi alongo ochokera m’mayiko ena omwe amadziwa bwino ntchito yomanga. Ena mwa anthu amenewa amasintha zinthu zina pa moyo wawo n’cholinga choti akathandize pa ntchito yomanga m’mayiko ena kwa milungu ingapo. Koma ena amadzipereka kuti agwire nawo ntchitoyi kwa zaka zambiri ndipo zimenezi zawachititsa kuti agwire nawo ntchitoyi m’malo osiyanasiyana.

Timo ndi Lina Lappalainen (Onani ndime 16)

16 Anthu amene amagwira ntchito yomanga m’mayiko ena amasangalala kugwira ntchitoyi ngakhale kuti amakumana ndi mavuto ena. Mwachitsanzo, Timo and Lina, omwe anakwatirana zaka 25 zapitazo athandiza nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Misonkhano komanso maofesi a nthambi m’mayiko a ku Asia, Europe ndi ku South America. Timo ananena kuti: “Pa zaka 30 zapitazi, ndakhala ndikusintha ntchito imene ndimagwira pafupifupi zaka ziwiri zilizonse.” Lina ananena kuti: “Ndakhala ndikutumikira ndi Timo m’mayiko 10. Pamafunika kuchita khama komanso zimatenga nthawi kuti uzolowere chakudya chatsopano, nyengo yatsopano, chinenero chatsopano, gawo lolalikira latsopano komanso kuti upeze anthu ocheza nawo.” c Kodi pali phindu lililonse lomwe anthu amenewa amapeza? Lina ananena kuti: “Pamene tikuyesetsa kuzolowera zinthu zatsopano m’pamenenso timaona kuti Mulungu akutidalitsa. Mwachitsanzo, taona Akhristu anzathu akutisonyeza chikondi, kutisamalira komanso taona kuti Yehova amatikonda kwambiri. Taonanso lonjezo la Yesu kwa ophunzira ake, lomwe lili pa Maliko 10:29, 30 likukwaniritsidwa. Tapeza abale, alongo komanso amayi athu ochuluka kwambiri m’gulu la Yehova.” Timo ananena kuti: “Timasangalala kwambiri kugwiritsa ntchito luso lathu pogwira nawo ntchito yolemekezeka kwambiri, yothandiza pomanga zinthu za Mfumu.”

17 Darren ndi Sarah, omwe akhala akuthandiza nawo pa ntchito ya zomangamanga ku Africa, Asia, Central America, Europe, South America ndi ku South Pacific, amaona kuti adalitsidwa ndi zinthu zambiri kuposa zimene apereka. Ngakhale kuti amakumana ndi mavuto osiyanasiyana, Darren ananena kuti: “Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kugwira ntchito ndi abale ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Ndimaona kuti chifukwa chakuti tonsefe timakonda Yehova timakhala ogwirizana kwambiri.” Sarah ananena kuti: “Ndaphunzira zinthu zambiri kwa abale ndi alongo azikhalidwe zosiyanasiyana. Chifukwa choona zinthu zimene akudzimana kuti atumikire Yehova ndimalimbikitsidwa kutumikira Yehova ndi mtima wanga wonse.”

18. Kodi ulosi womwe uli pa Salimo 110:1-3 ukukwaniritsidwa bwanji?

18 Mfumu Davide inalosera kuti ngakhale kuti nzika za Ufumu wa Mulungu zidzakumana ndi mavuto, ‘zidzadzipereka mofunitsitsa’ kuti zigwire ntchito ya Ufumu. (Werengani Salimo 110:1-3.) Aliyense amene akugwira nawo ntchito yokhudza Ufumu akukwaniritsa nawo ulosi umenewu. (1 Akor. 3:9) Tikaona kuchuluka kwa maofesi a nthambi, Malo a Misonkhano komanso Nyumba za Ufumu zimene zamangidwa padziko lonse, ndi umboni wakuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni ndipo panopa ukulamulira. Ndi mwayi waukulu kutumikira Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu, pogwira nawo ntchito yomwe ikuchititsa kuti Yehova alemekezeke kwambiri.

a Mu 2013, anthu ongodzipereka oposa 230,000 anavomerezedwa kuti azithandiza makomiti omanga a chigawo okwana 132 a ku United States. Chaka chilichonse makomiti a m’dzikoli ankayang’anira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu pafupifupi 75 komanso kuthandiza kukonzanso Nyumba za Ufumu pafupifupi 900.

b Chiwerengero chimenechi sichikuphatikizapo Nyumba za Ufumu zimene zinamangidwa m’mayiko omwe kulibe pulogalamu imeneyi.

c Ngakhale kuti anthu amene amatumikira m’mayiko ena nthawi yambiri amakhala akugwira ntchito yomanga, amagwira nawonso ntchito yolalikira pamodzi ndi mipingo ya m’deralo. Amagwira nawo ntchitoyi Loweruka ndi Lamlungu kapena madzulo, ngati ndi zotheka.