Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 22

Ufumu Udzakwaniritsa Zimene Mulungu Amafuna Padziko Lapansi

Ufumu Udzakwaniritsa Zimene Mulungu Amafuna Padziko Lapansi

CHOLINGA CHA MUTUWU

Ufumu udzakwaniritsa malonjezo onse a Mulungu okhudza anthu komanso dziko lapansi

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chingatichititse kuti tizikayikira za Paradaiso? (b) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu?

 TAYEREKEZERANI kuti mukuona m’bale wokhulupirika akufika pamisonkhano koma akuoneka kuti watopa kwambiri. Akuoneka choncho chifukwa chakuti abwana ake ovuta amamuchitira nkhanza, amakhala ndi nkhawa ya mmene angasamalire banja lake komanso chifukwa cha matenda amene mkazi wake akuvutika nawo. Pamene nyimbo yotsegulira misonkhano ikuyamba, akusangalala kuti wafika ku Nyumba ya Ufumu kudzasonkhana limodzi ndi abale ndi alongo ake. Nyimbo imene ikuyimbidwayo ikunena za moyo umene tikuyembekezera m’Paradaiso ndipo mawu a nyimboyo akumulimbikitsa kuti ayerekezere kuti iyeyo ali m’paradaisomo. Iye amaikonda kwambiri nyimboyi ndipo pamene akuimba ndi banja lake, chiyembekezo chimenechi chikumukhazika mtima m’malo.

2 Kodi inuyo zimenezi zinayamba zakuchitikirani? Ambirife zinatichitikirapo. Komabe ndi zoona kuti mavuto a m’dziko lakaleli angachititse kuti tizikayikira za moyo wopanda mavuto wa m’Paradaiso. Imene tikukhalayi ndi “nthawi yapadera komanso yovuta” ndipo m’dzikoli muli mavuto ambiri, mosiyana ndi mmene moyo wa m’Paradaiso amaufotokozera. (2 Tim. 3:1) Koma kodi n’chiyani chingatithandize kuona kuti zimene tikuyembekezerazi zidzachitikadi? Nanga tingadziwe bwanji kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uyamba kulamuliradi anthu onse? Tiyeni tikambirane maulosi angapo a Yehova omwe anthu ake akale anaona akukwaniritsidwa. Kenako tikambirana mmene maulosi omwewo komanso ena ofanana nawo akukwaniritsidwira mochititsa chidwi masiku ano. Pomaliza, chikhulupiriro chathu chitalimba ndi zimenezi, tikambirana mmene maulosi amenewa akukhudzira tsogolo lathu.

Mmene Yehova Anakwaniritsira Malonjezo Ake Kale Kwambiri

3. Kodi ndi lonjezo lotani limene linalimbikitsa Ayuda omwe anali ku ukapolo ku Babulo?

3 Taganizirani mmene moyo wa Ayuda omwe anali ku ukapolo ku Babulo m’zaka za m’ma 500 B.C.E. unalili. Ambiri anakulira ku ukapolo ndipo mwina makolo awonso anakulira komweko komwe moyo wake unali wovuta kwambiri. Ababulo ankawanyoza chifukwa choti ankakhulupirira Yehova. (Sal. 137:1-3) Pa zaka zonsezi, Ayuda okhulupirika ankayembekezerabe zinthu zosangalatsa zimene Yehova anawalonjeza. Anawalonjeza kuti adzawabwezera kudziko lawo. Yehova anawauza kuti moyo wawo udzakhala wabwino kwambiri akadzabwerera kwawo. Ndipotu anayerekezera dziko la Yuda la pa nthawi imeneyi ndi munda wa Edeni womwe unali paradaiso. (Werengani Yesaya 51:3.) Polonjeza zimenezi, anagwiritsa ntchito mawu olimbikitsa komanso omveka bwino omwe ankatsimikizira anthu a Mulunguwa kuti zimenezi zidzachitikadi. Kodi anawafotokoza bwanji? Tiyeni tikambirane ena mwa maulosi amenewa.

4. Kodi Yehova anawatsimikizira bwanji Ayuda kuti adzakhala otetezeka akadzabwerera kwawo?

4 Chitetezo. Dziko limene Ayudawo amayenera kubwererako silinali paradaiso weniweni, koma linali dziko limene linakhala bwinja kwa zaka 70 ndiponso loti ambiri mwa anthuwo sanalionepo. M’madera ambiri a nthawi imeneyo amene amatchulidwa m’Baibulo, munkapezeka mikango, mimbulu, akambuku komanso zilombo zina zoopsa. Choncho n’kutheka kuti munthu amene anali ndi banja ankadzifunsa kuti, ‘Ndikakwanitsa bwanji kutetezera mkazi ndi ana anga? Nanga bwanji ng’ombe zanga ndi nkhosa?’ Aliyense akhoza kukhala ndi nkhawa imeneyi. Ndiyeno ganizirani zimene Mulungu analonjeza zomwe zinalembedwa pa Yesaya 11:6-9 ndiponso mmene zinawalimbikitsira. (Werengani.) Pogwiritsa ntchito mawu osanjidwa mwaluso amenewa, Yehova anatsimikizira anthu omwe anali ku ukapolowo kuti iwowo komanso ziweto zawo akakhala otetezeka. Mawu akuti mkango uzidzadya udzu ankasonyeza kuti sudzadya ng’ombe za Ayudawo. Anthu okhulupirika sadzakhala mwamantha chifukwa cha zilombo zimenezi. Yehova analonjeza kuti anthu ake akadzabwerera kudziko lawo la Yuda, adzakhala otetezeka ngakhale akapita kuchipululu kapena kunkhalango.​—Ezek. 34:25.

5. Kodi ndi maulosi ati amene anathandiza Ayuda obwerera kwawo kukhulupirira kuti Yehova adzawapatsa zinthu zochuluka?

5 Adzakhala ndi zinthu zochuluka. Komabe n’kutheka kuti akanakhalanso ndi nkhawa zina. Akanamadzifunsa kuti, ‘Kodi ndikabwerera ndizikatha kupeza chakudya cha banja langa? Nanga tizikakhala potani? Kodi ndikapeza ntchito? Ndipo ngati nditaipeza, kodi ikakhala yabwino kusiyana ndi ntchito ya ukapoloyi?’ Yehova anayankhanso mwachikondi mafunso amenewa pogwiritsa ntchito maulosi. Yehova analonjeza kuti m’dzikolo muzikagwa mvula yokwanira, zomwe zikachititse kuti nthaka izikabereka “chakudya chopatsa thanzi.” (Yes. 30:23) Pa nkhani ya malo okhala komanso ntchito, Yehova anafotokoza lonjezo ili ponena za anthu ake: “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya.” (Yes. 65:21, 22) Apatu zikuoneka kuti moyo wawo udzasiyana kwambiri ndi mmene unalili ali ku Babulo komwe anthu ake sankalambira Yehova. Nanga bwanji za mavuto akuluakulu omwe anthuwo anali nawo, omwe anachititsa kuti agwidwe kupita ku ukapolo?

6. Kodi anthu a Mulungu anali ndi matenda otani kwa nthawi yaitali, nanga Yehova anatsimikizira chiyani anthu omwe ankabwerera kwawowo?

6 Moyo wawo wauzimu. Anthu a Mulungu amenewa asanatengedwe kupita ku ukapolo, anali ndi matenda auzimu. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anafotokoza za anthu ake kuti: “Mutu wanu uli ndi zilonda zokhazokha, ndipo mtima wanu wafooka.” (Yes. 1:5) Mwauzimu, anthuwa anali akhungu komanso osamva, chifukwa anapitiriza kutseka makutu awo kuti asamve malangizo a Yehova ndiponso ankatseka maso awo kuti asaone kufunika kwa zimene akuwauza. (Yes. 6:10; Yer. 5:21; Ezek. 12:2) Koma ngati vuto limeneli litakayambiranso atabwerera kudziko lawo, kodi akatetezedwa bwanji? Kodi sizikanachititsa kuti Yehova awakwiyirenso? Zimene Yehova analonjeza zinali zolimbikitsa kwambiri. Ananena kuti: “M’tsiku limenelo, ogontha adzamva mawu a m’buku. Ngakhale maso a anthu akhungu adzamasuka ku mdima wandiweyani ndipo adzayamba kuona.” (Yes. 29:18) Apatu zikusonyeza kuti Yehova adzachiritsa mwauzimu anthu ake olapawo. Ngati iwo atapitiriza kumvera, Yehova adzawapatsa malangizo opatsa moyo.

7. Kodi zimene Mulungu analonjeza Ayuda zinakwaniritsidwa bwanji, nanga kukwaniritsidwa kumeneku n’kolimbikitsa bwanji kwa ifeyo?

7 Kodi Yehova anakwaniritsa zimene analonjezazi? Zinthu zimene zinachitika zikuyankha funso limeneli. Ayuda amene anabwerera anadalitsidwa ndi chitetezo, zinthu zochuluka, komanso anali ndi moyo wabwino wauzimu. Mwachitsanzo, Yehova anawateteza kwa mitundu yoyandikana nayo yomwe inali yamphamvu kwambiri komanso anthu ake anali ochuluka kuposa iwowo. Zilombo sizinawononge ziweto zawo. Ndi zoona kuti kukwaniritsidwa kwa maulosi amene Yesaya, Yeremiya komanso Ezekieli analemba, komwe Ayudawa anaona, sikunachite kufika pa mmene moyo wa m’paradaiso udzakhalire. Komabe kukwaniritsidwa kumeneku kunali kolimbikitsa komanso kogwirizana ndi zimene anthu a Mulungu ankafunikira pa nthawi imeneyo. Kuganizira zimene Yehova anachita pa nthawi imeneyi, kungalimbitse chikhulupiriro chathu. Ngati Ayuda anasangalala kwambiri ndi kukwaniritsidwa koyamba kwa maulosi amenewa, komwe kunali kochepa chabe, kodi zidzakhala bwanji maulosiwa akadzakwaniritsidwa komaliza? Tiyeni tikambirane zimene Yehova watichitira masiku ano.

Yehova Wayamba Kale Kukwaniritsa Malonjezo Ake M’nthawi Yathu

8. Kodi anthu a Mulungu masiku ano akukhala mu “dziko” lotani?

8 Anthu a Yehova a masiku ano si a mtundu umodzi ndiponso sakhala dziko limodzi. M’malomwake, Akhristu odzozedwa amapanga mtundu wauzimu, womwe ndi “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16) Anzawo a “nkhosa zina” amakhala nawo limodzi mu “dziko” lauzimu, lomwe ndi gulu la Yehova. Anthu onse m’dziko limeneli amalambira Yehova Mulungu mogwirizana. (Yoh. 10:16; Yes. 66:8) Moyo ‘m’dziko’ limene Yehova watipatsali ndi wosangalatsa kwambiri ndipo tili m’paradaiso wauzimu. M’dziko limeneli taona kukwaniritsidwa kwauzimu kwa malonjezo a Mulungu akuti moyo wathu udzakhala ngati mmene zinthu zinalili m’munda wa Edeni. Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo.

9, 10. (a) Kodi ulosi wa pa Yesaya 11:6-9 ukukwaniritsidwa bwanji masiku ano? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti anthu a Mulungu akukhala mwamtendere?

9 Chitetezo. Ulosi womwe uli pa Yesaya 11:6-9, umafotokoza za mgwirizano komanso mtendere wosangalatsa wapakati pa nyama zakutchire ndi anthu komanso ziweto. Kodi zimenezi zikukwaniritsidwa mwauzimu masiku ano? Inde. Mu vesi 9, timapeza zimene zikuchititsa kuti nyama zimenezi zisawononge zinthu komanso kuvulaza anthu. Vesili limati: “Chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.” Koma kodi ‘kudziwa Yehova’ kumasintha khalidwe la nyama? Ayi, ndi anthu okha omwe amasintha akadziwa za Mulungu Wam’mwambamwamba ndiponso akayamba kutsanzira makhalidwe ake olimbikitsa mtendere. N’chifukwa chake n’zolimbikitsa kuona zimenezi zikukwaniritsidwa m’paradaiso wauzimu amene tikukhala masiku ano. Otsatira a Khristu amene ali mu ulamuliro wa Ufumu akuphunzitsidwa kuti asiye makhalidwe akale aukali komanso ongokhala ngati zinyama, n’kuyamba kukhala mwamtendere komanso mogwirizana ndi abale ndi alongo awo auzimu.

10 Mwachitsanzo, m’bukuli takambirana zakuti Akhristu salowerera ndale. Taona mfundo za m’Malemba zimene zimatichititsa kusalowerera ndale komanso takambirana za mmene anthu a Mulungu azunzidwira chifukwa chotsatira mfundo imeneyi. Kodi si zochititsa chidwi kuti m’dziko lachiwawali, muli “mtundu” wa anthu womwe umakaniratu kuchita nawo zachiwawa zilizonse, ngakhale atawopsezedwa kuti aphedwa? Uwutu ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti anthu omwe akutsogoleredwa ndi Mfumu yomwenso ndi Mesiya, akusangalaladi ndi mtendere ngati umene Yesaya anafotokoza. Yesu ananena kuti otsatira ake azidzadziwika chifukwa cha chikondi. (Yoh. 13:34, 35) Khristu akugwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti aphunzitse Akhristu onse okhulupirika kuti azikhala mwamtendere, azikondana komanso azikhala okoma mtima.​—Mat. 24:45-47.

11, 12. Kodi ndi njala yotani imene anthu ambiri akuvutika nayo masiku ano, koma Yehova akupereka bwanji chakudya chochuluka kwa anthu ake?

11 Zinthu zochuluka. Anthu m’dzikoli akuvutika ndi njala yauzimu. Baibulo linachenjeza kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘taonani, masiku akubwera pamene ndidzatumiza njala m’dziko. Njala imeneyo siidzakhala ya chakudya kapenanso ludzu lofuna madzi ayi, koma idzakhala njala ndiponso ludzu lofuna kumva mawu a Yehova.’” (Amosi 8:11) Kodi nzika za Ufumu wa Mulungu zikuvutikanso ndi njala imeneyi? Yehova analonjeza kuti padzakhala kusiyana pakati pa anthu ake ndi adani ake. Iye anati: “Atumiki anga adzadya, koma inuyo mudzakhala ndi njala. Atumiki anga adzamwa, koma inuyo mudzakhala ndi ludzu. Atumiki anga adzasangalala, koma inuyo mudzachita manyazi.” (Yes. 65:13) Kodi inuyo mwaona mawu amenewa akukwaniritsidwa?

12 Zinthu zauzimu zimene timalandira zimangotsatizana. Zikungokhala ngati mtsinje umene ukungokulirakulirabe. Timalandira mabuku ofotokoza Baibulo, mavidiyo komanso zinthu zina zongomvetsera. Timakhalanso ndi misonkhano ya mpingo komanso ikuluikulu, limodzi ndi zinthu zina zosiyanasiyana zimene zimapezeka pa webusaiti yathu. Zinthu zonsezi zili ngati madzi ambiri omwe ndi malangizo auzimu amene tikulandira m’dziko lomwe lili pa njalali. (Ezek. 47:1-12; Yow. 3:18) Kodi inuyo simusangalala kuona kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova otipatsa zinthu zochuluka zofunikira pa moyo wathu? Kodi mumaonetsetsa kuti nthawi zonse mukudya patebulo la Yehova?

Mipingo imene timasonkhana imatithandiza kuti tizilandira chakudya chokwanira chauzimu, tizikhala otetezeka komanso athanzi labwino mwauzimu

13. Kodi inuyo mumaona kuti lonjezo la Yehova lakuti anthu akhungu adzayamba kuona komanso osamva adzayamba kumva likukwaniritsidwa panopa? Fotokozani.

13 Moyo wauzimu. Anthu ambiri masiku ano ali ndi vuto losaona komanso kusamva mwauzimu. (2 Akor. 4:4) Koma Khristu akuchiritsa matenda onse padzikoli. Kodi inuyo munaonapo munthu wakhungu atayamba kuona komanso wosamva atayamba kumva? Ngati munaonapo anthu atayamba kudziwa choonadi cha m’Mawu a Mulungu molondola, n’kusiya kutsatira bodza limene zipembedzo zina zimaphunzitsa, lomwe linachititsa kuti akhale akhungu komanso osamva, ndiye kuti munaona lonjezo lotsatirali likukwaniritsidwa: “M’tsiku limenelo, ogontha adzamva mawu a m’buku. Ngakhale maso a anthu akhungu adzamasuka ku mdima wandiweyani ndipo adzayamba kuona.” (Yes. 29:18) Chaka chilichonse, anthu ambirimbiri padziko lonse akuchiritsidwa mwauzimu ngati mmene lembali likunenera. Munthu aliyense amene amachoka m’Babulo Wamkulu n’kuyamba kulambira nafe limodzi m’paradaiso wauzimu, amapereka umboni wakuti malonjezo a Yehova akukwaniritsidwa.

14. Kodi tiyenera kumaganizira za chiyani kuti chikhulupiriro chathu chikhale cholimba?

14 Mutu uliwonse wa m’bukuli uli ndi umboni wosatsutsika wosonyeza kuti Khristu wathandiza otsatira ake kuti akhale m’paradaiso wauzimu m’masiku otsirizawa. Tiyeni nthawi zonse tiziganizira mmene Yehova watidalitsira m’paradaiso ameneyu masiku ano. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri zimene Yehova walonjeza kuti zichitika kutsogoloku.

“Ufumu Wanu Ubwere”

15. Kodi n’chiyani chimatitsimikizira kuti dziko lapansili lidzakhala paradaiso?

15 Kuyambira kalekale, Yehova wakhala ali ndi cholinga chosintha dziko lonse lapansili kuti likhale paradaiso. Anaika Adamu ndi Hava m’munda wokongola n’kuwapatsa lamulo loti abereke ana mpaka kudzaza dziko lapansi ndiponso kuti asamalire nyama zonse. (Gen. 1:28) Komatu Adamu ndi Hava anatsatira maganizo a Satana ndipo anapandukira Mulungu, zomwe zinachititsa kuti ana awo onse abadwe ndi uchimo, azidwala komanso azifa. Komabe, cholinga cha Mulungu sichinasinthe. Nthawi zonse zimene Mulungu wanena zimakwaniritsidwa. (Werengani Yesaya 55:10, 11.) Choncho, sitingakayikire zoti zidzukulu za Adamu ndi Hava zidzadzaza dzikoli lomwe lidzakhale paradaiso ndipo zizidzasamalira mwachikondi zinthu zonse zimene Yehova analenga. Pa nthawi imeneyo, maulosi onse amene anaperekedwa koyamba kwa Ayuda omwe anali ku ukapolo, onena kuti moyo wawo udzakhala wabwino kwambiri, adzakwaniritsidwa komaliza. Taonani zitsanzo zotsatirazi.

16. Kodi Baibulo limafotokoza bwanji chitetezo chimene tidzakhale nacho m’Paradaiso?

16 Chitetezo. Pamapeto pake, mawu olimbikitsa amene ali pa Yesaya 11:6-9 adzakwaniritsidwa komaliza. Amuna, akazi ndi ana adzakhala otetezeka kulikonse kumene angapite padziko lapansili. Sikudzakhala chinthu china chilichonse choopsa, kaya munthu kapena nyama. Taganizirani mmene mudzasangalalire nthawi imeneyo pamene dziko lonseli muzidzaliona ngati kwanu. Mudzakhala ndi ufulu wosambira m’mitsinje ndi m’nyanja komanso kuyenda m’mapiri ndi m’nkhalango popanda kuopa chilichonse ngakhale utakhala usiku. Pa nthawiyi mawu a pa Ezekieli 34:25 adzakhala atakwaniritsidwa ndipo zidzakhala zotheka kwa anthu a Mulungu ‘kukhala m’chipululu popanda chowaopsa ndiponso kugona m’nkhalango.’

17. N’chiyani chimatitsimikizira kuti Yehova adzatipatsa zonse zofunikira Ufumu ukadzayamba kulamulira dziko lonse lapansi?

17 Zinthu zochuluka. Taganizirani nthawi imene sikudzakhala mavuto monga umphawi, kuperewera zakudya, njala, kapena mabungwe othandiza anthu pa mavuto. Chakudya chochuluka chauzimu chimene anthu a Mulungu akusangalala nacho masiku ano ndi umboni wakuti Mfumu yomwenso ndi Mesiya izidzapereka chakudya chokwanira kwa anthu ake. Yesu ali padziko lapansi anasonyeza kuti akhoza kukwaniritsa malonjezo amenewa chifukwa anadyetsa anthu anjala ambirimbiri mpakana kukhuta pogwiritsa ntchito mikate yochepa ndi nsomba. (Mat. 14:17, 18; 15:34-36; Maliko 8:19, 20) Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira dziko lonse lapansi, maulosi ngati ulosi wotsatirawu adzakwaniritsidwa: “Mulungu adzabweretsa mvula pambewu zanu zimene munabzala munthaka, ndipo zokolola za munthakayo zidzakhala chakudya chopatsa thanzi. M’tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetserapo ziweto.”​—Yes. 30:23.

18, 19. (a) Kodi ulosi wa pa Yesaya 65:20-22 umakukhudzani bwanji? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti masiku athu “adzakhala ngati masiku a mtengo”?

18 Masiku ano anthu ambiri amaona kuti n’zosatheka kukhala ndi nyumba yabwino yawoyawo kapena kupeza ntchito yabwino. M’dziko lopanda chilungamoli, anthu ambiri amaona kuti amagwira ntchito yakalavulagaga kwa nthawi yaitali koma salandira malipiro okwanira iwowo kapena banja lawo. Amene amadyerera ntchitoyo ndi anthu olemera komanso adyera. Koma taganizirani mmene moyo udzakhalire ulosi uwu ukadzakwaniritsidwa: “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. Pakuti masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo, ndipo anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.”​—Yes. 65:20-22.

19 Kodi akutanthauza chiyani pamene akuti masiku athu “adzakhala ngati masiku a mtengo”? N’kutheka kuti mukaima pansi pa mtengo waukulu kwambiri mumagoma poganizira zaka zambiri zimene wakhalapo ndipo mwina unamera agogo awo a agogo anu asanabadwe. Ndipo ngati moyo wopanda ungwirowu ungapitirirebe, ndiye kuti inuyo mudzamwalira n’kuusiya ukupitirizabe kukula mwamtendere. Yehova ndi wachifundo kwambiri moti anatilonjeza kuti moyo wathu udzakhalanso wautali komanso wamtendere ngati mmene mtengo umakhalira. (Sal. 37:11, 29) Idzafika nthawi imene moyo wa mtengo uzidzaoneka waufupi ngati mmene timaonera udzu, chifukwa ifeyo tidzakhala ndi moyo wamuyaya.

20. Kodi zidzatheka bwanji kuti nzika zokhulupirika za Ufumu zikhale ndi moyo wathanzi?

20 Moyo wabwino. Masiku ano, matenda komanso imfa zimakhudza munthu aliyense. Tikhoza kunena kuti tonsefe tikudwala chifukwa tinatengera uchimo kwa makolo athu, womwe uli ngati matenda akupha. Mankhwala amene angatichiritse ndi dipo la Khristu lokha basi. (Aroma 3:23; 6:23) Pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu ndi anthu amene adzalamulire naye limodzi adzathandiza anthu kupindula ndi nsembe imeneyi. Adzachotsa pang’onopang’ono zinthu zonse zobwera chifukwa cha uchimo. Ulosi wa Yesaya udzakwaniritsidwa, womwe umati: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’ Anthu okhala mmenemo adzakhala amene machimo awo anakhululukidwa.” (Yes. 33:24) Taganizirani mmene moyo udzakhalire pa nthawi imeneyo, pamene sikudzakhala munthu wakhungu, wosamva, kapena wolumala. (Werengani Yesaya 35:5, 6.) Palibe matenda amene Yesu adzalephere kuwagonjetsa, moti nzika zonse zokhulupirika za Ufumu wake zidzakhala ndi moyo wathanzi.

21. Kodi n’chiyani chidzachitikire imfa, nanga zimenezi zimakulimbikitsani bwanji?

21 Nanga bwanji za imfa yomwe inabwera chifukwa cha uchimo? Imfa ndi ‘mdani wathu womalizira,’ yemwe timalephera kumugonjetsa. (1 Akor. 15:26) Koma kodi Yehova amaonanso kuti imfa ndi mdani wovuta kumugonjetsa? Taonani ulosi umene Yesaya ananena: “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.” (Yes. 25:8) Taganizirani mmene moyo udzakhalire pa nthawi imeneyo. Sikudzakhala maliro, manda kapena misozi yachisoni. M’malomwake kudzakhala misozi yachisangalalo pamene Yehova azidzakwaniritsa lonjezo lake loti adzaukitsa anthu amene anamwalira. (Werengani Yesaya 26:19.) Apatu chisoni chonse chobwera chifukwa cha imfa sichidzakhalaponso.

22. Kodi chidzachitike n’chiyani Ufumu wa Mesiya ukadzamaliza kuchita zimene Mulungu amafuna padziko lapansi?

22 Kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000, Ufumu udzamaliza kuchita zimene Mulungu amafuna pano padziko lapansi, ndipo Khristu adzabwezera ulamuliro kwa Atate ake. (1 Akor. 15:25-28) Anthu, omwe pa nthawiyi adzakhale ali angwiro, adzayesedwa komaliza pamene Satana adzatulutsidwe kuphompho kuja. Pamapeto pake, Khristu adzaphwanya njoka yoopsayo limodzi ndi atumiki ake onse. (Gen. 3:15; Chiv. 20:3, 7-10) Koma onse amene amakonda Yehova adzakhala ndi tsogolo labwino. Palibe mawu abwino ofotokozera mmene zinthu zidzakhalire nthawi imeneyo oposa amene Baibulo limafotokoza. Baibulo limalonjeza kuti anthu okhulupirika adzasangalala ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”​—Aroma 8:21.

Ufumu udzakwaniritsa malonjezo onse a Yehova okhudza anthu komanso dziko lapansi

23, 24. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zonse zimene Mulungu analonjeza zidzakwaniritsidwa? (b) Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

23 Kukhulupirira malonjezo amenewa si kuwerengera madzi a mphutsi. Zonse zimene Yehova analonjeza zidzakwaniritsidwa. N’chifukwa chiyani tikutero? Kumbukirani mawu a Yesu omwe tinakambirana m’mutu woyamba wa bukuli. Iye anauza ophunzira ake kuti azipemphera kwa Yehova kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mat. 6:9, 10) Ufumu wa Mulungu ndi weniweni, moti panopa ukulamulira kumwamba. Kwa zaka 100 tsopano, Ufumuwu wakhala ukukwaniritsa malonjezo a Yehova ndipo kukwaniritsidwa kumeneku kukuonekera bwino mumpingo wachikhristu. Zimenezi zikutichititsa kukhulupirira kuti malonjezo ena onse a Yehova adzakwaniritsidwa Ufumu wa Mulungu ukadzabwera kudzalamulira dziko lonse lapansi.

24 Tikudziwa kuti Ufumu wa Mulungu udzabweradi. Tikudziwanso kuti mawu onse a Yehova adzakwaniritsidwa. Tikutero chifukwa UFUMU WA MULUNGU UKULAMULIRA PANOPA. Koma funso limene aliyense akuyenera kudzifunsa ndi lakuti, ‘Kodi Ufumuwu ukundilamulira ineyo?’ Tiyeni tiyesetse panopa kuchita zinthu monga nzika zokhulupirika za Ufumu wa Mulungu, n’cholinga choti tidzasangalale ndi Ufumu wolungamawu kwamuyaya.