Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Okondedwa Ofalitsa Ufumu Anzathu:

TAYEREKEZERANI kuti ndinu wa m’banja la Beteli ku Brooklyn ndipo munalipo Lachisanu pa October 2, 1914. Mwakhala pamalo panu m’chipinda chodyera ndipo mukudikirira kuti M’bale C. T. Russell afike. Kenako mukuona M’bale Russell akulowa. Monga mwachizolowezi chake, akuima pang’ono n’kupereka moni ku banja lonse la Beteli mosangalala kuti “Mwadzuka bwanji nonse?” Koma m’malo mopita kukakhala pampando wake, akuwomba m’manja n’kulengeza mosangalala kuti: “Nthawi za anthu akunja zatha. Nthawi yoti mafumu awo alamulire yatha.” Mukusangalala kwambiri chifukwa ndi zimene mwakhala mukuyembekezera kwa nthawi yaitali. Inuyo pamodzi ndi anthu ena onse a m’banja la Beteli mukusangalala kwambiri ndipo mukuwomba m’manja kwa nthawi yaitali.

Panopa papita zaka zambiri kuchokera pamene M’bale Russell anapereka chilengezo chosangalatsachi. Kodi Ufumu wakwanitsa kuchita chiyani kuchokera nthawi imeneyo? Ufumuwu wachita zinthu zambiri. Pogwiritsa ntchito Ufumuwu, Yehova wakhala akuyenga komanso kuphunzitsa anthu ake pang’onopang’ono. Mu 1914 panali anthu a Mulungu masauzande ochepa chabe, koma panopa aposa 7.5 miliyoni. Kodi inuyo panokha mwathandizidwa bwanji ndi maphunziro amene mwalandira kudzera m’gulu lake?

Masiku ano abale athu ambiri amakonda kunena kuti, “Galeta la Yehova lakumwamba likuthamanga,” ndipo zimenezi ndi zoona. Kuphunzira bukuli kukuthandizani kudziwa kuti kuyambira mu 1914, galeta lakumwamba, lomwe ndi mbali yosaoneka ya gulu la Yehova, lakhala likuthamanga. Pofuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse, ofalitsa Ufumu akhala akugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana kuti akwanitse kuchita zimenezi. Njira zina zimene agwiritsa ntchito ndi manyuzipepala, zikwangwani, kuonetsa zithunzi, makadi olalikirira, galamafoni, wailesi komanso intaneti.

Chifukwa chakuti Yehova akudalitsa ntchito yathu, panopa tikufalitsa mabuku okongola ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’zinenero zoposa 670 ndipo mabukuwa sitigulitsa. Anthu ogwira ntchito mongodzipereka amagwira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Msonkhano komanso maofesi a nthambi. Amagwira ntchito imeneyi m’mayiko olemera ndi osauka omwe. Pakachitika masoka a chilengedwe, abale ndi alongo amapita mwamsanga kukathandiza anthu amene akhudzidwa ndi tsokalo, ndipo umenewu ndi umboni wakuti ‘anabadwira kuti athandize pakagwa mavuto.’​—Miy. 17:17.

Nthawi zina atsogoleri a zipembedzo ‘amayambitsa mavuto’ ponamizira kuti akutsatira “malamulo.” Komatu n’zolimbikitsa kudziwa kuti nthawi zambiri zolinga zawo zolakwikazi “zathandiza kupititsa patsogolo uthenga wabwino.”​—Sal. 94:20; Afil. 1:12.

Kunena zoona, timasangalala kutumikira nanu limodzi monga “antchito apakhomo.” Dziwani kuti timakukondani kwambiri nonsenu. Tikukhulupirira kuti mfundo zimene zili m’bukuli zikuthandizani kuyamikira kwambiri cholowa chathu chauzimu.​—Mat. 24:45.

Tikukufunirani zabwino zonse,

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova