Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumanzere: Mlongo akugwiritsa ntchito nkhani ya M’bale Rutherford polalikira ku Alabama, America cha kumapeto kwa zaka za m’ma 1930; Kumanja: Switzerland

GAWO 1

Zoona Zenizeni Zokhudza Ufumu​—Kugawa Chakudya Chauzimu

Zoona Zenizeni Zokhudza Ufumu​—Kugawa Chakudya Chauzimu

TAYEREKEZERANI kuti mukuona munthu amene mumaphunzira naye Baibulo akuoneka kuti akudabwa kwambiri chifukwa chomvetsa tanthauzo la lemba lomwe mwangowerenga kumene. Ndiyeno akufunsa kuti: “Mukutanthauza kuti Baibulo limaphunzitsa kuti n’zotheka kudzakhala ndi moyo m’Paradaiso pa dziko lapansi pompano mpaka kalekale?” Munthu amene mukulalikira naye limodzi akumwetulira n’kumuuza kuti: “N’zimenetu Baibulo limanena.” Kenako wophunzira Baibuloyo akupukusa mutu wake n’kunena kuti: “N’zodabwitsa kuti nthawi yonseyi ndinali ndisanaphunzireko zinthu ngati zimenezi.” Ndiyeno mukukumbukira kuti ananenanso mawu ngati omwewa milungu ingapo yapitayo atangophunzira kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.

Kodi zimenezi zinakuchitikiranipo? Atumiki a Yehova ambiri akumanako ndi zinthu ngati zimenezi. Zinthu zina zimene zimatichitikira zimatikumbutsa mphatso yapadera imene tinapatsidwa, yomwe ndi kudziwa choonadi. Koma taganizirani izi: Kodi zinatheka bwanji kuti muphunzire choonadi? M’chigawo chino tikambirana funso limeneli. Yehova wakhala akuphunzitsa anthu ake mfundo za uzimu pang’onopang’ono ndipo umenewu ndi umboni wakuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni. Kwa zaka 100, Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu umenewu, wakhala akugwira ntchito mwakhama n’cholinga choti anthu a Mulungu aphunzitsidwe choonadi.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 3

Yehova Anathandiza Anthu Kudziwa Cholinga Chake

Kodi mmene Yehova ankalenga anthu anali ndi cholinga choti kudzakhale Ufumu wa Mesiya? Kodi Yesu anathandiza bwanji anthu kudziwa za Ufumuwo?

MUTU 4

Yehova Analemekeza Dzina Lake

Kodi Ufumu wa Mulungu wakwanitsa kuchita zotani zokhudza dzina la Mulungu? Kodi inuyo mumachita zotani poyeretsa nawo dzina lakuti Yehova?

MUTU 5

Mfumu Inathandiza Anthu Kudziwa Bwino za Ufumu

Dziwani zinthu zokhudza Ufumu wa Mulungu, olamulira ake ndiponso anthu amene adzalamuliridwe komanso kufunika kokhala wokhulupirika.