Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kulamanzele: Mlongo amene ndi kopotala akulalikila ku Korea mu 1931; kulamanja: Alongo akulalikila m’cinenelo ca manja ku Korea

CIGAWO 2

Kulalikila za Ufumu—Kufalitsa Uthenga Wabwino Padziko Lonse

Kulalikila za Ufumu—Kufalitsa Uthenga Wabwino Padziko Lonse

YELEKEZELANI kuti mukukonzekela kupita muulaliki m’mamawa patsiku limene simukupita kunchito. Koma mukukaikila zopita muulaliki cifukwa cakuti mukumva kutopa, ndipo mukuona kuti ndi bwino mutapuma. Komabe pambuyo popemphelela nkhaniyo mukusankha kupita muulaliki. Pamene mukulalikila ndi mlongo wacikulile wokhulupilika, mukulimbikitsidwa poona kupilila ndi kukoma mtima kwake. Ndipo pamene mukulalikila uthenga wa coonadi kunyumba ndi nyumba, mukukumbukila kuti abale ndi alongo anu padziko lonse naonso akulengeza uthenga wofananawo mwa kugwilitsila nchito zofalitsa zofanana ndi zimene inu mukugwilitsila nchito ndiponso maphunzilo amodzimodzi amene munaphunzitsidwa. Pamene mukufika kunyumba, mukudzimva kuti mwalimbikitsidwa, ndipo ndinu wosangalala kuti simunangokhala panyumba.

Nchito yaikulu imene Ufumu wa Mulungu ukucilikiza masiku ano ndi yolalikila. Yesu ananenelatu kuti nchito yolalikila idzafalikila padziko lonse m’masiku otsiliza. (Mat. 24:14) Kodi ulosi wa Yesu umenewu wakwanilitsidwa bwanji? M’cigawo cino, tikambilana za anthu amene amagwila nchitoyi, njila zimene amagwilitsila nchito, ndi zida zimene zathandiza kwambili kuti nchito yolalikila ipite patsogolo. Nchito imeneyi ikuthandiza anthu mamiliyoni ambili padziko lonse lapansi kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni.

M'CIGAWO CINO

NKHANI 6

Anthu Amene Amalalikila—Atumiki Akudzipeleka Mofunitsitsa

N’cifukwa ciani Yesu anali ndi cidalilo cakuti adzakhala ndi atumiki odzipeleka m’masiku otsiliza? Nanga mungaonetse bwanji kuti mumaika Ufumuwo patsogolo pa moyo wanu?

NKHANI 7

Njila Zolalikilila—Kugwilitsila Nchito Njila Zosiyanasiyana Polalikila Anthu

Onani njila zamakono zimene anthu a Mulungu akhala akugwilitsila nchito kuti alengeze uthenga wabwino kwa anthu ambili mmene angathele mapeto asanafike.

NKHANI 8

Zida Zogwilitsila Nchito Polalikila—Kusindikiza Mabuku Ogaŵila Padziko Lonse Lapansi

Kodi nchito yathu yomasulila imapeleka bwanji umboni wakuti Yesu akucilikiza nchitoyi? Mukaganizila zofalitsa zathu, n’ciani cimakupangitsani kukhulupilila kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni?

NKHANI 9

Zotsatilapo za Nchito Yolalikila—“M’Mindamo, Mwayela Kale ndipo m’Mofunika Kukolola”

Yesu anaphunzitsa otsatila ake mfundo ziŵili zofunika kwambili zokhudza nchito yokolola mwa kuuzimu. Kodi mfundozo zikutikhudza motani masiku ano?