Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumanzere: M’bale akumangidwa chifukwa cholalikira mumzinda wa Eindhoven, ku Netherlands, mu 1945; Kumanja: Kodi kumene mukukhala malamulo amakulolani kulalikira?

GAWO 4

Milandu Imene Ufumuwu Wawina​—Kukhazikitsa Mwalamulo Ntchito ya Uthenga Wabwino

Milandu Imene Ufumuwu Wawina​—Kukhazikitsa Mwalamulo Ntchito ya Uthenga Wabwino

TAYEREKEZERANI kuti pamene mukulalikira khomo ndi khomo mukuona apolisi awiri akukutsatirani. Ndiyeno akukuimitsani ndipo inu ndi mnzanu amene mukuyenda naye mu utumiki mukuima. Apolisiwo akufika pafupi n’kukufunsani kuti: “Kodi ndinu a Mboni za Yehova? Tamva kuti mukusokoneza anthu kwambiri.” Mukuyankha mwaulemu n’kufotokoza kuti mukuuza anthu uthenga wa m’Baibulo. Kodi chichitike n’chiyani?

Zimene zichitike zidalira kwambiri zimene zakhala zikuchitika m’mbuyomu. Kodi boma la dziko lanu limaona bwanji Mboni za Yehova? Kodi m’dziko lanu muli ufulu wachipembedzo? Ngati zili choncho, n’kutheka kuti abale ndi alongo anu auzimu akhala akuyesetsa kwa zaka zambiri “kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.” (Afil. 1:7) Kaya mukukhala kuti, koma kuganizira milandu imene Mboni za Yehova zawina kungalimbitse chikhulupiriro chanu. M’chigawochi tikambirana ina mwa milandu imeneyi. Milandu imene tawina ndi umboni wakuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni chifukwa sitikanawina milandu yonseyi patokha.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 13

Olalikira Ufumu Anayamba Kupititsa Milandu Yawo Kukhoti

Masiku ano oweruza a makhoti ena amachita zinthu ngati mmene anachitira mphunzitsi wakale wa Chilamulo, dzina lake Gamaliyeli.

MUTU 14

Timakhala Okhulupirika ku Boma la Mulungu Lokha Basi

Mavuto, omwe anali ngati “mtsinje,” amene a Mboni za Yehova anakumana nawo chifukwa chosalowerera ndale, anathetsedwa ndi anthu omwe sankayembekezera kuti angawathandize.

MUTU 15

Kumenyera Ufulu Wolambira Mulungu Momasuka

Anthu a Mulungu amenyera ufulu woti azitsatira malamulo a Ufumu wa Mulungu.