Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumanzere: Msonkhano umene unachitikira pabwalo ku London, ku England, mu 1945; Kumanja: Msonkhano wapadera ku Malawi, mu 2012

GAWO 5

Maphunziro Amene Ufumu Umapereka​—Kuphunzitsa Atumiki a Mfumu

Maphunziro Amene Ufumu Umapereka​—Kuphunzitsa Atumiki a Mfumu

TAYEREKEZERANI kuti mukumvetsera nkhani imene m’bale wachinyamata akukamba ndipo mukugwedezera mutu pamene akufotokoza mfundo. M’baleyo ndi wa mumpingo mwanu ndipo akukamba nkhani yake yoyamba pamsonkhano. Pamene mukumvetsera nkhaniyo, mukuchita chidwi ndi maphunziro amene anthu a Mulungu amalandira. Mukukumbukira mmene m’baleyu anavutikira pokamba nkhani yake yoyamba kumpingo ndipo mukudabwa mukaona mmene amakambira nkhani panopa. Anasintha kwambiri atalowa Sukulu ya Utumiki Waupainiya. Chaposachedwapa, m’baleyu ndi mkazi wake analowa nawo Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Pamene mukuwomba m’manja kumapeto kwa nkhani yokomayo mukuyang’ana abale ndi alongo ena ndipo mukuganizira za maphunziro amene anthu onse a Mulungu amalandira.

Baibulo linaneneratu za nthawi imene anthu onse a Mulungu ‘adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’ (Yes. 54:13) Nthawi imene ankanenayo ndi inoyo. Timaphunzitsidwa kudzera m’mabuku, misonkhano ya mpingo, misonkhano ikuluikulu komanso kudzera m’masukulu osiyanasiyana omwe anakhazikitsidwa n’cholinga chotithandiza kuchita mautumiki osiyanasiyana m’gulu la Yehova. M’chigawochi tikambirana mmene maphunziro amenewa amasonyezera kuti panopa Ufumu wa Mulungu ukulamulira.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 16

Kusonkhana Kuti Tilambire Mulungu

Kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri ndi misonkhano imene timalambirako Yehova?

MUTU 17

Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu

Kodi masukulu a gulu athandiza bwanji atumiki a Ufumu kuti azisamalira bwino maudindo awo?