Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kumanzele: Msonkhano wa pamtetete ku London mu 1945; kulamanja: Msonkhano wa pamtetete ku Malawi

CIGAWO 5

Maphunzilo a Ufumu—Kuphunzitsa atumiki a Mfumu

Maphunzilo a Ufumu—Kuphunzitsa atumiki a Mfumu

TAYELEKEZELANI kuti m’bale wina akukamba nkhani pa pulatifomu. Pamene mukumuyang’ana mukumwetulila. M’baleyu ndi wacinyamata ndipo ndi wa mumpingo wanu. Iye akukamba nkhani yake yoyamba pa msonkhano waukulu. Pamene mukumvetsela nkhaniyo, mukusoŵa conena mukaganizila maphunzilo amene anthu a Mulungu amalandila. Mukakumbukila mmene m’baleyu anavutikila nthawi yoyamba pamene anakamba nkhani papulatifamu, mukucita cidwi ndi mmene wapitila patsogolo. Iye wapita patsogolo kwambili pambuyo poloŵa Sukulu ya Apainiya. Posacedwapa, m’baleyu ndi mkazi wake analoŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Pamene m’baleyu akumaliza nkhani yake yolimbikitsa, mukuomba m’manja. Ndiyeno mukuyang’ana anthu amene muli nao pafupi ndi kuyamikila maphunzilo amene anthu onse a Mulungu amalandila.

Baibulo linanenelatu za nthawi pamene anthu onse a Mulungu ‘adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’ (Yes. 54:13) Tikukhala m’nthawi imeneyo. Timaphunzitsidwa kupyolela m’zofalitsa zathu ndi pamisonkhano ya mpingo, kuphatikizapo misonkhano ikuluikulu. Timaphunzitsidwanso kudzela m’masukulu osiyanasiyana amene colinga cake ndi kutithandiza kusamalila mautumiki osiyanasiyana m’gulu la Yehova. M’cigawo cino, tidzaona mmene maphunzilo onsewa amapelekela umboni wamphamvu wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila masiku ano.

M'CIGAWO CINO

NKHANI 16

Kusonkhana Pamodzi Kuti Tilambile Mulungu

Kodi tingacite ciani kuti tipindule mokwanila ndi misonkhano imene timakhala nayo kuti tilambile Yehova?

NKHANI 17

Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu

Kodi masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu athandiza bwanji atumiki a Ufumu kukwanilitsa utumiki wao?