Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumanzere: Thandizo lochokera ku Switzerland lopita kwa abale athu ku Germany, mu 1946; Kumanja: Kumanganso Nyumba ya Ufumu ku Japan pambuyo pa kusefukira kwa madzi, mu 2011

GAWO 6

Thandizo Limene Ufumu Umapereka​—Kumanga Malo Olambirira Komanso Kuthandiza pa Nthawi ya Mavuto

Thandizo Limene Ufumu Umapereka​—Kumanga Malo Olambirira Komanso Kuthandiza pa Nthawi ya Mavuto

TAYEREKEZERANI kuti mwalowa mu Nyumba ya Ufumu yanu koma n’kupeza kuti chilichonse chasinthiratu. Mwakhala mukunyadira chifukwa chokhala ndi nyumba imeneyi ndipo mwina mumakumbukira zinthu zina zosangalatsa zimene zinkachitika pa nthawi imene munkagwira nawo ntchito yomanga nyumbayo. Koma panopa ndinu osangalala kwambiri chifukwa chakuti Nyumba ya Ufumuyo yasintha n’kukhala malo othandizirako anthu pa nthawi ya mavuto. Chifukwa cha mvula ya mphepo yomwe yachititsa kuti madzi asefukire m’dera lanulo, Komiti ya Nthambi yakonza zoti anthu amene akhudzidwa ndi vutoli alandire chakudya, zovala, madzi ndiponso zinthu zina. Katunduyo akusanjidwa mwadongosolo ndipo abale ndi alongo akubwera mu Nyumba ya Ufumuyo kudzalandira zinthu zofunikira kwinaku akutuluka misozi yachisangalalo.

Yesu ananena kuti anthu ake azidzadziwika chifukwa chokondana. (Yoh. 13:34, 35) M’chigawochi tikambirana mmene Mboni za Yehova zimasonyezerana chikondi chimenechi pa ntchito zomangamanga komanso kuthandizana pa nthawi ya mavuto. Kusonyezana chikondi kumeneku ndi umboni wakuti Ufumu wa Khristu ukulamulira.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 18

Mmene Timapezera Ndalama Zoyendetsera Ntchito za Ufumu

Kodi ndalama zimene amagwiritsa ntchito zimachokera kuti? Kodi ndalamazo zimagwira ntchito yanji?

MUTU 19

Ntchito Yomanga Yomwe Imalemekeza Yehova

Malo olambirira amalemekeza Mulungu, koma pali chinthu china chomwe Mulungu amachiona kuti n’chamtengo wapatali kwambiri.

MUTU 20

Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto

Kodi timadziwa bwanji ntchito yothandiza anthu ndi mbali ya utumiki wopatulika kwa Yehova?