Nyimbo 137
Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima
-
Polalikira Ufumu,
Kukweza dzina lanu.
Anthu ena amatsutsa,
Ndiponso kutinyoza.
Koma sitiwaopa
Timamvera inu nokha.
Choncho Yehova, tikupempha
Mutipatse mzimu wanu.
(KOLASI)
Polalikira uthenga,
Mutichotsere mantha.
Tikhale olimba mtima
Anthu amve uthenga.
Amagedo ikufika,
Tikhale olimba mtima,
Tithandizeni Yehova.
Tikupempha.
-
Pamene tichita mantha,
Mudziwa ndife fumbi.
Mudzatithandiza ndithu
Paja munalonjeza.
Imvani kuopseza,
Kwa anthu odana nafe.
Tithandizeni, tisaope.
Tikhale olimba mtima.
(KOLASI)
Polalikira uthenga,
Mutichotsere mantha.
Tikhale olimba mtima
Anthu amve uthenga.
Amagedo ikufika,
Tikhale olimba mtima,
Tithandizeni Yehova.
Tikupempha.
(Onaninso 1 Ates. 2:2; Aheb. 10:35.)