Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 2

Yesu Analemekezedwa Asanabadwe

Yesu Analemekezedwa Asanabadwe

LUKA 1:34-56

  • MARIYA ANAPITA KUKACHEZA KWA MBALE WAKE ELIZABETI

Mngelo Gabirieli anauza Mariya kuti adzabereka mwana wamwamuna yemwe adzamupatse dzina lakuti Yesu ndipo adzalamulira monga Mfumu mpaka kalekale. Zimenezi zinadabwitsa Mariya moti anafunsa kuti: “Zimenezi zidzatheka bwanji, pakuti sindinagonepo ndi mwamuna?”—Luka 1:34.

Gabirieli anayankha kuti: “Mzimu woyera udzafika pa iwe ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.”—Luka 1:35.

Pofuna kumuthandiza Mariya kuti akhulupirire zimene ankamuuzazo, Gabirieli ananenanso kuti: “M’bale wako Elizabeti, amene anthu amamunena kuti mkazi wosabereka, nayenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake, ndipo uno ndi mwezi wa 6. Izi zachitika chifukwa zimene Mulungu wanena, sizilephereka.”—Luka 1:36, 37.

Zimene Mariya anayankha zinasonyeza kuti anavomereza zimene Gabirieli ananena, chifukwa anayankha kuti: “Ndinetu kapolo wa Yehova! Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.”—Luka 1:38.

Gabirieli atangochoka, Mariya anayamba kukonza ulendo woti akacheze kwa Elizabeti, yemwe ankakhala ndi mwamuna wake Zekariya cha kumapiri a ku Yudeya pafupi ndi Yerusalemu. Kuchokera ku Nazareti kukafika kumene Elizabeti ankakhala unali ulendo wa masiku atatu kapena 4.

Kenako Mariya anafika kunyumba ya Zekariya. Pamene ankalowa n’kupereka moni kwa Elizabeti, mzimu woyera unafika pa Elizabeti ndipo ananena kuti: “Ndiwe wodalitsidwa mwa akazi onse. N’chodalitsidwanso chipatso cha mimba yako! Koma zatheka bwanji kuti dalitso limeneli lindigwere? Zatheka bwanji kuti mayi wa Mbuye wanga abwere kwa ine? Waona nanga! Pamenetu mawu a moni wako alowa m’makutu mwangamu, ndithu khanda ladumpha mosangalala kwambiri m’mimba mwangamu.”—Luka 1:42-44.

Mariya anayankha mosangalala kuti: “Moyo wanga ukulemekeza Yehova. Ndipo mzimu wanga sungaleke kusefukira ndi chimwemwe mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga. Chifukwa waona malo otsika a kapolo wake. Ndipo taonani! kuyambira tsopano mibadwo yonse idzanditcha wodala. Chifukwa Wamphamvuyo wandichitira zazikulu.” Ngakhale kuti anapatsidwa mwayi wobereka mwana wa Mulungu, Mariya anapereka ulemu wonse kwa Mulungu. Ananena kuti: “Dzina lake ndi loyera. Chifundo chake chakhala pa amene amamuopa ku mibadwomibadwo.”—Luka 1:46-50.

Mariya anapitiriza kulemekeza Mulungu ndipo ananena mawu omwe ndi ulosi kuti: “Wachita zamphamvu ndi dzanja lake, wabalalitsira kutali odzikweza m’zolinga za mitima yawo. Watsitsa anthu amphamvu zawo pamipando yachifumu, ndipo wakweza anthu wamba. Wakhutitsa anthu anjala ndi zinthu zabwino, amene anali ndi chuma wawapitikitsa chimanjamanja. Iye wathandiza mtumiki wake Isiraeli. Wachita zimenezi posonyeza kuti akukumbukira lonjezo lake lakuti adzasonyeza chifundo kwamuyaya, monga momwe anauzira makolo athu akale, Abulahamu ndi mbewu yake.”—Luka 1:51-55.

Mariya anakhala ndi Elizabeti kwa miyezi pafupifupi itatu ndipo ayenera kuti pa nthawi imeneyi ankamuthandiza ntchito zosiyanasiyana. Zimenezi zinali zothandiza kwambiri kwa Elizabeti chifukwa anali atangotsala pang’ono kubereka. Nthawi imene azimayi okhulupirikawa, omwe anatenga pakati mothandizidwa ndi Mulungu, anakhalira limodzi inali yosangalatsa komanso yapadera kwambiri.

Chochititsanso chidwi n’chakuti Yesu anayamba kulemekezedwa ngakhale asanabadwe. Mariya atangofika kunyumba kwa Elizabeti, Elizabeti anatchula mwana amene anali m’mimba mwa Mariyayo kuti “Mbuye wanga,” ndipo nthawi yomweyo mwana amene anali m’mimba mwa Elizabeti ‘anadumpha mosangalala kwambiri.’ Koma nkhani zakutsogoloku zikusonyeza kuti zimene zinachitika pa nthawi imeneyi ndi zosiyana kwambiri ndi zimene anthu ena anachitira Mariya komanso mwana amene anali atatsala pang’ono kubereka.