Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 4

Mariya Anakhala ndi Pakati Asanakwatiwe

Mariya Anakhala ndi Pakati Asanakwatiwe

MATEYU 1:18-25 LUKA 1:56

  • YOSEFE ANADZIWA ZOTI MARIYA NDI WOYEMBEKEZERA

  • MARIYA ANAKWATIWA NDI YOSEFE

Pa nthawi imene Mariya ankachoka kwa Elizabeti n’kuti atakwanitsa miyezi 4 ali woyembekezera. Pajatu atangokhala woyembekezera anapita kwa m’bale wake Elizabeti amene ankakhala m’dera la mapiri a ku Yudeya, kum’mwera kwa Nazareti. Koma Mariya atabwerera kwawo ku Nazareti sipanatenge nthawi yaitali kuti anthu adziwe zoti ndi woyembekezera. Tangoganizani mmene Mariya ankavutikira maganizo ndi nkhani imeneyi.

Chodetsa nkhawa chinanso chinali chakuti Mariya anali atalonjezana ndi Yosefe, yemwe anali kalipentala, kuti adzakwatirana. Mariya ankadziwanso kuti Chilamulo cha Mulungu, chimene chinaperekedwa kwa Aisiraeli, chinkanena kuti ngati mkazi walonjezedwa kukwatiwa koma wagona ndi mwamuna wina, ayenera kuphedwa mwa kuponyedwa miyala. (Deuteronomo 22:23, 24) Ngakhale kuti Mariya ankadziwa zoti sanagonane ndi mwamuna aliyense, ankaganizirabe mmene angamuuzire Yosefe za nkhaniyi komanso zimene zingachitike.

Mariya anali atachoka kwa miyezi itatu ndipo Yosefe ayenera kuti anali atamusowa kwambiri moti ankafunitsitsa kumuona. Atakumana, Mariya ayenera kuti anamuuza zimene zinamuchitikira ndipo n’kutheka kuti anayesetsa kumufotokozera kuti anali woyembekezera mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. N’zachidziwikire kuti zinali zovuta kwa Yosefe kuti amvetse ndi kukhulupirira zimenezi.

Yosefe ankadziwa kuti Mariya ndi mkazi wokongola komanso wakhalidwe labwino moti ankamukonda kwambiri. Komabe ngakhale anafotokoza zimenezi, n’kutheka kuti Yosefe anaganizabe kuti Mariya ayenera kuti anagona ndi mwamuna wina. Yosefe anaganiza kuti amusiye mwamseri chifukwa sankafuna kuti amuchititse manyazi kwa anthu komanso sankafuna kuti amuponye miyala kuti aphedwe. Nthawi imeneyo anthu amene alonjezana kuti adzakwatirana, ankaonedwa kuti akwatirana kale ndipo kuti chibwenzi chithe ankafunika kutsatira dongosolo lothetsera ukwati.

Kenako Yosefe anapita kukagona koma akuganizirabe za nkhaniyi. Mngelo wa Yehova anamuonekera m’maloto n’kumuuza kuti: “Usaope kutengera Mariya mkazi wako kunyumba, chifukwa chakuti pakati alinapopa pachitika mwa mphamvu ya mzimu woyera. Iye adzabereka mwana wamwamuna, ndipo dzina lake udzamutche Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”—Mateyu 1:20, 21.

Yosefe atadzuka anasangalala kwambiri chifukwa tsopano anali atadziwa zoona zake za nkhaniyi moti sanachedwe kuchita zimene mngeloyo anamuuza. Anatenga Mariya n’kupita naye kunyumba kwake. Zimene anachitazi zinali ngati mwambo wa ukwati ndipo zinathandiza anthu onse kudziwa kuti tsopano Yosefe ndi Mariya akwatirana. Komabe Yosefe sanagonane ndi Mariya pa nthawi yonse imene anali ndi pakati.

Patadutsa miyezi ingapo Yosefe ndi Mariya, yemwe pa nthawiyo anali wotopa, anafunika kukonzekera ulendo wochoka kwawo ku Nazareti. Kodi ankapita kuti poti nthawi imeneyi Mariya anali atatsala pang’ono kubereka?