Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 19

Yesu Analalikira Mayi wa ku Samariya

Yesu Analalikira Mayi wa ku Samariya

YOHANE 4:3-43

  • YESU ANALALIKIRA MAYI WA KU SAMARIYA KOMANSO ANTHU ENA

  • KUPEMBEDZA KUMENE MULUNGU AMAVOMEREZA

Atachoka ku Yudeya, Yesu ndi ophunzira ake anayamba ulendo wopita kumpoto ku Galileya ndipo anadutsa m’chigawo cha Samariya. Iwo anali atatopa ndi ulendowu ndipo cha m’ma 12 koloko masana anaima pa chitsime chomwe chinali pafupi ndi mzinda wa Sukari kuti apume. N’kutheka kuti Yakobo ndi amene anakumba chitsimechi zaka zambirimbiri m’mbuyomo kapena anachita kulipira anthu kuti achikumbe. Masiku ano, chitsimechi chili pafupi ndi mzinda wotchedwa Nablus.

Kenako, ophunzira a Yesu anapita mumzinda womwe unali pafupi kuti akagule chakudya koma Yesu anamusiya pachitsime pomwepo. Ophunzirawo atachoka, mayi wina wa ku Samariya anabwera kuti adzatunge madzi. Yesu anauza mayiyo kuti: “Mundipatseko madzi akumwa mayi.”—Yohane 4:7.

Pa nthawiyi, Ayuda ndi Asamariya sankagwirizana chifukwa cha chidani chomwe chinalipo pakati pa mitundu iwiriyi. Choncho mayiyo anadabwa kwambiri moti anafunsa Yesu kuti: “Popeza inu ndinu Myuda, bwanji mukupempha madzi akumwa kwa ine, mayi wachisamariya?” Yesu anamuyankha kuti: “Mukanadziwa mphatso yaulere ya Mulungu ndi amene akukuuzani kuti, ‘Mundipatseko madzi akumwa,’ mukanam’pempha iyeyo, ndipo akanakupatsani madzi amoyo.” Pamenepo mayiyo anafunsa kuti: “Bambo, mulibe n’chotungira chomwe, ndipo chitsimechinso n’chozama. Nanga madzi amoyowo mwawatenga kuti? Kodi inu ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi, chimenenso iyeyo, ana ake ndi ng’ombe zake anali kumwa?”—Yohane 4:9-12.

Yesu anamuyankha kuti: “Aliyense wakumwa madzi awa adzamvanso ludzu. Koma amene adzamwa madzi amene ine ndidzam’patse sadzamvanso ludzu m’pang’ono pomwe. Ndipo madzi amene ndidzam’patse, adzasanduka kasupe wa madzi otuluka mwa iye, opatsa moyo wosatha.” (Yohane 4:13, 14) N’zochititsa chidwi kuti ngakhale kuti Yesu anali atatopa, anali wokonzeka kuuzako mayi wa ku Samariyayo choonadi chomwe chikanamuthandiza kuti adzapeze moyo.

Kenako mayiyo ananena kuti: “Bambo, ndipatseni madzi amenewo, kuti ndisadzamvenso ludzu komanso kuti ndisamabwerenso kuno kudzatunga madzi.” Yesu anakhala ngati akusintha nkhaniyi ndipo anauza mayiyo kuti: “Pitani, kaitaneni mwamuna wanu abwere kuno.” Mayiyo anayankha kuti: “Ndilibe mwamuna.” Koma mayiyo anadabwa kwambiri atamva zimene Yesu ananena, kuti: “Mwanena zoona mmene mukuti, ‘Ndilibe mwamuna.’ Pakuti mwakwatiwapo ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye panopa si mwamuna wanu.”—Yohane 4:15-18.

Zimene Yesu ananenazi zinachititsa mayiyu kuzindikira mfundo inayake yofunika kwambiri ndipo ananena modabwa kuti: “Bambo, ndazindikira kuti ndinu mneneri.” Kenako zimene mayiyo ananena zinasonyeza kuti ankafuna kukambirana zinthu zauzimu ndi Yesu, chifukwa ananena kuti: “Makolo athu [Asamariya] anali kulambira m’phiri ili [phiri la Gerizimu lomwe linali chapafupi], koma anthu inu [Ayuda] mumanena kuti Yerusalemu ndiwo malo kumene anthu ayenera kulambirirako.”—Yohane 4:19, 20.

Komabe zimene Yesu anafotokoza zinasonyeza kuti chofunika kwambiri si malo amene anthu akulambirirawo koma zimene amachita polambirapo. Tikutero chifukwa Yesu ananena kuti: “Nthawi idzafika pamene anthu inu simudzalambira Atate m’phiri ili kapena ku Yerusalemu.” Anamuuzanso kuti: “Nthawi idzafika, ndipo ndi yomwe ino, pamene olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.”—Yohane 4:21, 23, 24.

Choncho zimene Mulungu amafuna kwa anthu amene amamulambira si malo amene anthuwo amamulambirira koma zimene amachita pomulambira. Zimenezi zinamufika pamtima mayiyu moti ananena kuti: “Ndikudziwa kuti Mesiya akubwera, wotchedwa Khristu. Ameneyo akadzafika, adzatifotokozera zonse poyera.”—Yohane 4:25.

Kenako Yesu anamuululira mfundo yofunika kwambiri yakuti: “Munthu ameneyo ndi ineyo amene ndikulankhula nanu.” (Yohane 4:26) Tangoganizani zimene zinachitikazi. Mayiyu anachoka kwawo ali ndi cholinga chokatunga madzi koma Yesu anamukomera mtima kwambiri pomuuza zinthu zimene anali asanafotokozerepo wina aliyense. Anamuululira kuti iyeyo ndi Mesiya.

ASAMARIYA AMBIRI ANAKHULUPIRIRA YESU

Kenako ophunzira a Yesu aja anabwera atagula chakudya kuchokera ku Sukari. Anapeza Yesu akadali pa chitsime pompaja koma akulankhula ndi mayi wa ku Samariya. Ophunzirawo atangofika, mayiyo anasiya mtsuko wake wa madzi n’kukalowa mumzinda wa Sukari.

Atangofika mumzindamo, mayi uja anafotokozera anthu zonse zimene Yesu anamuuza. Iye anauza anthuwo motsimikiza kuti: “Tiyeni kuno mukaone munthu amene wandiuza zonse zimene ndakhala ndikuchita.” Mwina pofuna kuwakopa chidwi, anawafunsa kuti: “Kodi ameneyu n’kukhala Khristu kapena?” (Yohane 4:29) Nkhani ya kubwera kwa Khristu inali yofunika kwambiri chifukwa anthu anayamba kufuna kudziwa zambiri zokhudza Khristu kuyambira m’nthawi ya Mose. (Deuteronomo 18:18) Choncho funsoli linachititsa kuti anthu a mumzinda wa Sukari apite kumene kunali Yesu kuti akamuone okha.

Pamene zonsezi zinkachitika n’kuti ophunzira aja akupempha Yesu kuti adye chakudya chimene anabweretsa chija. Koma iye anawayankha kuti: “Chakudya ndili nacho chimene inu simukuchidziwa.” Ophunzirawo anadabwa ndi zimene anawayankhazo moti anayamba kufunsana kuti: “Pali amene wamubweretsera chakudya ngati?” Kenako Yesu anawauza mokoma mtima mfundo yofunika kwambiri imene ophunzira ake onse ayenera kuitsatira. Iye anati: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.”—Yohane 4:32-34.

Ntchito imene Yesu ankanena sinali yokolola mbewu zenizeni yomwe kunali kutatsala miyezi 4 kuti iyambike. M’malomwake ankanena za ntchito yokolola mwauzimu. Tikutero chifukwa anapitiriza kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola. Moti pano wokolola akulandira kale malipiro ndipo akusonkhanitsa zipatso ku moyo wosatha, kuti wofesa mbewu ndi wokolola asangalalire pamodzi.”—Yohane 4:35, 36.

N’kutheka kuti Yesu ankadziwa zomwe zichitike pambuyo polalikira mayi wa ku Samariya uja. Anthu ambiri a ku Sukari anayamba kukhulupirira Yesu chifukwa cha zimene mayi wachisamariya anawauza zija. Iye anati: ‘Iye wandiuza zinthu zonse zimene ndakhala ndikuchita.’ (Yohane 4:39) Choncho anthu ochokera ku Sukariwo atafika kuchitsime kuja, anapempha Yesu kuti akhalebe nawo kwa masiku angapo n’cholinga choti awaphunzitse zinthu zambiri. Yesu anavomera ndipo anakhala ku Samariya kwa masiku awiri.

Asamariya ambiri atamvetsera uthenga wa Yesu anayamba kumukhulupirira, moti anauza mayi uja kuti: “Sikuti tikukhulupirira chifukwa cha mawu ako ajanso ayi, pakuti tadzimvera tokha ndipo tadziwa ndithu kuti munthu uyu ndi mpulumutsi wa dziko.” (Yohane 4:42) Kunena zoona, zimene mayi wa ku Samariyayu anachita ndi chitsanzo chabwino cha mmene tingathandizire anthu ena kudziwa za Khristu. Tiziyesetsa kulankhula mawu amene angachititse anthu kufuna kuphunzira zambiri.

N’kutheka kuti Yesu anakumana ndi mzimayi wa ku Samariyayu m’mwezi wa November kapena December. Tikutero chifukwa paja Yesu ananena kuti kunali kutatsala miyezi 4 kuti ntchito yokolola balere iyambe, yomwe m’derali inkayamba pakati pa mwezi wa March kapena April. Paja Yesu asanakumane ndi mkazi wa ku Samariyayu ankachokera ku mwambo wa Pasika wa mu 30 C.E., kenako anapita m’dera la Yudeya komwe anaphunzitsa ndi kubatiza anthu. Popeza mwambo wa Pasika unkachitika m’mwezi wa March kapena April, ndiye kuti mwambo wa Pasika utatha, Yesu ndi ophunzira ake anakhala miyezi 8 kapena kuposerapo akuphunzitsa komanso kubatiza anthu ku Yudeya. Atakhala masiku awiri ku Sukari, Yesu ndi ophunzira ake anapitiriza ulendo wawo ndipo analowera cha kumpoto ku Galileya komwe linali dera la kwawo. Kodi kumeneko anakumana ndi zotani?