Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 24

Yesu Analalikira M’madera Ambiri a ku Galileya

Yesu Analalikira M’madera Ambiri a ku Galileya

MATEYU 4:23-25 MALIKO 1:35-39 LUKA 4:42, 43

  • YESU ANALALIKIRA NDI OPHUNZIRA AKE 4 M’MADERA A KU GALILEYA

  • ANTHU AMBIRI ANAMVA ZIMENE YESU ANKACHITA NDIPONSO UTHENGA WAKE

Ali ku Kaperenao Yesu ndi ophunzira ake anatanganidwa kwambiri. Madzulo, anthu a mumzindawo anamubweretsera odwala kuti awachiritse. Chifukwa cha zimenezi Yesu anasowa nthawi yopuma komanso yochita zinthu zina payekha.

Ndiyeno tsiku lotsatira, m’mamawa kwambiri kukadali kamdima Yesu anadzuka n’kupita kumalo a yekha kuti akapemphere kwa Atate wake. Koma pasanapite nthawi yaitali, anthu anazindikira kuti Yesu sakuoneka ndipo “Simoni ndi ena amene anali naye” anayamba kumufunafuna. Zikuoneka kuti Petulo ndi amene ankatsogolera anthuwo chifukwa pa nthawiyi Yesu anali mlendo ku nyumba kwake.—Maliko 1:36; Luka 4:38.

Atamupeza, Petulo anati: “Anthu onse akukufunafunani.” (Maliko 1:37) Anthu a ku Kaperenao sankafuna kuti Yesu achoke. Anthuwa ankasangalala kwambiri ndi zimene Yesu ankachita moti “anayesa kumuletsa kuti asawasiye.” (Luka 4:42) Kodi cholinga chachikulu cha Yesu pobwera padziko lapansi chinali chodzachita zozizwitsa? Kodi anafunika kugwira ntchito yake m’dera lokhali basi? Kodi Yesu anayankha bwanji mafunso amenewa?

Yesu anayankha ophunzira ake kuti: “Tiyeni tipite kwina kumidzi yapafupi, kuti ndikalalikire kumenekonso, pakuti ndicho cholinga chimene ndinabwerera.” Ndipotu Yesu anauza anthu amene ankamukakamizawo kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.”—Maliko 1:38; Luka 4:43.

Choncho cholinga chachikulu chimene Yesu anabwerera padziko lapansi chinali kudzalalikira za Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu ndi umene udzayeretse dzina la Atate wake komanso kuthetseratu mavuto onse a anthu. Zimene Yesu anachita pochiritsa anthu mozizwitsa zinatsimikizira kuti anatumidwadi ndi Mulungu. Nayenso Mose anachita zinthu zambiri zodabwitsa kukadali zaka zambiri Yesu asanabwere padziko lapansi. Zimene anachitazi zinkatsimikizira kuti anatumidwa ndi Mulungu.—Ekisodo 4:1-9, 30, 31.

Kenako Yesu ndi ophunzira ake 4 anachoka ku Kaperenao n’kupita kukalalikira ku mizinda ina. Ophunzira amenewa anali Petulo ndi m’bale wake Andireya komanso Yohane ndi m’bale wake Yakobo. Pa nthawi imeneyi panali patangotha mlungu umodzi kuchokera pamene Yesu anawaitana kuti aziyenda naye.

Ntchito yolalikira imene Yesu ndi ophunzira ake anagwira ku Galileya inayenda bwino kwambiri. Moti anthu okhala m’madera akutali anamva za mbiri ya Yesu. “Mbiri yake inafalikira mu Siriya monse,” komanso m’dera la Dekapole lomwe linapangidwa ndi mizinda 10. Mbiriyi inafalikiranso mpaka kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano. (Mateyu 4:24, 25) Gulu la anthu ochokera m’madera amenewa komanso lochokera ku Yudeya linayamba kutsatira Yesu ndi ophunzira ake. Ambiri anabwera ndi anthu odwala kuti adzachiritsidwe. Posafuna kuwakhumudwitsa, Yesu anachiritsa odwalawo komanso kutulutsa mizimu yoipa mwa anthu ena.