Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 30

Kodi Pali Ubale Wotani Pakati pa Yesu ndi Mulungu?

Kodi Pali Ubale Wotani Pakati pa Yesu ndi Mulungu?

YOHANE 5:17-47

  • MULUNGU NDIYE ATATE AKE A YESU

  • YESU ANALONJEZA KUTI AKUFA ADZAUKA

Yesu atachiritsa munthu pa tsiku la Sabata, Ayuda ena anamuimba mlandu wophwanya Sabata. Poyankha Ayuda amenewa Yesu ananena kuti: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.”—Yohane 5:17.

Zimene Yesu anachita pa tsikuli zinali zosaletsedwa m’Chilamulo cha Mulungu. Yesu ankagwira ntchito yolalikira komanso kuchiritsa anthu potsanzira ntchito zabwino za Mulungu. Choncho Yesu ankachita zinthu zabwino tsiku lililonse, posatengera kuti tsikulo ndi la Sabata kapena ayi. Koma zimene Yesu anayankhazo zinawakwiyitsa kwambiri moti anayamba kufuna kumupha. N’chifukwa chiyani Ayudawo ankafuna kumupha?

Kuwonjezera pa zimene Yesu anachita pochiritsa munthu pa Sabata, Ayudawo anakwiyanso kwambiri atamva Yesu akunena kuti ndi Mwana wa Mulungu. Iwo ankaona ngati Yesu akunyoza Yehova Mulungu ponena kuti ndi Atate ake chifukwa kwa iwowo zinkakhala ngati akunena kuti iyeyo ndi wofanana ndi Mulungu. Komabe Yesu sanachite mantha chifukwa anapitiriza kuwafotokozera zambiri zokhudza ubale wake ndi Mulungu. Yesu ananena kuti: “Atatewo amakonda Mwana wake. Amamuonetsa zonse zimene iwo akuchita.”—Yohane 5:20.

Atate ndi amene amapereka moyo ndipo anasonyezapo zimenezi m’mbuyomo pamene anapereka mphamvu kwa anthu ena kuti aukitse amene anamwalira. Yesu ananenanso kuti: “Pakuti monga Atate amaukitsa akufa ndi kuwapatsa moyo, nayenso Mwana amapereka moyo kwa amene iye wafuna kuwapatsa.” (Yohane 5:21) Zimene Yesu ananenazi n’zolimbikitsa kwambiri tikaganizira zimene zidzachitike m’tsogolo. Ngakhale panopo, Mwanayu akupitirizabe kuukitsa anthu amene anali akufa mwauzimu. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Iye wakumva mawu anga ndi kukhulupirira amene anandituma ine ali nawo moyo wosatha, ndipo salowa m’chiweruzo koma wachoka ku imfa, waolokera ku moyo.”—Yohane 5:24.

Pa nthawiyi Yesu anali asanaukitsepo munthu aliyense, koma anauza anthu amene ankamuimba milanduwo kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa. Iye ananena kuti: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.

Ngakhale kuti Yesu ali ndi udindo waukulu umenewu, iye ananena momveka bwino kuti amamvera Mulungu. Iye anati: “Ine sindingachite chilichonse chongoganiza ndekha. . . . Sinditsatira chifuniro changa, koma chifuniro cha amene anandituma.” (Yohane 5:30) Koma Yesu anafotokoza za udindo wake pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu, umene pa nthawiyi anali asanauonetsepo pa gulu la anthu. Ndipotu ena mwa anthu amene ankaimba mlandu Yesuwa anali akudziwa kale zinthu zambiri zokhudza Yesu. N’chifukwa chake Yesu anawakumbutsa kuti: “Inu munatumiza anthu kwa Yohane [M’batizi], ndipo iye anachitira umboni choonadi.”—Yohane 5:33.

N’kutheka kuti anthu amene ankaimba milandu Yesu, anali atamvapo zimene zinachitika zaka ziwiri m’mbuyomo. Pa nthawiyo Yohane anauza atsogoleri achipembedzo Achiyuda za Munthu wina amene ankabwera m’mbuyo mwake yemwe ankadziwika ndi dzina lakuti “Mneneri” komanso “Khristu.” (Yohane 1:20-25) Yesu anapitiriza kuwakumbutsa za mmene ankaonera Yohane, yemwe pa nthawiyi anali m’ndende. Iye anati: “Kwa kanthawi kochepa inu munali ofunitsitsa kusangalala m’kuwala kwakeko.” (Yohane 5:35) Koma pa nthawiyi, Yesu anawapatsa umboni wamphamvu kuposa umene Yohane M’batizi anawapatsa.

Kenako Yesu anawauza kuti: “Ntchito zimene ine ndikuchita [kuphatikizapo ntchito yochiritsa imene anali atangoigwira], zikundichitira umboni kuti Atate ananditumadi.” Ananenanso kuti: ‘Atate amene anandituma anandichitira umboni.’ (Yohane 5:36, 37) Mwachitsanzo, Mulungu anachitira umboni za Yesu pa nthawi imene ankabatizidwa.—Mateyu 3:17.

Choncho anthuwa analibe zifukwa zokwanira zokanira Yesu chifukwa Malemba amene ankafufuza ankachitira kale umboni za Yesu. Ndiyeno Yesu anamaliza n’kuwauza kuti: “Ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso ine, pakuti iyeyo analemba za ine. Koma ngati simukhulupirira zolemba za ameneyo, mungakhulupirire bwanji mawu anga?”—Yohane 5:46, 47.