Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 42

Yesu Anadzudzula Afarisi

Yesu Anadzudzula Afarisi

MATEYU 12:33-50 MALIKO 3:31-35 LUKA 8:19-21

  • YESU ANATCHULA ZA “CHIZINDIKIRO CHA YONA”

  • ANKAKONDANA KWAMBIRI NDI OPHUNZIRA AKE KUPOSA ACHIBALE AKE

Alembi ndi Afarisi akanaimbidwa mlandu wochimwira mzimu woyera chifukwa choti ankatsutsa zoti Yesu ankatulutsa ziwanda pogwiritsa ntchito mphamvu yochokera kwa Mulungu. Kodi zimene ankachitazi zinkasonyeza kuti anali kumbali ya Mulungu kapena ya Satana? Yesu ananena kuti: “Anthu inu mumachititsa mtengo ndi zipatso zake kukhala zabwino, kapena mumavunditsa mtengo ndi zipatso zake, chifukwa mtengo umadziwika ndi zipatso zake.”—Mateyu 12:33.

Kunena zoona, n’kupanda nzeru kunena kuti Yesu ankachita ntchito zabwino monga kutulutsa ziwanda ndi mphamvu yochokera kwa Satana. Yesu ananena mosabisa mawu pa ulaliki wake wa paphiri kuti ngati mtengo wabereka zipatso zabwino, ndiye kuti mtengowo ndi wabwino osati wowola. Ndiyeno zimene Afarisi ankanena ponyoza Yesu, zomwe tingaziyerekezere ndi zipatso, zinasonyeza kuti anali owola. Yesu anawauza kuti: “Ana a njoka inu, mungalankhule bwanji zinthu zabwino, pamene muli oipa? Pakuti pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.”—Mateyu 7:16, 17; 12:34.

Zimene timalankhula zimasonyeza zimene zili mumtima mwathu ndipo zimene timalankhulazo zingachititse kuti tidzapulumuke kapena ayi. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Ndikukuuzani kuti pa Tsiku la Chiweruzo, anthu adzayankha mlandu pa mawu alionse opanda pake amene iwo amalankhula. Pakuti ndi mawu ako udzaweruzidwa kuti ndiwe wolungama, ndipo ndi mawu akonso udzaweruzidwa kuti ndiwe wolakwa.”—Mateyu 12:36, 37.

Ngakhale kuti Yesu anachita zinthu zambiri zamphamvu, alembi ndi Afarisi ankafuna kuti Yesu achitebe zinthu zambiri. Iwo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, tikufuna mutionetse chizindikiro.” Kaya anamuonapo akuchita zinthu zozizwitsa kapena ayi, koma panali umboni wooneka ndi maso wosonyeza kuti Yesu anachita zizindikiro zambiri. Choncho Yesu anauza atsogoleri achiyudawo kuti: “M’badwo woipa ndi wachigololo ukufunitsitsabe chizindikiro. Sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse koma chizindikiro cha mneneri Yona chokha.”—Mateyu 12:38, 39.

Yesu anawafotokozera zimene ankatanthauza ponena mawu amenewa. Iye anati: “Monga momwe Yona anakhalira m’mimba mwa chinsomba chachikulu masiku atatu, usana ndi usiku, chimodzimodzinso Mwana wa munthu adzakhala mumtima wa dziko lapansi masiku atatu, usana ndi usiku.” Yona anamezedwa ndi chinsomba chachikulu koma kenako chinamulavula, zomwe zinali ngati waukitsidwa. Choncho Yesu ananeneratu zimene zidzamuchitikire kuti adzafa ndipo adzaukitsidwa pa tsiku lachitatu. Ndiyeno Yesu ataphedwa n’kuukitsidwa, atsogoleri achiyuda anakana kulapa komanso kusintha, komwe kunali ngati kukana ‘chizindikiro cha Yona.’ (Mateyu 27:63-66; 28:12-15) “Anthu a ku Nineve” anali osiyana kwambiri ndi atsogoleri achiyudawo chifukwa analapa Yona atawalalikira. Choncho anthu a ku Nineve adzatsutsa anthu a m’badwo umenewu. Yesu ananenanso kuti nayonso mfumukazi ya ku Sheba idzatsutsa anthu a m’badwo umenewu chifukwa inafunitsitsa kumva nzeru za Solomo ndipo inagoma kwambiri ndi nzeru zakezo. Koma Yesu ananena kuti: “Wina woposa Solomo ali pano.”—Mateyu 12:40-42.

Yesu anayerekezera m’badwo woipawo ndi munthu amene mzimu woipa watuluka mumtima mwake. (Mateyu 12:45) Chifukwa chakuti munthuyo sanaike zinthu zabwino mumtima mwake, mzimu woipawo umabwereranso ndi mizimu ina 7 yoipa kwambiri kuposa woyambawo ndipo imakhazikika mumtima mwake. Zimenezi n’zofanana ndi zimene zinachitikira mtundu wa Isiraeli. Mtundu wa Isiraeli unayeretsedwa n’kusintha ngati munthu amene mzimu woipa watuluka mumtima mwake. Koma kenako mtunduwo unakana aneneri a Mulungu ndipo zinthu zinafika poipa kwambiri pamene unakana Yesu, yemwe zinkachita kuonekeratu kuti akutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu. Zimene Aisiraeliwa anachita zinasonyezeratu kuti anaipa kuposa mmene analili poyamba.

Pamene Yesu ankalankhula, mayi ake ndi azichimwene ake anafika n’kuima kumbuyo kwa gululo. Ndiyeno anthu ena amene anali pafupi ndi Yesu anamuuza kuti: “Mayi anu ndi abale anu aima panjapo akufuna kuonana nanu.” Zimene Yesu anayankha zinasonyeza kuti ankakonda kwambiri ophunzira ake ndipo ankawaona ngati azichimwene ake, azichemwali ake komanso ngati amayi ake. Analoza ophunzira akewo n’kunena kuti: “Mayi anga ndi abale anga ndi awa amene amamvetsera mawu a Mulungu ndi kuwachita.” (Luka 8:20, 21) Zimenezi zinasonyeza kuti ngakhale kuti ankagwirizana kwambiri ndi abale ake, koma ubale wake ndi ophunzira ake unali wofunika kwambiri. N’zolimbikitsa kwambiri kukhala ndi abale ndi alongo auzimu amene timakondana nawo kwambiri makamaka pamene anthu akutikayikira, kutinyoza kapena kunyoza ntchito zabwino zimene timachita.