Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 47

Kamtsikana Kanakhalanso ndi Moyo

Kamtsikana Kanakhalanso ndi Moyo

MATEYU 9:18, 23-26 MALIKO 5:22-24, 35-43 LUKA 8:40-42, 49-56

  • YESU ANAUKITSA MWANA WAMKAZI WA YAIRO

Yairo anaona Yesu atachiritsa mzimayi amene anali ndi matenda otaya magazi. Ataona zimenezi anakhulupirira kuti Yesu akhoza kuchiritsanso mwana wake ngakhale kuti pa nthawiyi ankadziwa kuti ‘mwana wake wamkazi wamwalira kale.’ (Mateyu 9:18) Kodi zikanatheka kuti mwanayo athandizidwe?

Pamene Yesu ankalankhula ndi mzimayi amene anamuchiritsa uja panafika amuna ena ochokera kunyumba kwa Yairo. Iwo anamuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalira!” Ndipo anamuuzanso kuti: “Musiyeni mphunzitsiyu musamuvutitse.”—Maliko 5:35.

Yairo atamva uthenga umenewu ayenera kuti anasokonezeka maganizo kwambiri. Ngakhale kuti ankalemekezedwa kwambiri m’derali koma anasowa mtengo wogwira atadziwa zoti mwana wake mmodzi yekha amene anali naye wamwalira. Yesu atamva zimene zinachitikazo anatembenukira kwa Yairo n’kumulimbikitsa kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi.”—Maliko 5:36.

Kenako Yesu anatsagana ndi Yairo ndipo atafika kunyumba kwake anapeza kuti kuli anthu ambiri. Anthuwo ankalira kwambiri komanso kudzimenya chifukwa cha chisoni. Yesu atalowa m’nyumbamo ananena mawu omwe anadabwitsa anthuwo. Iye ananena kuti: “Mwana wamng’onoyu sanamwalire ayi, koma akugona.” (Maliko 5:39) Anthuwo atamva zimenezi anayamba kuseka kwambiri chifukwa ankadziwa kuti mtsikanayo anali atamwaliradi. Koma Yesu ankafuna kuwasonyeza kuti akhoza kugwiritsa ntchito mphamvu zochokera kwa Mulungu poukitsa anthu amene amwalira ngati mmene angadzutsire munthu amene akugona.

Kenako Yesu anauza anthuwo kuti atuluke m’nyumbamo kupatulapo Petulo, Yakobo, Yohane ndi makolo a mtsikanayo. Ndiyeno Yesu anatengana ndi anthu 5 amenewa n’kupita nawo pamene anagoneka kamtsikanako. Yesu anagwira dzanja la mtsikanayo n’kunena kuti: “‘Talʹi·tha cuʹmi,’ mawu amene powamasulira amatanthauza kuti: ‘Kamtsikana iwe, ndikunena ndi iwe, Dzuka!’” (Maliko 5:41) Nthawi yomweyo mtsikanayo anadzuka n’kuyamba kuyenda. Tangoganizani mmene Yairo ndi mkazi wake anamvera ataona zimenezi. Pofuna kusonyeza anthuwo kuti mwanayo analidi moyo, Yesu anawauza kuti amupatse chakudya.

Mwina mungakumbukire kuti m’mbuyomu Yesu ankaletsa anthu amene anawachiritsa kuti asauze anthu ena zimene anawachitirazo ndipo ndi zimene anauzanso makolo a kamtsikanaka. Komabe makolo a kamtsikanaka ndiponso anthu ena anafalitsa nkhaniyi “m’dera lonselo.” (Mateyu 9:26) Kodi mukanakhala kuti wachibale wanu waukitsidwa, simukanasangalala kuuzako anthu ena zimene zachitikazo? Pa anthu amene Yesu anawaukitsa, nkhani ya kuukitsidwa kwa mtsikanayu ndi yachiwiri kulembedwa m’Baibulo.