Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 49

Analalikira ku Galileya Komanso Anaphunzitsa Atumwi

Analalikira ku Galileya Komanso Anaphunzitsa Atumwi

MATEYU 9:35-38; 10:1-15 MALIKO 6:6-11 LUKA 9:1-5

  • YESU ANAPITANSO KU GALILEYA

  • ANATUMIZA ATUMWI KUTI AKALALIKIRE

Yesu anali atagwira mwakhama ntchito yolalikira kwa zaka pafupifupi ziwiri. Koma sanaganize zoti apume kapena kusiya ntchito yolalikira. M’malomwake, Yesu “anayamba ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse [ya ku Galileya]. Anali kuphunzitsa m’masunagoge awo, kulalikira uthenga wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.” (Mateyu 9:35) Zimene Yesu anaona pa nthawiyi zinamuchititsa kutsimikiza mtima kuti alalikire m’madera enanso. Koma kodi akanakwanitsa bwanji kuchita zimenezi?

Pamene Yesu ankayenda anaona kuti anthu ambiri ankafunika kuthandizidwa komanso kulimbikitsidwa mwauzimu. Anthuwo anali ngati nkhosa zopanda m’busa, onyukanyuka ndi otayika. Iye anawamvera chisoni ndipo anauza ophunzira ake kuti: “Inde, zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.”—Mateyu 9:37, 38.

Yesu ankadziwa bwino zimene akanachita kuti athandize anthuwo. Anaitana atumwi ake 12 ndi kuwagawa awiriawiri ndipo anapanga magulu 6. Kenako anawapatsa malangizo omveka bwino kuti: “Musapite mumsewu wa anthu a mitundu ina, ndipo musalowe mumzinda wa Asamariya. M’malomwake, nthawi zonse muzipita kwa nkhosa zosochera za nyumba ya Isiraeli. Pitani ndi kulalikira kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’”—Mateyu 10:5-7.

Ufumu umene anauzidwa kuti akalalikire ndi umene Yesu ananena mu pemphero lachitsanzo. ‘Ufumu wakumwamba unali utayandikira’ chifukwa Yesu Khristu, yemwe anali Mfumu yoikidwa ndi Mulungu, anali pakati pawo. Koma n’chiyani chikanachititsa anthu kukhulupirira kuti ophunzira a Yesu ankaimiradi Ufumu wakumwamba? Pa nthawiyi Yesu anapatsa ophunzira ake mphamvu zochiritsa komanso kuukitsa akufa. Ophunzirawo sankafunika kulipiritsa anthu akachita zimenezi. Ndiyeno kodi akanapeza bwanji zinthu zofunika pa moyo wawo ngati chakudya?

Pa ulendowu Yesu anauza ophunzira ake kuti asatenge kalikonse. Sanafunike kutenga golide, siliva kapena mkuwa m’zikwama zawo za ndalama. Iwo sanafunike kutenganso matumba a chakudya, malaya awiri a mkati kapena nsapato. N’chifukwa chiyani sanafunike kutenga zinthu zimenezi? Yesu anawatsimikizira kuti: “Wantchito ayenera kulandira chakudya chake.” (Mateyu 10:10) Anthu okonda choonadi amene akanakumana nawo ndi omwe akanapatsa ophunzirawo zinthu zofunikira pa moyo wawo. Kenako Yesu ananena kuti: “Mukafika pakhomo lililonse, khalani pamenepo mpaka nthawi yochoka kumeneko itakwana.”—Maliko 6:10.

Yesu anauzanso ophunzira ake zimene ayenera kuchita akafika pakhomo la munthu kuti amuuze uthenga wa Ufumu. Iye anawauza kuti: “Pamene mukulowa m’nyumba, perekani moni kwa a m’banja limenelo. Ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere umene mukuifunira ukhale panyumbayo, koma ngati si yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. Kulikonse kumene munthu sakakulandirani kapena kumvetsera mawu anu, potuluka m’nyumba imeneyo kapena mumzinda umenewo sansani fumbi kumapazi anu.”—Mateyu 10:12-14.

Kodi chikanachitika n’chiyani ngati mzinda wonse kapena mudzi wonse wakana kumvetsera uthenga wawo? Yesu ananena kuti mzindawo kapena mudziwo udzalandira chilango chachikulu. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, Chilango cha Sodomu ndi Gomora pa Tsiku la Chiweruzo chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi cha mzinda umenewo.”—Mateyu 10:15..