Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 53

Wolamulira Amene Akhoza Kulamulira Mphepo Yamphamvu

Wolamulira Amene Akhoza Kulamulira Mphepo Yamphamvu

MATEYU 14:22-36 MALIKO 6:45-56 YOHANE 6:14-25

  • ANTHU ANKAFUNA KUMUVEKA YESU UFUMU

  • YESU ANAYENDA PAMADZI KOMANSO ANALETSA MPHEPO YAMPHAMVU

Anthu ataona kuti Yesu wadyetsa anthu masauzande ambiri pochulukitsa chakudya mozizwitsa, ananena kuti: “Mosakayika uyu ndi mneneri uja amene anati adzabwera padziko.” Ponena kuti mneneri anthuwo ankanena za Mesiya moti ankaona kuti Yesu akhoza kukhala wolamulira wabwino chifukwa akanakwaniritsa zimene iwo ankafuna. (Yohane 6:14; Deuteronomo 18:18) Choncho anthuwo anapangana kuti agwire Yesu n’kumuveka ufumu.

Koma Yesu anadziwa zimene anthuwa ankafuna kuchita. Kenako Yesu anayamba kuuza anthuwo kuti azipita kwawo ndipo anauzanso ophunzira ake kuti akwere boti. Kodi ophunzirawo analowera kuti? Analowera cha ku Betsaida koma ulendo wawo unali wopita ku Kaperenao. Pa nthawiyi Yesu anapita yekha kuphiri kuti akapemphere usiku umenewo.

Kutatsala pang’ono kucha, Yesu ankatha kuona boti ali chapatali chifukwa kunali mwezi. Panyanjapo panali mphepo yamphamvu yomwe inkachititsa mafunde moti atumwiwo ‘ankapalasa movutika, chifukwa ankalimbana ndi mphepo yamphamvu.’ (Maliko 6:48) Yesu anatsika m’phirimo n’kuyamba kuyenda pamadzi kulowera kumene kunali ophunzirawo. Pamene zimenezi zinkachitika n’kuti ophunzirawo “atapalasa makilomita pafupifupi 5 kapena 6.” (Yohane 6:19) Ophunzirawo anaona ngati Yesu akufuna kuwapitirira ndipo anafuula kuti: “Amenewa ndi masomphenya ndithu!”—Maliko 6:49.

Yesu anawalimbikitsa kuti: “Limbani mtima, ndine. Musachite mantha.” Koma Petulo ananena kuti: “Ambuye, ngati ndinudi, ndiuzeni ndiyende pamadzipa ndibwere kuli inuko.” Yesu anamuuza kuti: “Bwera!” Nthawi yomweyo Petulo anatsika m’botilo n’kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. Koma ataona mphepo yamphamvuyo anachita mantha ndipo anayamba kumira. Kenako anafuula kuti: “Ambuye, ndipulumutseni!” Pamenepo Yesu anatambasula dzanja lake ndipo anagwira dzanja la Petulo n’kumuuza kuti: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, n’chifukwa chiyani wakayikira?”—Mateyu 14:27-31.

Ndiyeno Petulo ndi Yesu anakwera m’boti ndipo mphepoyo inasiya. Ophunzirawo anadabwa kwambiri, koma kodi anayeneradi kudabwa? Ophunzirawo akanamvetsa tanthauzo la chozizwitsa chimene Yesu anachita pamene anadyetsa anthu masauzande ambiri, sanafunike kudabwa ataona Yesu akuyenda pamadzi komanso kuletsa mphepo ya mphamvu. Chifukwa cha zimene anaonazo anamugwadira n’kunena kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.”—Maliko 6:52; Mateyu 14:33.

Patapita nthawi yochepa anafika m’dera lokongola la Genesarete, chakum’mwera kwa Kaperenao. Derali linali la chonde kwambiri. Anaimika boti lawo kumeneko n’kupita kumtunda. Anthu a m’derali anam’zindikira Yesu moti anthuwo komanso a m’madera ena apafupi anabweretsa anthu odwala kuti Yesu awachiritse. Odwalawo ankati akangogwira m’munsi mwa malaya akunja a Yesu ankachira nthawi yomweyo.

Pamene zimenezi zinkachitika n’kuti anthu amene anadyetsedwa mozizwitsa aja atazindikira kuti Yesu wachoka m’deralo. Choncho maboti ang’onoang’ono ochokera ku Tiberiyo atafika, anthuwo anakwera mabotiwo n’kupita ku Kaperenao kuti akafunefune Yesu. Atamupeza anamufunsa kuti: “Rabi, mwafika nthawi yanji kuno?” (Yohane 6:25) Yesu anawadzudzula ndipo nkhani yotsatira ifotokoza chifukwa chomveka chimene iye anachitira zimenezi.