Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 57

Yesu Anachiritsa Mtsikana Komanso Munthu Wogontha

Yesu Anachiritsa Mtsikana Komanso Munthu Wogontha

MATEYU 15:21-31 MALIKO 7:24-37

  • YESU ANACHIRITSA MWANA WA MAYI WA KU FOINIKE

  • ANACHIRITSA MUNTHU WOGONTHA KOMANSO WOSALANKHULA

Yesu atadzudzula Afarisi chifukwa chotsatira miyambo yokomera iwowo, anachoka ku Kaperenao pamodzi ndi ophunzira ake. Iwo nalowera kumadera a Turo ndi Sidoni m’chigawo cha Foinike, chomwe chinali kumpoto chakumadzulo kwa Kaperenao.

Atafika kumeneko Yesu anapeza nyumba yoti azikhalako ndipo sanafune kuti anthu adziwe zoti ali kumeneko koma anthuwo anadziwabe. Mayi wina wachigiriki, yemwe anabadwira m’dera limeneli, anakumana ndi Yesu ndipo anayamba kumuchonderera kuti: “Ndichitireni chifundo Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi wagwidwa ndi chiwanda mochititsa mantha.”—Mateyu 15:22; Maliko 7:26.

Patapita kanthawi, ophunzira a Yesu anauza Yesuyo kuti: “Muuzeni kuti azipita, chifukwa akupitirizabe kufuula m’mbuyo mwathumu.” Zimene Yesu anayankha zinasonyeza kuti anasankha dala kuti asamuyankhe mayiyo. Iye anati: “Ine sananditumize kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” Komabe mayiyo sanasiyire pompo. Anapita pamene panali Yesu n’kugwada kenako anamuchonderera kuti: “Ambuye, ndithandizeni!”—Mateyu 15:23-25.

Pofuna kuona ngati mayiyo analidi ndi chikhulupiriro cholimba, Yesu anagwiritsa ntchito mawu amene Ayuda ankagwiritsa ntchito ponyoza anthu a mitundu ina. Iye ananena kuti: “Si bwino kutenga chakudya cha ana n’kuponyera tiagalu.” (Mateyu 15:26) Ponena kuti “tiagalu” Yesu anasonyeza kuti ankachitiranso chifundo anthu omwe sanali Ayuda ndipo n’kutheka kuti pamene ankanena mawu amenewa, nkhope yake komanso mawu ake zinkasonyeza zimenezi.

Mayiyu sanakhumudwe ndi zimene Yesu ananenazi, moti anagwiritsanso ntchito mawu amene Yesu ananena. Iye anayankha kuti: “Inde Ambuye, komatu tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa patebulo la ambuye awo.” Yesu anazindikira kuti mayiyo anali ndi mtima wabwino ndipo anamuuza kuti: “Mayi iwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu. Zimene ukufuna zichitike kwa iwe.” (Mateyu 15:27, 28) Ndipo ndi zimene zinachitikadi. Mwana wamkazi wa mayiyo anachira ngakhale kuti mwanayo anali kwina. Mayiyo atabwerera kunyumba anakamupeza mwanayo atagona pabedi koma ali bwinobwino, “chiwandacho chitatuluka.”—Maliko 7:30.

Kenako Yesu ndi ophunzira ake anachoka m’dera la Foinike n’kulowera kumtsinje wa Yorodano womwe unali kumpoto chakumtunda kwa nyanja ya Galileya. Anawoloka mtsinje wa Yorodanowo n’kupita m’dera la Dekapole. Atafika kumeneko anakakwera phiri lina koma gulu la anthu linakawapeza komweko. Anthuwo anamubweretsera Yesu anthu olumala, othyoka ziwalo, akhungu komanso osalankhula ndipo anawaika pafupi ndi pamene anakhala moti anawachiritsa. Anthuwo anadabwa ndi zimene Yesu anachitazo ndipo analemekeza Mulungu wa Isiraeli.

Koma Yesu anathandiza mwapadera munthu wina amene anali wogontha komanso wovutika kulankhula. Tangoganizani mmene munthuyo ankamvera pa gulu la anthulo. Yesu ataona mmene munthuyo ankachitira mantha anachoka naye pagulupo n’kupita naye pambali. Ali kwa okha, Yesu anachita zinthu zomwe zinathandiza munthuyo kudziwa zimene Yesu amuchitire. Anapisa zala zake m’makutu a munthuyo ndipo analavula malovu n’kukhudza lilime la munthuyo. Kenako Yesu anayang’ana kumwamba n’kulankhula mawu omwe amatanthauza kuti “Tseguka.” Nthawi yomweyo munthuyo anayamba kumva komanso kulankhula bwinobwino. Yesu sanafune kuti nkhaniyi idziwike kwa anthu ambiri chifukwa ankafuna kuti anthuwo azimukhulupirira, osati chifukwa cha zinthu zimene amva kwa anthu ena, koma chifukwa cha zinthu zimene aona kapena kudzimvera okha.—Maliko 7:32-36.

Anthuwo ‘anadabwa kwambiri’ kuona kuti Yesu anali ndi mphamvu zotha kuchiritsa. Iwo ananena kuti: “Wachita zinthu zonse bwinobwino ndithu. Ngakhale ogontha akumva ndipo osalankhula akuwalankhulitsa.”—Maliko 7:37.