Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 58

Anachulukitsa Mikate Komanso Anachenjeza Ophunzira Ake za Zofufumitsa

Anachulukitsa Mikate Komanso Anachenjeza Ophunzira Ake za Zofufumitsa

MATEYU 15:32–16:12 MALIKO 8:1-21

  • YESU ANADYETSA AMUNA 4,000

  • ANACHENJEZA OPHUNZIRA AKE ZA ZOFUFUMITSA ZA AFARISI

Pa nthawi imene Yesu anali m’dera la Dekapole, lomwe linali kum’mawa kwa nyanja ya Galileya, anthu ambiri anapita kwa iye kuti akamve zimene ankaphunzitsa komanso kuti akawachiritse. Popita kumeneko anthuwo anatenga mabasiketi akuluakulu a zakudya za paulendo.

Koma patapita nthawi, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Khamu la anthuli likundimvetsa chisoni, chifukwa anthuwa akhala ndi ine masiku atatu tsopano ndipo alibe chakudya. Koma ndikawauza kuti azipita kwawo ndi njala, alenguka panjira. Ndipo ena a iwo achokera kutali kwambiri.” Ophunzirawo anamufunsa kuti: “Munthu angaipeze kuti mitanda ya mkate yokwanira kudyetsa anthu onsewa kutchire ngati kuno?”—Maliko 8:2-4.

Yesu anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate?” Ophunzirawo ananena kuti: “Tili nayo 7, ndi tinsomba towerengeka.” (Mateyu 15:34) Pamenepo Yesu anauza anthuwo kuti akhale pansi. Anatenga mikate ndi nsombazo n’kupemphera kwa Mulungu. Atapemphera anazipereka kwa ophunzira ake kuti agawire anthuwo. Zinali zodabwitsa kwambiri kuti onse anadya n’kukhuta moti zina zinatsala. Zotsalazo zinadzaza madengu 7, ngakhale kuti panali amuna 4,000 komanso akazi ndi ana amene anadya zakudyazo.

Anthuwo atamaliza kudya, Yesu anawauza kuti azipita koma iye ndi ophunzira ake anakwera boti n’kupita ku dera la Magadani, lomwe linali chakumadzulo kwa nyanja ya Galileya. Ali kumeneko anakumana ndi Afarisi omwe anali ndi anthu ena a m’gulu la mpatuko la Asaduki. Iwo anapempha Yesu kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba koma anachita zimenezi pofuna kungomuyesa.

Yesu anazindikira maganizo awo ndipo anawayankha kuti: “Kunja kukamada mumanena kuti, ‘Nyengo ikhala yabwino, chifukwa kumwamba kwachita cheza.’ Koma m’mawa mumanena kuti, ‘Lero kukuoneka kuti kugwa mvula, chifukwa kumwamba kwachita cheza koma kuli mdima wamvula.’ Mumadziwa kumasulira kaonekedwe ka kumwamba, koma simungathe kumasulira zizindikiro za nthawi ino.” (Mateyu 16:2, 3) Yesu anauza Afarisi ndi Asadukiwo kuti sadzapatsidwa chizindikiro chilichonse kupatulapo chizindikiro cha Yona.

Kenako Yesu ndi ophunzira ake anakwera boti n’kuyamba ulendo wopita ku Betsaida, kumpoto chakum’mawa kwa nyanja ya Galileya. Ali m’njira, ophunzirawo anazindikira kuti aiwala kutenga mikate yokwanira. Anali ndi mkate umodzi wokha basi. Pokumbukira zimene zinachitika atakumana ndi Afarisi komanso Asaduki, omwe anali kumbali ya Herode, Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Khalani maso! Chenjerani ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi cha Herode.” Ophunzirawo atamva Yesu akutchula za zofufumitsa ankaganiza kuti akunena za mikate yomwe anaiwala ija. Koma Yesu ataona kuti ophunzirawo sanamve zimene ankatanthauza, anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukukangana nkhani yosowa mikate?”—Maliko 8:15-17.

Yesu anali atangodyetsa kumene anthu masauzande ambiri. Ndiye ophunzirawo akanadziwa kuti Yesu sankadandaula ndi zoti alibe mikate yeniyeni. N’chifukwa chake iye anawafunsa kuti: “Simukukumbukira kodi, kuchuluka kwa madengu a zotsala zimene munatolera, pamene ndinanyemanyema mitanda isanu ya mkate koma n’kukwanira amuna 5,000?” Ophunzirawo anayankha kuti: “Anali madengu 12.” Yesu anawafunsanso kuti: “Pamene ndinanyemanyema mitanda 7 ya mkate koma inakwanira amuna 4,000, kodi munatolera madengu akuluakulu angati a zotsala?” Iwo anayankha kuti: “Analipo 7.”—Maliko 8:18-20.

Kenako Yesu anawafunsa kuti: “Nanga bwanji simukuzindikira kuti sindikunena za mitanda ya mkate?” Anawauzanso kuti: “Samalani ndi zofufumitsa za Afarisi ndi Asaduki.”—Mateyu 16:11.

Pamene ananena mawu amenewa, ophunzirawo anamvetsa zimene Yesu ankatanthauza. Zofufumitsa zimachititsa kuti mkate ufufume. Yesu anagwiritsa ntchito mophiphiritsa mawu akuti zofufumitsa pofuna kutanthauza zinthu zimene zingasokoneze mmene munthu amaganizira. Choncho ankawachenjeza ophunzira ake kuti asamale ndi ‘zimene Afarisi ndi Asaduki ankaphunzitsa’ kuti zingawasokoneze.—Mateyu 16:12.