Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 80

M’busa Wabwino Komanso Makola Awiri a Nkhosa

M’busa Wabwino Komanso Makola Awiri a Nkhosa

YOHANE 10:1-21

  • YESU ANANENA ZA M’BUSA WABWINO KOMANSO ZA MAKOLA AWIRI A NKHOSA

Pamene Yesu ankaphunzitsa anthu ku Yudeya, anafotokoza za nkhosa komanso makola a nkhosazo, zomwe anthu ambiri ankazidziwa bwino. Komabe Yesu anatchula zinthu zimenezi ngati fanizo. N’kutheka kuti Ayuda anakumbukira mawu amene Davide ananena akuti: “Yehova ndi M’busa wanga. Sindidzasowa kanthu. Amandigoneka m’mabusa a msipu wambiri.” (Salimo 23:1, 2) Koma wolemba masalimo wina anauza anthu onse kuti: “Bwerani timuweramire ndi kumupembedza. Tiyeni tigwade pamaso pa Yehova amene ndiye Wotipanga. Pakuti iye ndi Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu ake. Iye amatisamalira ngati nkhosa zimene akuweta.” (Salimo 95:6, 7) Choncho Aisiraeli amene kwa nthawi yaitali ankagwiritsa ntchito Chilamulo ankayerekezeredwa ndi gulu la nkhosa.

Aisiraeli amenewa anali ngati “nkhosa” zimene zinali ‘m’khola’ chifukwa atabadwa ankatsogoleredwa ndi Chilamulo chimene Yehova anawapatsa atachita pangano ndi Mose. Chilamulo chinali ngati mpanda womwe unkawateteza kuti asatengere makhalidwe oipa a anthu omwe sankatsatira chilamulochi. Koma Aisiraeli ena ankachitira nkhanza anthu a Mulungu omwe anali ngati nkhosa. Ponena za anthu amenewa Yesu ananena kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Wolowa m’khola la nkhosa mochita kukwera pamalo ena osati kudzera pakhomo, ameneyo ndi wakuba ndiponso wofunkha. Koma wolowera pakhomo, ameneyo ndiye m’busa wa nkhosazo.”—Yohane 10:1, 2.

N’kutheka kuti Yesu atanena mawu amenewa anthuwa ankaganizira za anthu ena omwe ankanamizira kuti anali Mesiya kapena Khristu. Iwo ankaona kuti anthu amenewa ndi amene anali ngati akuba komanso ofunkha ndipo anthu sankayenera kuwatsatira. Koma ankafunika kutsatira “m’busa wa nkhosazo” yemwe Yesu anamufotokoza kuti:

“Mlonda wa pakhomo amamutsegulira ameneyu, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Nkhosa zakezo amazitchula mayina ndi kuzitsogolera kutuluka nazo. Akatulutsa zake zonse kunja, amazitsogolera, ndipo nkhosazo zimamutsatira, chifukwa zimadziwa mawu ake. Mlendo sizidzamutsatira ayi koma zidzamuthawa, chifukwa sizidziwa mawu a alendo.”—Yohane 10:3-5.

Yohane M’batizi, yemwe anali ngati mlonda wa pakhomo, ananena kuti anthu amene ankatsatira Chilamulo, omwe anali ngati nkhosa, ayenera kutsatira Yesu. Ndipo anthu ena amene ankakhala ku Galileya komanso ku Yudeya anazindikira mawu a Yesu. Kodi Yesu ‘anawatsogolera’ kuti anthuwa? Nanga kodi zinthu zinawayendera bwanji chifukwa chotsatira Yesu? N’kutheka kuti anthu ena amene anamva fanizolo anadabwa chifukwa “sanadziwe tanthauzo la zinthu zimene anali kuwauzazo.”—Yohane 10:6.

Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Ine ndine khomo la nkhosa. Onse amene abwera m’malo mwa ine ndi akuba ndiponso ofunkha, ndipo nkhosa sizinawamvere. Ine ndine khomo. Aliyense wolowa kudzera mwa ine adzapulumuka, ndipo azidzalowa ndi kutuluka, kukapeza msipu.”—Yohane 10:7-9.

Apatu zikuonetsa kuti Yesu anayambitsa nkhani ina yatsopano. Anthuwo ankadziwa kuti Yesu sanali khomo la chipangano cha Chilamulo chomwe chinali chitagwira ntchito kwa zaka zambiri. Choncho ayenera kuti ankanena kuti nkhosa zimene ‘ankazitsogolerazo’ zidzalowa m’khola lina. Koma n’chifukwa chiyani ananena zimenezi?

Yesu anapitiriza kufotokoza za udindo wake ndipo anati: “Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, inde kuti akhale nawo wochuluka. Ine ndine m’busa wabwino. M’busa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.” (Yohane 10:10, 11) Nthawi ina Yesu analimbikitsa ophunzira ake powauza kuti: “Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.” (Luka 12:32) Choncho anthu amene akupanga “kagulu ka nkhosa” ndi amene Yesu adzawatsogolere ku khola lina kuti “akhale ndi moyo, inde kuti akhale nawo wochuluka.” Ndi mwayitu waukulu kwambiri kukhala m’gulu limeneli la nkhosa.

Komabe Yesu sanasiyire pomwepo, ananenanso kuti: “Ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za khola ili, zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.” (Yohane 10:16) Choncho pamene Yesu ananena kuti “nkhosa zina zimene sizili za khola ili,” ayenera kuti ankatanthauza kuti pali khola lina la nkhosa losiyana ndi la “kagulu ka nkhosa” komwe kadzalandire Ufumu. Anthu amene ali m’makola awiri amenewa akuyembekezera zinthu zosiyana. Komabe anthu onsewa adzasangalala ndi zimene Yesu adzachite pokwaniritsa udindo wake. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Chimene Atate amandikondera n’chakuti, ndikupereka moyo wanga.”—Yohane 10:17.

Anthu ambiri atamva zimenezi ananena kuti: “Ameneyu ali ndi chiwanda ndipo ndi wamisala.” Komabe ena anamvetsera mwachidwi ndipo ankafunitsitsa kutsatira M’busa wabwino moti ananena kuti: “Amenewa si mawu a munthu wogwidwa ndi chiwanda ayi. Kodi chiwanda chingatsegule maso a anthu akhungu?” (Yohane 10:20, 21) Anthuwa ananena zimenezi atakumbukira zimene Yesu anachita nthawi ina atachiritsa munthu amene anabadwa wosaona.