Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 84

Kukhala Wophunzira wa Yesu Ndi Udindo Waukulu

Kukhala Wophunzira wa Yesu Ndi Udindo Waukulu

LUKA 14:25-35

  • ZIMENE MUNTHU AYENERA KUCHITA KUTI AKHALE WOPHUNZIRA WA YESU

Yesu anaphunzitsa anthu mfundo zothandiza kwambiri pamene ankadya chakudya kunyumba kwa mtsogoleri wa Afarisi uja. Atachoka kumeneko anapitiriza ulendo wake wolowera ku Yerusalemu ndipo gulu la anthu linkamutsatira. Koma n’chifukwa chiyani anthuwa ankamutsatira? Kodi ankafunitsitsadi kuti akhale otsatira ake? Kodi akanakwanitsa kuchita zonse zimene otsatira a Yesu amafunika kuchita?

Ali pa ulendowu Yesu ananena zinthu zimene zinadabwitsa ena mwa anthuwo. Iye anati: “Ngati wina wabwera kwa ine, koma osadana ndi bambo ake, mayi ake, mkazi wake, ana ake, abale ake ndi alongo ake, ngakhale moyo wake umene, sangakhale wophunzira wanga.” (Luka 14:26) Kodi ankatanthauza chiyani ponena zimenezi?

Yesu sankatanthauza kuti aliyense amene wasankha kukhala wotsatira wake ayenera kudana ndi achibale ake. Koma ankatanthauza kuti ayenera kukonda kwambiri Yesu kuposa achibale ake, osati ngati munthu wa m’fanizo lija yemwe anakana kubwera ataitanidwa chifukwa choti anali atangokwatira kumene. (Luka 14:20) Baibulo limanena kuti Yakobo, yemwe anali kholo la mtundu wa Ayuda, ‘ankada’ Leya koma ankakonda Rakele, zomwe zinkatanthauza kuti Yakobo anakonda kwambiri Rakele kuposa Leya.—Genesis 29:31, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Yesu ananenanso kuti wophunzira wake ayenera kudana ndi “moyo wake.” Zimenezi zikutanthauza kuti wophunzira weniweni ayenera kukonda kwambiri Yesu kuposa mmene amakondera moyo wake moti akhoza kulolera kuutaya. Choncho kukhala wophunzira wa Khristu ndi udindo waukulu moti munthu ayenera kuganizira mofatsa asanasankhe kukhala wotsatira wa Khristu.

Munthu akasankha kukhala wotsatira wa Khristu akhoza kukumana ndi mavuto aakulu komanso kuzunzidwa. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Aliyense wosanyamula mtengo wake wozunzikirapo ndi kunditsatira ine sangakhale wophunzira wanga.” (Luka 14:27) Wophunzira weniweni wa Yesu ayenera kukhala wokonzeka kunyozedwa ngati mmene zinakhalira ndi Yesu. Yesu ananenanso kuti ankayembekezera kufera m’manja mwa adani ake.

Anthu amene ankayenda ndi Yesu pa ulendowu ankafunika kuganizira mofatsa asanasankhe kukhala otsatira ake. Pofuna kuwathandiza kuti amvetse mfundo imeneyi, Yesu ananena fanizo. Iye anati: “Mwachitsanzo, ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo? Akapanda kutero, angayale maziko koma osatha kuimaliza.” (Luka 14:28, 29) Choncho anthuwo asanakhale ophunzira a Yesu ankafunika kusankha ndi mtima wawo wonse kuti adzakwaniritsa udindo wawo monga ophunzira a Yesu. Yesu ananenanso fanizo lina kuti anthuwo amvetse mfundo imeneyi. Iye anati:

“Kapena ndi mfumu yanji, imene popita kukakumana ndi mfumu inzake pa nkhondo, siyamba yakhala pansi ndi kuganiza mofatsa ngati asilikali ake 10,000 angathe kulimbana ndi asilikali 20,000 a mfumu yobwera kudzalimbana naye? Koma akaona kuti sangakwanitse, mwamsanga amatumiza akazembe kwa mfumu inayo isanafike pafupi, kukapempha mtendere. Choncho, dziwani ichi, ndithu palibe aliyense wolephera kulekana ndi chuma chake chonse amene angathe kukhala wophunzira wanga.”—Luka 14:31-33.

Yesu sananene zimenezi kwa anthu okhawo amene anali nawo pa ulendowu. Aliyense amene waphunzira za Khristu ayenera kukhala wokonzeka kutsatira zimene Yesu ananenazi. Zimenezi zikutanthauza kuti aliyense amene wasankha kukhala wotsatira wa Yesu ayenera kukhala wokonzeka kusiya chilichonse chimene ali nacho ngakhalenso kutaya moyo wake. Imeneyi ndi nkhani yofunika kuiganizira kwambiri komanso kuipempherera.

Ndiyeno Yesu anafotokoza mfundo ina imene anaitchulanso pa ulaliki wake wa paphiri pamene ananena kuti ophunzira ake ndi “mchere wa dziko lapansi.” (Mateyu 5:13) Potchula mfundo imeneyi ayenera kuti ankatanthauza kuti monga mmene mchere umatetezera zakudya kuti zisawonongeke, ophunzira akenso anali ndi mphamvu zoteteza anthu kuti akhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu komanso kuti azikhala ndi makhalidwe abwino. Pa nthawiyi n’kuti Yesu atatsala pang’ono kumaliza ntchito imene anabwerera padziko lapansi ndipo ananena kuti: “Kunena zoona, mchere ndi wabwino. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, kodi mphamvu yake ingabwezeretsedwe bwanji?” (Luka 14:34) Anthuwo ankadziwa kuti mchere wina umene unkapezeka pa nthawiyo sunali wabwino chifukwa unali wosakanikirana ndi dothi moti unalibe mphamvu.

Pamenepa Yesu anasonyeza kuti anthu amene akhala ophunzira ake kwa nthawi yaitali ayenera kusamala kuti asayambe kufooka. Ngati zimenezi zitachitika ndiye kuti ophunzirawo akhoza kukhala opanda ntchito ngati mmene umakhalira mchere umene watha mphamvu. Zimenezi zingachititse kuti anthu aziwanyoza komanso kuti asakhale oyenera kutumikira Mulungu ndipo akhoza kunyozetsa dzina la Mulungu. Ndiyeno Yesu ananena kufunika kosamala kuti munthu asayambe kufooka ponena kuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”—Luka 14:35.