Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 97

Fanizo la Anthu Ogwira Ntchito M’munda wa Mpesa

Fanizo la Anthu Ogwira Ntchito M’munda wa Mpesa

MATEYU 20:1-16

  • “OMALIZIRA” KUGWIRA NTCHITO M’MUNDA WA MPESA NDI AMENE ANAKHALA “OYAMBIRIRA”

Yesu ali ku Pereya ananena kuti anthu “ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza, ndipo omaliza adzakhala oyamba.” (Mateyu 19:30) Pofuna kuthandiza anthuwo kumvetsa mfundo imeneyi, Yesu anafotokoza fanizo lonena za aganyu omwe ankagwira ntchito m’munda wa mpesa. Iye anati:

“Pakuti ufumu wakumwamba uli ngati mwinimunda wa mpesa, amene analawirira m’mawa kwambiri kukafuna anthu aganyu kuti akagwire ntchito m’munda wake wa mpesa. Aganyu amenewa atagwirizana nawo kuti aziwapatsa ndalama ya dinari imodzi pa tsiku, anawatumiza kumunda wake wa mpesa. Pafupifupi 9 koloko m’mawa anapitanso kukafuna anthu ena, ndipo anaona ena atangoimaima pamsika alibe chochita. Amenewonso anawauza kuti, ‘Inunso kagwireni ntchito m’munda wa mpesa. Ndidzakupatsani malipiro oyenerera.’ Chotero iwo anapita. Pafupifupi 12 koloko ndi 3 koloko masana, mwinimunda uja anapitanso kukachita chimodzimodzi. Pamapeto pake, pafupifupi 5 koloko madzulo anapitanso ndipo anakapeza ena atangoimaima. Iye anawafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mwangoimaima pano tsiku lonse osagwira ntchito?’ Iwo anamuyankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba ganyu.’ Iye anawauza kuti, ‘Inunso pitani kumunda wanga wa mpesa.’”—Mateyu 20:1-7.

Anthu amene Yesu ankalankhula nawo ayenera kuti anaganiza za Yehova Mulungu atamva Yesu akunena za “ufumu wakumwamba” komanso za “mwinimunda.” Malemba amayerekeza Yehova ndi mwinimunda wa mpesa ndipo mundawo unkaimira mtundu wa Aisiraeli. (Salimo 80:8, 9; Yesaya 5:3, 4) Anthu amene anali mu pangano la Chilamulo anali ngati ogwira ntchito m’munda wa mpesa. Ponena fanizoli Yesu sankafotokoza zinthu zimene zinachitika m’mbuyo koma ankafotokoza zimene zinkachitika nthawi imeneyoyo.

Zikuoneka kuti atsogoleri achipembedzo, mwachitsanzo Afarisi amene anayesa Yesu pomufunsa nkhani zokhudza kuthetsa banja, anali ngati akhala akugwira ntchito mwakhama potumikira Mulungu. Anali ngati anthu amene ankagwira ntchito nthawi zonse ndipo ankayembekezera kulandira malipiro onse ndipo malipiro ake anali dinari imodzi, yomwe inali malipiro a tsiku limodzi.

Ansembe komanso anthu ena omwe anali m’gulu la atsogoleri achipembedzo ankaona kuti Ayuda wamba sankatumikira kwambiri Mulungu ndipo anali ngati aganyu m’munda wa mpesa wa Mulungu. M’fanizo la Yesuli, Ayuda wambawa anali ngati aganyu amene anawalemba ntchito cha m’ma 9 koloko m’mawa kapena amene anayamba cha m’ma 12 koloko, 3 koloko komanso cha m’ma 5 koloko madzulo.

Atsogoleri achipembedzo ankaona kuti amuna ndi akazi amene ankatsatira Yesu anali ngati anthu ‘otembereredwa.’ (Yohane 7:49) Kwa nthawi yaitali anthu amenewa ankagwira ntchito yausodzi komanso ankagwira maganyu osiyanasiyana. Ndiyeno pofika m’mwezi wa July kapena August m’chaka cha 29 C.E., “mwinimunda” anatumiza Yesu kuti akaitane anthu otsikawa kuti adzagwire ntchito ya Mulungu monga ophunzira a Khristu. Anthuwa anali antchito “omalizira” amene Yesu anawatchula, omwe anayamba kugwira ntchito m’munda wa mpesa cha m’ma 5 koloko madzulo.

Yesu anamaliza fanizoli ponena zimene zinachitika pamene tsikulo linkatha. Iye anati: “Madzulowo, mwinimunda wa mpesa uja anauza kapitawo wake kuti, ‘Itana antchito aja uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira, kutsiriza ndi oyambirira.’ Anthu amene anayamba ntchito 5 koloko aja atafika, aliyense analandira dinari imodzi. Chotero oyambirira aja atafika, anaganiza kuti alandira zambiri, koma nawonso malipiro amene analandira anali dinari imodzi. Atalandira, anayamba kung’ung’udza kwa mwinimunda wa mpesa uja kuti, ‘Omalizirawa agwira ntchito ola limodzi lokha, koma mwawapatsa malipiro ofanana ndi ife amene tagwira ntchito yakalavulagaga tsiku lonse padzuwa lotentha!’ Koma poyankha kwa mmodzi wa iwo, mwinimundayo anati, ‘Bwanawe, sindikukulakwira ayi. Tinapangana malipiro a dinari imodzi, si choncho kodi? Ingolandira malipiro ako uzipita. Ndikufuna kupatsa womalizirayu malipiro ofanana ndi amene ndapereka kwa iwe. Kodi n’kosaloleka kuchita zimene ndikufuna ndi zinthu zanga? Kapena diso lako lachita njiru chifukwa chakuti ndine wabwino?’ Choncho omalizira adzakhala oyambirira ndipo oyambirira adzakhala omalizira.”—Mateyu 20:8-16.

N’kutheka kuti ophunzira a Yesu ankafuna kudziwa kuti mbali yomaliza ya fanizo la Yesu inkatanthauza chiyani. Kodi atsogoleri achipembedzo achiyuda omwe ankadziona ngati “oyambirira” anakhala bwanji “omalizira”? Nanga ophunzira a Yesu anakhala bwanji “oyambirira”?

Ophunzira a Yesu omwe Afarisi ankawaona ngati “omalizira,” anakhala “oyambirira” kulandira malipiro awo onse. Yesu atafa, Mulungu anasiya kuona mzinda wa Yerusalemu ngati wopatulika ndipo anasankha mtundu watsopano wa “Isiraeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16; Mateyu 23:38) Yohane M’batizi ankanena za mtundu umenewu pamene anafotokoza za kubatizidwa ndi mzimu woyera. Anthu omwe anali “omalizira,” anakhala oyamba kubatizidwa ndi mzimu woyera umenewu komanso kulandira mwayi wochitira umboni za Yesu “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Machitidwe 1:5, 8; Mateyu 3:11) Ophunzirawo atamvetsa za kusintha kumene Yesu anafotokoza anadziwa kuti atsogoleri achipembedzo, omwe anakhala “omalizira,” adzadana nawo kwambiri.