Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 98

Atumwi Anasonyezanso Kuti Ankafuna Udindo Wapamwamba

Atumwi Anasonyezanso Kuti Ankafuna Udindo Wapamwamba

MATEYU 20:17-28 MALIKO 10:32-45 LUKA 18:31-34

  • YESU ANANENANSO ZA IMFA YAKE

  • ANATHANDIZA ATUMWI OMWE ANKAFUNA UDINDO WAPAMWAMBA

Yesu ndi ophunzira ake anawoloka mtsinje wa Yorodano chakufupi ndi mzinda wa Yeriko pamene ankachoka kum’mwera kwa Pereya kupita ku Yerusalemu. Pa ulendowu analinso ndi anthu ena amene ankapita kumwambo wa Pasika wa mu 33 C.E.

Yesu ankayenda patsogolo pa ophunzirawo chifukwa ankafuna kuti akafike nthawi yabwino kuti akachite nawo mwambo wa Pasika. Koma pa nthawiyi ophunzira a Yesu anali ndi mantha. Kumbukirani kuti Lazaro atamwalira, Yesu ankafuna kupita ku Yudeya ndipo Tomasi anauza ophunzira enawo kuti: “Ifenso tiyeni tipite, kuti tikafere naye limodzi.” (Yohane 11:16, 47-53) Choncho kupita ku Yerusalemu kunali koopsa ndipo mpake kuti ophunzirawo ankachita mantha.

Pofuna kuwakonzekeretsa ophunzira ake zimene iyeyo ankayembekezera kukumana nazo, Yesu anawauza kuti: “Tsopano tikupita ku Yerusalemu. Kumeneku, Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo akamuweruza kuti aphedwe. Akam’pereka kwa anthu a mitundu ina kuti am’chitire chipongwe, kum’kwapula ndi kum’pachika pamtengo, ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”—Mateyu 20:18, 19.

Aka kanali kachitatu kuti Yesu auze ophunzira ake za imfa yake komanso kuti adzaukitsidwa. (Mateyu 16:21; 17:22, 23) Pa nthawiyi anawauza kuti akapachikidwa pamtengo koma ophunzirawo sanamvetse zimene ankatanthauza. Mwina ophunzirawo ankaganiza kuti Yesu abwezeretsa Ufumu wa Isiraeli padziko lapansi. Iwo ankayembekezera kusangalala ndi ulemerero komanso kuti azilemekezedwa polamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumuwo.

Salome, yemwe anali mayi a Yakobo ndi Yohane, anali nawo pa ulendowu. Yesu anapatsa Yakobo ndi Yohane, dzina limene linkatanthauza “Ana a Bingu” chifukwa ankachita zinthu mwachangu komanso ankakwiya msanga. (Maliko 3:17; Luka 9:54) Kwa nthawi yaitali ophunzira awiriwa ankafuna malo apamwamba mu Ufumu wa Khristu ndipo mayi awo ankadziwanso zimenezi. Ndiyeno amayi awowo anapita kwa Yesu, kukagwada n’kumupempha kuti awachitire zina zake. Kenako Yesu anafunsa kuti: “Mukufuna chiyani?” Salome anayankha kuti: “Lonjezani kuti ana angawa adzakhala, mmodzi kudzanja lanu lamanja, wina kumanzere kwanu, mu ufumu wanu.”—Mateyu 20:20, 21.

Ngakhale kuti Salome ndi amene anakapempha kwa Yesu, koma Yakobo ndi Yohane ndi amene anawatuma. Popeza anali atawauza kale zinthu zochititsa manyazi zimene ankayembekezera kukumana nazo, Yesu anawauzanso kuti: “Anthu inu simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwe zimene ine ndatsala pang’ono kumwa?” Iwo anati: “Inde tingamwe.” (Mateyu 20:22) Ngakhale kuti iwo anayankha choncho, n’kutheka kuti sanamvetse zimene Yesu ankatanthauza.

Komabe Yesu anawauza kuti: “Inde mudzamwadi zimene ndatsala pang’ono kumwa. Koma kunena zokhala kudzanja langa lamanja ndi lamanzere, si ine wopereka mwayi umenewo, koma Atate wanga adzaupereka kwa amene anawakonzera.”—Mateyu 20:23.

Atumwi enawo atamva zimene Yakobo ndi Yohane anapempha anakwiya kwambiri. N’kutheka kuti Yakobo ndi Yohane ndi amene m’mbuyomo anayambitsa nkhani imene inachititsa kuti atumwiwa akangane pofuna kudziwa kuti wamkulu ndani. (Luka 9:46-48) Zimene ophunzirawa anapempha zikusonyeza kuti atumwi 12 aja sanatsatire malangizo amene Yesu anawapatsa oti asamadzione kuti ndi apamwamba. Zikuoneka kuti ophunzirawa ankafunabe udindo wapamwamba.

Yesu anaganiza zothetsa mkangano umenewo komanso mavuto amene nkhaniyi inkayambitsa. Anaitana ophunzira ake 12 aja ndi kuwapatsa malangizo mwachikondi. Iye anati: “Inu mukudziwa kuti amene amaoneka ngati akulamulira anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu awo amasonyeza mphamvu zawo pa iwo. Sizili choncho pakati panu. Koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki wanu. Amene akufuna kukhala woyamba pakati panu ayenera kukhala kapolo wa onse.”—Maliko 10:42-44.

Yesu anauza ophunzirawo kuti atengere chitsanzo chake. Anati: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Yesu anatumikira anthu ena kwa zaka pafupifupi zitatu ndipo anachita zimenezi mpaka kufika pofera anthu onse. Ophunzira ake ayenera kukhala ndi maganizo omwe Khristu anali nawo otumikira ena m’malo mofuna kutumikiridwa komanso kudziona kuti ndi otsika m’malo mofuna udindo wapamwamba.