Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 100

Fanizo la Ndalama 10 za Mina

Fanizo la Ndalama 10 za Mina

LUKA 19:11-28

  • YESU ANANENA FANIZO LA NDALAMA 10 ZA MINA

N’kutheka kuti Yesu anakhalabe ku nyumba kwa Zakeyu pamodzi ndi ophunzira ake ngakhale kuti ulendo wake unali wopita ku Yerusalemu. Ophunzira a Yesu ankakhulupirira kuti “Ufumu wa Mulungu” unali utatsala pang’ono kukhazikitsidwa ndipo Yesu adzakhala Mfumu ya Ufumuwo. (Luka 19:11) Ophunzirawo sanamvetse nkhani ya kukhazikitsidwa kwa Ufumuwu ngati mmene sanamvetsetserenso nkhani ya imfa ya Yesu. Choncho Yesu anawafotokozera fanizo pofuna kuwathandiza kudziwa kuti Ufumuwu unali kudzakhazikitsidwa m’tsogolo.

Iye anati: “Munthu wina wa m’banja lachifumu anapita kudziko lakutali kuti akalandire ufumu ndi kubwerako.” (Luka 19:12) Ulendo umenewu unali wotenga nthawi yaitali. Yesu ndi ‘munthu wa m’banja lachifumu’ amene “anapita kudziko lakutali,” komwe ndi kumwamba ndipo anapita kumeneko kuti Atate wake akamupatse ufumu.

Pofotokoza fanizoli Yesu ananena kuti ‘munthu wa m’banja lachifumuyu’ asanachoke anaitana antchito ake 10 ndipo anapatsa wantchito aliyense ndalama ya siliva ya mina. Anawauzanso kuti: “Muchite malonda mpaka nditabwera.” (Luka 19:13) Ndalama ya siliva ya mina inali ndalama yamphamvu kwambiri chifukwa mina imodzi inali yokwanira malipiro a miyezi itatu a munthu amene ankagwira ntchito yolima.

Chifukwa chakuti pa nthawi ina Yesu anayerekezera ophunzira akewa ndi antchito okolola, ophunzirawo ayenera kuti anazindikira kuti iwowo anali ngati antchito 10 a m’fanizoli. (Mateyu 9:35-38) N’zoona kuti pa nthawiyi Yesu sanapemphe ophunzira ake kuti abweretse zokolola koma zokololazo zinkaphatikizapo ophunzira ena omwe angadzapeze malo mu Ufumu wa Mulungu. Ophunzirawo anagwiritsa ntchito zinthu zamtengo wapatali zimene anali nazo kuti apeze anthu ena oti adzalowe mu Ufumu.

Yesu anafotokozanso mfundo zina kuchokera m’fanizoli. Iye ananena kuti “nzika zinzake zinadana [ndi munthu wa m’banja lachifumu uja] ndipo m’mbuyo muno zinatumiza akazembe kuti apite akanene kuti, ‘Ife sitikufuna kuti munthu uyu akhale mfumu yathu.’” (Luka 19:14) Ophunzirawo ankadziwa kuti Ayuda ankakana Yesu komanso kuti ena ankafuna kumupha. Yesu ataphedwa n’kupita kumwamba, Ayuda anasonyeza kuti ankadana naye pozunza ophunzira ake. Zimene anachitazi zinasonyezeratu kuti sankafuna kuti Yesu akhale Mfumu.—Yohane 19:15, 16; Machitidwe 4:13-18; 5:40.

Pa nthawi imene ‘munthu wa m’banja lachifumu’ uja anapita kukalandira “ufumu” mpaka kubwerako, kodi antchito 10 aja anagwiritsira ntchito bwanji ndalama zimene anapatsidwa? Yesu ananena kuti: “Atabwerera kwawo pambuyo polandira ufumuwo, analamula kuti akapolo ake aja amene anawapatsa ndalama zasiliva abwere kwa iye, kuti awerengerane ndi kuona mmene apindulira pa malonda awo. Woyamba anafika ndipo ananena kuti, ‘Mbuyanga, ndalama yanu ya mina ija inapindula ndalama zina 10 za mina.’ Iye anamuuza kuti, ‘Unagwira ntchito, ndiwe kapolo wabwino! Chifukwa wasonyeza kukhulupirika pa chinthu chaching’ono, ndakupatsa ulamuliro woyang’anira mizinda 10.’ Kenako wachiwiri anafika, ndipo anati, ‘Ambuye ndalama yanu ija ya mina yapindula zinanso zisanu.’ Iye anauzanso ameneyu kuti, ‘Nawenso ukhala woyang’anira mizinda isanu.’”—Luka 19:15-19.

Ngati ophunzirawo akanazindikira kuti iwo anali ngati antchito omwe anagwiritsa ntchito zinthu zawo zamtengo wapatali kuti apange ophunzira ambiri, akanazindikiranso kuti Yesu ankasangalala kwambiri ndi zimene anachitazo. Akanakhulupiriranso kuti Yesu adzawadalitsa chifukwa cha khama lawo. N’zoona kuti ophunzira a Yesu ankakumana ndi zinthu zosiyanasiyana pa moyo wawo komanso aliyense anali ndi luso losiyana ndi la mnzake. Koma Yesu, yemwe ankayembekezera kulandira “ufumu,” adzawadalitsa chifukwa chogwira ntchito yopanga ophunzira mwakhama komanso mokhulupirika.—Mateyu 28:19, 20.

Pomaliza fanizoli, Yesu anafotokoza kusiyana pakati pa zimene antchito 9 aja anachita ndi zimene wantchito wina anachita. Iye anati: “Tsopano panafika [wantchito] wina ndipo ananena kuti, ‘Ambuye, ndalama yanu ya mina ija nayi. Ndinaimanga pansalu ndi kuisunga. Ndinachita zimenezi chifukwa ndinali kukuopani. Inutu ndinu munthu wouma mtima. Mumatenga zimene simunasungitse ndi kukolola zimene simunafese.’ Iye anamuuza kuti, ‘Ndikuweruza mwa zotuluka pakamwa pako, kapolo woipa iwe. Ukuti unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wotenga zimene sindinasungitse ndi kukolola zimene sindinafese? Nangano n’chifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga yasilivayo kwa osunga ndalama? Ukanatero, ine pobwera ndikanaitenga limodzi ndi chiwongoladzanja chake.’ “Atatero anauza anthu amene anaima chapafupi kuti, ‘Mulandeni ndalama ya mina imeneyo ndi kuipereka kwa winayo amene ali ndi ndalama 10.’”—Luka 19:20-24.

Chifukwa chakuti wantchitoyu analephera kuchulukitsa chuma cha mbuye wake yemwe anali Mfumu, zinthu sizinamuyendere bwino. Atumwi ankayembekezera nthawi imene Yesu adzayambe kulamulira mu Ufumu wa Mulungu. Choncho ayenera kuti anamvetsa zimene Yesu ankatanthauza ponena za wantchito mmodzi uja. Iwo anazindikira kuti ngati adzakhale aulesi, sadzapeza malo mu Ufumuwo.

Zimene kenako Yesu ananena ziyenera kuti zinalimbikitsa ophunzira okhulupirikawo kuti azigwira ntchito mwakhama. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, Aliyense amene ali nazo, adzamuwonjezera zochuluka, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.” Ananenanso kuti adani ake, omwe sankafuna kuti iye ‘akhale mfumu yawo’ adzaphedwa. Kenako Yesu anapitiriza ulendo wake wopita ku Yerusalemu.—Luka 19:26-28.