Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 110

Tsiku Lomaliza Limene Yesu Anapezeka pa Kachisi

Tsiku Lomaliza Limene Yesu Anapezeka pa Kachisi

MATEYU 23:25–24:2 MALIKO 12:41–13:2 LUKA 21:1-6

  • YESU ANAPITIRIZA KUDZUDZULA ATSOGOLERI ACHIPEMBEDZO

  • ANANENERATU KUTI KACHISI ADZAWONONGEDWA

  • MKAZI WAMASIYE ANAPONYA TIMAKOBIDI TIWIRI TATING’ONO

Pa nthawi imene Yesu anapezeka pa kachisi komaliza, anapitiriza kuulula zinthu zachinyengo zimene alembi ndi Afarisi ankachita moti anawatchula mosapita m’mbali kuti ndi onyenga. Ponena zimenezi Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo. Iye anati: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumayeretsa kunja kwa kapu ndi mbale, koma mkati mwake mutadzaza zolanda ndi kusadziletsa. Mfarisi wakhungu iwe, yeretsa mkati mwa kapu ndi mbale choyamba, kuti kunja kwakenso kukhale koyera.” (Mateyu 23:25, 26) Ngakhale kuti Afarisi ankayesetsa kwambiri kuti azioneka bwino komanso kutsatira mwambo wodziyeretsa, iwo sankafuna kusintha makhalidwe awo komanso kukonza mitima yawo.

Afarisi anasonyezanso kuti anali achinyengo chifukwa ankayesetsa kumanga ndi kukongoletsa manda a aneneri chonsecho Yesu ananena kuti anali “ana a anthu amene anapha aneneri.” (Mateyu 23:31) Ndipo zimene Yesu ananenazi zinalidi zoona chifukwa anthuwo ankafunanso kumupha.—Yohane 5:18; 7:1, 25.

Kenako Yesu anafotokoza zimene atsogoleri achipembedzowa ankayembekezera kukumana nazo ngati sakanalapa. Iye anati: “Njoka inu, ana a mphiri, mudzathawa bwanji chiweruzo cha Gehena?” (Mateyu 23:33) Anthu ankawotcha zinyalala m’chigwa cha Hinomu chomwe chinali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu ndipo zimene Yesu ananenazi zinathandiza anthuwo kumvetsa kuti alembi ndi Afarisi adzawonongedwa ndipo sadzakhalakonso ngati mmene zinkakhalira ndi zinthu zimene zinkaponyedwa m’chigwachi.

Ophunzira a Yesu ndi amene anadzakhala omuimira monga “aneneri, anthu anzeru ndi aphunzitsi” iye atapita kumwamba. Koma kodi anthu anawachitira zotani ophunzirawa? Pamene Yesu ankalankhula ndi atsogoleri achipembedzowo ananena kuti: “Ena [mwa ophunzira anga] mudzawapha ndi kuwapachika, ndipo ena mudzawakwapula m’masunagoge mwanu ndi kuwazunza mumzinda ndi mzinda, kuti magazi onse olungama okhetsedwa padziko lapansi abwere pa inu, kuyambira magazi a Abele wolungama mpaka magazi a Zekariya . . . amene inu munamupha.” Anawachenjezanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti, Zinthu zonsezi zidzaubwerera m’badwo uwu.” (Mateyu 23:34-36) Izi ndi zimene zinachitika mu 70 C.E. pamene asilikali a Aroma anawononga Yerusalemu ndipo Ayuda ambiri anaphedwa.

Yesu anavutika maganizo kwambiri ataganizira zinthu zochititsa mantha zimenezi. Chifukwa cha chisoni iye ananena kuti: “Yerusalemu, Yerusalemu, wakupha aneneri iwe ndi woponya miyala anthu otumizidwa kwa iwe. Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, muja nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko. Koma anthu inu simunafune zimenezo. Tsopano tamverani! Mulungu wachoka n’kukusiyirani nyumba yanuyi.” (Mateyu 23:37, 38) Anthu amene anamva Yesu akunena zimenezi ayenera kuti anadabwa kuti ankanena za “nyumba” iti. Kodi mwina Yesu ankanena za kachisi wokongola kwambiri wa ku Yerusalemu amene ankaoneka ngati ankatetezedwa ndi Mulungu?

Kenako Yesu ananenanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Kuyambira tsopano simudzandionanso kufikira pamene mudzanene kuti, ‘Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!’” (Mateyu 23:39) Ponena mawu amenewa, Yesu ankanena ulosi wopezeka pa Salimo 118:26 womwe umati: “Wodala ndi Iye wobwera m’dzina la Yehova.Takudalitsani anthu inu potuluka m’nyumba ya Yehova.” Zimenezi zinasonyeza kuti kachisiyo akadzawonongedwa, palibe aliyense amene azidzapitako kuti akapemphere m’dzina la Mulungu.

Tsopano Yesu anapita kumbali ina ya kachisiyo komwe kunali mabokosi oponyamo ndalama. Mabokosi amenewa anali ndi kabowo pamwamba ndipo anthu ankaponya zopereka zawo mmenemo. Yesu ankayang’anitsitsa Ayuda ambiri amene ankapereka ndalama zawo. Anthu olemera ‘ankaponyamo makobidi ambiri.’ Koma kenako Yesu anaona mayi wina wosauka amenenso anali wamasiye akuponya “timakobidi tiwiri tating’ono.” (Maliko 12:41, 42) Yesu anadziwa kuti Mulungu anasangalala kwambiri ndi mphatso ya mayiyo.

Ndiyeno, Yesu anaitana ophunzira ake n’kuwauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa onse amene aponya ndalama moponya zoperekamo.” Yesu anafotokoza chifukwa chake ananena zimenezi. Iye anati: “Zili choncho chifukwa onsewo aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zochirikizira moyo wake.” (Maliko 12:43, 44) Mayiyu ankaganiza komanso kuchita zinthu mosiyana kwambiri ndi atsogoleri achipembedzo.

Tsopano Yesu anachoka pa kachisi ndipo limeneli linali tsiku lomaliza kupezeka pakachisi. Tsikuli linali Nisani 11. Pamene ankachoka, wophunzira wake wina ananena kuti: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikuonekera!” (Maliko 13:1) Miyala ina imene anamangira kachisiyo inali yaikulu kwambiri ndipo inkachititsa kuti kachisiyo azioneka wokongola komanso wolimba kwambiri. Choncho ophunzirawo anadabwa kwambiri Yesu atanena kuti: “Kodi waziona nyumba zapamwamba zimenezi? Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”—Maliko 13:2.

Yesu atanena zimenezi, iye ndi ophunzira ake anawoloka khwawa la Kidironi n’kupita pamalo enaake m’phiri la Maolivi. Pa nthawi imeneyi Yesu anali ndi ophunzira ake 4. Ophunzirawo anali Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane. Ali pamalo amenewa Yesu ndi ophunzira akewo ankatha kuona kachisi wokongola uja yemwe anali m’munsi mwa phirilo.