Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 115

Yesu Anachita Mwambo Womaliza wa Pasika

Yesu Anachita Mwambo Womaliza wa Pasika

MATEYU 26:1-5, 14-19 MALIKO 14:1, 2, 10-16 LUKA 22:1-13

  • YUDASI ISIKARIYOTI ANAPATSIDWA NDALAMA KUTI APEREKE YESU

  • ATUMWI AWIRI ANAKONZA MALO OCHITIRA PASIKA

Yesu anamaliza kuphunzitsa komanso kuyankha mafunso a atumwi ake 4 pamene anali paphiri la Maolivi. Atumwiwo ankafuna kudziwa zimene zidzachitike pa nthawi ya kukhalapo kwake komanso dziko la Satana likadzatsala pang’ono kuwonongedwa.

Yesu anachita zinthu zambiri pa Nisani 11. N’kutheka kuti pa nthawi imene ankabwerera ku Betaniya kuti akagone ndi pamene anauza atumwi ake kuti: “Inu mukudziwa kuti pasika achitika pakangopita masiku awiri, ndipo Mwana wa munthu aperekedwa kuti akapachikidwe.”—Mateyu 26:2.

Zikuoneka kuti tsiku lotsatira lomwe linali Lachitatu, Yesu ndi atumwi ake anakakhala kwaokha. Chadzulo lake lomwe linali Lachiwiri, iye anali atadzudzula atsogoleri achipembedzo komanso kunena poyera zinthu zoipa zimene ankachita. Chifukwa chakuti atsogoleri achipembedzowa ankafuna kumupha, Yesu sanaonekere poyera pa Nisani 12. Anachita zimenezi kuti pasapezeke chinthu chomulepheretsa kukhala nawo pa mwambo wa Pasika limodzi ndi atumwi ake. Mwambowu unachitika madzulo a tsiku lotsatira pamene tsiku la Nisani 14 linkayamba.

Koma mwambo wa Pasika usanachitike ansembe aakulu ndi akulu anasonkhana m’bwalo la mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa. Anthuwa anali atakhumudwa chifukwa Yesu ankanena poyera zinthu zoipa zimene iwowo ankachita. Anagwirizana “zoti agwire Yesu mochenjera ndi kumupha.” Kodi akanachita bwanji zimenezi? Iwo anakambirana kuti: “Tisadzamugwire pa chikondwerero, kuopera kuti anthu angadzachite chipolowe.” (Mateyu 26:4, 5) Ananena zimenezi chifukwa ankadziwa kuti anthu ambiri ankakonda Yesu.

Kenako atsogoleri achipembedzowo analandira mlendo. Iwo anadabwa kwambiri ataona kuti mlendoyo anali Yudasi Isikariyoti yemwe anali mtumwi wa Yesu. Satana ndiye anachititsa Yudasi kukhala ndi maganizo ofuna kupereka Mbuye wake. Ndiyeno Yudasi anawafunsa kuti: “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikamupereka kwa inu?” (Mateyu 26:15) Atsogoleri achipembedzowa anasangalala kwambiri moti “anagwirizana kuti amupatse ndalama zasiliva.” (Luka 22:5) Kodi anamupatsa ndalama zingati? Anagwirizana zomupatsa ndalama 30 za siliva. Pa nthawiyo mtengo wogulira kapolo unali ndalama zokwana masekeli 30. (Ekisodo 21:32) Choncho polonjeza ndalama zimenezi, atsogoleriwo anasonyeza kuti ankadana kwambiri ndi Yesu ndipo ankamuona ngati munthu wamba. Ndiyeno Yudasi anayamba “kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke kwa iwo popanda khamu la anthu pafupi.”—Luka 22:6.

Tsiku la Nisani 13 linayamba Lachitatu madzulo dzuwa litalowa ndipo linali tsiku la 6 komanso tsiku lomaliza kuti Yesu apezeke ku Betaniya. Tsiku lotsatira anamaliza kukonzekera zinthu zofunika pa mwambo wa Pasika. Anayenera kupeza mwana wa nkhosa kuti amuphe ndi kumuotcha wathunthu tsiku la Nisani 14 litayamba. Kodi ndani anakonza chakudyacho ndipo anakadyera kuti? Yesu sanauze aliyense za malo amene akadyere komanso amene akonze chakudyacho. Chifukwa chakuti Yudasi sankadziwa chilichonse pa nkhani imeneyi sakanauza akulu a ansembe chilichonse.

Zikuoneka kuti Lachinayi masana ndi pamene Yesu anatumiza Petulo ndi Yohane kuchokera ku Betaniya. Iye anauza ophunzira akewa kuti: “Pitani mukatikonzere pasika kuti tidye.” Ophunzirawo anafunsa Yesu kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti?” Iye anawauza kuti: “Mukalowa mumzinda, mwamuna wina wosenza mtsuko wa madzi akumana nanu. Mukamutsatire kunyumba imene akalowe. Ndipo mukauze mwininyumba imeneyo kuti, ‘Mphunzitsi akufunsa kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti, mmene ine ndidyeremo pasika pamodzi ndi ophunzira anga?”’ Ndiyeno munthu ameneyo akakusonyezani chipinda chachikulu cham’mwamba chokonzedwa bwino. Mukakonzere mmenemo.”—Luka 22:8-12.

Mosakayikira mwini wake wa nyumbayo analinso wophunzira wa Yesu. Zikuoneka kuti mwini wake wa nyumbayo ankayembekezera kuti Yesu amupempha kuti achitire mwambo wa Pasikawo m’nyumba yake. Atumwi awiri aja atafika ku Yerusalemu, anapeza kuti zinthu zinalidi mmene Yesu anawauzira. Choncho ophunzirawo anaonetsetsa kuti mwana wankhosa komanso chakudya cha pa mwambo wa Pasika chokwana anthu 13, omwe ndi Yesu ndi atumwi ake 12, chakonzedwa.