Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 119

Yesu Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

Yesu Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

YOHANE 14:1-31

  • YESU ANAPITA KUKAKONZA MALO

  • ANALONJEZA OTSATIRA AKE KUTI ADZAWATUMIZIRA MTHANDIZI

  • ATATE NDI WAMKULU KUPOSA YESU

Mwambo wa chakudya chamadzulo utatha, Yesu anakhalabe m’chipinda chapamwamba chija ndi atumwi ake. Iye anawauza kuti: “Mitima yanu isavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupiriraninso ine.”—Yohane 13:36; 14:1.

Yesu analimbikitsa atumwi ake okhulupirika kuti asadzadandaule iye akadzachoka. Anawauza kuti: “M’nyumba ya Atate wanga muli malo ambiri okhalamo. . . . Ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengerani kwathu, kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko.” Koma atumwiwo sanadziwe kuti Yesu ankanena zoti akupita kumwamba. Moti Tomasi anafunsa kuti: “Ambuye, ife sitikudziwa kumene mukupita. Ndiye njira yake tingaidziwe bwanji?”—Yohane 14:2-5.

Yesu anayankha kuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo.” Pamenepa iye ankatanthauza kuti munthu akhoza kulowa m’nyumba yakumwamba ya Atate wake ngati munthuyo atakhulupirira Yesu, kukhulupirira zimene amaphunzitsa komanso kutsatira zimene ankachita pa moyo wake. N’chifukwa chake ananena kuti: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”—Yohane 14:6.

Filipo, yemwe ankamvetsera mwatcheru pamene Yesu ankalankhula, anapempha kuti: “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo tikhutira.” Zikuoneka kuti Filipo ankafuna kuona Mulungu m’masomphenya ngati mmene zinachitikira kwa Mose, Eliya komanso Yesaya. Koma atumwiwo sankafunika kuchita kuona masomphenya chifukwa Yesu ananena kuti: “Anthu inu, ndakhala nanu nthawi yonseyi, koma kodi iwe Filipo sunandidziwebe? Amene waona ine waonanso Atate.” Yesu anali ndi makhalidwe ofanana ndi a Atate wake, choncho anthu amene ankakhala ndi Yesu komanso kuona zimene ankachita anali ngati akuona Atate wake. Komabe Atate ndi wamkulu kwa Mwana chifukwa Yesu ananena kuti: “Zinthu zimene ine ndimanena kwa inu sindilankhula za m’maganizo mwanga.” (Yohane 14:8-10) Pamenepatu atumwiwo ayenera kuti anadziwa kuti zonse zimene Yesu ankaphunzitsa zinkachokera kwa Atate wake.

Atumwi anamuona Yesu akuchita zinthu zodabwitsa komanso anamumva akulalikira uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu. Koma tsopano iye anawauza kuti: “Wokhulupirira ine, nayenso adzachita ntchito zimene ine ndimachita, ndipo adzachita ntchito zazikulu kuposa zimenezi.” (Yohane 14:12) Yesu sankatanthauza kuti atumwi ake adzachita zinthu zazikulu kuposa zimene iye anachita. Koma ankatanthauza kuti adzalalikira kwa nthawi yaitali, m’madera akutali komanso kwa anthu ambiri.

Pamene Yesu ankachoka sikuti atumwi akewo anangowasiya. Iye anawalonjeza kuti: “Ngati mutapempha chilichonse m’dzina langa, ine ndidzachichita.” Anawauzanso kuti: “Ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani mthandizi wina kuti adzakhale nanu kosatha. Mthandizi ameneyo ndi mzimu wa choonadi.” (Yohane 14:14, 16, 17) Anawalonjeza kuti adzawatumizira mzimu woyera womwe udzawathandize ndipo zimenezi zinachitika pa tsiku la mwambo wa Pentekosite.

Kenako Yesu ananena kuti: “Kwatsala kanthawi pang’ono ndipo dziko silidzandionanso. Koma inu mudzandiona, chifukwa ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo.” (Yohane 14:19) Ponena mawu amenewa, Yesu ankatanthauza kuti akadzaukitsidwa, ophunzira ake adzamuona ndi thupi ngati lathuli komanso kuti m’tsogolo adzawaukitsa ndi matupi auzimu kuti akakhale naye kumwamba.

Ndiyeno Yesu ananena mfundo ina yosavuta kumvetsa. Iye anati: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda. Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda ndipo ndidzadzionetsera bwinobwino kwa iye.” Yesu atanena mawu amenewa mtumwi Yudasi yemwe ankadziwikanso kuti Tadeyo anafunsa kuti: “Ambuye, bwanji mukufuna kudzionetsera bwinobwino kwa ife koma osati ku dzikoli?” Yesu anamuyankha kuti: “Ngati munthu amandikonda, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda. . . . Amene sandikonda ine sasunga mawu anga.” (Yohane 14:21-24) Mosiyana ndi otsatira ake, anthu a m’dzikoli saona Yesu ngati njira, choonadi ndi moyo.

Kodi ophunzira akanatha bwanji kukumbukira zinthu zonse zimene Yesu anawaphunzitsa? Yesu anawauza kuti: “Koma mthandizi, amene ndi mzimu woyera, amene Atate wanga adzatumiza m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse ndi kukukumbutsani zonse zimene ndinakuuzani.” Mawu amenewa anali olimbikitsa kwambiri kwa atumwiwa chifukwa anali ataonapo Yesu akuchita zinthu zamphamvu mothandizidwa ndi mzimu woyera. Anawauzanso kuti: “Ndikusiyirani mtendere, ndikupatsani mtendere wanga. . . . Mitima yanu isavutike kapena kuchita mantha.” (Yohane 14:26, 27) Choncho ophunzirawo sankafunika kudandaula chifukwa Yesu anawalonjeza kuti Atate wake adzawatsogolera komanso kuwateteza.

Ophunzirawo anali atatsala pang’ono kuona umboni wosonyeza kuti Mulungu adzawateteza. Yesu ananena kuti: “Wolamulira wa dziko akubwera. Iye alibe mphamvu pa ine.” (Yohane 14:30) Mdyerekezi anakwanitsa kulowa mwa Yudasi n’kuyamba kumulamulira. Koma Mdyerekezi sakanasokoneza maganizo a Yesu kuti achite zinthu zotsutsana ndi Mulungu chifukwa Yesu analibe uchimo. Komanso sakanachititsa kuti Yesu akhalebe m’manda mpaka kalekale. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yesu ananena kuti: “Ndikuchita izi kutsatira lamulo limene Atatewo anandipatsa.” Yesu ankakhulupirira kuti Atate wake adzamuukitsa.—Yohane 14:31.