Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 131

Mfumu Yosalakwa Inavutika Itapachikidwa Pamtengo

Mfumu Yosalakwa Inavutika Itapachikidwa Pamtengo

MATEYU 27:33-44 MALIKO 15:22-32 LUKA 23:32-43 YOHANE 19:17-24

  • ANTHU ANAKHOMERERA YESU PAMTENGO WOZUNZIKIRAPO

  • CHIKWANGWANI CHIMENE ANAKHOMA PAMTENGO WA YESU CHINACHITITSA KUTI ANTHU AMUNYOZE

  • YESU ANALONJEZA MUNTHU WINA KUTI ADZAKHALA NDI MOYO M’PARADAISO PADZIKO LAPANSI

Asilikali achiroma anatenga Yesu komanso anthu awiri omwe anali akuba kuti akawaphe. Anthuwa anapita nawo kumalo otchedwa Gologota kapena kuti Malo a Chibade omwe anali pafupi ndi mzinda. Munthu ankatha kuona zimene zinkachitika pamalowa ngakhale ataima “chapatali.”—Maliko 15:40.

Atafika pamalowa anawavula zovala n’kuwapatsa vinyo wosakaniza ndi mule komanso ndulu. Azimayi omwe ankakhala ku Yerusalemu ndi amene ankakonza vinyoyu ndipo vinyoyu ankathandiza kuti anthu amene akupita kukaphedwawo asamve kupweteka kwambiri. Aroma sankaletsa kuti anthu omwe akukaphedwa amwe vinyoyo. Koma Yesu atalawa vinyoyo anakana kuti amwe. N’chifukwa chiyani anakana? Iye ankafuna kuti pa nthawi yovutayi asasokonezeke maganizo, zomwe zikanamuthandiza kudziwa chilichonse chimene chinkachitika komanso ankafuna kuti akhale wokhulupirika mpaka pamapeto a moyo wake.

Yesu anamugoneka pamtengo womwe ankafuna kum’pachikawo. (Maliko 15:25) Asilikali aja anakhomerera manja ndi mapazi a Yesu ndi misomali zomwe zinachititsa kuti amve kupweteka kwambiri. Pamene ankadzutsa mtengowo, Yesu anamva kupweteka kwambiri chifukwa kulemera kwa thupi lake kunkachititsa kuti mmene anamukhomerera ndi misomali muja muzing’ambika. Koma Yesu sanakalipire asilikaliwo m’malomwake anapemphera kuti: “Atate, akhululukireni, chifukwa sakudziwa chimene akuchita.”—Luka 23:34.

Aroma ankati akapachika munthu, ankaika chikwangwani chomwe ankalembapo mlandu umene munthuyo wapalamula. Pa nthawi imene ankapachika Yesu, Pilato analemba chikwangwani chonena kuti: “Yesu Mnazareti, Mfumu ya Ayuda.” Analemba mawu amenewa mu Chiheberi, Chilatini ndi Chigiriki moti aliyense ankatha kuwerenga. Zimene Pilato analembazi zinasonyeza kuti anadana kwambiri ndi Ayuda omwe anakakamira kuti Yesu aphedwe. Ansembe aakulu anakwiya ndi zimenezi ndipo anamuuza Pilato kuti “Musalembe kuti ‘Mfumu ya Ayuda,’ koma kuti iye ananena kuti, ‘Ndine Mfumu ya Ayuda.’” Koma Pilato sanafunenso kuti achite zimene Ayudawo ankafuna ndipo anawayankha kuti: “Zimene ndalemba, ndalemba.”—Yohane 19:19-22.

Chifukwa chokwiya, ansembewo anabwerezanso umboni wabodza umene ananena poimba Yesu mlandu ku khoti la Sanihedirini. N’chifukwa chake anthu amene ankadutsa pamalopo ankangopukusa mitu yawo n’kumanena monyoza kuti: “Iwe wogwetsa kachisi ndi kum’manga m’masiku atatu, dzipulumutse. Tsika pamtengo wozunzikirapowo.” Nawonso ansembe aakulu ndi alembi ankanena monyoza kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikum’kanika! Tsopanotu Khristu, Mfumu ya Isiraeli, itsike pamtengo wozunzikirapowo, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” (Maliko 15:29-32) Nazonso zigawenga zija zinayamba kunyoza Yesu ngakhale kuti anali wosalakwa. Chigawenga china chinali kudzanja lamanzere ndipo china chinali kumanja kwake.

Asilikali 4 achiroma omwe anali pamalopo anayambanso kumuseka Yesu. Asilikaliwa ayenera kuti ankamwa vinyo wowawasa ndiye pofuna kunyoza Yesu anatenga vinyo wina n’kumuyandikitsa kukamwa kwake, ngakhale kuti sakanatha kulandira kuti amwe. Aroma ataona zimene zinalembedwa pa chikwangwani chomwe anachikhomerera pamwamba pamtengo wa Yesu, anayamba kumunyoza kuti: “Ngati ulidi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” (Luka 23:36, 37) Zimenezitu zinali zomvetsa chisoni kwambiri. Munthu yemwe anasonyeza kuti anali njira, choonadi ndi moyo ananyozedwa komanso anamuchitira zachipongwe. Koma anapirira zonsezi molimba mtima popanda kunyoza asilikali achiroma omwe ankamuchitira zachipongwe, Ayuda omwe ankaonerera zomwe zinkachitikazo komanso zigawenga ziwiri zomwe zinapachikidwa naye limodzi.

Asilikali 4 omwe ankalondera Yesu, anatenga malaya ake akunja n’kuwagawa m’zigawo 4 ndipo anachita mayere kuti agawane. Koma malaya am’kati a Yesu anali apamwamba kwambiri chifukwa “analibe msoko, anali owombedwa kuchokera pamwamba mpaka pansi.” Asilikaliwo anakambirana kuti: “Malaya awa tisawang’ambe, koma tiyeni tichite maere kuti tidziwe amene angatenge malaya amenewa.” Pochita zimenezi anakwaniritsa zimene Malemba amanena kuti: “Iwo anagawana malaya anga akunja pakati pawo, ndipo anachita maere pa malaya anga amkati.”—Yohane 19:23, 24; Salimo 22:18.

Patapita nthawi, mmodzi wa zigawenga zija anazindikira kuti Yesu analidi mfumu. Munthu ameneyu anadzudzula mnzakeyo ndipo ananena kuti: “Kodi iwe suopa Mulungu eti, poona kuti nawenso ukulandira chilango chofanana ndi cha munthu ameneyu? Ifetu m’pake kulangidwa chonchi, pakuti tikulandiriratu zonse zotiyenera malinga ndi zimene tinachita. Koma munthu uyu sanalakwe chilichonse.” Kenako anapempha Yesu kuti: “Mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.”—Luka 23:40-42.

Yesu anamuyankha kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine” osati mu Ufumu koma “m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Zimene Yesu analonjeza munthuyu zinali zosiyana ndi zimene analonjeza atumwi ake. Iye anauza atumwi ake kuti adzakhala pamipando yachifumu pamodzi ndi iyeyo mu Ufumu. (Mateyu 19:28; Luka 22:29, 30) Koma zikuoneka kuti munthuyu, yemwe anali Myuda, anamvapo za Paradaiso wa padziko lapansi yemwe Yehova anapatsa Adamu ndi Hava kuti akhalemo ndi ana awo. Tsopano munthuyu anafa ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi.