Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 136

Anaonekera M’mbali Mwanyanja ya Galileya

Anaonekera M’mbali Mwanyanja ya Galileya

YOHANE 21:1-25

  • YESU ANAONEKERA KU NYANJA YA GALILEYA

  • PETULO KOMANSO ATUMWI ENA ANAPATSIDWA NTCHITO YODYETSA NKHOSA

Tsiku lomaliza limene Yesu anakhala ndi moyo padziko lapansi anauza atumwi kuti: “Ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola kukafika ku Galileya inu musanafikeko.” (Mateyu 26:32; 28:7, 10) Ndiyeno Yesu ataukitsidwa, otsatira ake anayamba ulendo wopita ku Galileya. Koma kodi ankakatani kumeneko?

Atafika, panapita kanthawi ndithu kenako Petulo anauza atumwi anzake 6 kuti: “Ine ndikupita kukapha nsomba.” Ndiyeno atumwiwo anamuuza kuti: “Ifenso tipita nawe.” (Yohane 21:3) Atumwiwo anaswera usiku wonse panyanja koma sanaphe nsomba ngakhale imodzi. Cham’bandakucha, Yesu anaonekera m’mbali mwa nyanja koma atumwiwo sanamuzindikire. Yesu anafunsa kuti: “Ana inu, kodi muli ndi chakudya chilichonse?” Iwo anayankha kuti: “Ayi!” Kenako Yesu anawauza kuti: “Ponyani ukonde kumbali ya kudzanja lamanja kwa ngalawayo ndipo mupeza kenakake.” (Yohane 21:5, 6) Anachitadi zimene anawauzazo ndipo anagwira nsomba zambiri moti ankakanika kukokera ukondewo m’boti lawolo.

Kenako Yohane anauza Petulo kuti: “Ndi Ambuye!” (Yohane 21:7) Atangonena zimenezo, Petulo anavala malaya ake akunja mofulumira chifukwa anawavula pamene ankapha nsombazo. Anadumphira m’madzi n’kuyamba kusambira. Anasambira mtunda wa mamita pafupifupi 90 kenako anafika kumtunda. Atumwi ena aja ankabwera m’mbuyo mwake ali m’boti lomwe linkayenda pang’onopang’ono chifukwa cholemedwa ndi nsomba.

Onse atafika kumtunda anaona “moto wamakala uli potero pali nsomba, ndipo anaonanso mkate.” Kenako Yesu ananena kuti: “Bweretsani kuno zina mwa nsomba zimene mwaphazo.” Petulo anakoka ukonde uja womwe unali ndi nsomba zokwana 153 zikuluzikulu. Yesu anawauza kuti: “Bwerani mudzadye chakudya cham’mawa.” Palibe amene anamufunsa kuti, “Ndinu ndani?” chifukwa anazindikira kuti ndi Yesu. (Yohane 21:10-12) Aka kanali kachitatu kuti Yesu aonekere kwa ophunzira ake ali gulu.

Yesu anapatsa aliyense mkate ndi nsomba kuti adye. Kenako anafunsa kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?” N’kutheka kuti Yesu anafunsa funsoli akuyang’ana nsomba zija. Kodi Petulo ankakonda kwambiri bizinezi yake ya nsomba poyerekeza ndi ntchito imene Yesu ankafuna kumupatsa? Poyankha funso lija, Petulo ananena kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu anamulimbikitsa kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.”—Yohane 21:15.

Kenako Yesu anamufunsanso Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda?” Mwina Petulo anayankha funsoli modabwa kwambiri. Iye anayankha molimba mtima kuti: “Inde Ambuye, mukudziwa inunso kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu anamuuzanso zimene anamuuza poyamba zija kuti: “Weta ana a nkhosa anga.”—Yohane 21:16.

Koma Yesu anafunsanso Petulo kachitatu kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda kwambiri?” Mwina Petulo anayamba kuganiza kuti Yesu sakumukhulupirira ndipo anayankha mwamphamvu kuti: “Ambuye, inu mumadziwa zonse, mukudziwanso bwino kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu ananenanso ntchito imene Petulo ankayenera kuchita. Iye anati: “Dyetsa ana a nkhosa anga.” (Yohane 21:17) Zimenezi zikusonyeza kuti amene akutsogolera m’gulu la Yehova ayenera kusamalira anthu amene Yehova anawakokera m’khola lake.

Yesu anamangidwa komanso kuphedwa chifukwa chogwira ntchito imene Mulungu anamupatsa. Zimene kenako Yesu ananena zinasonyeza kuti Petulo adzakumananso ndi zomwezo. Iye ananena kuti: “Pamene unali mnyamata, unali kuvala wekha ndi kupita kumene unali kufuna. Koma ukadzakalamba, udzatambasula manja ako ndipo munthu wina adzakuveka, ndi kukunyamula kupita nawe kumene iwe sukufuna.” Koma anamulimbikitsa kuti: “Pitiriza kunditsatira.”—Yohane 21:18, 19.

Atanena zimenezi, Petulo anayang’ana mtumwi Yohane n’kufunsa Yesu kuti: “Ambuye, nanga uyu adzachita chiyani?” Pofunsa funso limeneli, Petulo ankafuna kudziwa tsogolo la mtumwi yemwe Yesu ankamukonda kwambiri. Koma Yesu anayankha kuti: “Ngati ine nditafuna kuti akhalebe kufikira ndikadzabwera, kodi iwe uli nazo kanthu?” (Yohane 21:21-23) Yesu ankatanthauza kuti Petulo ankafunika kungotsatira Yesuyo, osaganizira kwambiri zimene ena akuchita. Komabe zimene ananenazi zinasonyezanso kuti Yohane adzakhala ndi moyo wautali poyerekeza ndi atumwi enawo ndipo adzaona Yesu atayamba kulamulira mu Ufumu wake m’masomphenya.

Pali zinthu zambiri zimene Yesu anachita ndipo sizikanakwana kuzilemba m’mipukutu.