Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 139

Yesu Adzabweretsa Paradaiso Kenako Adzamaliza Kugwira Ntchito Imene Anapatsidwa

Yesu Adzabweretsa Paradaiso Kenako Adzamaliza Kugwira Ntchito Imene Anapatsidwa

1 AKORINTO 15:24-28

  • ZIMENE ZIDZACHITIKIRE NKHOSA KOMANSO MBUZI

  • ANTHU AMBIRI ADZASANGALALA M’PARADAISO PADZIKO LAPANSI

  • YESU ADZASONYEZA KUTI NDI NJIRA, CHOONADI NDI MOYO

Satana ankafunitsitsa kuti Yesu asachite zimene anabwerera padziko lapansi. Iye anayamba kuyesa Yesu atangobatizidwa kumene ndipo nthawi imeneyi, Yesu anali asanayambe utumiki wake. Ndipotu Mdyerekezi anayesa Yesu mobwerezabwereza. Patapita nthawi Yesu ananena kuti: “Wolamulira wa dziko akubwera. Iye alibe mphamvu pa ine.”—Yohane 14:30.

Mtumwi Yohane anaona masomphenya omwe anasonyeza zimene zidzachitikire ‘chinjokacho, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.’ Yohane anaona mdani wankhanzayu, yemwe wakhala akuvutitsa anthu kwa nthawi yaitali, akuponyedwa pansi kuchoka kumwamba, “ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:9, 12) Akhristu ali ndi zifukwa zimene zimawachititsa kukhulupirira kuti akukhala mu “kanthawi kochepa” komanso kuti posachedwapa ‘chinjokacho, njoka yakale ija’ chidzaponyedwa kuphompho komwe sichidzatha kuchita kalikonse kwa zaka 1,000. Pa nthawi imeneyi Yesu adzakhala akulamulira mu Ufumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 20:1, 2.

Kodi zinthu zidzakhala bwanji padziko lapansi pa nthawi imeneyi? Yesu anayankha funso limeneli. Pofotokoza fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Yesu anasonyeza zomwe zidzachitikire anthu olungama omwe ali ngati nkhosa, amene amagwirizana komanso kuchitira zabwino abale ake a Yesu. Anasonyezanso zimene zidzachitikire anthu omwe ali ngati mbuzi. Iye anati: “Iwowa [anthu omwe ali ngati mbuzi] adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu, koma olungama [anthu omwe ali ngati nkhosa] ku moyo wosatha.”—Mateyu 25:46.

Mawu amenewa akutithandiza kumvetsa zimene Yesu anauza chigawenga chomwe chinapachikidwa pambali pake chija. Yesu sanalonjeze munthu ameneyu madalitso amene analonjeza atumwi ake okhulupirika, omwe ndi kukalamulira pamodzi naye mu Ufumu wakumwamba. M’malomwake Yesu analonjeza munthu amene anasonyeza kulapayu kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Munthuyu anakhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo m’Paradaiso, omwe ndi malo okongola kwambiri. Apatu n’zoonekeratu kuti anthu amene akuchita zinthu ngati nkhosa masiku ano, omwe akupita “ku moyo wosatha,” adzakhalanso m’Paradaiso ameneyu.

Zimenezi zikugwirizana ndi zimene mtumwi Yohane ananena pofotokoza mmene moyo udzakhalire padziko lapansi. Iye anati: “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Munthu amene anali chigawenga uja adzafunika kuukitsidwa kuti adzasangalale ndi moyo m’Paradaiso koma padzakhalanso anthu ambiri amene adzaukitsidwe. Tikutero chifukwa Yesu ananena kuti: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka. Amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo. Amene anali kuchita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.”—Yohane 5:28, 29.

Nanga atumwi okhulupirika komanso anthu ena ochepa omwe adzakhale kumwamba ndi Yesu azidzatani? Baibulo limanena kuti: “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.” (Chivumbulutso 20:6) Anthu amenewa, omwe adzalamulire ndi Khristu, anakhalapo anthu [amuna ndi akazi] padziko lapansi. Choncho adzakhala olamulira omvetsa zinthu komanso achifundo.—Chivumbulutso 5:10.

Yesu adzagwiritsa ntchito dipo limene anapereka pochotsa uchimo umene anthu anatengera kwa Adamu ndi Hava. Iye pamodzi ndi anthu amene adzalamulire naye adzathandiza anthu onse okhulupirika kuti akhale opanda uchimo. Kenako anthu adzasangalala ndi moyo mmene Mulungu ankafunira poyamba pamene anauza Adamu ndi Hava kuti adzaze dziko lapansi. Ndipo imfa, yomwe inabwera chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu, siidzakhalaponso.

Zimenezi zikadzachitika ndiye kuti Yesu adzakhala atamaliza kugwira ntchito imene Yehova anamupatsa. Zaka 1,000 zikadzatha, Yesu adzapereka Ufumu komanso banja la anthu angwiro kwa Atate wake. Yesu akadzachita zimenezi adzasonyeza kuti ndi wodzichepetsa kwambiri. Pofotokoza za khalidwe la kudzichepetsa lomwe Yesu adzasonyezeli, mtumwi Paulo analemba kuti: “Zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwanayonso adzadziika pansi pa amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.”—1 Akorinto 15:28.

Kunena zoona Yesu ali ndi udindo waukulu pokwaniritsa zolinga za Mulungu. Zolinga zimenezi zikamadzakwaniritsidwa, Yesu adzapitirizabe kukhala “njira, choonadi ndi moyo.”—Yohane 14:6.