Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 70

Yesu Anachiritsa Munthu Amene Anabadwa Wosaona

Yesu Anachiritsa Munthu Amene Anabadwa Wosaona

YOHANE 9:1-18

  • ANACHIRITSA WOPEMPHAPEMPHA AMENE ANABADWA WOSAONA

Yesu akuyenda ndi ophunzira ake mumzinda wa Yerusalemu pa tsiku la Sabata, anaona munthu wina wopemphapempha yemwe anabadwa ali wakhungu. Ndiyeno ophunzirawo anafunsa Yesu kuti: “Rabi, anachimwa ndani kuti munthu uyu abadwe wakhungu chonchi? Ndi iyeyu kapena makolo ake?”—Yohane 9:2.

Ophunzirawo ankadziwa kuti munthu alibe mzimu umene umakhala ndi moyo kwinakwake munthuyo asanabadwe. Koma mwina ankadzifunsa ngati n’zotheka kuti munthu achimwe adakali m’mimba mwa mayi ake. Yesu anawayankha kuti: “Munthuyu kapena makolo ake, onsewa palibe amene anachimwa. Izi zinachitika kuti ntchito za Mulungu zionekere kudzera mwa iye.” (Yohane 9:3) Choncho munthuyo sanakhale wakhungu chifukwa chakuti iyeyo kapena makolo ake analakwitsa chinachake. Koma chifukwa chakuti Adamu anachimwa anthu onse amabadwa ali ochimwa ndipo amathanso kubadwa ndi zilema zosiyanasiyana ngati kukhala wakhungu. Chifukwa chakuti munthuyo anabadwa wakhungu, Yesu anapeza mpata woonetsa ntchito za Mulungu ngati mmene anachitira m’mbuyomo pamene anachiritsa anthu odwala.

Yesu anafotokoza kuti ntchito zimenezi ziyenera kuchitika mwamsanga. Iye anati: “Tiyenera kugwira ntchito za iye amene anandituma ine kudakali masana. Usiku ukubwera pamene munthu sangathe kugwira ntchito. Pamene ine ndili m’dziko, ndine kuwala kwa dzikoli.” (Yohane 9:4, 5) Yesu ananena mawu amenewa chifukwa ankadziwa kuti anali atatsala pang’ono kuphedwa. Imfayo ikanakhala ngati waponyedwa mumdima chifukwa sakanatha kuchita chilichonse ali m’manda. Koma pa nthawi imene anali ndi moyo, Yesu anali kuwala kwa dziko.

Koma kodi Yesu anamuthandiza bwanji munthu wakhungu uja? Yesu analavula malovu pansi ndipo anawasakaniza ndi dothi. Ndiyeno anatenga matopewo n’kuwapaka m’maso mwa munthuyo, kenako anamuuza kuti: “Pita ukasambe m’dziwe la Siloamu.” (Yohane 9:7) Munthuyo atachita zimene Yesu anamuuza anayamba kuona. Tangoganizirani mmene munthuyo anasangalalira atayamba kuona.

Anthu amene ankakhala naye pafupi komanso anthu ena anadabwa kwambiri ataona kuti munthuyu wayamba kuona. Iwo anayamba kufunsana kuti: “Si uyu kodi amene anali kukhala pansi n’kumapemphapempha uja?” Ena ankayankha kuti: “Ndi yemweyu.” Koma ena sankakhulupirira ndipo ankanena kuti: “Iyayi, wangofanana naye.” Koma mwiniwake anati: “Ndine amene.”—Yohane 9:8, 9.

Anthuwo anamufunsa kuti: “Nanga maso akowa atseguka bwanji?” Iye anawayankha kuti: “Munthu wina dzina lake Yesu anakanda thope ndi kupaka m’maso mwangamu, ndiyeno anandiuza kuti, ‘Pita ku Siloamu ukasambe.’ Ndinapitadi kukasamba ndipo ndayamba kuona.” Pamenepo anthuwo anamufunsa kuti: “Ali kuti munthu ameneyo?” Iye anati: “Sindikudziwa.”—Yohane 9:10-12.

Kenako anthuwo anapita ndi munthu uja kwa Afarisi chifukwa nawonso ankafuna kudziwa zimene zinachitika kuti ayambe kuona. Munthuyo anauza Afarisiwo kuti: “Iye anapaka thope m’maso mwanga, ndiyeno ndinapita kukasamba, basi kenako ndayamba kuona.” Afarisi ankayenera kusangalala kuti munthu yemwe poyamba anali wosaona uja wayamba kuona. Koma m’malo mosangalala iwo anayamba kunyoza Yesu kuti: “Munthu ameneyu si wochokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata.” Koma ena ananena kuti: “Koma munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro zoterezi?” (Yohane 9:15, 16) Choncho anthuwo anagawanika.

Chifukwa cha kusiyana maganizoko, anthuwo anafunsa munthu amene anayamba kuona uja kuti: “Nanga iwe ukuti bwanji za munthu ameneyu, popeza kuti wakutsegula maso?” Munthuyo sanakayikire Yesu ndipo anayankha kuti: “Ndi mneneri.”—Yohane 9:17.

Koma Ayudawo anakana kuvomereza zimene munthuyo ananena. Iwo ankaganiza kuti Yesu anachita kupangana ndi munthu yemwe anali wakhunguyo kuti aziuza anthu zoti wayamba kuona chifukwa chakuti Yesu wamuchiritsa. Pamapeto pake iwo anaona kuti njira yabwino yothetsera nkhaniyo inali kukafunsa makolo ake a munthuyo ngati mwana wawoyo analidi wosaona.