Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 71

Afarisi Anatsutsana ndi Munthu Amene Anali Wakhungu

Afarisi Anatsutsana ndi Munthu Amene Anali Wakhungu

YOHANE 9:19-41

  • AFARISI ANAKUMANA NDI MUNTHU AMENE POYAMBA ANALI WAKHUNGU

  • ATSOGOLERI ACHIPEMBEDZO ANALI “AKHUNGU”

Afarisi anaitana makolo a munthu amene poyamba anali wakhungu chifukwa chakuti sanakhulupirire kuti Yesu anachiritsadi munthuyo. Makolo ake a munthuyo ankadziwa kuti nkhaniyi ikanachititsa kuti ‘achotsedwe musunagoge.’ (Yohane 9:22) Ndipo ngati akanachotsedwa musunagoge ndiye kuti sakanakhalanso ndi mwayi wocheza komanso kuchita malonda ndi Ayuda anzawo.

Afirisiwo anafunsa makolo a munthu uja mafunso awiri kuti: “Kodi uyu ndi mwana wanu amene mukuti anabadwa wakhungu? Nanga zatheka bwanji kuti tsopano aziona?” Makolowo anayankha kuti: “Tikudziwa kuti uyu ndi mwana wathu ndi kuti anabadwa wakhungu. Koma za mmene wayambira kuona tsopano, ndi amene wamutsegula maso, zimenezo sitikudziwapo kanthu ayi.” Ngakhale kuti munthuyo anauza makolo ake zimene zinachitika, makolo akewo anayankha mochenjera kwambiri. Iwo anati: “Mufunseni mwiniwakeyu. Ndi wamkulu, afotokoze yekha.”—Yohane 9:19-21.

Zitatero Afarisiwo anaitananso munthu uja n’kumupanikiza ndi mafunso komanso anamuuza kuti Yesu amupeza ndi milandu. Ndiyeno anauza munthuyo kuti: “Lemekeza Mulungu, ife tikudziwa kuti munthu ameneyu ndi wochimwa.” Munthuyo atadziwa zimene Afarisiwo ankafuna kuchita, anawayankha kuti: “Zakuti iye ndi wochimwa, ine sindikudziwa.” Ananenanso kuti: “Chimodzi chokha chimene ine ndikudziwa n’chakuti, poyamba ndinali wakhungu, koma tsopano ndikuona.”—Yohane 9:24, 25.

Chifukwa chakuti Afarisiwo sanafune kuti nkhaniyi ithere pomwepo anamufunsanso kuti: “Anakuchita chiyani? Watsegula bwanji maso ako?” Munthuyo analimba mtima n’kuwayankha kuti: “Ndakuuzani kale, koma inu simunamvetsere. Nanga n’chifukwa chiyani mukufuna kumvanso? Kapena inunso mukufuna kukhala ophunzira ake?” Zimenezi zinawakwiyitsa kwambiri Afarisiwo ndipo ananena kuti: “Iweyo ndiye wophunzira wa munthu amene uja, ifetu ndife ophunzira a Mose. Tikudziwa kuti Mulungu analankhula ndi Mose, koma za munthu uyu, sitikudziwa kuti iye akuchokera kuti.”—Yohane 9:26-29.

Munthuyo anadabwa kwambiri ndi zimene Afarisiwo ananena ndipo anati: “Izi n’zodabwitsa ndithu, simukudziwa kumene wachokera, chikhalirecho wanditsegula maso.” Kenako munthuyo ananena mfundo imene aliyense ankaidziwa bwino yofotokoza za munthu amene Mulungu amamvetsera mapemphero ake komanso amene amamuvomereza. Iye anati: “Tikudziwa kuti Mulungu samvetsera ochimwa, koma ngati munthu ali woopa Mulungu ndipo amachita chifuniro chake, ameneyo amamumvetsera. Sizinamveke n’kale lonse kuti wina watsegula maso a munthu amene anabadwa wakhungu.” Chifukwa cha mfundo imeneyi munthuyo anamaliza n’kunena kuti: “Munthu uyu akanapanda kuchokera kwa Mulungu, sakanatha kuchita kanthu.”—Yohane 9:30-33.

Afarisiwo ataona kuti alephera kutsutsa zimene munthuyo ananena, anayamba kumunyoza kuti: “Wobadwira mu uchimo wokhawokha iwe, ukufuna kuphunzitsa ife kodi?” Kenako anamuchotsa musunagoge.—Yohane 9:34.

Yesu anamva zimene zinachitikazo ndipo atakumananso ndi munthuyo anamufunsa kuti: “Kodi ukukhulupirira mwa Mwana wa munthu?” Munthuyo anayankha kuti: “Kodi mwana wa munthuyo ndani ndimudziwe bambo, kuti ndikhulupirire mwa iye?” Yesu anamutsimikizira munthuyo kuti: “Wamuona kale, ndi amene akulankhula nawe panopa.”—Yohane 9:35-37.

Kenako munthuyo anati: “Ndakhulupirira mwa iye Ambuye.” Munthuyo anagwadira Yesu pofuna kusonyeza kuti ankamulemekeza komanso kumukhulupirira. Ndiyeno Yesu ananena kuti: “Ndinabwera m’dziko lino kudzapereka chiweruzo ichi: Osaona ayambe kuona, ndipo oona akhale akhungu.”—Yohane 9:38, 39.

Pamene Yesu ankalankhula mawu amenewa, Afarisi anali pomwepo ndipo ankadziona kuti sanali akhungu. Poganizira kuti anali ndi udindo wotsogolera anthu pa zinthu zauzimu, kodi Afarisiwo anamva bwanji ndi zimene Yesu ananenazi? Pofuna kudziikira kumbuyo, anafunsa Yesu kuti: “Kodi ifenso tingakhale akhungu?” Yesu anawayankha kuti: “Mukanakhala akhungu, simukanakhala ndi tchimo. Koma popeza mukunena kuti, ‘Tikuona.’ Tchimo lanu likhalabe chikhalire.” (Yohane 9:40, 41) Akanakhala kuti Afarisiwa sanali ndi udindo wophunzitsa Ayuda, zikanakhala zomveka kukana zoti Yesu ndi Mesiya. Koma chifukwa chakuti ankadziwa Chilamulo, zimene anachita pokana Yesu linali tchimo lalikulu.