Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi mungayankhe kuti ndi . . .

  • chinachake chimene chimakhala mu mtima mwa munthu aliyense?

  • mawu ongophiphiritsira?

  • boma limene lili kumwamba?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.”—Danieli 2:44, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Ife tapatsidwa mwana wamwamuna, ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.”—Yesaya 9:6.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?

Inde tingazikhulupirire pa zifukwa ziwiri izi:

  • Yesu anasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere komanso kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Yesu anasonyeza mmene Mulungu adzayankhire pemphero limeneli.

    Pamene Yesu anali padziko lapansi anadyetsa anthu anjala, kuchiritsa odwala ndiponso kuukitsa akufa. (Mateyu 15:29-38; Yohane 11:38-44) Zimene anachitazi zinasonyeza zimene Ufumuwo udzachitire anthu Yesu akadzayamba kulamulira dziko lapansili monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 11:15.

  • Zimene zikuchitika m’dzikoli zikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Yesu ananeneratu kuti Ufumu wa Mulungu usanabweretse mtendere padziko lapansi, m’dzikoli mudzakhala nkhondo, njala komanso zivomezi.—Mateyu 24:3, 7.

    Zimenezi ndi zomwe zikuchitika masiku ano. Choncho sitikukayikira kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uthetsa mavuto onsewa.

GANIZIRANI MFUNDO IYI

Kodi moyo udzakhala wotani mu Ufumu wa Mulungu?

Baibulo limayankha funso limeneli pa SALIMO 37:29 ndi pa YESAYA 65:21-23.