Onani zimene zilipo

Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani?

Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani?

Kodi mungayankhe kuti ndi  . . .

  • cinacake cimene cili mumtima wanu?

  • mau okuluwika?

  • boma lakumwamba?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzaonongedwa ku nthawi zonse.”—Danieli 2:44, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Ife tapatsidwa mwana wamwamuna, ndipo paphewa pake padzakhala ulamulilo [kapena kuti boma].”—Yesaya 9:6.

UBWINO WOKHULUPILILA ZIMENEZI

  •  Mudzasangalala ndi boma lolungama limene lidzakupindulitsani inuyo panokha.—Yesaya 48:17, 18.

  • M’dziko latsopano limene likubwelalo, mudzakhala ndi thanzi labwino ndiponso mudzakhala wacimwemwe.—Chivumbulutso 21:3, 4.

KODI TINGAKHULUPILILEDI ZIMENE BAIBULO LIMANENA?

Inde, pa zifukwa ziŵili izi:

  • Yesu anaonetsa zimene Ufumu wa Mulungu udzacita. Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele ndi kuti cifunilo ca Mulungu cicitike padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Yesu anaonetsa mmene pemphelo limeneli lidzayankhidwila.

    Pamene anali padziko lapansi, Yesu anadyetsa anjala, anacilitsa odwala, ndi kuukitsa akufa. (Mateyu 15:29-38; Yohane 11:38-44) Popeza kuti Yesu ndiye Wolamulila mu Ufumu wa Mulungu, iye anasonyezelatu zimene Ufumuwo udzacitila nzika zake.—Chivumbulutso 11:15.

  • Zimene zikucitika padziko lapansi ndi umboni wakuti Ufumu wa Mulungu udzabwela posacedwapa. Yesu ananenelatu kuti padziko lapansi padzakhala nkhondo, njala, ndi zivomezi, Ufumu wa Mulungu ukatsala pang’ono kubweletsa mtendele.—Mateyu 24:3, 7.

    Zinthu zimenezi tikuziona masiku ano. Conco tili ndi cikhulupililo kuti Ufumu wa Mulungu udzacotsa mavuto onsewa posacedwapa.

GANIZILANI FUNSO ILI

Kodi moyo udzakhala wotani mu Ufumu wa Mulungu?

Baibulo limayankha funso limeneli pa SALIMO 37:29 ndi pa YESAYA 65:21-23.