Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mulungu Ali Nafe Colinga Canji?

Kodi Mulungu Ali Nafe Colinga Canji?

MUKAŴELENGA nyuzipepala, kutamba T.V., kapena kumvela wailesi, mumaona ndi kumva nkhani zambili za upandu, nkhondo, ndi ucigaŵenga. Mwina inunso ndinu wodwala kapena ndinu wacisoni cifukwa cakuti munthu wina amene munali kukonda anamwalila.

Koma dzifunseni kuti:

  • Kodi n’zimene Mulungu afuna kuti nizivutika conco, pamodzi ndi abanja langa?

  • Ningapeze kuti thandizo pa mavuto anga?

  • Kodi mtendele wazoona udzabweladi?

Baibulo imapeleka mayankho okhutilitsa pa mafunso amenewa.

BAIBULO IMAPHUNZITSA KUTI MULUNGU ADZACITA ZINTHU ZABWINO KWAMBILI PA DZIKO LAPANSI.

  • Anthu sadzamvelanso zopweteka, sadzakalamba, kapena kufa. —Chivumbulutso 21:4

  • ‘Munthu wolemala adzakwela phili ngati mmene imacitila mbawala yamphongo.’—Yesaya 35:6

  • “Maso a anthu akhungu adzatsegulidwa.” —Yesaya 35:5

  • Akufa adzaukitsidwa. —Yohane 5:28, 29

  • Palibe amene adzadwala. —Yesaya 33:24

  • Aliyense pa dziko lapansi adzakhala ndi cakudya ca mwana alilenji.—Salimo 72:16

ZIMENE BAIBULO IMAPHUNZITSA N’ZOTHANDIZA

Mwina mungaganize kuti zimene mwaŵelenga pa masamba oyambilila m’buku ino n’zosatheka. Koma Mulungu analonjeza kuti, lomba apa, adzasintha zinthu pa dziko lapansi. Ndipo Baibulo imafotokoza mmene Mulungu adzacitila zimenezo.

Siikamba cabe za kutsogolo. Imatiuzanso zimene ife tifunikila kucita kuti tikhale ndi umoyo wokondweletsa ngakhale pali pano. Imani pang’ono ndi kuganizila zinthu zimene zimakudetsani nkhawa. Ingakhale nkhani ya ndalama, banja, thanzi, kapena imfa ya munthu amene munali kukonda. Koma Baibulo ingakuthandizeni kudziŵa mocitila ndi nkhawa zimenezi. Ndipo ingakukhazikeni mtima pansi poyankha mafunso monga akuti:

Kuŵelenga kwanu buku ino kuonetsa kuti mumafuna kudziŵa zimene Baibulo imaphunzitsa. Ndipo idzakuthandizani kudziŵa zambili. Muli ndime ndi mafunso ake, zimene zidzakuthandizani kumvetsetsa bwino zimene Baibulo imaphunzitsa. Anthu mamiliyoni ambili aikonda njila imeneyi yophunzilila Baibulo ndi Mboni za Yehova. Tili ndi cikhulupililo kuti inunso mudzaikonda. Tingoti Mulungu akudalitseni pamene muyamba kudziŵa zimene Baibulo ingakuphunzitseni.