Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 4

Kodi Yesu Khiristu N’ndani?

Kodi Yesu Khiristu N’ndani?

1, 2. (a) Kodi kudziŵa cabe dzina la munthu wochuka ndiye kuti mum’dziwa bwino? Fotokozani. (b) Kodi anthu amati Yesu n’ndani?

PA DZIKO LAPANSI, pali anthu ochuka ambili-mbili. Mosapeneka, inunso mudziŵako munthu wina wochuka, ngakhalenso dzina lake. Koma kungodziŵa cabe dzina lake sindiye kuti mumam’dziŵa bwino munthuyo, umoyo wake ndi zimene amakonda.

2 Ngakhale kuti Yesu Khiristu anali pa dziko lapansi zaka ngati 2,000 zapitazo, muyenela kuti munamvapo za iye. Koma anthu ambili sadziŵa kuti Yesu anali munthu wabwanji. Ena amati anali munthu wabwino, ena amati anali mneneli, ndipo ena amakhulupilila kuti ni Mulungu. Nanga inu mudziŵapo ciani?—Onani Zakumapeto 12.

3. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti mudziŵe Yehova Mulungu ndi Yesu Khiristu?

3 Mufunika kudziŵa zoona pa Yesu. Cifukwa ciani? Baibulo imati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khiristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Inde, kuti mudzapeze moyo wosatha m’paradaiso pa dziko lapansi, mufunika kudziŵa bwino Yehova ndi Yesu. (Yohane 14:6) Kum’dziŵa bwino Yesu kudzakuthandizani, cifukwa iye anatipatsa citsanzo ca mokhalila bwino ndi anthu anzathu. (Yohane 13:34, 35) M’Nkhani 1, tinaphunzila kuti Mulungu n’ndani kweni-kweni. M’nkhani ino, Baibulo idzatiphunzitsa kudziŵa bwino za Yesu.

IFE TAPEZA MESIYA!

4. Kodi maina akuti “Mesiya” ndi “Khiristu” atanthauza ciani?

4 Zaka zambili Yesu asanabadwe, Yehova analonjeza m’Baibulo kuti adzatumiza Mesiya, kapena kuti Khiristu. Liu lakuti “Mesiya” n’la Ciheberi, ndipo lakuti “Khiristu” n’la Cigiriki. Mau amenewa ni maina audindo, ndipo atanthauza kuti Mulungu adzasankha Mesiya amene adzapatsa udindo wapadela. Mesiya ameneyo anali kudzakwanilitsa malonjezo onse a Mulungu. Yesu angakuthandizeni ngakhale pa nthawi ino. Koma Yesu asanabadwe, anthu ambili anali kudzifunsa kuti, ‘Kodi n’ndani amene adzakhala Mesiya?’

5. Kodi ophunzila a Yesu anakhulupilila kuti iye anali Mesiya?

5 Ophunzila a Yesu sanakaikile kuti iye anali Mesiya wolonjezedwa. (Yohane 1:41) Mwacitsanzo, Simoni Petulo anauza Yesu kuti: “Ndinu Khiristu.” (Mateyu 16:16) Nanga ife tingatsimikize bwanji kuti Yesu alidi Mesiya?

6. Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu oona mtima kudziŵa Mesiya?

6 Zaka zambili Yesu asanabadwe, aneneli a Mulungu analembelatu zimene zidzathandiza anthu kumudziŵa Mesiya. Kodi zimenezo zinathandiza bwanji? Tinene kuti mwauzidwa kuyenda ku siteshoni ya basi kuti mulandile mlendo amene simunamuonepo. Ngati wina anakulongosolelani bwino-bwino maonekedwe a mlendoyo, mudzam’dziŵa mosavuta. N’zimene Yehova anacita. Kupitila mwa aneneli, anafotokoza bwino-bwino zimene Mesiya adzacita, ndi zimene zidzacitika kwa iye. Maulosi onse amenewo anakwanilitsika. N’zimene zimathandiza anthu oona mtima kutsimikiza kuti Yesu alidi Mesiya.

7. Ni maulosi aŵili ati amene amatsimikizila kuti Yesu ni Mesiya?

7 Lomba tiyeni tikambilane maulosi aŵili. Ulosi woyamba ukamba za kubadwa kwake. Zaka 700 Yesu asanabadwe, Mika analosela kuti Mesiya adzabadwila mu mzinda ung’ono wa Betelehemu. (Mika 5:2) Ndipo Yesu anabadwiladi mu mzinda umenewo. (Mateyu 2:1, 3-9) Ulosi waciŵili ni wa Danieli. Iye analosela kuti Mesiya adzaonekela m’caka ca 29 C.E. (Danieli 9:25) Tangokambapo maulosi aŵili cabe. Koma pali maulosi ambili-mbili otsimikizila kuti Yesu ndiye Mesiya amene analonjezedwa.—Onani Zakumapeto 13.

Yesu anakhala Mesiya, kapena kuti Khiristu pa ubatizo wake

8, 9. N’ciani cinacitika pa ubatizo wa Yesu cimene cimatsimikizila kuti iye analidi Mesiya?

8 Yehova anaonetsa poyela kuti Yesu ndiye Mesiya. Analonjeza Yohane M’batizi kuti adzam’patsa cizindikilo com’thandiza kuzindikila Mesiya. Yohane anaona cizindikilo cimeneco pamene Yesu anayenda kwa iye kuti akam’batize mu mtsinje wa Yorodano m’caka ca 29 C.E. Baibulo imatiuza zimene zinacitika. Imati: “Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzamutela. Panamvekanso mau ocokela kumwamba onena kuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.’” (Mateyu 3:16, 17) Yohane ataona cizindikilo cimeneco ndi kumvela mau, anadziŵa kuti Yesu ndiye Mesiya. (Yohane 1:32-34) Tsiku limenelo, pamene Yehova anatumiza mzimu wake pa Yesu, m’pamene Yesu anakhala Mesiya. Ni amene Mulungu anamusankha kukhala Mtsogoleli ndi Mfumu.—Yesaya 55:4.

9 Zonse izi, maulosi a m’Baibulo, mau a Yehova, ndi cizindikilo cimene Mulungu anapeleka pa ubatizo wa Yesu, zimatsimikizila kuti Yesu ni Mesiya. Koma kodi Yesu anacokela kuti, nanga anali munthu wabwanji? Tiyeni tione zimene Baibulo imakamba.

KODI YESU ANACOKELA KUTI?

10. Kodi Baibulo imatiuza ciani za umoyo wa Yesu asanabwele pa dziko lapansi?

10 Baibulo imatidziŵitsa kuti Yesu akalibe kubwela pa dziko lapansi, anali kumwamba kwa zaka zambili-mbili. Mwacitsanzo, Mika anakamba kuti Mesiya analipo “kuyambila nthawi zoyambilila.” (Mika 5:2) Ngakhale Yesu mwini wake, anakamba mobweleza-bweleza kuti iye anali kumwamba asanabwele kudzabadwa monga munthu. (Ŵelengani Yohane 3:13; 6:38, 62; 17:4, 5.) Ngakhale asanabwele pa dziko lapansi, Yesu anali kale paunansi wapadela ndi Yehova.

11. N’cifukwa ciani Yesu ali wapadela kwambili kwa Yehova?

11 Yesu ni mwana wa Yehova wapamtima. Cifukwa ciani? Cifukwa ni amene Mulungu anayambilila kulenga asanalenge cina ciliconse. Mwa ici, Yesu amachedwa “woyamba kubadwa wa cilengedwe conse.” * (Akolose 1:15) Cifukwa cina cimene Yesu alili wapamtima kwa Yehova n’cakuti ni yekhayo amene anamulenga mwacindunji, mosapitila mwa wina. Pa cifukwa cimeneci, Yesu amachedwa “Mwana wake wobadwa yekha.” (Yohane 3:16) Cinanso n’cakuti, ni Yesu yekha amene Yehova anamugwilitsila nchito kulenga zinthu zonse. (Akolose 1:16) Ndiponso, Yesu yekha ni amene amachedwa “Mau,” cifukwa Yehova anam’gwilitsila nchito kupeleka mauthenga ndi malangizo kwa angelo ndi anthu.—Yohane 1:14.

12. Tidziŵa bwanji kuti Yesu ndi Mulungu ni osiyana?

12 Pali anthu ena amene amakhulupilila kuti Yesu ndiye Mulungu amene. Koma si zimene Baibulo imatiphunzitsa. Iyo imatiuza kuti Yesu anacita kulengedwa, kutanthauza kuti anali ndi ciyambi. Koma Yehova amene analenga zinthu zonse analibe ciyambi, analiko nthawi zonse. (Salimo 90:2) Pokhala Mwana, Yesu sanaganizepo zofuna kulingana ndi Mulungu. Baibulo imatiphunzitsa momveka bwino kuti Atate ndi wamkulu kuposa Mwana. (Ŵelengani Yohane 14:28; 1 Akorinto 11:3.) Yehova yekha ndiye “Mulungu Wamphamvuyonse.” (Genesis 17:1) Iye ni wamkulu-kulu ndi wamphamvu kupambana wina aliyense.—Onani Zakumapeto 14.

13. N’cifukwa ciani Baibulo imati Yesu ni “cifanizilo ca Mulungu wosaonekayo”?

13 Asanalenge kumwamba ndi dziko lapansi, Yehova anagwila nchito pamodzi ndi Mwana wake, Yesu, kwa zaka mabiliyoni ambili. Ayenela kuti anali kukondana zedi! (Yohane 3:35; 14:31) Yesu anatengela makhalidwe a atate wake kwambili cakuti Baibulo imati iye ni “cifanizilo ca Mulungu wosaonekayo.”—Akolose 1: 15.

14. Zinacitika bwanji kuti mwana wokondedwa wa Mulungu abadwe monga munthu?

14 Mwana wapamtima wa Yehova ameneyu, anadzipeleka kucoka kumwamba ndi kudzabadwa monga munthu pa dziko lapansi. Zinacitika bwanji zimenezo? Mwa cozizwitsa, Yehova anasamutsa moyo wa Mwana wake kucoka kumwamba ndi kuuika m’mimba mwa namwali Mariya. Conco, Mariya anakhala ndi mimba popanda kugona ndi mwamuna. Mwa ici, Mariya anabala mwana wangwilo, ndipo anamucha Yesu.—Luka 1:30-35.

KODI YESU ANALI MUNTHU WABWANJI?

15. N’ciani cingakuthandizeni kumudziŵa bwino Yehova?

15 Ngati mufuna kudziŵa zambili za Yesu, umoyo wake, ndi makhalidwe ake, mukaŵelenge mabuku a m’Baibulo a Mateyu, Maliko, Luka, ndi Yohane. Mabuku anayi amenewa amachedwa Mauthenga Abwino. Cifukwa Yesu anatengela kwambili Atate wake, zimene mudzaŵelenga zidzakuthandizani kumudziŵa bwino Yehova. Ndiye cifukwa cake Yesu anakamba kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.”—Yohane 14:9.

16. Kodi Yesu anaphunzitsa ciani? Nanga zimene anali kuphunzitsa zinali kucokela kuti?

16 Anthu ambili anali kuitana Yesu kuti “Mphunzitsi.” (Yohane 1:38; 13:13) Cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili zimene Yesu anaphunzitsa anthu unali “uthenga wabwino wa Ufumu.” Kodi Ufumu umenewu n’ciani? Ni boma la Mulungu la kumwamba limene lidzalamulila dziko lonse lapansi ndi kudalitsa anthu amene amamvela Mulungu. (Mateyu 4:23) Zonse zimene Yesu anaphunzitsa zinacokela kwa Yehova. Yesu anati: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ni za amene anandituma.” (Yohane 7:16) Yesu anadziŵa kuti Yehova afuna kuti anthu amvele uthenga wabwino wakuti Ufumu wa Mulungu udzalamulila dziko lonse lapansi.

17. Kodi Yesu anali kuphunzitsa kuti? N’cifukwa ciani anali wolimbikila kuphunzitsa anthu?

17 Kodi Yesu anali kuphunzitsa kuti? Kulikonse kumene anali kupeza anthu, m’midzi, m’mizinda, pamaliketi, m’malo olambilila, ndi panyumba za anthu. Sanali kuyembekeza kuti anthu abwele kwa iye. Kaŵili-kaŵili anali kupita kuli anthu. (Maliko 6:56; Luka 19:5, 6) Yesu anali kugwila nchito molimbika, kutaila nthawi yambili pa kuphunzitsa anthu. Anali wolimbikila conco panchito cifukwa anali kudziŵa kuti n’zimene Mulungu afuna, ndipo cifukwa anali womvela kwa Atate wake. (Yohane 8:28, 29) Cinanso n’cakuti Yesu anali kumvelela anthu cifundo. (Ŵelengani Mateyu 9:35, 36.) Yesu anali kuona kuti abusa acipembedzo sanali kuphunzitsa anthu coonadi ca Mulungu ndi Ufumu wake. Conco anafuna kuthandiza anthu ambili kuti amvele uthenga wabwino.

18. Ni makhalidwe ati a Yesu amene akufikani pamtima?

18 Yesu anali munthu wokonda anthu ndi woganizila ena. Anali wokoma mtima ndi wosavuta kukamba naye. Ngakhale ana anali kukonda kuceza naye. (Maliko 10:13-16) Yesu analibe kondela ngakhale pang’ono. Ziphuphu, katangale, ndi kupotoza cilungamo zinali mdani kwa iye. (Mateyu 21:12, 13) Panthawiyo, akazi analibe ufulu m’zinthu zambili ndipo sanali kuŵelengeledwa kweni-kweni. Koma Yesu anali kulemekeza akazi nthawi zonse. (Yohane 4:9, 27) Analinso munthu wodzicepetsa kwambili. Mwacitsanzo, tsiku lina anasambika mapazi a atumwi ake. Koma imeneyi inali nchito ya kapolo.—Yohane 13:2-5, 12-17.

Yesu anali kulalikila kulikonse kumene anali kupeza anthu

19. Tidziŵa bwanji kuti Yesu anali kudziŵa bwino zosoŵa za anthu, ndipo anali wofunitsitsa kuwathandiza?

19 Yesu anali kudziŵa bwino zosoŵa za anthu, ndipo anali kuwathandiza. Zimenezi zinaonekela bwino pamene anagwilitsila nchito mphamvu ya Mulungu kucilitsa anthu. (Mateyu 14:14) Mwacitsanzo, munthu wakhate anabwela kwa Yesu ndi kum’pempha kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeletsa.” Yesu anacita cifundo poona mmene munthuyo anali kuvutikila. Conco Yesu anatambasula dzanja lake ndi kugwila munthu wakhate uja, ndi kukamba kuti: “Ndikufuna. Khala woyela.” Basi munthu uja anacila. (Maliko 1:40-42) Muganiza munthu uja anakondwela ndi kuyamikila? Ngako!

NTHAWI ZONSE ANALI WOKHULUPILIKA KWA ATATE WAKE

20, 21. N’cifukwa ciani Yesu ali citsanzo cabwino kopambana pankhani yomvela Mulungu?

20 Yesu ni citsanzo cabwino koposa pankhani yomvela Mulungu. Zivute zitani, kaya adani ake amucitile zoipa bwanji, Yesu sanagwedezeke pa kukhulupilika kwa Atate wake. Mwacitsanzo, Satana anayesa-yesa kuti amucimwitse, koma Yesu sanagonje. (Mateyu 4:1-11) Panthawi ina, ngakhale abululu ŵake ena sanali kukhulupilila kuti anali Mesiya. Mpaka anafika pokamba kuti “wacita misala.” Koma Yesu sanabwelele m’mbuyo pa nchito ya Mulungu. (Maliko 3:21) Ngakhale pamene adani ake anamucitila nkhanza, Yesu anakhalabe nga nga nga kwa Mulungu, ndipo sanawabwezele.—1 Petulo 2:21-23.

21 Ngakhale pamene Yesu anayang’anizana ndi imfa yozunza ndi yoŵaŵa, sanataye cikhulupililo cake kwa Yehova. (Ŵelengani Afilipi 2:8.) Gaganizani cabe unkhalwe umene anapilila patsiku limene anaphedwa. Adani ake kum’manga, mboni zonama kumunamizila kuti ananyoza Mulungu, oweluza acinyengo kumugamulila cilango ca kuphedwa, khamu la anthu aciwawa kumuseka ndi kumutonza, asilikali kumuzunza ndi kum’pacika mwa kumukhomelela misomali pamtengo. Pamene anali kutsilizika, iye anafuula kuti: “Ndakwanilitsa cifunilo canu!” (Yohane 19:30) Patapita masiku atatu, Yehova anamuukitsa ndi kum’patsa thupi lamzimu. (1 Petulo 3:18) Pambuyo pa milungu yoŵelengeka, Yesu anabwelela kumwamba ndipo “anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu,” kuyembekezela kuti Yehova akam’patse Ufumu.—Aheberi 10:12, 13.

22. Ni mwayi wanji umene tili nawo cifukwa ca kukhulupilika kwa Yesu?

22 Cifukwa cakuti Yesu anakhalabe wokhulupilika kwa Atate wake, ife lomba tili ndi ciyembekezo ca moyo wamuyaya m’paradaiso. Ndico cinali colinga ca Yehova kucokela paciyambi. Ndiye cifukwa cake m’nkhani yotsatila, tidzaphunzila mmene imfa ya Yesu inatipatsila mwayi wodzakhala ndi moyo wamuyaya.

^ ndime 11 Yehova ni Atate wathu cifukwa ndiye anatilenga. (Yesaya 64:8) Yesu ni Mwana wa Mulungu cifukwa nayenso ni Yehova anam’lenga. Angelo nawo, ngakhale Adamu, amachedwa ana a Mulungu.—Yobu 1:6; Luka 3:38.