Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 5

Dipo Ndiyo Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse

Dipo Ndiyo Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse

1, 2. (a) Ni mphatso yanji imene imakhala ya mtengo wapatali kwa inu? (b) Dipo ni mphatso ya mtengo wapatali yocokela kwa Mulungu. Cifukwa ciani?

KODI munalandilapo mphatso imene inakugwilani mtima kwambili? Mphatso sifunika kucita kukhala yodula kuti mukondwele nayo. Ngati mphatso mwaikonda, ndipo mwaona kuti idzakuthandizani, mumakondwela ndi kuyamikila amene wakupatsani.

2 Pa mphatso zonse zimene Mulungu watipatsa, pali imodzi yopambana zonse. Imeneyo ndiye mphatso yofunika kwambili imene Mulungu anapatsa anthu. M’nkhani ino, tidzaphunzila kuti Yehova anatumiza Mwana wake, Yesu Khiristu, kuti ife tikapeze moyo wosatha. (Ŵelengani Mateyu 20:28.) Yehova potumiza Mwana wake kudzatifela monga dipo, anaonetsa kuti amatikonda kwambili.

KODI DIPO N’CIANI?

3. N’cifukwa ciani ife anthu timafa?

3 Dipo ni njila imene Yehova anagwilitsila nchito kumasula anthu ku ucimo ndi imfa. (Aefeso 1:7) Kuti timvetsetse cifukwa cake dipo linakhala lofunikila, tiyenela kudziŵa zimene zinacitika m’munda wa Edeni kale-kale. Makolo athu oyambilila Adamu ndi Hava anacimwa. Ndipo anafa cifukwa ca kucimwa kwawo. Nafenso timafa cifukwa tinatengela ucimo kwa iwo.—Onani Zakumapeto 9.

4. Kodi Adamu anali ndani? Nanga anali anapatsidwa ciani?

4 Pamene Yehova analenga munthu woyamba, Adamu, anam’patsa cinthu cina ca mtengo wapatali kwambili. Anam’patsa moyo wangwilo. Adamu anali ndi maganizo angwilo ndi thupi langwilo. Sanali kudwala, conco sakanakalamba ndi kufa. Yehova anali tate kwa Adamu cifukwa ndiye anam’lenga. (Luka 3:38) M’pake kuti Yehova anali kukambitsana ndi Adamu nthawi zonse. Anali kuuza Adamu zoyenela kucita, ndipo anam’patsa nchito yokondweletsa.—Genesis 1:28-30; 2:16, 17.

5. Kodi Baibulo imatanthauzanji pamene imati Adamu analengedwa “m’cifanizilo ca Mulungu”?

5 Adamu analengedwa “m’cifanizilo ca Mulungu.” (Genesis 1:27) Ici citanthauza kuti Yehova polenga Adamu, anaika mwa iye makhalidwe ena ofanana ndi ake. Makhalidwe amenewo ni cikondi, nzelu, cilungamo, ndi mphamvu. Koma anamupatsanso ufulu wosankha zimene afuna. Adamu sanali monga makina amene amangocita zinthu osaganiza, kapena ciloboti. Mulungu anam’lenga ndi ufulu wosankha kucita cabwino kapena coipa. Sembe Adamu anasankha kumvela Mulungu, akanakhala ndi moyo kwamuyaya m’Paradaiso.

6. Kodi Adamu anataya ciani pamene anapandukila Mulungu? Nanga cinacitika kwa ife n’ciani cifukwa ca zimenezi?

6 Cifukwa cakuti Adamu sanamvele Mulungu anaweluzidwa kuti adzafa. Anataya zinthu za mtengo wapatali kwambili: unansi wake wapadela ndi Yehova, moyo wake wangwilo, ndi Paradaiso. (Genesis 3:17-19) Adamu ndi Hava anacita kusankha kuti apandukile Mulungu. Ndiye cifukwa cake kwa iwo kube ciyembekezo ciliconse. Ndipo cifukwa ca zimene Adamu anacita, ucimo unaloŵa m’dziko kupitila mwa munthu mmodzi, ndi imfa kupitila mwa ucimo, conco imfa inafalikila kwa anthu onse, ndipo anthu onse anakhala ocimwa. (Aroma 5:12) Adamu atacimwa, “anadzigulitsa” yekha, ndipo anagulitsanso ife tonse kukhala akapolo ku ucimo ndi imfa. (Aroma 7:14) Nanga ife, kodi tili ndi ciyembekezo cokamasuka ku ukapolo umenewu? Inde cilipo.

7, 8. Kodi dipo n’ciani?

7 Kodi dipo n’ciani? Dipo limatanthauza zinthu ziŵili. Coyamba, dipo ni malipilo amene amapelekedwa kuombola munthu kapena cinthu cinacake. Caciŵili, dipo ni malipilo okwanila pa mtengo wa cinthu cimene cinataika kapena kuwonongeka.

8 Palibe munthu amene akanakwanitsa kulipillila zimene Adamu anawononga pamene anacimwa ndi kubweletsa imfa. Koma Yehova anakonza njila yotiwombolela ku ucimo ndi imfa. Lomba tiyeni tione mmene dipo limagwilila nchito ndi mmene lingatipindulitsile.

MMENE YEHOVA ANAPELEKELA DIPO

9. Kodi panafunikila dipo la mtundu wanji?

9 Pakati pa ife anthu ocimwa, palibe aliyense amene akanakwanitsa kupeleka dipo lolipilila moyo wangwilo umene Adamu anataya. (Salimo 49:7, 8) Dipo limene linafunikila ni moyo wangwilo wolingana ndi umene Adamu anataya. Ndiye cifukwa cake limachedwa “dipo lokwanila ndendende,” kapena kuti dipo lolingana.—1 Timoteyo 2:6.

10. Kodi Yehova anacita ciani kuti apeleke dipo?

10 Kodi Yehova anacita ciani kuti apeleke dipo? Anatumiza pa dziko lapansi Mwana wake wokondedwa. Mwana ameneyo ni Yesu, ndipo ndiye anali woyamba kulengedwa. (1 Yohane 4:9, 10) Yesu anali wokonzeka kusiya Atate wake kumwamba ndi kubwela pa dziko lapansi. (Afilipi 2:7) Yehova anasamutsa moyo wa Yesu kucoka kumwamba kubwela pa dziko lapansi, ndiyeno Yesu anabadwa monga munthu wangwilo, wopanda ucimo.—Luka 1:35.

Yehova anapeleka Mwana wake wokondedwa monga dipo lotiwombola

11. Kodi dipo la munthu mmodzi linakwanitsa bwanji kuwombola anthu onse?

11 Pamene munthu woyamba, Adamu, anapandukila Yehova, anataila anthu onse moyo wangwilo. Kodi alipo wina aliyense amene akanakwanitsa kucotsa imfa kwa ana a Adamu? Inde alipo. (Ŵelengani Aroma 5:19.) Ameneyo ni Yesu. Iye analibe ucimo, ndipo anapeleka moyo wake wangwilo monga dipo. (1 Akorinto 15:45) Moyo wake wangwilo unali ndi mphamvu yocotsa imfa kwa ife tonse ana a Adamu.—1 Akorinto 15:21, 22.

12. N’cifukwa ciani Yesu analola kuti avutike conco?

12 Baibulo imafotokoza mmene Yesu anazunzikila asanafe. Anam’kwapula mwankhanza ndi kum’khomelela pa mtengo, cakuti anafa imfa ya pang’ono-pang’ono yoŵaŵa koopsa. (Yohane 19:1, 16-18, 30) Koma n’cifukwa ciani Yesu analola kuvutika conco? Cifukwa Satana anatsutsa Mulungu kuti palibe munthu amene angakhulupilike kwa Iye ngati akumana ndi ciyeso coŵaŵa. Conco, Yesu anafuna kuonetsa kuti munthu wangwilo akhoza kukhulupilika kwa Mulungu ngakhale avutike bwanji, ndipo anakwanitsa kucita zimenezo. Ganizani cabe mmene Yehova anamunyadila Yesu!—Miyambo 27:11; onani Zakumapeto 15.

13. Kodi dipo linapelekedwa bwanji?

13 Kodi dipo linapelekedwa bwanji? Yesu anapatsa Atate wake mtengo wa moyo wake. Anacita bwanji zimenezi? M’caka ca 33 pa Nisani 14, Yehova analola kuti adani amuphe Yesu. (Aheberi 10:10) Patapita masiku atatu, Yehova anaukitsa Yesu monga munthu wamzimu. Ndiyeno pambuyo pake, Yesu anabwelela kwa Atate wake kumwamba. M’pamene anapeleka mtengo wa moyo wake wangwilo kwa Yehova monga dipo. (Aheberi 9:24) Motelo, cifukwa ca dipo limene Yesu anapeleka, tili ndi mwayi womasulidwa ku ucimo ndi imfa.—Ŵelengani Aroma 3:23, 24.

KODI DIPO LIMATIPINDULITSA BWANJI?

14, 15. N’ciani cimene tiyenela kucita kuti macimo athu akhululukidwe?

14 Tinayamba kale kupindula ndi mphatso ya dipo. Tiyeni tione mapindu a pali pano, ndi a mtsogolo.

15 Mulungu amatikhululukila macimo athu. Ife anthu cimativuta kucita zabwino nthawi zonse. Timalakwa, ndipo nthawi zina timacita zinthu zoipa, kapena kutaya m’kamwa. (Akolose 1:13, 14) Kodi cofunika n’ciani kuti Mulungu atikhululukile? Tiyenela kulapa macimo athu, ndi kupempha Yehova modzicepetsa kuti atikhululukile. Tikacita zimenezi, tisakaikile kuti macimo athu akhululukidwa.—1 Yohane 1:8, 9.

16. N’ciani cofunika kuti tikhale ndi cikumbumtima coyela?

16 Tikhoza kukhala ndi cikumbumtima coyela. Cikumbumtima cathu cikatiuza kuti tacita cinthu coipa, timadziimba mlandu, kutaya mtima, ngakhale kudzimva wopanda pake. Koma tisalefuke. Tikapemphela kwa Yehova kuti atikhululukile, amamvela ndipo amatikhululukila. (Aheberi 9:13, 14) Yehova amafuna kuti tizimuuza mavuto athu ndi zofooka zathu zonse. (Aheberi 4:14-16) Pamenepo timakhala pa mtendele ndi Mulungu.

17. Kodi tidzapeza madalitso anji cifukwa ca imfa ya Yesu?

17 Tili ndi ciyembekezo ca moyo wamuyaya. Baibulo imati: “Malipilo a ucimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khiristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Cifukwa Yesu anatifela, tili ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wamuyaya ndi thanzi labwino. (Chivumbulutso 21:3, 4) Koma tiyenela kucitanji kuti tikalandile madalitso amenewo?

KODI MUDZAILANDILA MPHATSO YA DIPO?

18. Tidziŵa bwanji kuti Yehova amatikonda?

18 Kodi sim’mayamikila mumtima mwanu ngati munthu wina wakupatsani mphatso yabwino? Dipo ndiyo mphatso ya mtengo wapatali kupambana iliyonse, ndipo tiyenela kuyamikila Yehova. Pa Yohane 3:16 pamati: “Pakuti Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha.” Zoona, Yehova amatikonda kwambili, cakuti anatipatsa Yesu, Mwana wake wokondedwa. Ndipo timadziŵa kuti Yesu naye amatikonda, cifukwa anavomela kudzatifela. (Yohane 15:13) Cifukwa ca mphatso ya dipo, muyenela kuvomeleza ndi mtima wonse kuti Yehova ndi Yesu, amakukondani kwambili.—Agalatiya 2:20.

Mukapitiliza kuphunzila za Yehova, mudzakhala bwenzi lake, ndipo cikondi canu pa iye cidzakulilako-kulilako

19, 20. (a) Mufunika kucita ciani kuti mukhale bwenzi la Yehova? (b) Nanga mungaonetse bwanji kuti munailandila ndi mtima wonse nsembe ya Yesu?

19 Popeza lomba mwadziŵa kuti Mulungu ni wa cikondi cacikulu, kodi mungacite ciani kuti mukhale bwenzi lake? N’cinthu covuta kukonda munthu amene simudziŵa. Pa Yohane 17:3, Baibulo imakamba kuti tifunika kum’dziŵa Yehova. Mukacita zimenezo, cikondi canu pa iye cidzakula, mudzayamba kucita zinthu zimene iye afuna. Pamenepo mudzakhala bwenzi lake. Conco, osaleka kuphunzila Baibulo kuti mum’dziŵe bwino Yehova.—1 Yohane 5:3.

20 Ilandileni ndi mtima wonse nsembe ya Yesu. Baibulo imatiuza kuti: “Iye wokhulupilila mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:36) Kodi kukhala ndi cikhulupililo kumatanthauza ciani? Kumatanthauza kucita zimene Yesu anatiphunzitsa. (Yohane 13:15) Kungokamba cabe pakamwa kuti timakhulupilila Yesu sikokwanila. Tiyenela kucitapo kanthu. Pa Yakobo 2:26, Baibulo imakamba kuti: “Cikhulupililo copanda nchito zake ndi cakufa.”

21, 22. (a) N’cifukwa ciani tifunika kupezeka pa Cikumbutso ca imfa ya Khiristu caka ndi caka? (b) Tidzakambilana ciani m’Nkhani 6 ndi 7?

21 Muzipezeka pa cikumbutso ca imfa ya Khiristu. Usiku wakuti Yesu aphedwa maŵa, analamula kuti tizicita cikumbutso ca imfa yake. Caka ndi caka, timacita mwambo umenewu wa Cikumbutso, kapena Mgonelo wa Ambuye. (1 Akorinto 11:20; Mateyu 26:26-28) Yesu amafuna kuti tizikumbukila kuti anapeleka moyo wake wangwilo monga dipo lotiwombola. Iye anati: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.” (Ŵelengani Luka 22:19.) Mukapezeka pa Cikumbutso, mumaonetsa kuti mumakumbukila dipo, ndi cikondi cacikulu cimene Yehova ndi Yesu ali naco pa ife.—Onani Zakumapeto 16.

22 Dipo ndiyo mphatso yopambana iliyonse imene tingalandile. (2 Akorinto 9:14, 15) Mphatso imeneyi idzapindulitsanso ngakhale anthu ambili amene ali kumanda. M’Nkhani 6 ndi 7 tidzakambilana mmene zidzacitikila.